Malembo Oyera
Alima 6


Mutu 6

Mpingo wamu Zarahemula uyeretsedwa ndi kuikidwa mu dongosolo—Alima apita ku Gideoni kukalalikira. Mdzaka dza pafupifupi 83 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo tsopano zidachitika kuti Alima atamaliza kuyankhula kwa anthu a mu mpingo, umene udakhazikitsidwa mu mzinda wa Zarahemula, iye adadzodza ansembe ndi akulu, powasanjika manja ake molingana ndi dongosolo la Mulungu, kuti atsogolere ndi kuyang’anira mpingowo.

2 Ndipo zidachitika kuti aliyense amene sadali wa mumpingo amene adalapa machimo awo adabatizidwa mu kulapa, ndipo adalandiridwa mu mpingo.

3 Ndiponso zidachitikanso kuti aliyense amene adali mu mpingo amene sadalape machimo ku zoipa zawo ndi kudzichepetsa okha pamaso pa Mulungu—ine ndikutanthauza iwo amene adakwezedwa m’kunyada kwa mitima yawo—omwewo adakanidwa, ndipo maina awo adafufutidwa, kuti maina awo sadawerengedwe pamodzi ndi olungama.

4 Ndipo motero iwo adayamba kukhazikitsa dongosolo la mpingo mu mzinda wa Zarahemula.

5 Tsopano ndikufuna kuti mumvetsetse kuti mawu a Mulungu adali operekedwa mwaulele kwa onse, kuti padalibe amene adakanizidwa mwayi wakusonkhana okha pamodzi kuti amve mawu a Mulungu.

6 Komabe, ana a Mulungu adalamulidwa kuti adzisonkhana pamodzi kawirikawiri, ndi kugwirizana mu kusala kudya ndi kupemphera mwa mphamvu m’malo mwa ubwino wa miyoyo ya iwo amene sankadziwa Mulungu.

7 Ndipo tsopano zidachitika kuti pamene Alima adapanga malamulowa adachoka kwa iwo, inde, kuchokera ku mpingo umene udali mu mzinda wa Zarahemula, ndi kupita kutsidya chakum’mawa kwa mtsinje wa Sidoni, ku chigwa cha Gidioni, kumeneko kudali kutamangidwa mzinda, umene udatchedwa mzinda wa Gidioni, umene udali mu chigwa chotchedwa Gideoni, umene udatchedwa motsatira munthu amene adaphedwa ndi dzanja la Neho ndi lupanga.

8 Ndipo Alima adapita ndi kuyamba kulengeza mawu a Mulungu kwa mpingo umene udakhazikitsidwa mu chigwa cha Gideoni, molingana ndi vumbulutso la choonadi cha mawu amene adayankhulidwa ndi makolo ake, ndi molingana ndi mzimu wa uneneri umene udali mwa iye, molingana ndi umboni wa Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu, amene adzabwera kudzawombola anthu ake ku machimo awo, ndi dongosolo loyera limene iye adaitanidwa nalo. Ndipo motere zalembedwa. Ameni.