Malembo Oyera
Alima 30


Mutu 30

Koriho, wotsutsa Khristu, anyoza Khristu, chitetezero, ndi mzimu wa uneneri—Iye aphunzitsa kuti kulibe Mulungu, kulibe kugwa kwa munthu, kulibe chilango cha tchimo, ndipo kulibe Khristu—Alima achitira umboni kuti Khristu adzabwera ndipo zinthu zonse zimasonyeza kuti kuli Mulungu—Koriho apempha chizindikiro ndipo akanthidwa ndikukhala wosayankhula—Mdyerekezi adaonekera kwa Koriho monga mngelo ndipo adam’phunzitsa zoti anene—Koriho apondedwa pansi ndipo amwalira. Mdzaka dza pafupifupi 76–74 Yesu asadabadwe.

1 Taonani, tsopano zidachitika kuti atamaliza anthu a Amoni kukhazikika mu dziko la Yeresoni, inde, ndiponso Alamani atathamangitsidwa kunja kwa dzikolo, ndipo akufa awo adakwiliridwa ndi anthu am’dzikolo—

2 Tsopano akufa awo sadawerengedwe chifukwa cha kuchuluka kwa chiwerengero chawo; ngakhalenso akufa a Anefi sadawerengedwe—koma zidachitika kuti atatha kukwilira akufa awo, komanso atamaliza masiku akusala kudya, ndi kulira, ndi pemphero, (ndipo chidali chaka chakhumi ndi chisanu ndi chimodzi cha ulamuliro wa oweruza pa anthu a Nefi) kudayamba kukhala mtendere wopitilira ku dziko lonselo.

3 Inde, ndipo anthuwo adatsata kusunga malamulo a Ambuye; ndipo adali okhwima pakusunga miyambo ya Mulungu, molingana ndi lamulo la Mose; pakuti iwo adaphunzitsidwa kusunga lamulo la Mose kufikira ilo lidzakwaniritsidwe.

4 Ndipo choncho anthuwo sadakhale ndi chisokonezo mu chaka chonse cha khumi ndi chisanu n’chimodzi cha ulamuliro wa oweruza pa anthu a Nefi.

5 Ndipo zidachitika kuti kumayambiliro kwa chaka cha khumi ndi chisanu ndi ziwiri cha ulamuliro wa oweruza, kudali mtendere wopitilira.

6 Koma zidachitika kumapeto a chaka chakhumi ndi chisanu ndi ziwiri, kudabwera munthu mudziko la Zarahemula, ndipo adali wotsutsa Khristu, pakuti adayamba kulalikira kwa anthu motsutsana ndi mauneneri amene adanenedwa ndi aneneri, zokhudzana ndi kubwera kwa Khristu.

7 Tsopano kudalibe lamulo lotsutsa chikhulupiliro cha munthu; pakuti zidali zosemphana kwambiri ndi malamulo a Mulungu kuti kukhale lamulo limene likuyenera kubweretsa anthu ku zifukwa zosalingana.

8 Pakuti malembo oyera amati: Sankhani inu lero lino, amene inu mudzamtumikira.

9 Tsopano ngati munthu akhumba kutumikira Mulungu, udali mwayi wake; kapena kuti, ngati iye akhulupilira mwa Mulungu udali mwayi wake kumtumikira iye; koma ngati iye sadakhulupilire mwa iye kudalibe lamulo lomulanga iye.

10 Koma ngati iye apha ankalangidwa pakuphedwa; ndipo ngati iye walanda ankalangidwanso; ndipo ngati iye waba ankalangidwanso; ndipo ngati iye wachita chigololo ankalangidwanso; inde, pa zoipa zonsezi iwo ankalangidwa.

11 Pakuti padali lamulo kuti anthu akuyenera kuweruzidwa molingana ndi zolakwa zawo. Komabe, kudalibe lamulo loletsa chikhulupiliro cha munthu; kotero, munthu ankalangidwa pa zoipa zimene iye wachita basi; kotero anthu onse adali pa zifukwa zofanana.

12 Ndipo wotsutsa Khristuyu, amene dzina lake lidali Koriho, (ndipo lamulo silikadatha kugwira ntchito pa iye) adayamba kulalikira kwa anthu kuti sikudzakhala Khristu. Ndipo moteremu iye ankalalikira, nati:

13 O inu amene mwamangidwa pansi pa chiyembekezo chopusa ndi chopanda pake, n’chifukwa chiyani mumadzimanga m’goli ndi zinthu zopusa chotere? N’chifukwa chiyani mukuyang’anira pa Khristu? Pakuti palibe munthu amene angathe kudziwa chilichonse chimene chili nkudza.

14 Taonani, zinthu izi zimene inu mumazitcha mauneneri, zimene inu mukuti zaperekedwa kuchokera kwa aneneri oyera, taonani, ndi miyambo yopusa ya makolo anu.

