Malembo Oyera
Alima 58


Mutu 58

Helamani, Gidi, ndi Teomineri atenga mzinda wa Manti mwa dongosolo—Alamani athawa—Ana aamuna a anthu a Amoni atetezedwa pamene iwo ayima nji potetezera ufulu wawo ndi chikhulupiliro. Mdzaka dza pafupifupi 63–62 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo taona, tsopano zidachitika kuti cholinga chathu chotsatira chidali kutenga mzinda wa Manti; koma taona, padalibe njira ina yomwe tikadawatsogolera iwo kutuluka mu mzindawo ndi kagulu kathu kochepa. Pakuti taona, iwo adakumbukira icho chimene ife tidawachitira; kotero sitikadawanyengeza iwo kuchoka m’malinga awo.

2 Ndipo iwo adali ochuluka kwambiri kuposera ankhondo athu kuti sitikadapita ndi kuwaukira iwo m’malinga awo

3 Inde, ndipo kudakhala kofunikira kuti ife tiuze anthu athu ateteze zigawo zadziko zimene tidazilanditsa; kotero kudakhala kofunikira kuti tidikilire, kuti tilandire mphamvu zochuluka kuchokera ku dziko la Zarahemula ndiponso chithandizo chatsopano cha chakudya.

4 Ndipo zidachitika kuti ine ndidatumiza kazembe kwa bwanam’kubwa wa dziko lathu, kukamudziwitsa iye zokhudzana ndi zochitika za anthu athu. Ndipo zidachitika kuti tidadikira kulandira chakudya ndi mphamvu kuchokera ku dziko la Zarahemula.

5 Koma taona, izi zidatipindulira ife koma pang’ono; pakuti Alamani ankalandiranso mphamvu zazikulu kuchokera tsiku ndi tsiku, ndiponso zakudya zambiri; ndipo motero ndi m’mene ife tidaliri pa nyengo ya nthawi imeneyi.

6 Ndipo Alamani ankatulukira motsutsana nafe kwa nthawi ndi nthawi, kugwirizana mwachinyengo kuti atiwononge ife; komabe ife sitikadatha kubwera kudzamenyana nawo, chifukwa cha kobisalira kwawo ndi malinga awo.

7 Ndipo zidachikita kuti ife tidayembekezerabe mu nyengo zimenezi zovuta kwa nthawi ya miyezi yambiri, ngakhale kufikira tidali pafupi kuwonongeka chifukwa chakusowa chakudya.

8 Koma zidachitika kuti tidalandira chakudya, chimene chidabweretsedwa kwa ife ndi ankhondo zikwi ziwiri kudzatithandiza ife; ndipo ichi chidali chithandizo chonse chomwe ife tidalandira, kuti tidziteteze tokha ndi dziko lathu kuti lisagwere m’manja mwa adani athu, inde, kulimbana ndi m’dani amene adali wosawerengeka.

9 Ndipo tsopano chifukwa cha manyazi athuwa, kapena chifukwa chimene iwo sadatitumizire ife thandizo, sitidadziwe; kotero tidali ndi chisoni ndipo tidadzadza ndi mantha, kuopa mwa njira iliyonse ziweruzo za Mulungu zingadze pa dziko lathu, m’kugwetsedwa kwathu ndi kutiwonongeratu.

10 Kotero tidatsanulira miyoyo yathu mu pemphero kwa Mulungu, kuti iye atipatse mphamvu ndi kutipulumutsa ife kuchoka m’manja mwa adani athu, inde, ndiponso kutipatsa ife mphamvu kuti titenge mizinda yathu, ndi maiko athu, ndi katundu wathu, kuti tithandizire anthu athu.

11 Inde, ndipo zidachitika kuti Ambuye Mulungu wathu adatiyendera ife ndi chitsikimizo choti iye adzatipulumutsa ife; inde, kufikira kuti adayankhula mtendere ku miyoyo yathu, ndipo adapereka kwa ife chikhulupiliro chachikulu, ndipo adachititsa ife kuti tikhale ndi chiyembekezo cha chipulumutso chathu mwa iye.

12 Ndipo tidayamba kulimba mtima ndi kagulu kathu kankhondo kamene tidalandira, ndipo tidakhazikika pa kutsimikizika mtima kogonjetsa adani athu, ndi kuteteza dziko lathu ndi katundu wathu, ndi akazi athu, ndi ana athu, ndi cholinga cha ufulu wathu.

