Malembo Oyera
Alima 3


Mutu 3

Aamiliki adadziika chizindikiro okha molingana ndi mawu a uneneri—Alamani adatembeleredwa chifukwa cha kupanduka kwawo—Anthu amadzibweretsera okha matembelero—Anefi agonjetsa gulu lina lankhondo la Alamani. Mdzaka dza pafupifupi 87–86 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo zidachitika kuti Anefi amene sadaphedwe ndi zida za nkhondo, atakwilira iwo amene adaphedwa—tsopano chiwerengelo cha omwe adaphedwa sichidawerengedwe, chifukwa cha kuchulukwa kwa chiwerengelo chawo—atamaliza kukwilira akufa awo adabwelera ku dziko lawo, ndi kunyumba zawo, ndi kwa akazi awo, ndi kwa ana awo.

2 Tsopano akazi ambiri ndi ana adaphedwa ndi lupanga, ndiponso zambiri mwa nkhosa zawo ndi ng’ombe zawo; ndiponso minda yawo yambewu idawonongedwa, chifukwa zidaponderezedwa ndi makamu a anthu.

3 Ndipo tsopano ambiri mwa Alamani ndi Aamiliki amene adaphedwa mphepete mwa mtsinje wa Sidoni adaponyedwa m’madzi a Sidoni; ndipo taonani mafupa awo ali m’kuya kwa nyanja, ndipo ndi ambiri.

4 Ndipo Aamiliki ankasiyanitsidwa ndi Anefi, popeza adali atadziika chizindikiro okha ndi zofiira pa chipumi pawo monga ngati Alamani; komabe iwo sadamete mitu yawo ngati Alamani.

5 Tsopano mitu ya Alamani idali yometa: ndipo adali amaliseche, kupatula chikopa chimene chidamangiliridwa mchiuno mwawo, ndiponso zida zawo zimene adadzimangilira ndi mauta awo, ndi mthungo zawo, ndi miyala yawo ndi malegeni awo ndi zina zotero.

6 Ndipo khungu la Alamani lidali lakuda, molingana ndi chizindikiro chimene chidaikidwa pa makolo awo, chimene chidali thembelero pa iwo chifukwa cha kulakwitsa kwawo ndi kupanduka kwawo motsutsana ndi abale awo, amene adali Nefi, Yakobo ndi Yosefe ndi Samu, amene adali anthu olungama ndi oyera mtima.

7 Ndipo abale awo adafuna kuwawononga iwo, kotero adatembeleredwa; ndipo Ambuye Mulungu adaika chizindikiro pa iwo, inde, pa Lamani ndi Lemueli, ndiponso pa ana a Ismaeli, ndi azimayi a Aismaeli

8 Ndipo izi zidachitika kuti mbewu yawo isiyanitsidwe kwa mbewu ya abale awo, kuti mwa kutero Ambuye Mulungu akasunge anthu ake, kuti iwo asasakanikire ndi kukhulupilira mu zikhalidwe zolakwika zimene zingatsimikizire chiwonongeko chawo.

9 Ndipo zidachitika kuti aliyense amene adasakaniza mbewu yake ndi iyo ya Alamani adabweretsa thembelero lomwelo pa mbewu yake.

10 Kotero, aliyense amene adadzilora yekha kutsogoleredwa ndi Alamani ankatchedwa pa mutu umenewo ndipo padali chizindikiro choikidwa pa iye.

11 Ndipo zidachitika kuti aliyense amene sadakhulupilire mu chikhalidwe cha Alamani, koma adakhulupilira mu zolemba zimene zidabweretsedwa kuchokera ku dziko la Yerusalemu, ndiponso mu chikhalidwe cha makolo awo, chimene chidali cholondora, amene adakhulupilira mu malamulo a Mulungu ndi kuwasunga, adatchedwa Anefi, kapena anthu a Nefi, kuchokera pa nthawi imeneyo kupita mtsogolo—

12 Ndipo iwo ndi amene adasunga zolemba zimene zili zoona za anthu awo, ndiponso za anthu a Alamani.

13 Tsopano ife tidzabweleranso kwa Aamiliki, pakuti iwonso adali ndi chizindikiro choikidwa pa iwo, inde, adadziika okha chizindikiro, inde, ngakhale chizindikiro chofiira pa chipumi chawo.