15 Mukudziwa bwanji za chitsimikizo chawo? Taonani, inu simungadziwe za zinthu zimene simukuziona; kotero simungadziwe kuti kudzakhala Khristu.

16 Inu mukuyang’ana kutsogolo ndikunena kuti mukuona chikhululukiro cha machimo anu. Koma taonani, izi ndi zotsatira za maganizo openga; ndipo kusokonezeka kwa maganizoku kukubwera chifukwa cha miyambo ya makolo anu, imene ikukutsogolerani inu mu kukhulupilira zinthu zimene sizili choncho.

17 Ndipo zinthu zina zambiri iye adanena kwa iwo, kuwauza iwo kuti sikudzakhala chitetezero chopangidwa ku machimo a anthu, koma munthu aliyense adzakhala mudziko lapansili molingana ndi kakhalidwe ka cholengedwa; kotero munthu aliyense amachita bwino molingana ndi luso lake, ndipo kuti munthu aliyense adagonjetsa molingana ndi mphamvu zake; ndipo chilichonse chomwe munthu ankachita sichidali mulandu.

18 Ndipo motere iye adalalikira kwa iwo, kusocheretsetsa mitima ya anthu ambiri, kuwapangitsa iwo kukweza mitu yawo ku zoipa zawo, inde, kutsogolera azimayi ambiri, ndiponso azibambo, kuchita zachiwerewere—kuwauza iwo kuti pamene munthu wamwalira, amenewo ndi mathero ake.

19 Tsopano munthu uyu adapitanso ku dziko la Yeresoni, kukalalikira zinthu izi pakati pa anthu a Amoni, amene poyamba adali anthu Achilamani.

20 Koma taonani iwo adali anzeru kuposa ambiri Achinefi; pakuti iwo adamtenga iye, ndi kum’manga, ndi kumutengera iye pamaso pa Amoni, amene adali mkulu wansembe pa anthu amenewo.

21 Ndipo zidachitika kuti iye adachititsa kuti iye anyamulidwe kunja kwa dzikolo. Ndipo adabwera ku dziko la Gideoni, ndipo adayamba kulalikiranso kwa iwo; ndipo uku iye sadakhale ndi chipambano chachikulu, pakuti adatengedwa ndi kumangidwa ndi kutengeredwa pamaso pa mkulu wansembe, ndiponso mkulu wa oweruza pa dzikolo.

22 Ndipo zidachitika kuti mkulu wansembe adati kwa iye: N’chifukwa chiyani umayendayenda kupotoza njira za Ambuye? N’chifukwa chiyani umaphunzitsa anthu awa kuti sikudzakhala Khristu, kuti usokoneze chikondwelero chawo? N’chifukwa chiyani iwe umayankhula motsutsana ndi mauneneri onse a aneneri oyera?

23 Tsopano dzina la mkulu wansembeyo lidali Gidona. Ndipo Koriho adati kwa iye: Chifukwa sindiphunzitsa miyambo yopusa ya makolo anu, ndipo chifukwa sindiphunzitsa anthu awa kuti adzimangilire pansi pa miyambo yopusa ndi machitidwe amene adaikidwa ndi ansembe akale, kuti alande mphamvu ndi ulamuliro pa iwo, kuwasunga iwo mu umbuli, kuti iwo asakweze mitu yawo, koma kuti agwetsedwe pansi molingana ndi mawu anu.

24 Inu mukuti anthu awa ndi anthu aufulu. Taonani, ine ndikuti iwo ali mu ukapolo. Inu mukunena kuti mauneneri akale ndi woona. Taonani, ine ndikunena kuti inu simukudziwa kuti ndi woona.

25 Inu mukunena kuti anthu awa ndi olakwa komanso anthu akugwa, chifukwa cha kulakwitsa kwa kholo. Taonani, ine ndikunena kuti mwana sali olakwa chifukwa cha makolo ake.

26 Ndipo inu mukunena kuti Khristu adzabwera. Koma taonani, ine ndikunena kuti inu simukudziwa kuti kudzakhala Khristu. Ndipo inu mukunena kuti iye adzaphedwa chifukwa cha machimo a dziko lapansi—

27 Ndipo choncho mukusocheletsa anthu awa potsata miyambo yopusa ya makolo anu, ndipo molingana ndi zikhumbo zanu; ndipo mumawasunga pansi, inde monga ngati zidaliri mu ukapolo, cholinga inu muzidyelera ndi ntchito za manja awo, kuti iwo asayerekeze kuyang’ana m’mwamba ndi kulimba mtima, ndipo kuti iwo asayerekeze kukondwera ndi maufulu ndi mwayi wawo.

