Malembo Oyera
Alima 48


Mutu 48

Amalikiya awutsa Alamani motsutsana ndi Anefi—Moroni akonzekeretsa anthu ake kuteteza ntchito ya Akhristu—Iye akondwera mu kumasuka ndi ufulu ndipo ndi munthu wamphamvu wa Mulungu. Mdzaka dza pafupifupi 72 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo tsopano zidachitika kuti, posakhalitsa pamene Amalikiya adatenga ufumuwo iye adayamba kulimbikitsa mitima ya Alamani motsutsana ndi anthu a Nefi, inde, iye adasankha anthu kuti ayankhule kwa Alamani kuchokera ku nsanja zawo, motsutsana ndi Anefi.

2 Ndipo motero iye adalimbikitsa mitima yawo motsutsana ndi Anefi, kotero kuti kumapeto kwa chaka cha khumi ndi chisanu ndi chinayi cha ulamuliro wa oweruza iye atakwaniritsa zofuna zake choncho, inde, atapangidwa kukhala mfumu pa Alamani, iye adafunanso kulamulira pa dziko lonselo, inde, ndi anthu onse amene adali mu dzikolo, Anefi komanso Alamani.

3 Kotero iye adakwaniritsa zofuna zake, pakuti iye adali atalimbitsa mitima ya Alamani ndipo adachititsa khungu maganizo awo, ndipo adawautsira iwo mkwiyo, kufikira kuti iye adasonkhanitsa pamodzi khamu lochuluka kuti apite kunkhondo motsutsana ndi Anefi.

4 Pakuti iye adali wotsimikizika, chifukwa cha kukula kwa chiwerengero cha anthu ake, kuti agonjetsa Anefi ndi kuwabweretsa iwo mu ukapolo.

5 Ndipo motero iye adasankha akulu ankhondo a Azoramu, iwo pokhala odziwa kwambiri za mphamvu za Anefi, ndi malo awo obisalira, ndi madera ofooka a mizinda yawo; kotero iye adasankha iwo kukhala akulu ankhondo pa ankhondo ake.

6 Ndipo zidachitika kuti iwo adatenga msasa wawo, ndi kupita chakufupi ndi dziko la Zarahemula m’chipululu.

7 Tsopano zidachitika kuti pamene Amalikiya adapeza mphamvu choncho mwa chinyengo ndi ukamberembere, Moroni, ku dzanja linali, adali akukonzekeretsa maganizo a anthu kukhala wokhulupirika kwa Ambuye Mulungu wawo.

8 Inde, iye adali akulimbikitsa ankhondo achinefi, ndi kukhazikitsa malinga ang’onoang’ono, kapena malo obisaliramo; kuponya mizere ya dothi mozungulira kuti azizinga magulu ankhondo ake, ndi kumanganso makoma a miyala kuti awazungulire iwo, mozungulira mizinda yawo ndi malire a dziko lawo; inde, kuzungulira dziko lonselo.

9 Ndipo mu malinga awo ofooka iye adaikamo chiwerengero cha anthu chokulirapo; ndipo motero iye adalimbitsa ndi kulimbikitsa dzikolo limene lidali la Anefi.

10 Ndipo motero iye adali kukonzekera kuthandizira ufulu wawo, dziko lawo, akazi awo, ndi ana awo, ndi mtendere wawo, ndipo kuti akathe kukhala ndi moyo kwa Ambuye Mulungu wawo, komanso kuti akathe kusunga icho chimene chidatchedwa ndi adani awo cholinga cha Akhristu.

11 Ndipo Moroni adali munthu wolimba ndi wamphamvu; adali munthu wa luntha langwiro; inde, munthu amene sankakondwera mukukhetsa mwazi; munthu amene mzimu wake udali osangalalamu kumasuka ndi ufulu wa dziko lake, ndi abale ake kuchokera mu msinga ndi ukapolo.

12 Inde, munthu amene mtima wake udasefukira ndi chiyamiko kwa Mulungu wake, chifukwa cha mwayi ndi madalitso wochuluka amene iye adapereka pa anthu ake; munthu amene adagwira ntchito mopambanitsa chifukwa cha ubwino ndi chitetezo cha anthu ake.

