Malembo Oyera
Alima 50


Mutu 50

Moroni alimbitsa maiko Achinefi—Iwo amanga mizinda yatsopano yambiri—Nkhondo ndi chiwonongeko zigwera pa Anefi m’masiku a zoipa ndi zonyansa zawo—Moriyantoni ndi ogalukira ake agonjetsedwa ndi Teyankumu—Nefiha amwalira, ndipo mwana wake wamwamuna Pahorani alowa pa mpando wa chiweruzo. Mdzaka dza pafupifupi 72–67 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo tsopano zidachitika kuti Moroni sadasiye kuchita zokonzekera nkhondo, kapena kutetezera anthu ake motsutsana ndi Alamani; pakuti iye adapangitsa kuti ankhondo ake ayambepo chakumayambiliro a chaka cha makumi awiri cha ulamuliro wa oweruza, kuti iwo ayambe kukumba nthumbira zadothi kuzungulira mizinda yonse, kuzungulira maiko onse amene ankakhalidwa ndi Anefi.

2 Ndipo pamwamba pa nthumbira zadothipo iye adapangitsa kuti pakhale matabwa, inde, ntchito za matabwa zomangidwa kufika msinkhu wa munthu, kuzungulira mizindayo.

3 Ndipo iye adachititsa kuti pa ntchito zamatabwapo pamangidwe zomanga zosongola pamatabwapo mozungulira, ndipo zidali zolimba ndi zotalika.

4 Ndipo iye adachititsa kuti nsanja zikhomedwe zimene zimayang’ana ku ntchito ya zomanga zosongolazo, ndipo adachititsa malo a chitetezo kuti amangidwe pansanjapo, kuti miyala ndi mivi ya Alamani isawavulaze.

5 Ndipo iwo adakonzekera kuti akathe kuponya miyala kuchokera pamwamba pake, molingana ndi kukonda kwawo ndi mphamvu zawo, ndi kupha iye amene angayesere kufika pafupi ndi makoma a mzindawo.

6 Motero Moroni adakonza malinga motsutsana ndi kubwera kwa adani awo, mozungulira mizinda yonse mu dziko lonselo.

7 Ndipo zidachitika kuti Moroni adachititsa kuti ankhondo ake apite ku chipululu chakum’mawa; inde, ndipo iwo adapita ndi kuthamangitsira Alamani onse amene adali m’chipululu cha kum’mawako ku maiko awo, amene adali kum’mwera kwa dziko la Zarahemula.

8 Ndipo dziko la Nefi lidali loyenda njira yolunjika kuchokera ku nyanja ya kum’mawa kupita kumadzulo.

9 Ndipo zidachitika kuti pamene Moroni adathamangitsa Alamani onse kuchoka ku chipululu chakum’mawako, chimene chidali kumpoto kwa maiko awo, iye adachititsa kuti okhalako amene adali mu dziko la Zarahemula ndi mu dziko lozungulira apite ku chipululu chakum’mawako, ngakhale kumalire a gombe lanyanja, ndi kutenga dzikolo.

10 Ndipo iye adaika ankhondo chakum’mwera, kumalire kwawo, ndi kuchititsa iwo kuti aike mipanda kuti atetezere ankhondo awo ndi anthu awo m’manja mwa adani awo

11 Ndipo motero iye adadula malinga onse a Alamani chakum’mawa kwa chipululu, inde, ndiponso chakumadzulo, kulimbitsa malire pakati pa Anefi ndi Alamani, pakati pa dziko la Zarahemula ndi dziko la Nefi, kuchokera ku nyanja ya kumadzulo, kudzera ku mutu wamtsinje wa Sidoni—Anefi kukhala ndi dziko lonse lakumpoto, inde, ngakhale dziko lonse limene lidali chakumpoto kwa dziko la Chuluka, molingana ndi kukonda kwawo.

12 Motero Moroni, ndi ankhondo ake amene ankachulukira tsiku ndi tsiku chifukwa cha chitsimikizo cha chitetezo chimene ntchito zake zidabweretsa kwa iwo, adafuna kudula nyonga ndi mphamvu za Alamani kuchoka ku maiko awo, kuti iwo asakhale ndi mphamvu pa maiko awo.

13 Ndipo zidachitika kuti Anefi adayamba maziko a mzinda, ndipo adatcha dzina la mzindawo Moroni, ndipo udali chakunyanja ya kum’mawa; ndipo udali chakum’mwera pa malire wokhalako Alamani.