13 Ndipo motero tidapita ndi mphamvu zathu zonse motsutsana ndi Alamani, amene adali mu mzinda wa Manti; ndipo tidakhoma mahema athu pambali pa chipululu, chimene chidali pafupi ndi mzindawo.

14 Ndipo zidachitika kuti m’mawa mwake, kuti pamene Alamani adaona kuti ife tili mu malire amchipululu chimene chidali pafupi ndi mzindawo, kuti iwo adatumiza akazitape awo kutizungulira ife kuti adziwe chiwerengero ndi mphamvu za ankhondo athu.

15 Ndipo zidachitika kuti pamene iwo adaona kuti sitidali ndi mphamvu, molingana ndi chiwerengero chathu, ndi kuopa kuti tingawadulire ku chithandizo chawo pokhapokha iwo abwere kudzamenyana nafe ndi kutipha, ndiponso poganiza kuti akadatha kutiwononga mosavuta ndi unyinji wawo waukulu, kotero iwo adayamba kukonzekera kubwera kudzalimbana nafe kunkhondo.

16 Ndipo pamene ife tidaona kuti iwo akuchita zokonzekera kubwera kudzamenyana nafe, taona, ndidachititsa kuti Gidi, ndi chiwerengero chochepa cha anthu, adzibise yekha m’chipululu, ndiponso kuti Teomineri ndi chiwerengero chochepa cha anthu apitenso akadzibise okha m’chipululu.

17 Tsopano Gidi ndi anthu ake adali kumanja ndipo ena adali kumanzere; ndipo pamene iwo adadzibisa okha choncho, taona, ndidatsalira, ndi otsalira a ankhondo anga, mu malo omwewo kumene tidakhoma mahema athu koyamba isadafike nthawi imene Alamani akubwera kudzalimbana nafe.

18 Ndipo zidachitika kuti Alamani adatulukira ndi ankhondo awo ochuluka motsutsana nafe. Ndipo pamene iwo adabwera ndipo adali pafupi kutigwera ife ndi lupanga, ndidachititsa kuti anthu anga, amene adali nane, athawire m’chipululu.

19 Ndipo zidachitika kuti Alamani adatitsatira ife ndi liwiro lalikulu, pakuti iwo adali kukhumba kwambiri kutipeza ife kuti athe kutipha; kotero iwo adatitsatira ife m’chipululu; ndipo ife tidadutsa pakati pa Gidi ndi Teomineri, kufikira kuti sadaonedwe ndi Alamani.

20 Ndipo zidachitika kuti pamene Alamani adadutsa, kapena pamene ankhondo adadutsa, Gidi ndi Teomineri adadzuka ku malo awo obisika, ndi kuwadula akazitape Achilamani kuti asabwelerenso ku mzindawo.

21 Ndipo zidachitika kuti pamene iwo adadulidwa, adathawira ku mzindawo ndi kukagwera kwa alonda amene adasiyidwa mu mzindawo, kufikira kuti iwo adawawononga ndi kulanda mzindawo.

22 Tsopano izi zidachitika chifukwa Alamani adalora ankhondo onse, kupatula alonda ochepa okha, kuti asocheletsedwe m’chipululu.

23 Ndipo zidachitika kuti Gidi ndi Teomineri mu njira imeneyi adatenga malinga awo. Ndipo zidachitika kuti tidatenga njira yathu, titamaliza kuyenda kwambiri m’chipululu cha ku dziko la Zarahemula.

24 Ndipo pamene Alamani adaona kuti ife tidali kugubira cha ku dziko la Zarahemula, adali ndi mantha kwambiri, kuopa kuti kudali dongosolo loikidwa kuti iwo liwatsogolere ku chiwonongeko; kotero iwo adayamba kuthawira m’chipululu kachiwiri, inde, ngakhale kubwelera m’njira imene iwo adadzera.

25 Ndipo taonani, udali usiku ndipo iwo adakhoma mahema awo, pakuti akulu ankhondo Achilamani adaganiza kuti Anefi adali atatopa chifukwa cha kuguba kwawo; ndipo poganiza kuti adathamangitsa ankhondo awo onse kotero iwo sadaganizire zokhudzana ndi mzinda wa Manti.

