Malembo Oyera
Alima 52


Mutu 52

Amoroni alowa m’malo mwa Amalikiya ngati mfumu ya Alamani—Moroni, Teyankumu, ndi Lehi atsogolera Anefi mu nkhondo yachipambano motsutsana ndi Alamani—Mzinda wa Muleki ulandidwanso, ndipo Yakobo M’zoramu aphedwa. Mdzaka dza pafupifupi 66–64 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo tsopano, zidachitika m’chaka cha makumi awiri ndi zisanu n’chimodzi cha ulamuliro wa oweruza pa anthu a Nefi, taonani, pamene Alamani adadzuka pa m’mawa oyambilira wa mwezi oyamba, taonani, iwo adapeza Amalikiya atamwalira mu hema lake; ndiponso adaona kuti Teyankumu adali wokonzeka kumenyana nawo tsiku limenelo.

2 Ndipo tsopano, pamene Alamani adaona izi iwo adachita mantha; ndipo adasiya madongosolo awo ogubila ku dziko lakumpoto, ndi kuthawira ndi ankhondo awo onse ku mzinda wa Muleki, ndipo adafuna chitetezo mu malinga awo.

3 Ndipo zidachitika kuti m’bale wa Amalikiya adasankhidwa kukhala mfumu pa anthuwo; ndipo dzina lake lidali Amoroni; motero mfumu Amoroni, m’bale wa mfumu Amalikiya, adasankhidwa kulamulira m’malo mwake.

4 Ndipo zidachitika kuti iye adalamula kuti anthu ake asamalire mizinda imeneyo, imene iwo adatenga mwakukhetsa mwazi; pakuti iwo sadatenge mizindayo popanda kukhetsa mwazi wochuluka.

5 Ndipo tsopano, Teyankumu adaona kuti Alamani adatsimikizika kusunga mizinda imeneyo imene iwo adatenga, ndi mbali za dziko zimene iwo adalanda; ndiponso poona kukula kwa chiwerengero chawo, Teyankumu adaganiza kuti sikudali koyenera kuti ayesere kuwaukira iwo mu malinga awo.

6 Koma iye adasunga anthu ake mozungulira, ngati kuti akupanga zokonzekera ku nkhondo; inde, ndipo zoona iye adali kukonzekera kudziteteza motsutsana nawo, pokweza makoma mozungulira ndi kukonzekeretsa malo othawirako.

7 Ndipo zidachitika kuti iye adapitilira kukonzekera nkhondoyo kufikira Moroni adatumiza gulu la anthu kuti alimbikitse ankhondo ake.

8 Ndipo Moroni adatumizanso malamulo kwa iye kuti asunge akaidi onse amene adagwa m’manja mwake; pakuti monga Alamani adatenga akaidi ambiri, kuti ye abwenzeretse akaidi ake onse Achilamani ngati dipo la iwo amene Alamani adatenga.

9 Ndipo iye adatumizanso malamulo kwa iye kuti alimbitse dziko la Chuluka, ndi kusunga kanjira kakang’ono kamene kamalowa m’dziko la ku mpoto, kuopa Alamani angapeze polowera ndi kukhala ndi mphamvu zowasautsira iwo kumbali zonse.

10 Ndipo Moroni adatumizanso kwa iye, kufuna iye kuti akhale wokhulupirika posamalira gawo ili la dzikolo, ndipo kuti iye afufuze mwayi uliwonse kuti akanthe Alamani m’chigawo chimenechi, monga mwa kuchuluka kwa mphamvu zake, kuti mwina iye angathe kutenganso mwa njira imeneyo kapena njira ina mizinda imeneyo yomwe idatengedwa m’manja mwawo; ndipo kuti iye akalimbitsa ndi kukhwimitsa mizinda yozungulira, imene siidagwe m’manja mwa Alamani.

11 Ndipo iye adatinso kwa iye, ndikadabwera kwa iwe, koma taona, Alamani ali pa ife m’malire a dziko chakumadzulo a nyanja; ndipo taona, ine ndipita kukamenyana nawo, kotero sindingathe kubwera kwa iwe.

12 Tsopano, mfumu (Amoroni) idali itachoka ku dziko la Zarahemula, ndipo idali itadziwitsa mfumukazi zokhudzana ndi imfa ya m’bale wake, ndipo adasonkhanitsa pamodzi gulu lalikulu la anthu, ndi kugubira kwa Anefi chakumalire ndi nyanja yakumadzulo.

