Malembo Oyera
Alima 49


Mutu 49

Alamani aupandu alephera kutenga mizinda yotchingidwa ndi mipanda yolimba ya Amoniha ndi Nowa—Amalikiya atembelera Mulungu ndipo alumbira kumwa mwazi wa Moroni—Helamani ndi abale ake apitiriza kulimbitsa mpingo. Mdzaka dza pafupifupi 72 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo tsopano zidachitika kuti mu mwezi wa khumi ndi umodzi wa m’chaka cha khumi ndi chisanu ndi chinayi, pa tsiku la khumi la mweziwo, ankhondo achilamani adaonedwa akuyandikira dziko la Amoniha.

2 Ndipo taonani, mzindawo udali utamangidwanso, ndipo Moroni adaika gulu la ankhondo cha kumalire a mzindawo, ndipo iwo adali ataponya dothi mozungulira kuti adziteteze ku mivi ndi miyala ya Alamani; pakuti taonani, iwo adamenya ndi miyala ndi mivi.

3 Taonani, ndanena kuti mzinda wa Amoniha udamangidwanso. Ndikunena kwa inu, inde, kuti mbali ina idamagwidwanso ya m’zigawo, ndipo chifukwa Alamani adauwonongapo chifukwa cha kusaweruzika kwa anthu, iwo adaganiza kuti ukhalanso osavuta kwa iwo kuugonjetsa.

4 Koma taonani, kudali kwakukulu bwanji kukhumudwa kwawo, pakuti taonani, Anefi adakumba chimulu cha dothi chozungulira iwo, chimene chidali chachitali kwambiri mwakuti Alamani sakadatha kuponya miyala yawo ndi mivi yawo kwa iwo kuti zikagwire ntchito, ngakhale kutha kubwera kwa iwo kupatula kudzera pamalo polowera pawo.

5 Tsopano pa nthawi imeneyi mkulu wa ankhondo wa Alamani adazizwa kwambiri, chifukwa cha nzeru za Anefi pokonza malo awo a chitetezo.

6 Tsopano atsogoleri a Alamani adaganiza, chifukwa cha kuchuluka kwa chiwerengero chawo, inde, iwo adaganiza kuti adali ndi mwayi obwera pa iwo monga m’mene adachitira kufikira tsopano; inde, ndipo iwo adadzikonzeranso ndi zishango, ndi zapachifuwa; ndiponso adadzikonzera zovala za zikopa, inde, zovala zokhuthala kuti aveke umaliseche wawo.

7 Ndipo pokhala okonzeka motere iwo adaganiza kuti ayenera kuwagonjetsa mosavuta ndi kuwaika abale awo mu goli la ukapolo, kapena kuwapha ndi kuwasakaza molingana ndi kufuna kwawo.

8 Koma taonani, mkudabwitsika kwawo kwakukulu, iwo adali atawakonzekera, mu njira imene idali isadadziwikepo pakati pa ana a Lehi. Tsopano iwo adakonzekera Alamani, kuti amenyane potsatira njira ya malangizo a Moroni.

9 Ndipo zidachitika kuti Alamani, kapena Aamalikiya, adali ozizwa kwambiri pa njira yawo yokonzekera pa nkhondo.

10 Tsopano, ngati mfumu Amalikiya akadabwera ku dziko la Nefi, patsogolo pa ankhondo ake, mwinamwake akadachititsa kuti Alamani athire nkhondo Anefi pa mzinda wa Amoniha; pakuti taonani, iye sankasamala za mwazi wa anthu ake.

11 Koma taonani, Amalikiya sadabwere nawo kunkhondo. Ndipo taonani, wamkulu wa ankhondo ake sadayerekeze kuthira nkhondo Anefi pa mzinda wa Amoniha, pakuti Moroni adali atasintha machitidwe a zochitika pakati pa Anefi, kotero kuti Alamani adakhumudwitsidwa mu malo awo othawira ndipo sakadatha kubwera pa iwo.

12 Kotero iwo adathawira mu chipululu, ndi kutenga msasa wawo ndikugubira kufupi ndi ndi dziko la Nowa, poganiza kuti kumeneko kukhala malo abwino otsatira kuti abwere kukamenya nkhondo ndi Anefi.

13 Pakuti iwo sadadziwe kuti Moroni adali atatchinga, kapena adali atamanga malinga achitetezo, pa mzinda uliwonse mu dziko lonse lozungulira; kotero, iwo adagubira ku dziko la Nowa ndi kutsimikizika mtima; inde, akulu ankhondo awo adabwera patsogolo ndi kutenga lumbiro kuti adzawononga anthu amumzindawo.

14 Koma taonani, mkudabwitsika kwawo, mzinda wa Nowa, umene udali malo ofooka kufikira tsopano, udali tsopano, mwa njira ya Moroni, utakhala wamphamvu, inde, ngakhale kuposera mphamvu za mzinda wa Amoniha.

15 Ndipo tsopano, taonani, izi zidali nzeru mwa Moroni; pakuti iye adaganiza kuti iwo adzaopsezedwa ku mzinda wa Amoniha; ndipo monga mzinda wa Nowa kufikira tsopano udali chigawo chofooketsetsa cha dzikolo, kotero iwo adzaguba kumeneko kudzamenyana, ndipo motero zidali molingana ndi zokhumba zake.

