Malembo Oyera
Alima 55


Mutu 55

Moroni akana kusinthanitsa akaidi—Alonda achilamani anyengeleledwa kuti aledzere, ndipo akaidi achinefi amasulidwa—Mzinda wa Gidi utengedwa popanda kukhetsa mwazi. Mdzaka dza pafupifupi 63–62 Yesu asadabadwe.

1 Tsopano zidachitika kuti pamene Moroni adalandira kalatayi adali okwiya kwambiri, chifukwa adadziwa kuti Amoroni adali ndi chidziwitso chonse chazolakwa zake, inde, ankadziwa kuti Amoroni akudziwa kuti sichidali chifukwa chenicheni chimene iye adamemera nkhondo motsutsana ndi anthu a Nefi.

2 Ndipo iye adati: Taona, inde sindisinthanitsa akaidi ndi Amoroni pokhapokha iye achotse zolinga zake, monga ine ndanenera mu kalata yanga; pakuti sindidzalora kwa iye kuti akhale ndi mphamvu zinanso zoposera zomwe alinazo.

3 Taonani, ndikudziwa malo amene Alamani akulondera anthu anga amene iwo adawatenga ukaidi; ndipo monga Amoroni sakufuna kuvomeleza mkalata yanga, taonani, ndidzamupatsa iye molingana ndi mawu anga; inde, ndidzafuna imfa pakati pawo kufikira iwo atapempha mtendere.

4 Ndipo tsopano zidachitika kuti pamene Moroni adanena mawu awa, iye adachititsa kuti kafukufuku achitike pakati pa anthu ake, kuti mwina apeze munthu amene adali chidzukulu cha Lamani pakati pawo.

5 Ndipo zidachitika kuti iwo adapeza m’modzi, amene dzina lake lidali Lamani; ndipo adali m’modzi mwa antchito a mfumu imene idaphedwa ndi Amalikiya.

6 Tsopano Moroni adachititsa kuti Lamani ndi kagulu kochepa ka anthu ake apite kwa alonda amene adali kuyang’anira a Anefi.

7 Tsopano Anefiwo ankalonderedwa mu mzinda wa Gidi; kotero Moroni adasankha Lamani ndi kuchititsa kagulu ka anthu ake apite naye.

8 Ndipo pamene udali madzulo Lamani adapita kwa alonda amene adali kuyang’anira Anefi, ndipo taonani, iwo adamuona iye akubwera ndipo adamuitana iye; koma iye adati kwa iwo: Musaope; taonani, ine ndi Mlamani. Taonani, ife tathawa kuchokera kwa Anefi, ndipo iwo akugona; ndipo ife tatenga vinyo wawo ndi kubwera naye.

9 Tsopano pamene Alamaniwo adamva mawu awa adamulandira iye mwa chimwemwe; ndipo adati kwa iye: Tipatse ife vinyo wakoyo, kuti ife timwe; ndife okondwa kuti iwe watengako vinyo pakuti ife tatopa.

10 Koma Lamani adati kwa iwo: tiyeni tisunge vinyo wathu kufikira titapita kukamenyana ndi Anefi ku nkhondo. Koma mawu awa adangowapangitsa iwo kufuna kumwa vinyoyo;

11 Pakuti, iwo adati: Ife tatopa, kotero tilore titengeko vinyoyo, ndipo pang’ono ndi pang; ono tidzimwa pa chakudya chathu, chimene chidzatilimbitsa kupita kukamenyana ndi Anefi.

12 Ndipo Lamani adati kwa iwo: Mungathe kuchita molingana ndikufuna kwanu.

13 Ndipo zidachitika kuti iwo adatenga vinyoyo mwaulere; ndipo adali okoma pa lilime lawo, kotero iwo adamumwa momasuka; ndipo adali wamphamvu, atakonzedwa mwa mphamvu yake.

14 Ndipo zidachitika kuti iwo adamwa ndipo adakondwa, ndipo pang’ono ndi pang’ono onse adaledzera.

15 Ndipo tsopano pamene Lamani ndi anthu ake adaona kuti onse adali ataledzera, ndipo adali mu tulo tatikulu, iwo adabwelera kwa Moroni ndi kumuuza iye zinthu zonse zomwe zidachitika.

16 Ndipo tsopano izi zidali molingana ndi dongosolo la Moroni. Ndipo Moroni adakozekeretsa anthu ake ndi zida zankhondo; ndipo iye adapita ku mzinda wa Gidi, pamene Alamani adali mu tulo tatikulu ndi kuledzera, ndipo adaponyera zida zankhondo kwa akaidiwo, kotero kuti onse adali ndi zida.