13 Ndipo motero iye adayesera kuzunza Anefi, ndi kuthamangitsa gawo la ankhondo awo kumbali imeneyo ya dzikolo, pamene iye adalamula iwo amene adawasiya kuti atenge mizinda imene iye adalanda, kuti iwonso akavutitse Anefi cha kumalire kwa nyanja yakum’mawa, ndipo atenge dziko lawo monga mwa mphamvu zawo, molingana ndi mphamvu za adani awo.

14 Ndipo motero Anefi adali mu zochitika zoopsya zotero kumapeto kwa chaka cha makumi awiri ndi zisanu n’chimodzi cha ulamuliro wa oweruza pa anthu a Nefi.

15 Koma taonani, zidachitika mu chaka cha makumi awiri ndi zisanu n’chiwiri cha ulamuliro wa oweruza, kuti Teyankumu, molamulidwa ndi Moroni—amene adakhazikitsa ankhondo kuti ateteze malire a ku’mmwera ndi kumadzulo kwa dzikolo, ndipo adayamba kugubira ku dziko la Chuluka, kuti akathandizire Teyankumu ndi anthu ake potenganso mizinda imene iwo adalandidwa—

16 Ndipo zidachitika kuti Teyankumu adalandira malamulo kuti awukire pa mzinda wa Muleki, ndi kuwutenganso ngati kudali kotheka.

17 Ndipo zidachitika kuti Teyankumu adapanga zokonzekera kukawukira pa mzinda wa Muleki, ndipo adagubira ndi ankhondo ake motsutsana ndi Alamani; koma iye adaona kuti kudali kosatheka kuti akadawagonjetsa iwo pamene adali m’malinga awo; kotero iye adasiya malingaliro ake ndi kubweleranso ku dziko la Chuluka, kukadikira kubwera kwa Moroni, kuti athe kulandira mphamvu kwa ankhondo ake.

18 Ndipo zidachitika kuti Moroni adafika ndi ankhondo ake ku dziko la Chuluka, chakumapeto kwa chaka cha makumi awiri ndi chisanu n’chiwiri cha ulamuliro wa oweruza pa anthu a Nefi.

19 Ndipo chakumayambiliro kwa chaka cha makumi awiri ndi chisanu n’chitatu, Moroni ndi Teyankumu ndi ambiri mwa akulu ankhondo adakhala ndi zokambirana za nkhondo—zomwe angathe kuchita kuti apangitse Alamani kuti abwere kudzamenyana nawo kunkhondo; kapena kuti athe kudzera m’njira ina yowanyengelera iwo kutuluka kumalinga awo, kuti iwo athe kupeza mwayi pa iwo ndi kutenganso mzinda wa Muleki.

20 Ndipo zidachitika kuti adatumiza akazembe kwa ankhondo Achilamani, amene ankateteza mzinda wa Muleki, kwa mtsogoleri wawo, amene dzina lake lidali Yakobo, kufuna iye kuti atuluke ndi ankhondo ake kukakumana nawo pa chigwa chapakati pa mizinda iwiriyo. Koma taonani, Yakobo, amene adali M’zoramu sadatuluke ndi ankhondo ake kukakumana pa chigwapo.

21 Ndipo zidachitika kuti Moroni, pokhala opanda chiyembekezo chokumana nawo pazifukwa zabwino, kotero, iye adaganiza dongosolo lofuna kuwanyengelera Alamani kutuluka m’malinga awo

22 Kotero iye adachititsa kuti Teyankumu atenge kagulu kochepa ka anthu ake ndi kugubira kufupi ndi gombe la nyanja; ndipo Moroni ndi ankhondo ake, pa usiku, adagubira ku chipululu, chakumadzulo kwa mzinda wa Muleki; ndipo motero, m’mawa mwake, pamene alonda Achilamani adamuzindikira Teyankumu, adathamanga ndi kukauza Yakobo, mtsogoleri wawo.

23 Ndipo zidachitika kuti ankhondo Achilamani adaguba kupita kukamenyana ndi Teyankumu, poganizira mwa kuchuluka kwa chiwerengero chawo kuti angagonjetse Teyankumu chifukwa cha kuchepa kwa chiwerengero chake. Ndipo pamene Teyankumu adaona ankhondo Achilamani akubwera motsutsana naye, iye adayamba kuthawira chaku gombe lanyanja, chakumpoto.

