Malembo Oyera
Alima 29


Mutu 29

Alima akhumbira kulalikira zakulapa ndi changu cha angelo—Ambuye apereka aphunzitsi a maiko wonse—Alima atamandira mu ntchito ya Ambuye komanso mu chipambano cha Amoni ndi abale ake. Mdzaka dza pafupifupi 76 Yesu asadabadwe.

1 O kuti ndikadakhala mngelo, ndi kukhala ndi zofuna za mtima wanga, kuti ndikhonza kupita ndi kuyankhula ndi lipenga la Mulungu, ndi mawu ogwedeza dziko lapansi, ndi kulalika zakulapa kwa anthu aliwonse!

2 Inde, ndikadalalikira kwa moyo uliwonse, monga ndi mawu a bingu, kulapa ndi dongosolo la chiwombolo, kuti iwo akuyenera kulapa ndi kubwera kwa Mulungu wathu, kuti kusakhale zisoni pa nkhope ya dziko lonse lapansi.

3 Koma taonani, ine ndine munthu, ndipo ndimachimwa mu zokhumba zanga, pakuti ndikuyenera kukhutiritsidwa ndi zinthu zomwe Ambuye adandipatsa ine.

4 Sindikuyenera kuzingwa mu zokhumba zanga lamulo lolimba la Mulungu wolungama, pakuti ndikudziwa kuti iye amapereka kwa anthu molingana ndi zokhumba zawo, ngakhale ziri kwa imfa kapena moyo, ndikudziwa kuti iye amapereka kwa anthu, inde, amalamula kwa iwo malamulo amene ali osasinthika, molingana ndi zokhumba zawo, ngakhale ziri kwa chipulumutso kapena chiwonongeko.

5 Inde, ndipo ndikudziwa kuti zabwino ndi zoipa zabwera pamaso pa anthu onse; iye amene samadziwa zabwino ku zoipa ali wopanda cholakwa; koma iye amene amadziwa zabwino ndi zoipa, kwa iye kwapatsidwa molingana ndi zokhumba zake, ngakhale iye akhumbe zabwino kapena zoipa, moyo kapena imfa, chisangalalo kapena chisoni cha chikumbu mtima.

6 Tsopano, poona kuti ndikudziwa zinthu zimenezi, ndikhumbiranji kuchita zambiri kuposa ntchito imene ine ndidaitanidwira?

7 Ndikhumbiranji kuti ndikhale mngelo, kuti ndiyankhule kwa anthu kumathero wonse a dziko lapansi?

8 Pakuti taonani, Ambuye amapereka kwa maiko wonse, a dziko lawo ndi lilime lawo lomwe, kuti aphunzitse mawu ake, inde, mu nzeru, zonse zimene iye waona zoyenera kuti iwo akhale nazo; kotero tikuona kuti Ambuye amalangiza mwa nzeru, molingana ndi zimene ziri zolungama ndi zoona.

9 Ndikudziwa zimene Ambuye wandilamula ine, ndipo ine ndimatamandira mu izo. Sindimadzitamandira mwa ine ndekha, koma ndimatamandira mu zomwe Ambuye andilamula ine, inde, ndipo uwu ndiwo ulemelero wanga, kuti mwina ndikhale chida m’manja mwa Mulungu chobweretsera moyo wina m’kulapa; ndipo ichi ndiye chisangalalo changa.

10 Ndipo taonani, pamene ine ndaona kuti abale anga alapa moonadi, ndi kubwera kwa Ambuye Mulungu wawo, pamenepo moyo wanga ndiodzala ndi chisangalalo; kenako ndikukumbukira zimene Ambuye achita kwa ine, inde, ngakhale kuti iye wamva pemphero langa; inde, kenako ndikukumbukira mkono wake wachifundo umene watambasulidwa kwa ine.

11 Inde, ndiponso ndikukumbukira ukapolo wa makolo anga; pakuti indedi ndikudziwa kuti Ambuye adawapulumutsa iwo ku ukapolo, ndipo pa ichi adakhazikitsa mpingo wake; inde, Ambuye Mulungu, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isaki, ndi Mulungu wa Yakobo, adawapulumutsa iwo mu ukapolo.

12 Inde, ndakhala nthawi zonse ndikukumbukira za ukapolo wa makolo anga; Mulungu yemweyo amene adapulumutsa iwo kuchoka m’manja mwa Aigupto adawapulumutsa iwo mu ukapolo.

13 Inde, ndipo Mulungu yemweyo adakhazikitsa mpingo pakati pa iwo; inde, ndipo Mulungu yemweyo waitana ine mu mayitanidwe oyera, kuti ndilalikire mawu kwa anthu awa, ndipo wandipatsa ine chipambano chambiri, momwe chisangalalo changa chadzadza.

14 Koma ine sindisangalala mu chipambano changa chokha, koma chisangalalo changa chili chodzadza kwambiri chifukwa cha chipambano cha abale anga, amene akhala mu dziko la Nefi.

15 Taonani, iwo agwira ntchito kwambiri, ndipo abweretsa zipatso zochuluka; ndipo idzakhala yaikulu bwanji mphotho yawo!

16 Tsopano, pemene ine ndiganiza za kupambana kwa awa abale angawa mzimu wanga umatengedwera kutali, ngakhale m’kulekanitsidwa kwake ndi thupi, monga zidaliri, choncho chisangalalo changa n’chachikulu.

17 Ndipo tsopano Ambuye apereke kwa awa, abale anga, kuti iwo adzakhale pansi mu ufumu wa Mulungu; inde, ndiponso wonse amene ali zipatso za ntchito yawo kuti iwo asatulukemonso, koma kuti adzamutamande iye kwamuyaya. Ndipo Mulungu apereke kuti zichitike monga mwa mawu anga, ngakhale monga ine ndayankhulira. Ameni.

Print