Mutu 43
Alima ndi ana ake aamuna alalikira mawu—Azoramu ndi Anefi ena otsutsa akhala Alamani—Alamani abwera kudzamenyana ndi Anefi mu nkhondo—Moroni aveka Anefi ndi zida zodzitetezera—Ambuye aulura kwa Alima njira ya Alamani—Anefi ateteza nyumba zawo, maufulu, mabanja, ndi chipembedzo—Ankhondo a Moroni ndi Lehi azungulira Alamani. Mdzaka dza pafupifupi 74 Yesu asadabadwe.
1 Ndipo tsopano zidachitika kuti ana aamuna a Alima adapita pakati pa anthu, kukalalikira mawu kwa iwo. Ndipo Alima, nayenso, iyemwini, sadathe kupuma, ndipo nayenso adapita.
2 Tsopano sitidzakambanso zambiri zokhudzana ndi ulaliki wawo, kupatula kuti iwo adalalikira mawu, ndi choonadi, molingana ndi mzimu wa uneneri ndi vumbulutso; ndipo iwo adalalikira potsatira dongosolo loyera la Mulungu limene iwo adaitanidwira.
3 Ndipo tsopano ndibwelera ku nkhani ya nkhondo zapakati pa Anefi ndi Alamani, mu chaka cha khumi ndi chisanu ndi zitatu cha ulamuliro wa oweruza.
4 Pakuti taonani, zidachitika kuti Azoramu adakhala Alamani; kotero, kumayambiliro kwa chaka cha khumi ndi chisanu ndi zitatu, anthu achinefi adaona kuti Alamani adali kubwera pa iwo; kotero iwo adachita zokonzekera nkhondo, inde, iwo adasonkhanitsa pamodzi ankhondo awo mu dziko la Yerisoni.
5 Ndipo zidachitika kuti Alamani adabwera mu zikwi zawo; ndipo adabwera ku dziko la Antionamu, limene liri dziko la Azoramu; ndipo munthu otchedwa Zerahemuna adali mtsogoleri wawo.
6 Ndipo tsopano, monga Aamaleki adali anthu oipitsitsa ndi akhalidwe lokupha kuposera m’mene Alamani adaliri, mwa iwo ndi za iwo okha, kotero, Zerahemuna adasankha akulu ankhondo pa Alamani, ndipo onse adali Aamaleki ndi Azoramu.
7 Tsopano izi iye adachita kuti athe kusunga udani wawo kwa Anefi, kuti athe kuwabweretsa iwo m’kugonjera kwa kukwaniritsa zolinga zake.
8 Pakuti taonani, zolinga zake zidali zoti awutse Alamani ku mkwiyo motsutsana ndi Anefi; izi iye adachita kuti akhale ndi mphamvu zazikulu pa iwo, ndiponso kuti iye athe kupeza mphamvu pa Anefi powabweretsa iwo mu ukapolo.
9 Ndipo tsopano zolinga za Anefi zidali zoti ateteze dziko lawo ndi nyumba zawo, ndi akazi awo, ndi ana awo, kuti athe kuwateteza iwo m’manja mwa adani awo; ndiponso kuti akhonze kuteteza maufulu awo ndi mwayi wawo, inde, ndiponso ufulu wawo, kuti iwo ankhonze kulambira Mulungu molingana ndi zokhumba zawo.
10 Pakuti iwo adadziwa kuti ngati angagwe m’manja mwa Alamani, kuti aliyense amene angapembedze Mulungu mu mzimu ndi m’choonadi, Mulungu woona ndi wa moyo, Alamani adzawawononga.
11 Inde, ndipo iwo adadziwanso udani woipitsitsa wa Alamani kwa abale awo amene adali anthu a Anti-Nefi-Lehi, amene ankatchedwa anthu a Amoni—ndipo iwo sakadatha kutenga zida, inde, iwo adali atalowa mupangano ndipo sakadaliphwanya—kotero, ngati iwo angagwe m’manja mwa Alamani adzawonongedwa.
12 Ndipo Anefi sakadalora kuti iwo awonongedwe, kotero iwo adawapatsa iwo dziko la cholowa chawo.
13 Ndipo anthu a Amoni adapereka kwa Anefi gawo lalikulu la chuma chawo kuthandizira ankhondo awo; ndipo motero Anefi adakakamizika, okha, kulimbana motsutsana ndi Alamani, amene adali gulu la Lamani ndi Lemueli, ndi ana aamuna a Ismaeli, ndi onse amene adagawikana kuchoka kwa Anefi, amene adali Aamaleki ndi Azoramu, ndi zidzukulu za ansembe a Nowa.