24 Ndipo zidachitika kuti pamene Alamani adaona kuti iye wayamba kuthawa, adalimba mtima ndikuyamba kuwathamangitsa mwamphamvu. Ndipo pamene Teyankumu adali kuwatsogolera kutali Alamani amene adali kuwathamangitsa iwo pachabe, taonani, Moroni adalamula kuti gawo lina la ankhondo ake amene adali naye agubire kumzindawo ndi kukaulanda.

25 Ndipo motero iwo adachita, ndi kupha iwo amene adasiyidwa kuti ateteze mzindawo, inde, onse amene sadapereke zida zawo zankhondo.

26 Ndipo motero Moroni adalanda mzinda wa Muleki ndi gawo la ankhondo ake, pamene iye adagubira ndi otsalirawo kukakumana ndi Alamani pamene adali kubwelera kothamangitsa Teyankumu.

27 Ndipo zidachitika kuti Alamani adamthamangitsa Teyankumu kufikira iye adafika kufupi ndi mzinda wa Chuluka, ndipo kenako adakumanizana ndi Lehi ndi ankhondo ake ochepa, amene adasiyidwa kuti ateteze mzinda wa Chuluka.

28 Ndipo tsopano, pamene wamkulu wa ankhondo Achilamani adaona Lehi ndi ankhondo ake akubwera motsutsana nawo, iwo adathawa muchisokonezo chachikulu, kuopa kuti mwina sangatenge mzinda wa Muleki Lehi asadawapambane; pakuti iwo adali atatopa chifukwa cha kuguba kwawo, ndipo anthu a Lehi adali asadatope.

29 Tsopano Alamani sadadziwe kuti Moroni adali kumbuyo kwawo ndi ankhondo ake; ndipo onsewo chimene iwo ankaopa adali Lehi ndi anthu ake.

30 Tsopano Lehi sankafuna kuti awapambane iwo mpaka atakumana ndi Moroni ndi ankhondo ake.

31 Ndipo zidachitika kuti Alamani asadathawire patali adazungulilidwa ndi Anefi, ndi anthu a Moroni kumbali imodzi, ndi anthu a Lehi kumbali inayi, onse amene adali osatopa ndi odzadza nyonga; koma Alamani adali otopa chifukwa chakutalika kwa kuguba kwawo.

32 Ndipo Moroni adalamula anthu ake kuti agwe pa iwo kufikira atule pansi zida zawo zankhondo.

33 Ndipo zidachitika kuti Yakobo, pokhala mtsogoleri wawo, pokhalanso Mzoramu, ndipo okhala ndi mzimu osagonjetseka, adatsogolera Alamani kunkhondo ndi ukali wochuluka motsutsana ndi Moroni.

34 Moroni pokhala mkati mwa ogubawo, kotero Yakobo adatsimikizika kuwapha ndi kudula njira yake kulowera ku mzinda wa Muleki. Koma taonani, Moroni ndi anthu ake adali ndi mphamvu zambiri; kotero sadapereke njira pamaso pa Alamani.

35 Ndipo zidachitika kuti adamenyana ku mbali zonse ndi ukali wochuluka; ndipo kudali ophedwa ambiri mbali zonse; inde, ndipo Moroni adavulazidwa ndipo Yakobo adaphedwa.

36 Ndipo Lehi adawakankhira kumbuyo ndi ukali wotere ndi anthu ake amphamvu, mpaka Alamani akumbuyo kwawo adapereka zida zawo zankhondo; ndipo otsalira a iwo, pokhala osokonezeka kwambiri, sadadziwe kolowera kapena komenya.

37 Tsopano Moroni poona kusokonezeka kwawo, iye adati kwa iwo: Ngati mutabweretse zida zanu zankhondo ndi kuzipereka, taonani ife tidzasiya kukhetsa mwazi wanu.

38 Ndipo zidachitika kuti pamene Alamani adamva mawu amenewa, akulu awo ankhondo, onse amene sadaphedwe, adabwera ndi kuponya zida zawo zankhondo pamapazi a Moroni, ndiponso kulamula anthu awo kuti achite chimodzimodzi.

39 Koma taonani, padali ambiri amene sadafune; ndipo iwo amene sadapereke malupanga awo adatengedwa ndi kumangidwa, ndipo zida zawo zankhondo zidalandidwa kwa iwo, ndipo adakakamizidwa kuguba pamodzi ndi abale awo kupita mu mzinda wa Chuluka.

40 Ndipo tsopano chiwerengero cha akaidi amene adatengedwa chidapamba kwambiri chiwerengero cha iwo amene adaphedwa, inde, kuposera iwo amene adaphedwa kumbali zonse ziwiri.

Print