14 Ndipo iwo adayambanso maziko a mzinda wapakati pa mzinda wa Moroni ndi mzinda wa Aroni, kulumikiza malire a Aroni ndi Moroni; ndipo adatcha dzina la mzindawo, kapena dzikolo, Nefiha.

15 Ndipo iwo adayambanso mu chaka chomwecho kumanga mizinda yambiri chakumpoto, umodzi m’njira inayake umene adautcha Lehi, umene udali kumpoto chakumalire a gombe la nyanja.

16 Ndipo motero chidatha chaka cha makumi awiri.

17 Ndipo munyengo zakuchita bwino zimenezi anthu a Nefi adali m’mayambiliro chaka cha makumi awiri ndi chimodzi cha ulamuliro wa oweruza pa anthu a Nefi

18 Ndipo iwo adachita bwino kwambiri, ndipo adakhala olemera kwambiri; inde, ndipo adachulukana ndi kukula m’mphamvu mudzikolo.

19 Ndipo motero tikuona momwe machitidwe onse a Ambuye alili achifundo ndi olungama, kuti akwaniritse mawu ake onse kwa ana a anthu; inde, tikhonza kuona kuti mawu ake atsimikizidwa, ngakhale pa nthawi imeneyi, imene iye adayankhula kwa Lehi, kuti:

20 Odala ndi iwe ndi ana ako; ndipo adzadalitsika, pamene iwo adzasunga malamulo anga, iwo adzachita bwino mu dziko. Koma kumbukira, kuti pamene iwo sadzasunga malamulo anga, iwo adzachotsedwa kuchoka pamaso pa Ambuye.

21 Ndipo tikuona kuti malonjezo awa atsimikizidwa kwa anthu a Nefi; pakuti idali mitsutsano yawo, ndi mikangano yawo, inde, kuphana kwawo, ndi umbanda wawo, ndi kupembedza mafano kwawo, ndi zigololo zawo, ndi zadama zawo, ndi zonyansa zawo, zimene zidali pakati pawo, zimene zidabweretsa pa iwo nkhondo zawo ndi chiwonongeko chawo.

22 Ndipo iwo amene adali wokhulupirika pakusunga malamulo a Ambuye adapulumutsidwa mu nthawi zonse, pamene zikwi za abale awo oipa zidatengedwa ku ukapolo, kapena kuwonongeka ndi lupanga, kapena kucheperachepera m’kusakhulupilira, ndi kusanganikirana ndi Alamani.

23 Koma taonani sikudakhalepo nthawi yachimwemwe pakati pa anthu a Nefi, kuyambira m’masiku a Nefi kuposa m’masiku a Moroni, inde, ngakhale pa nthawi imeneyi, mu chaka cha makumi awiri ndi chimodzi cha ulamuliro wa oweruza.

24 Ndipo zidachitika kuti chaka cha makumi awiri ndi ziwiri cha ulamuliro wa oweruza chidathanso mumtendere; inde, ndiponso chaka cha makumi awiri ndi zitatu.

25 Ndipo zidachitika kuti kumayambiliro kwa chaka cha makumi awiri ndi chinayi cha ulamuliro wa oweruza, kukadakhalanso mtendere pakati pa anthu a Nefi kukadapanda kukhala mkangano umene udachitika pakati pa iwo okhudzana ndi dziko la Lehi, ndi dziko la Moriyantoni, limene lidakumanizana pa malire a Lehi, onse amene adali ku malire ndi gombe lanyanja.

26 Pakuti taonani, anthu amene adali mu dziko la Moriyantoni adatenga mbali ya dziko la Lehi; kotero padayamba kukhala mkangano wotentha pakati pawo, kufikira kuti anthu a Moriyantoni adatenga zida motsutsana ndi abale awo, ndipo iwo adali otsimikizika ndi lupanga kuti awaphe iwo.

27 Koma taonani, anthu amene adali mu dziko la Lehi adathawira ku msasa wa Moroni, ndipo adapempha kwa iye chithandizo; pakuti taonani iwo sadali olakwa.

28 Ndipo zidachitika kuti pamene anthu a Moriyantoni, amene ankatsogoleredwa ndi munthu amene dzina lake lidali Moriyantoni, adapeza kuti anthu a Lehi adathawira ku msasa wa Moroni, iwo adali ndi mantha aakulu kuopa kuti ankhondo a Moroni angabwere pa iwo ndi kudzawawononga.

29 Kotero, Moriyantoni adachiika ichi m’mitima mwawo kuti iwo athawire ku dziko limene lidali chakumpoto, limene lidali lokutidwa ndi madzi ambiri, ndi kulitenga dzikolo limene lidali chakumpoto.