14 Tsopano zidzukuludzo zidali zochuluka, pafupifupi, monga adaliri Anefi; ndipo motero Anefi adali okakamizidwa kulimbana ndi abale awo, ngakhale m’kukhetsa mwazi.
15 Ndipo zidachitika pamene ankhondo a Alamani adasonkhana pamodzi mu dziko la Antionamu, taonani, ankhondo a Anefi adali okonzeka kukumana nawo mu dziko la Yerisoni.
16 Tsopano, mtsogoleri wa Anefi; kapena munthu amene adasankhidwa kukhala mkulu wa ankhondo pa Anefi—tsopano mkulu wa ankhondoyu adatenga ulamuliro wa ankhondo onse a Anefi—ndipo dzina lake lidali Moroni.
17 Ndipo Moroni adatenga ulamuliro, ndi utsogoleri wa nkhondo zawo. Ndipo iye adali wa dzaka makumi awiri ndi zisanu zokha pamene iye adasankhidwa mkulu wa ankhondo pa ankhondo Achinefi.
18 Ndipo zidachitika kuti iye adakumana ndi Alamani m’malire a Yerisoni, ndipo anthu ake adali atanyamula malupanga, ndi zikwanje, ndi mitundu yonse ya zida zankhondo.
19 Ndipo pamene ankhondo Achilamani adaona kuti anthu a Nefi, kapena kuti Moroni, adakonzekeretsa anthu ake ndi zapachifuwa ndi zishango za mkono, inde, ndiponso zishango zoteteza mitu yawo, ndiponso adali atavala zovala zokhuthala—
20 Tsopano ankhondo a Zerahemuna sadakonzekere ndi chinthu chonga ichi; iwo adali ndi malupanga awo basi ndi zikwanje zawo, ndi mauta awo, ndi mikondo yawo, ndi miyala yawo ndi malegeni awo; ndipo adali amaliseche, kupatula chikopa chodzimangilira mchiuno mwawo; inde, onse adali maliseche, kupatula Azoramu ndi Aamaleki.
21 Koma iwo sadavale zapachifuwa, kapena zishango—kotero, iwo adaopa kwambiri chifukwa cha ankhondo Achinefi chifukwa cha zovala zawo, posatengera chiwerengero chawo chokhala chochuluka kwambiri kuposera cha Anefi.
22 Taonani, tsopano zidachitika kuti iwo sadayerekeze kubwera kudzamenyana ndi Anefi ku malire a Yerisoni; kotero iwo adachoka m’dziko la Antionamu kupita m’chipululu, ndipo adatenga ulendo mozungulira m’chipululu, kutali ndi mutu wa mtsinje wa Sidoni, kuti athe kubwera ku dziko la Manti ndi kulanda dzikolo; pakuti iwo sadaganizire kuti magulu ankhondo a Moroni angadziwe kumene iwo adapita.
23 Koma zidachitika, atangochoka kupita m’chipululu Moroni adatumiza akazitape ku chipululu kukasunzumira msasa wawo; ndipo Moroninso, podziwa za uneneri wa Alima, adatumiza amuna ena kwa iye, kufuna iye kuti afunse kwa Ambuye kumene ankhondo achinefi apite kuti akadziteteze okha motsutsana ndi Alamani.
24 Ndipo zidachitika kuti mawu a Ambuye adadza kwa Alima, ndipo Alima adauza anthenga a Moroni, kuti ankhondo achilamani adali kuguba mozungulira m’chipululu, kuti iwo akhonze kubwera ku dziko la Manti, kuti akhonze kuyamba kuwukira mbali yofooka ya anthu. Ndipo anthengawo adapita ndi kukapereka uthengawo kwa Moroni.
25 Tsopano Moroni, adasiya gawo la ankhondo ake mu dziko la Yerisoni, kuopa kuti mwa njira iliyonse gawo la Alamani lingabwere kulowa mudzikolo ndi kulanda mzindawo, natenga gawo lotsalira la ankhondo ake ndi kugubira ku dziko la Manti.