17 Inde, ngakhale azimayi ndi ana awo onse, ochuluka amene akadatha kugwiritsa ntchito chida chankhondo, pamene Moroni adapereka zida kwa akaidi onsewo; ndipo zinthu zonsezo zidachitika mwakachetechete.

18 Koma akadawadzutsa Alamaniwo, taonani adali ataledzera ndipo Anefi akadatha kuwapha.

19 Koma taonani, ichi sichidali chikhumbo cha Moroni; iye sankakondwera mu kupha kapena kukhetsa mwazi, koma iye ankakondwera mu kupulumutsa anthu ake kuchiwonongeko; ndipo pachifukwa ichi iye sangabweretse pa iye chosalungama, iye sakadagwera pa Alamani ndi kuwawononga iwo mkuledzera kwawo.

20 Koma iye adapeza zokhumba zake; pakuti iye adapereka zida kwa akaidi Achinefi amene adali mkati mwa makoma a mzindawo, ndipo adawapatsa iwo mphamvu zotenga mbali zomwe zidali mkati mwa mzindawo.

21 Ndipo kenako iye adachititsa kuti amuna amene adali naye kuti asunthe pang’ono, ndi kuwazungulira ankhondo Achilamani.

22 Tsopano taonani izi zidachitika mkati mwa usiku, kotero kuti pamene Alamani ankadzuka m’mawa iwo adaona kuti azunguliridwa ndi Anefi kunja, ndipo kuti akaidi awo adali ndi zida mkati.

23 Ndipo motero iwo adaona kuti Anefi adali ndi mphamvu pa iwo; munyengo zimenezi iwo adapeza kuti kudali kosafunikira kuti amenyane ndi Anefi; kotero akulu awo ankhondo adafunsa zida zawo zankhondo, ndipo zidabweretsedwa ndi kuponyedwa pamapazi a Anefi, kuchondelera kuchitiridwa chifundo.

24 Tsopano taonani, ichi chidali chikhumbo cha Moroni. Iye adatenga iwo ukaidi wankhondo, ndipo adalanda mzindawo, ndi kuchititsa kuti akaidi onse amasulidwe, amene adali Anefi; ndipo adadziphatikiza ndi ankhondo a Moroni, ndipo adali nyonga yaikulu kwa ankhondo ake.

25 Ndipo zidachitika kuti iye adachititsa kuti Alamani, amene adatengedwa ukaidi, kuti akuyenera kuyamba ntchito yolimbitsa malinga ozungulira mzinda wa Gidi.

26 Ndipo zidachitika kuti pamene iye adamanga malinga ku mzinda wa Gidi, molingana ndi zikhumbo zake, iye adachititsa kuti akaidiwo atengedwere ku mzinda wa Chuluka; Ndiponso adalondera mzindawo ndi ankhondo amphamvu zoposa.

27 Ndipo zidachitika kuti adachita, posatengera ziwembu zonse za Alamani, zowasunga ndi kuteteza akaidi onse amene iwo adawatenga, ndiponso adasamala nthaka yonse ndi zabwino zimene iwo adazitenganso.

28 Ndipo zidachitika kuti Anefi adayambanso kukhala opambana, ndi kutenganso maufulu ndi mwayi wawo.

29 Nthawi zambiri Alamani ankayesera kuwazungulira iwo usiku, koma mkuyesera kutero adataya ambiri mwa akaidi.

30 Ndipo nthawi zambiri iwo ankayesera kupereka vinyo wawo kwa Anefi, kuti athe kuwawononga ndi mankhwala a chiphe kapena ndi kuledzera.

31 Koma taonani, Anefi sadali ochedwa pokumbukira Ambuye Mulungu wawo mu nthawi imeneyi ya masautso awo. Iwo sakadatheka kutengedwa mu misampha yawo; inde, iwo sadamwepo vinyo wawo, pokhapokha atayamba apereka wina kwa akaidi Achilamani.

32 Ndipo motero adali ochenjera kuti padalibe mankhwala a chiphe omwe adaperekedwa pakati pawo; pakuti ngati vinyo wawo angaphe Mlamani akadaphanso Mnefi; ndipo motero iwo ankayesa chakumwa chawo chonse.

33 Ndipo tsopano zidachitika kuti kudali kofunikira kwa Moroni kupanga zokonzekera kukaukira mzinda wa Moriyantoni; pakuti taonani, Alamani adali, mwa ntchito zawo, akulimbitsa mzinda wa Moriyantoni mpaka udakhala linga lalikulu.

34 Ndipo iwo adali mosalekeza kubweretsa ankhondo atsopano mu mzinda umenewo, komanso katundu watsopano wa chakudya.

35 Ndipo motero chidatha chaka cha makumi awiri ndi zisanu ndi zinayi cha ulamuliro wa oweruza pa anthu a Nefi.

Print