30 Ndipo taonani, iwo akadakwaniritsa dongosolo limeli kuti litheke, (limene likadakhala chifukwa chodandaulitsa) koma taonani, Moriyantoni wokhala munthu wachikhumbo chochuluka, kotero iye adakwiya ndi m’modzi mwa antchito ake aakazi, ndipo iye adagwa pa iye ndi kum’menya kwambiri.

31 Ndipo zidachitika kuti iye adathawa, ndi kufika ku msasa wa Moroni, ndi kumuuza Moroni zinthu zonse zokhudzana ndi nkhaniyo, ndiponso zokhudzana ndi zolinga zawo zothawira ku dziko lakumpoto.

32 Tsopano taonani, anthu amene adali ku dziko la Chuluka, kapena kuti Moroni, adaopa kuti iwo atha kumvetsera mawu a Moriyantoni ndi kugwirizana ndi anthu ake, ndipo choncho iye adzalanda mbali zimenezo za dziko, zimene zikadatha kuika maziko a zotsatira zazikulu pakati pa anthu a Nefi, inde, zimene zotsatira zake zikadapangitsa kugwetsedwa kwa ufulu wawo.

33 Kotero Moroni adatumiza ankhondo, ndi msasa wawo, kuti awaimitse anthu a Moriyantoni, kuti aletse kuthawira kwawo ku dziko lakumpoto.

34 Ndipo zidachitika kuti iwo sadawaimitse mpakana iwo adafika ku malire a dziko la Bwinja; ndipo kumeneko iwo adawaimitsa, pakanjira kakan’gono kamene kamadzera kufupi ndi nyanja ku dziko lakumpoto, inde, kufupi ndi nyanja, chakumadzulo komanso kum’mawa.

35 Ndipo zidachitika kuti ankhondo amene adatumizidwa ndi Moroni, amene ankatsogoleredwa ndi munthu amene dzina lake lidali Teyankumu, adakumana ndi anthu a Moriyantoni; ndipo anthu a Moriyantoni adali amakani, (polimbikitsidwa ndi kuipa kwake ndi mawu ake opusitsa) kuti nkhondo idayambika pakati pawo, imene mkati mwake Teyankumu adapha Moriyantoni ndi kugonjetsa ankhondo ake, ndi kuwatenga iwo ukaidi, ndi kubwelera ku msasa wa Moroni. Ndipo motero chidatha chaka cha makumi awiri ndi zinayi cha ulamuliro wa oweruza pa anthu a Nefi.

36 Ndipo motero anthu a Moriyantoni adabwenzeretsedwa. Ndipo pamene adapanga pangano lawo losunga mtendere iwo adabwenzeretsedwa ku dziko la Moriyantoni, ndipo mgwirizano udachitika pakati pawo ndi anthu a Lehi; ndipo iwo adabwenzeretsedwanso ku maiko awo.

37 Ndipo zidachitika kuti mu chaka chomwecho chimene anthu a Nefi adali atabwenzeretsedwa mtendere wawo, kuti Nefiha, mkulu wa oweruza wachiwiri, adamwalira, atakhala pa mpando wa chiweruzo mwa chilungamo changwiro pamaso pa Mulungu.

38 Komabe, iye adamkanira Alima kutenga zolemba zimenezo ndi zinthu izo zimene zidalemekezedwa ndi Alima ndi makolo ake kukhala zopatulika kwambiri; kotero Alima adazipereka kwa mwana wake, Helamani.

39 Taonani, zidachitika kuti mwana wamwamuna wa Nefiha adasankhidwa kukhala pa mpando wa chiweruzo, m’malo mwa bambo ake; inde, iye adasankhidwa mkulu wa oweruza ndi kazembe wa anthu, ndi lumbiro ndi mwambo opatulika kuti akaweruze mwachilungamo, ndi kusunga mtendere ndi ufulu wa anthu, ndi kuwapatsa iwo mwayi wawo wopatulika wa kupembedza Ambuye Mulungu wawo, inde, kuthandiza ndi kusamala ntchito ya Mulungu m’masiku ake onse, ndi kubweretsa oipa kuchilungamo molingana ndi mulandu wawo.

40 Tsopano taonani, dzina lake lidali Pahorani. Ndipo Pahorani adakhala pa mpando wa atate ake, ndipo adayamba ulamuliro wake kumapeto kwa chaka cha makumi awiri ndi chinayi, pa anthu a Nefi.

Print