26 Ndipo iye adachititsa kuti anthu onse ku m’chigawo cha dziko chimenecho asonkhane pamodzi kuti amenyane ndi Alamani, kuteteza malo awo ndi dziko lawo, mwayi wawo ndi maufulu awo; kotero iwo adakonzekera molingana ndi nthawi yobwera ya Alamani.
27 Ndipo zidachitika kuti Moroni adachititsa kuti ankhondo ake abisale mu chigwa chimene chidali pafupi ndi mphepete mwa mtsinje wa Sidoni, chimene chidali kumadzulo kwa mtsinje wa Sidoni mu chipululu.
28 Ndipo Moroni adaika akazitape mozungulira, kuti iye akathe kudziwa pamene msasa wa Alamani udzabwera.
29 Ndipo tsopano, monga Moroni ankadziwa cholinga cha Alamani, kuti chidali cholinga chawo kuwononga abale awo, kapena kuwalamulira iwo ndi kuwabweretsa iwo mu ukapolo kuti akhonze kukhazikitsa ufumu kwa iwo eni pa dziko lonselo;
30 Ndipo iye podziwanso kuti chidali chikhumbo chokha cha Anefi kuteteza malo awo, ndi ufulu wawo, ndi mpingo wawo, kotero iye adaganiza kuti silidali tchimo kuti iye awateteze iwo mwaukathyali; kotero, adapeza kudzera mwa akazitape ake njira imene Anefi ankayenera kudutsa.
31 Kotero, iye adagawa ankhondo ake ndi kubweretsa gawo lina ku chigwa, ndi kuwabisa iwo cha kum’mawa, ndi cha kum’mwera kwa phiri la Ripila.
32 Ndipo otsalawo iye adawabisa ku chigwa chakumadzulo, chakumadzulo kwa mtsinje wa Sidoni, ndiponso kumusi kwa malire a dziko la Manti.
33 Ndipo motero ataika ankhondo ake molingana ndi khumbo lake, iye adali okonzeka kukumana nawo.
34 Ndipo zidachitika kuti Alamani adabwera cha ku mpoto kwa phiri, kumene gawo lina la ankhondo a Moroni adabisala.
35 Ndipo pamene Alamani adadutsa phiri la Ripila, ndikubwera ku chigwa, ndi kuyamba kuwoloka mtsinje wa Sidoni, ankhondo amene adabisala cha kumadzulo kwa phiri, amene ankatsogoleredwa ndi munthu amene dzina lake lidali Lehi, ndipo iye adatsogolera ankhondo ake ndi kuzungulira Alamani cha kum’mawa kumbuyo kwawo.
36 Ndipo zidachitika kuti Alamani, pamene adaona Anefiwo akubwera pa iwo chakumbuyo kwawo, adawatembenukira ndi kuyamba kulimbana ndi ankhondo a Lehi.
37 Ndipo ntchito yophana idayambika ku mbali zonse, koma idali yowopsya kwambiri ku mbali ya Alamani, chifukwa cha umalicheche wawo udakumana ndi nkhonya zazikulu za Anefi ndi malupanga awo ndi zikwanje zawo, zimene zidabweretsa imfa pafupifupi pa kumenya kulikonse.
38 Pamene kumbali inayi, kudali apa ndi apo munthu kugwa pakati pa Anefi, ndi malupanga ndi kutaya magazi, iwo potetezedwa ku ziwalo zofunikira za thupi, kapena ziwalo zofunikira kwambiri za thupi lawo zidali zotetezedwa ku nkhonya za Alamani, ndi zapachifuwa zawo, ndi zishango zawo, ndi zisoti zawo; ndipo motero Anefi adapitiriza ntchito yakupha pakati pa Alamani.
39 Ndipo zidachitika kuti adachita mantha, chifukwa cha chiwonongeko chachikulu pakati pawo, mpakana kufikira adayamba kuthawira chakumtsinje wa Sidoni.
40 Ndipo adathamangitsidwa ndi Lehi ndi anthu ake; ndipo adathamangitsidwa ndi Lehi ku madzi a Sidoni, ndipo adawoloka madzi a Sidoni. Ndipo Lehi adaimitsa ankhondo ake mu mphepete mwa mtsinje wa Sidoni kuti iwo asawoloke.
41 Ndipo zidachitika kuti Moroni ndi ankhondo ake adakumana ndi Alamani mu chigwa, kutsidya lina la mtsinje wa Sidoni, ndipo adayamba kugwera pa paiwo ndi kuwapha.