16 Ndipo taonani, Moroni adasankha Lehi kukhala mkulu wa ankhondo pa anthu a mzindawo; ndipo adali Lehi yemweyo amene adamenyana ndi Alamani mu chigwa cha kum’mawa kwa mtsinje wa Sidoni.

17 Ndipo tsopano taonani zidachitika, kuti pamene Alamani adapeza kuti Lehi akulamulira mzindawo adali okhumudwa kachiwiri, pakuti iwo adamuopa Lehi kwambiri; komabe akulu a ankhondo awo adalumbira ndi lumbiro lowukira mzindawo; kotero, iwo adabweretsa ankhondo awo.

18 Tsopano taonani, Alamani sakadatha kulowa mu malinga achitetezo awo mwa njira ina iliyonse kupatula kudzera polowera, chifukwa cha kutalika kwa chimzere chimene chidakwezedwa, ndi kuya kwa dzenje lake limene lidakumbidwa mozungulira, pokhapokha kudzera polowerapo.

19 Ndipo motero Anefi adali okonzekera kuwononga onse otero amene angayesere kukwera kuti alowe mu linga mu njira iliyonse, poponya miyala ndi mivi kwa iwo.

20 Motero iwo adakonzekera, inde, gulu la anthu awo amphamvu kwambiri, ndi malupanga awo, ndi malegeni awo, kukantha onse amene angayesere kulowa mu malo awo a chitetezo pakhomo polowera; ndipo choncho adali okonzekera kudziteteza motsutsana ndi Alamani.

21 Ndipo zidachitika kuti akulu a ankhondo a Alamani adabweretsa ankhondo awo pafupi ndi malo olowera, ndipo adayamba kulimbana ndi Anefi, kuti alowe mu malo awo achitetezo; koma taonani, iwo adathamangitsidwa m’mbuyo kuchokera ku nthawi ndi nthawi, kufikira kuti iwo adaphedwa ndi kuphedwa kwakukulu.

22 Tsopano pamene iwo adapeza kuti sakadatha kupeza mphamvu pa Anefi pakhomopo, iwo adayamba kukumba mizere yawo ya dothi kuti athe kupeza njira ya ankhondo awo, kuti akhonze kukhala ndi mwayi ofanana wakumenyana; koma taonani, mu kuyesera kumeneku iwo adasesedwa ndi miyala ndi mivi imene imaponyedwa kwa iwo; ndipo m’malo mwa kudzadzitsa ngalande zawo pogwetsa mizere ya dothi, adadzadzidwa mu mlingo wake ndi anthu akufa ndi matupi ovulala.

23 Motero Anefi adali ndi mphamvu pa adani awo; ndipo motero Alamani adayesera kuti awononge Anefi mpaka akulu awo ankhondo onse adaphedwa; inde, ndipo oposera chikwi achilamani adaphedwa; pamene, ku mbali inayi, kudalibe munthu ngakhale m’modzi wa Anefi amene adaphedwa.

24 Adalipo pafupifupi makumi asanu amene adavulazidwa, amene adalasidwa ku mivi ya Alamani podutsa pachikhomo, koma adatetezedwa ndi zishango zawo, ndi zapachifuwa zawo, ndi zisoti zakumutu kwawo, kotero kuti mabala awo adali mu miyendo yawo, ambiri amene adali ovulala kwambiri.

25 Ndipo zidachitika, kuti pamene Alamani adaona kuti akulu awo ankhondo onse aphedwa iwo adathawira m’chipululu. Ndipo zidachitika kuti iwo adabwelera ku dziko la Nefi, kuti akadziwitse mfumu yawo, Amalikiya, amene adali mnefi pachibadwe, zokhudzana ndi kutayika kwawo kwakukulu.

26 Ndipo zidachitika kuti iye adakwiya kwambiri ndi anthu ake, chifukwa iye sadapeze chikhumbo chake pa Anefi; iye sadawaike iwo ku goli la ukapolo.

27 Inde, iye adali wokwiya kwambiri, ndipo adatembelera Mulungu, ndiponso Moroni, kulumbira ndi lumbiro kuti iye adzamwa mwazi wake; ndipo izi chifukwa Moroni adasunga malamulo a Mulungu pokonzekera chitetezo cha anthu ake.

28 Ndipo zidachitika, kuti ku mbali inayi, anthu a Nefi adathokoza Ambuye Mulungu wawo, chifukwa cha mphamvu zake zosayerekezeka powawombola iwo m’manja mwa adani awo.

29 Ndipo motero chidatha chaka cha khumi ndi chisanu ndi chinayi cha ulamuliro wa oweruza pa anthu a Nefi.

30 Inde, ndipo kudali mtendere wosalekeza pakati pawo, ndi kuchita bwino kopambana kwakukulu mu mpingo chifukwa cha kumvera kwawo ndi khama limenee iwo adapereka ku mawu a Mulungu, amene adalalikidwa kwa iwo ndi Helamani, ndi Shibuloni, ndi Koriyantoni, ndi Amoni ndi abale ake, inde, ndi onse amene adadzodzedwa mwa dongosolo loyera la Mulungu, pobatizidwa m’kulapa, ndi kutumizidwa kukalalikira pakati pa anthu.