28 Inde, iwo sakuyerekeza kugwiritsa ntchito zomwe zili zawo kuopa kuti angakhumudwitse ansembe awo, amene amawamanga m’goli iwo molingana ndi zokhumba zawo, ndipo awabweretsa iwo m’kukhulupilira, mwa miyambo yawo ndi maloto awo ndi mafuno awo, ndi masomphenya awo, ndi zinsinsi zopeka, kuti adzichita, ngati iwo sadachite molingana ndi mawu awo, akhumudwitse munthu wina osadziwika, amene iwo amati ndi Mulungu—munthu amene sadaonekepo kapena kudziwika, amene sadakhalepo kapena kudzakhalapo.

29 Tsopano pamene mkulu wansembe ndi mkulu wa oweruza adaona kuuma mtima kwake, inde, pamene adaona kuti iye akunyoza ngakhale Mulungu, iwo sadamuyankhe kalikonse ku mawu ake; koma adachititsa kuti iye amangidwe; ndipo adamubweretsa iye m’manja mwa adindo, ndi kumutumiza iye ku dziko la Zarahemula, kuti iye akapititsidwe pamaso pa Alima, ndi mkulu wa oweruza amene adali olamulira dziko lonselo.

30 Ndipo zidachitika kuti pamene iye adabweretsedwa pamaso pa Alima ndi mkulu wa oweruza, iye adapitiriza momwe adachitira pamene adali mudziko la Gideoni; inde iye adapitiriza kunyoza.

31 Ndipo iye adaima mu mawu otukumuka pamaso pa Alima, ndipo iye adanyoza ansembe ndi aphunzitsi, kuwazenga iwo kuti akusocheretsa anthu potsata miyambo yopusa ya makolo awo, ndi cholinga chofuna kukhuta pa ntchito za anthu.

32 Tsopano Alima adati kwa iye: Iwe ukudziwa kuti ife sitidzikhutitsa tokha pa ntchito za anthu awa; pakuti taona ine ndagwira ntchito ngakhale pachiyambi cha ulamuliro wa oweruza kufikira tsopano, ndi manja anga kuti ndidzithandize, posaganizira za maulendo anga ambiri kuzungulira dziko lonseli kulalikira mawu a Mulungu kwa anthu anga.

33 Ndipo posaganizira ntchito zambiri zimene ine ndidachita mu mpingo, sindidalandire kanthu ngakhale monga senine m’modzi pa ntchito yanga; ngakhale abale anga kulandira, kupatula ndiri pa mpando wa chiweruzo; ndipo pamenepo ife talandira zokhazo zolingana ndi lamulo la nthawi yathu.

34 Ndipo tsopano, ngati ife sitilandira kalikonse pa ntchito yathu mu mpingo, zitipindulira chiyani ife kugwira ntchito mu mpingomo kupatula kulalikira choonadi, kuti ife tikhale ndi chisangalaro mu chimwemwe cha abale athu?

35 Nanga bwanji iwe ukunena kuti ife timalalikira kwa anthu awa kuti tipeze phindu, pamene iwe, mwa wekha, ukudziwa kuti ife sitilandirapo phindu? Ndipo tsopano, kodi ukukhulupilira kuti ife tikunamiza anthu awa, zimene zimabweretsa chimwemwe chotere m’mitima mwawo?

36 Ndipo Koriho adamuyankha iye, Inde.

37 Ndiye Alima adati kwa iye: Kodi ukukhulupilira kuti kuli Mulungu?

38 Ndipo iye adayankha, Ayi.

39 Tsopano Alima adati kwa iye: Kodi udzakananso kuti kuli Mulungu, ndiponso kumukana Khristu? Pakuti taona, ndikunena kwa iwe, ndikudziwa kuti kuli Mulungu, ndiponso kuti Khristu adzabwera.

40 Ndipo tsopano kodi ndi umboni wanji umene uli nawo kuti kulibe Mulungu, kapena kuti Khristu sadzabwera? Ndikunena kwa iwe kuti ulibe, kupatula akhale mawu ako okha.

41 Koma, taona, ine ndili ndi zinthu zonse ngati umboni kuti zinthu izi ndi zoona; ndipo iwenso uli ndi zinthu zonse ngati umboni kwa iwe kuti ndi zoona; ndipo kodi iwe uzikana zimenezo? Kodi ukukhulupilira kuti zinthu izi ndi zoona?

42 Taona, ndikudziwa kuti iwe umakhulupilira, koma iwe wagwidwa ndi mzimu wabodza, ndipo iwe wathamangitsa Mzimu wa Mulungu kuti usakhale ndi malo mwa iwe; koma mdyerekezi ali ndi mphamvu pa iwe, ndipo iye amakunyamula iwe, kupanga njira zoti awononge ana a Mulungu.