26 Tsopano zidachitika kuti pamene usiku udafika, ndidachititsa kuti anthu anga asagone, koma kuti agubire kutsogolo podzera njira ina kuyandikira ku dziko la Manti.

27 Ndipo chifukwa cha kuguba uku mkati mwa nthawi yausiku, taonani, m’mawa mwake tidawapitilira Alamani, kufikira kuti ife tidafka iwo asadafike mu mzinda wa Manti.

28 Ndipo motero zidachitika, kuti mu njira imeneyi tidalanda mzinda wa Manti popanda kukhetsa mwazi.

29 Ndipo zidachitika kuti pamene ankhondo Achilamani adafika kufupi ndi mzindawo, ndi kuona kuti tidali okonzeka kukumana nawo, iwo adali odabwa kwambiri ndi kugwidwa ndi mantha aakulu, kufikira kuti iwo adathawira m’chipululu.

30 Inde, ndipo zidachitika kuti ankhondo Achilamani adathawa kuchoka ku kachigawo kameneka ka dzikoli. Koma taona, iwo anyamula nawo azimayi ambiri ndi ana kuchoka m’dzikoli.

31 Ndipo mizinda imeneyo imene idatengedwa ndi Alamani, yonse pa nyengo ino ya nthawi ili m’manja mwathu; ndipo azibambo athu ndi amayi athu akubwelera kunyumba zawo, onse kupatula iwo amene adatengedwa ukaidi ndi kutengedwa ndi Alamani.

32 Koma taona, ankhondo athu ndi ochepa kuti ateteze chiwerengero chachikulu cha mizinda ndi katundu wambiriyu.

33 Koma taona, ife tikudalira mwa Mulungu wathu amene watipatsa ife chigonjetso pa maiko amenewo, kotero kuti tatenga mizindayo ndi maiko amenewo, amene adali athu omwe.

34 Tsopano sitikudziwa chifukwa chimene boma silikutipatsa ife mphamvu zowonjezera; ngakhale anthu amene adabwera kwa ifewo sakudziwa chimene sitikulandilira mphamvu zowonjezera.

35 Taona, ife sitikudziwa koma chomwe simudakwanitsire, ndipo kuti inu mwathamangitsa ankhondo kumbali imeneyo ya dziko; ngati ndichoncho, ife sitikufuna kuwiringula.

36 Ndipo ngati sichoncho, taona, tikuopa kuti alipo ena ambali yaboma, amene sakutumiza anthu ena kudzatithandiza ife; pakuti ife tikudziwa kuti alipo ambiri kuposa amene atumiza.

37 Koma, taona, zilibe kanthu—tikukhulupilira Mulungu adzatipulumutsa, ngakhale ankhondo athu ndiofooka, inde, ndipo atiwombotsa ife kuchoka m’manja mwa adani athu.

38 Taona, ichi ndi chaka cha makumi awiri ndi zisanu ndi zinayi, kumapeto, ndipo talanda maiko athu; ndipo Alamani athawira ku dziko la Nefi.

39 Ndipo ana aja a anthu a Amoni, amene za iwo ndayankhulapo kwambiri, ali ndi ine mu mzinda wa Manti; ndipo Ambuye waathandiza iwo, inde, ndipo waasunga iwo kuti asagwe ndi lupanga, kotero kuti ngakhale munthu m’modzi sadaphedwe.

40 Koma taona, iwo alandira mabala ambiri; komabe ayima nji mu ufulu umene Mulungu waamasula; ndipo ali wosamalitsa pokumbukira Ambuye Mulungu wawo mu tsiku ndi tsiku; inde, iwo amatsata kusunga malemba ake, ndi ziweruzo zake, ndi malamulo ake mosalekeza; ndipo chikhulupiliro chawo ndi cholimba mu mauneneri okhudzana ndi zimene zili nkudza.

41 Ndipo tsopano, m’bale wanga, Moroni, Ambuye Mulungu wathu, amene watiwombola ife ndi kutipanga ife omasulidwa, akusunge iwe kosalekeza pamaso pake; inde, ndipo akondere anthu awa, ngakhale kuti mukhale ndi kuthekera kotenga zonse zimene Alamani adatitengera ife, zimene zidali chithandizo chathu. Ndipo tsopano taona, ndikutseka kalata yanga. Ndine Helamani, mwana wa Alima.