13 Inde, ndipo adali munthu amene adali wokhazikika mu chikhulupiliro cha Khristu, ndipo iye adalumbira ndi lumbiro kuti adzateteza anthu ake, maufulu ake, ndi dziko lake, ndi chipembedzo chake, ngakhale kufikira kutaya mwazi wake.

14 Tsopano Anefi adaphunzitsidwa kudziteteza okha motsutsana ndi ndi adani awo, ngakhale mpakana kukhetsa mwazi ngati kudali kofunikira; inde, ndipo adaphunzitsidwanso kusayambitsa ndewu, ndi kusakweza konse lupanga pokhapokha ngati kutakhala kotsutsana ndi adani, pokhapokha ngati kuli kuteteza miyoyo yawo.

15 Ndipo ichi chidali chikhulupiliro chawo, kuti pakutero Mulungu adzawachititsa bwino mu dzikolo, kapena mu mawu ena, ngati iwo adali okhulupirika mu kusunga malamulo a Mulungu kuti iye adzawachititsa bwino mu dziko; inde, kuwachenjeza iwo kuti athawe, kapena kukonzekera nkhondo, molingana ndi chiopsyezo chawo.

16 Ndiponso, kuti Mulungu adzadziwitsa kwa iwo kumene akuyenera kupita kuti adziteteze kwa adani awo, ndipo pakutelo, Ambuye adzawapulumutsa iwo; ndipo ichi chidali chikhulupiliro cha Moroni, ndipo mtima wake udanyadira mwa ichi; osati mwa kukhetsa mwazi koma mu kuchita zabwino, mu kusunga anthu ake, inde, mu kusunga malamulo a Mulungu, inde, mu kukana zoipa.

17 Inde, indetu, indetu ndinena ndi inu, ngati anthu onse adali, ndipo akadali, ndipo adzakhalepo, monga Moroni, taonani, mphamvu zomwe za gahena zikadagwedezeka kunthawi zosatha; inde, mdyerekezi sakadakhala ndi mphamvu pa mitima ya ana a anthu.

18 Taonani, iye adali munthu ngati Amoni, mwana wa Mosiya, inde, ndipo ngakhale ana aamuna ena a Mosiya, inde, ndiponso Alima ana ake, pakuti onsewa adali anthu a Mulungu.

19 Tsopano taonani, Helamani ndi abale ake sadali ocheperapo kutumikira anthu monga momwe adaliri Moroni; pakuti iwo adalalikira mawu a Mulungu, ndipo adabatiza m’kulapa anthu onse amene akadamvera mawu awo.

20 Ndipo motero iwo adapita patsogolo, ndipo anthu adadzichepetsa okha chifukwa cha mawu awo, kufikira kuti iwo adakonderedwa kwambiri ndi Ambuye, ndipo motero iwo adali omasulidwa ku nkhondo ndi mikangano pakati pawo, inde, ngakhale kwa nthawi ya dzaka zinayi.

21 Koma, monga ndanenera, m’masiku otsiliza amchaka cha khumi ndi chisanu ndi chinayi, inde, posatengera za mtendere wawo pakati pawo, adakakamizika monyinyirika kumenyana ndi abale awo, Alamani.

22 Inde, ndipo pamapeto pake, nkhondo zawo sizidathe kwa nthawi ya dzaka zambiri ndi Alamani, posatengera kunyinyirika kwawo.

23 Tsopano, iwo adali achisoni kutenga zida motsutsana ndi Alamani, chifukwa iwo sadakondwere ndi kukhetsa mwazi; inde; ndipo izi sizokhazo—iwo adali achisoni pokhala njira yotumizira abale awo kuchokera m’dziko lapansi ku dziko lamuyaya, asadakonzekere kukumana ndi Mulungu wawo.

24 Komabe, iwo sakadalora kutaya moyo wawo, kuti akazi awo ndi ana awo aphedwe mwa nkhanza zosaneneka za iwo amene kale adali abale awo, inde, ndipo adagalukira kuchoka mu mpingo wawo, ndipo adali atawasiya iwo ndipo adali atapita kukawawononga iwo polumikizana ndi Alamani.

25 Inde, iwo sakadalora kuti abale awo akondwere pa mwazi wa Anefi, malinga ngati padali aliyense amene adayenera kusunga malamulo a Mulungu, pakuti lonjezo la Ambuye lidali, ngati iwo angasunge malamulo ake adzachita bwino mu dzikolo.