14 Choncho mawu a Mulungu amakwanilitsidwa, chifukwa awa ndi mawu amene iye adanena kwa Nefi: Taonani, Alamani ndawatembelera, ndipo ndidzaika chizindikiro pa iwo kuti iwo ndi mbewu yawo alekanitsidwe ndi iwe ndi mbewu yako, kuchokera ku nthawi ino kupita mtsogolo ndi kunthawi zosatha, pokhapokha atalapa ku kuipa kwawo ndi kutembenukira kwa ine kuti ndikakhale ndi chifundo pa iwo.

15 Ndiponso: Ndidzaika chizindikiro pa iye amene asakaniza mbewu zake ndi abale ako, kuti nawonso akhale otembeleredwa.

16 Ndiponso: ndidzaika chizindikiro pa iye amene amenyana ndi iwe ndi mbewu yako.

17 Ndiponso, ndikunena kuti iye amene wachoka kwa iwe sadzatchedwanso mbewu yako; ndipo ine ndidzakudalitsa iwe ndi wina aliyense amene adzatchedwe mbewu yako, kuyambira tsopano ndi kunthawi zonse; ndipo awa adali malonjezo a Ambuye kwa Nefi ndi kwa mbewu yake.

18 Tsopano Aamiliki sadadziwe kuti adali kukwanilitsa mawu a Mulungu pamene iwo adayamba kudziika okha chizindikiro pa chipumi chawo; komabe adali ataturukira poyera kupandukira Mulungu; n’chifukwa chake kudali kofunikira kuti thembelero liwagwere iwo.

19 Tsopano ndikufuna kuti muone kuti iwo adadzibweretsera pa iwo wokha thembelero; ndipo ngakhale momwemonso munthu wina aliyense amene watembeleredwa amadzibweretsa yekha ku chiweruzo.

20 Tsopano zidachitika kuti pasadathe masiku ambiri patatha nkhondo imene idamenyedwa ku dziko la Zarahemula, ndi Alamani ndi Aamiliki, kuti padali ankhondo ena a Alamani amene adabwera kwa anthu a Nefi, ku malo omwewo amene ankhondo oyamba adakumana ndi Aamiliki.

21 Ndipo zidachitika kuti padali ankhondo amene adatumidwa kuti awathamangitse iwo kuchoka m’dziko lawo.

22 Tsopano Alima mwiniyo atasautsidwa ndi bala sadapite nawo ku nkhondo pa nthawi iyi kukamenyana ndi Alamani.

23 Koma iye adawatumizira khamu lankhondo lambiri kukamenyana nawo; ndipo adapita ndi kukapha ambiri a Alamani, ndi kuthamangitsira otsalira a iwo ku malire a dziko lawo.

24 Ndipo kenako adabweleranso ndikuyamba kukhazikitsa mtendere m’dzikomo, osavutitsidwanso kwa nthawi ndi adani awo.

25 Tsopano zinthu zonsezi zidachitidwa, inde, nkhondo zonsezi ndi mikangano zidayamba ndi kutha mu chaka cha chisanu cha ulamuliro wa oweruza.

26 Ndipo mu chaka chimodzi zikwi ndi makuni a zikwi a miyoyo adatumizidwa ku dziko lamuyaya, kuti akakolole mphotho zawo monga mwa ntchito zawo, kaya zidali zabwino kapena zidali zoipa, kuti akolole chimwemwe chosatha kapena chisoni chosatha, monga mwa mzimu umene adasankha kuti iwo awumvere, kaya udali mzimu wabwino kapena mzimu oipa.

27 Pakuti munthu aliyense amalandira mphotho kwa iye amene wasankha kumumvera, ndipo ichi molingana ndi mawu a mzimu wa uneneri; kotero zikhale molingana ndi choonadi. Ndipo motero padatha dzaka dzisanu za ulamuliro wa oweruza.

Print