42 Ndipo Alamani adathawa kachiwiri pamaso pawo, kupita ku dziko la Manti; ndipo adakumananso ndi ankhondo a Moroni.
43 Tsopano mu nthawi iyi Alamani adamenyana kwambiri, inde, Alamani adali asadadziwikeponso kuti amenya nkhondo ndi mphamvu zochuluka ndi kulimba mtima kotere, ayi, ngakhale kuchokera pachiyambi.
44 Ndipo iwo adalimbikitsidwa ndi Azoramu ndi Aamaleki, amene adali akulu ankhondo awo ndi atsogoleri awo, ndipo ndi Zerahemuna, amene adali mkulu wa ankhondo wawo, kapena mtsogoleri wamkulu ndi olamulira; inde, iwo adamenyana ngati zinjoka, ndipo ambiri mwa Anefi adaphedwa ndi manja awo, inde, pakuti iwo adagaza pawiri mzisoti zawo, ndipo adalasa ambiri m’zapachifuwa zawo, ndipo adathyola mikono yawo yambiri; ndipo motero Alamani adaakantha mu mkwiyo wawo owopsya.
45 Komabe, Anefi adalimbikitsidwa ndi cholinga chabwino, pakuti iwo sadali kumenyera chifukwa cha ufumu kapena mphamvu koma adali kumenyera chifukwa cha nyumba zawo, ndi maufulu awo, akazi awo ndi ana awo, ndi zonse zawo, inde, chifukwa miyambo ya kupembedza kwawo ndi mpingo wawo.
46 Ndipo iwo adali kuchita zimene iwo adazimva kuti udali udindo umene adali nawo kwa Mulungu wawo; pakuti Ambuye adati kwa iwo ndiponso kwa makolo awo, kuti: Pamene monga inu simuli olakwa pa cholakwa choyamba, kapena chachiwiri, simudzazilora inu nokha kuphedwa ndi manja a adani anu.
47 Ndipo kachiwiri, Ambuye anena kuti: Mudzateteza mabanja anu ngakhale kufikira mu kukhetsa mwazi. Kotero pachifukwa ichi Anefi ankamenyana ndi Alamani, kuti adziteteze okha, ndi mabanja awo, ndi malo awo, ndi dziko lawo, ndi maufulu awo, ndi chipembedzo chawo.
48 Ndipo zidachitika kuti pamene anthu a Moroni adaona kukangalika ndi mkwiyo wa Alamani, adatsala pang’ono kusiya ndi kuthawa kwa iwo. Ndipo Moroni, poona cholinga chawo, adatuma ndi kulimbikitsa mitima yawo ndi maganizo awa—inde, maganizo a malo awo, maufulu awo, inde ufulu wawo kuchokera mu ukapolo.
49 Ndipo zidachitika kuti adatembenukira kwa Alamani, ndipo adafuula ndi mawu amodzi kwa Ambuye Mulungu wawo, chifukwa cha ufulu wawo ndi kumasulidwa kwawo ku ukapolo.
50 Ndipo adayamba kuima motsutsana ndi Alamani mwamphamvu; ndipo mu nthawi yomweyo yomwe iwo adafuula kwa Ambuye pa ufulu wawo, Alamani adayamba kuthawa pamaso pawo; ndipo adathawira ngakhale mpaka ku madzi a Sidoni.
51 Tsopano, Alamaniwo adali ochuluka kwambiri, inde, kuposera kawiri chiwerengero cha Anefi; komabe, adathamangitsidwa mpakana kuti iwo adasonkhanitsidwa pamodzi mu thupi limodzi mu chigwa, pa mphepete pa mtsinje wa Sidoni.
52 Kotero ankhondo a Moroni adawazungulira iwo, inde ngakhale kumbali zonse za mtsinje, pakuti taonani, chakum’mawa kudali anthu a Lehi.
53 Kotero pamene Zerahemuna adaona anthu a Lehi chakum’mawa kwa mtsinje wa Sidoni, ndi ankhondo a Moroni chakumadzulo kwa mtsinje wa Sidoni, kuti iwo azunguliridwa ndi Anefi, adagwidwa ndi mantha.
54 Tsopano Moroni, pamene adaona mantha awo, adalamulira anthu ake kuti asiye kukhetsa mwazi wawo.