Malembo Oyera
Alima 10


Mutu 10

Lehi adachokera kwa Manase—Amuleki afotokoza lamulo la mngelo kuti asamale Alima—Mapemphero a olungama apangitsa anthu kuti apulumutsidwe—Oimila milandu ndi oweruza osalungama aika maziko a chiwonongeko cha anthu. Mdzaka dza pafupifupi 82 Yesu asadabadwe.

1 Tsopano awa ndiwo mawu amene Amuleki adalalikira kwa anthu amene adali mu dziko la Amoniha, nati:

2 Ine ndine Amuleki; ine ndine mwana wa Gidona, amene adali mwana wa Ismaeli, amene adali mdzukulu wa Aminadi; ndipo ndiyemweyo Aminadi amene adamasulira zolemba zimene zidali pa khoma la kachisi, zimene zidalembedwa ndi chala cha Mulungu.

3 Ndipo Aminadi adali mdzukulu wa Nefi, amene adali mwana wa Lehi, amene adachokera ku dziko la Yerusalemu, amene adali mdzukulu wa Manase, amene adali mwana wa Yosefe amene adagulitsidwa ku Igupto ndi manja a abale ake.

4 Ndipo taonani, ine ndinenso munthu wa mbiri yosachepa pakati pa onse amene amandidziwa; inde, ndipo taonani, ndiri ndi abale ndi anzanga ambiri, ndipo ndapezanso chuma chambiri m’dzanja la ntchito yanga.

5 Komabe, pakutha pa izi zonse, sindinkadziwa zambiri za njira za Ambuye, ndi zinsinsi zake ndi mphamvu zake zodabwitsa. Ndanena sindinkadziwa zambiri za zinthu izi; koma taonani, ndalakwitsa, pakuti ndaona zambiri za zinsinsi ndi mphamvu zake zodabwitsa, inde, ngakhale m’kuteteza kwa moyo wa anthu awa.

6 Komabe, ndidalimbitsa mtima wanga, pakuti ndidaitanidwa nthawi zambiri ndipo sindidamve; kotero ndidadziwa zokhudzana ndi zinthu izi, komabe sindikadadziwa; kotero ndidapitiriza kuukira motsutsana ndi Mulungu, mu kuipa kwa mtima wanga, ngakhale kufikira tsiku lachinayi la mwezi wa chisanu ndi chiwiri, umene uli mu chaka cha khumi cha ulamuliro wa oweruza.

7 Pamene ndidali paulendo kukaona wachibale wapafupi, taonani mngelo wa Ambuye adaonekera kwa ine ndipo adati: Amuleki, bwelera ku nyumba yako, pakuti udzadyetsa mneneri wa Ambuye; inde munthu oyera, amene ali munthu wosankhidwa ndi Mulungu; pakuti wasala kudya kwa masiku ambiri chifukwa cha machimo a anthu awa, ndipo ali ndi njala, ndipo iwe udzamulandira mu nyumba mwako ndi kumudyetsa iye, ndipo iye adzakudalitsa iwe ndi nyumba yako; ndipo dalitso la Ambuye lidzakhala pa iwe ndi nyumba yako.

8 Ndipo zidachitika kuti ndidamvera mawu a mngeloyo, ndipo ndidabwelera kunyumba yanga. Ndipo pamene ndidali kupita kumeneko ndidapeza munthu amene mngelo adanena kwa ine: Udzamulandire m’nyumba mwako—ndipo taonani adali munthu yemweyo amene wakhala akuyankhula kwa inu zokhudzana ndi zinthu za Mulungu.

9 Ndipo mngeloyo adati kwa ine, ndi munthu oyera; kotero ndikudziwa kuti ndi munthu oyera chifukwa zidanenedwa ndi mngelo wa Mulungu.

10 Ndiponso, ndikudziwa kuti zinthu zimene iye wachitira umboni ndi zoona; pakuti taonani ndikunena kwa inu, kuti monga Ambuye ali wamoyo, ngakhale momwemonso watumiza mngelo wake kuti aonetsere zinthu izi kwa ine; ndipo izi wachita pamene Alima ameneyu akukhala m’nyumba mwanga.

11 Pakuti taonani, wadalitsa nyumba yanga, wandidalitsa ine, ndi azimayi anga, ndi ana anga, ndi atate anga, ndi azibale anga; inde ngakhale mtundu wanga wonse waudalitsa, ndipo dalitso la Ambuye lakhala pa ife monga mwa mawu amene iye adayankhula.

12 Ndipo tsopano, pamene Amuleki adanena mawu awa anthu adayamba kuzizwa, poona kuti padali mboni yoposera imodzi imene idachitira umboni za zinthu zimene iwo amadzudzulidwa, ndiponso za zinthu zimene zidali nkudza, monga mwa mzimu wa uneneri umene udali mwa iwo.

13 Komabe, padali ena mwa iwo amene adaganiza zowafunsa iwo, kuti mwa njira zawo zochenjera awagwire mu mawu awo, kuti apeze umboni otsutsana nawo, kuti akawapereke kwa oweruza awo amene akhonza kuwaweruza molingana ndi chilamulo, ndipo kuti awaphe kapena kuwaponya mu ndende, molingana ndi mulandu umene akadatha kuupanga kuonekera kapena kuchitira umboni otsutsana nawo.

14 Tsopano adali amuna aja amene adafuna kuti awawononge, amene adali oimira mulandu, amene adalembedwa ganyu kapena wosankhidwa ndi anthu kuti adziyendetsa malamulo pa nthawi ya milandu, kapena pa milandu ya zolakwa za anthu pamaso pa oweruza.

15 Tsopano azamalamulo awa adali ophunzira mu luso lonse ndi ukathyali wa anthu; ndipo izi zidali zowathandiza iwo kuti akhale a luso mu ntchito yawo.

16 Ndipo zidachitika kuti iwo adayamba kufunsa mafunso Amuleki, kuti potero amupangitse iye kusemphanitsa mawu ake, kapena kutsutsana ndi mawu amene iye akuyenera kuyankhula.

17 Tsopano iwo sankadziwa kuti Amuleki akhonza kudziwa mapangidwe awo. Koma zidachitika kuti pamene iwo adayamba kumufunsa iye, iye adadziwa maganizo awo, ndipo adati kwa iwo: O inu oipa ndi m’badwo wokhota, inu azamalamulo ndi onyenga, pakuti mukuyala maziko a mdyerekezi; pakuti mukutchera mbuna ndi misampha kuti mugwire woyera a Mulungu.

18 Mukuyala madongosolo oti mupotoze njira za wolungama, ndi kugwetsa mkwiyo wa Mulungu pamitu yanu, ngakhale chiwonongeko chotheratu cha anthu awa.

19 Inde, Mosiya adanena bwino, amene adali mfumu yathu yomaliza, pamene adali pafupi kupereka ufumu, opanda wina kuti ampatse, kuchititsa kuti anthu awa kuti alamulidwe ndi mawu awo omwe—inde, iye adanena bwino kuti ngati nthawi idzafika kuti mawu a anthu awa adzasankha kusaweruzika, ndiko kuti, ngati nthawiyo idzafike kuti anthu awa adzagwa mu kulakwitsa, adzakhala atafika poyenera chiwonongeko.

20 Ndipo tsopano ndikunena kwa inu kuti Ambuye amaweruza bwino zolakwa zanu; amafuula bwino kwa anthu awa, ndi mawu a angelo ake: Lapani inu, lapani, pakuti ufumu wa kumwamba wayandikira.

21 Inde, iye amafuula bwino, mwa mawu a angelo ake kuti: Ndidzatsika pansi pakati pa anthu anga, ndi kusaona nkhope ndi chilungamocho m’manja mwanga.

22 Inde, ndipo ndikunena kwa inu kuti kukadapanda mapemphero a olungama, amene tsopano ali mu dziko, kuti ngakhale tsopano inu mukadayenderedwa ndi chiwonongeko chotheratu; koma sikudzakhala ndi chigumula, ngati m’mene adalili anthu m’masiku a Nowa, koma kudzakhala mwa chilala, ndi mliri ndi lupanga.

23 Koma ndi chifukwa cha mapemphero a wolungama kuti mwapulumutsidwa; tsopano kotero, ngati mudzatulutsa olungama kuchoka pakati panu pamenepo ambuye sadzaletsa dzanja lake; koma mu mkwiyo wake woopsa adzakutulukirani kutsutsana nanu; pamenepo mudzakanthidwa ndi chilala, ndi mliri ndi lupanga; ndipo nthawi ikuyandikira mwansanga pokhapokha mulape.

24 Ndipo tsopano zidachitika kuti anthuwo adakwiya kwambiri ndi Amuleki, ndipo adafuula, nati: Munthu uyu akulimbana ndi malamulo athu amene ali olungama, ndi azamalamulo athu anzeru amene ife tidawasankha

25 Koma Amuleki adatambasula dzanja lake, ndi kufuula mwamphamvu kwa iwo, nati: O inu oipa ndi m’badwo wokhotakhota, chifukwa chiyani Satana wagwiritsa chotere pa mitima yanu? N’chifukwa chiyani mukudzipereka nokha kwa iye kuti akhale ndi mphamvu pa inu, kuchititsa khungu maso anu, kuti inu musamvetse mawu amene akuyankhulidwa molingana ndi chilungamo chawo?

26 Pakuti taonani, kodi ndachitira umboni motsutsana ndi chilamulo chanu? Inu simukumvetsa; mukuti ine ndayankhula motsutsana ndi lamulo lanu; koma sindidatelo, koma ndayankhula mokomera chilamulo chanu, kuchiweruzo chanu.

27 Ndipo tsopano taonani, ndikunena kwa inu, kuti maziko a chiwonongeko cha anthu awa akuyamba kukhazikitsidwa ndi kusalungama kwa azamalamulo anu ndi oweruza.

28 Ndipo tsopano zidachitika kuti pamene Amuleki adayankhula mawu awa anthu adafuula motsutsana naye, nati: Tsopano ife tikudziwa kuti munthu uyu ndi mwana wa mdyerekezi, pakuti watinamiza ife, pakuti wayankhula motsutsana ndi chilamulo chathu. Ndipo tsopano iye akuti sadayankhule motsutsana nacho.

29 Ndiponso, wanyoza azamalamulo athu ndi oweruza athu.

30 Ndipo zidachitika kuti azamalamulo adachiyika ichi m’mitima yawo kuti akumbukire zinthu izi motsutsana naye.

31 Ndipo padali m’modzi mwa iwo yemwe dzina lake adali Zeziromu. Tsopano iye adali oyambilira kumuzenga Amuleki ndi Alima, iye okhala m’modzi mwa akatswiri pakati pawo, pokhala ndi tchito yambiri yoti achite pakati pa anthu.

32 Tsopano chofuna cha azamalamulowa chidali kuti apindule; ndipo adapindula molingana ndi ntchito yawo.