43 Ndipo tsopano Koriho adati kwa Alima: Ngati iwe ungandionetse ine chizindikiro, kuti ndithe kutsimikizilidwa kuti kuli Mulungu, inde, undionetse ine kuti iye ali ndi mphamvu, ndipo pamenepo ine ndidzatsimikizika za choona cha mawu ako.

44 Koma Alima adati kwa iye: iwe ulinazo zizindikiro zokwanira; kodi udzayesa Mulungu wako? Kodi udzati, Ndionetseni ine chizindikiro, pamene iwe uli ndi umboni wa abale ako onsewa, ndiponso aneneri oyera onse? Malembo oyera aikidwa pamaso pako, inde, ndipo zinthu zonse zimasonyeza kuti kuli Mulungu; inde, ngakhale dziko lapansi, ndi zinthu zonse zimene ziri pa nkhope yake, inde, ndi kayendedwe kake, inde, ndiponso mapulaneti onse amene amayenda mu kakonzedwe kake zimachitira umboni kuti kuli Mlengi Wamkulu.

45 Ndipo chonchobe iwe umayendayenda, kusocheletsa mitima ya anthu awa, kuchitira umboni kwa iwo kuti kulibe Mulungu? Ndipo choncho kodi iwe ukukanabe motsutsana ndi mboni zonsezi? Ndipo iye adati: Inde, ndidzakana, pokhapokha mutandionetsa chizindikiro.

46 Ndipo tsopano zidachitika kuti Alima adanena kwa iye: Taona, ine ndili ndi chisoni chifukwa cha kuuma kwa mtima kwako, inde: kuti iwe ukukanabe mzimu wa choonadi, kuti moyo wako ukhonza kuwonongedwa.

47 Koma taona, ndikwabwino kuti moyo wako uwonongedwe koposa kuti iwe ukhale njira yobweretsera miyoyo yochuluka kuchiwonongeko, ndi bodza lako ndi mawu ako wopusitsa; kotero ngati iwe udzakanebe, taona Mulungu adzakukantha iwe kuti udzakhala wosayankhula, kuti iwe sudzatsekulanso kamwa lako, kuti iwe usadzanamizenso anthu awa.

48 Tsopano Koriho adati kwa iye: ine sindikukana za kupezeka kwa Mulungu, koma sindikhulupilira kuti kuli Mulungu; ndipo ndikunenanso, kuti iwe sukudziwa kuti kuli Mulungu; ndipo pokhapokha undionetse ine chizindikiro, ine sindidzakhulupilira.

49 Tsopano Alima adati kwa iye: Ichi ndidzakupatsa iwe ngati chizindikiro, kuti iwe udzakanthidwa kuti ukhala wosayankhula, molingana ndi mawu anga; ndipo ndikunena, kuti mu dzina la Mulungu, iwe udzakanthidwa nkukhala osayankhula, kuti iwe sudzayankhulanso.

50 Tsopano pamene Alima adanena mawu awa, Koriho adakanthidwa kukhala osayankhula, kuti iye sadathenso kuyankhula molingana ndi mawu a Alima.

51 Ndipo tsopano pamene mkulu wa oweruza adaona izi, adatambasula dzanja lake ndipo adalemba kwa Koriho, nati: Tsopano watsimikiza za mphamvu ya Mulungu? Mwa amene iwe umakhumba kuti Alima akuonetse chizindikiro chake? Kodi ukufuna kuti iye asautse ena, kuti awonetse kwa iwe chizindikiro? Taona, iye wakuonetsa iwe chizindikiro; ndipo tsopano kodi upitiriza kutsutsa?

52 Ndipo Koriho adatambasula dzanja lake ndi kulemba, nati: Ndikudziwa kuti ndine osayankhula, pakuti sindingayankhule; ndipo ndikudziwa kuti palibe chilichonse kupatula mphamvu ya Mulungu ingabweretse ichi pa ine; inde, ndipo nthawi zonse ndinkadziwa kale kuti kuli Mulungu.

53 Koma taonani, mdyerekezi adandinamiza ine; pakuti adaonekera kwa ine ngati mngelo, ndipo adati kwa ine: Pita ndi kapulumutse anthu awa, pakuti wonsewo asochera potsata Mulungu osadziwika. Ndipo adati kwa ine: Kulibe Mulungu, inde, ndipo adandiphunzitsa ine zoti ndiyankhule. Ndipo ine ndaphunzitsa mawu ake; ndipo ndawaphunzitsa chifukwa adali okoma kwa maganizo achithupithupi; ndipo ine ndawaphunzitsa iwo, kufikira ndidakhala ndi chipambano chachikulu, mpakana kuti ine ndidakhulupiliradi kuti adali woona; ndipo pachifukwa ichi ndidakanitsitsa choonadi, ngakhale kufikira ndabweretsa thembelero lalikulu ili pa ine.

54 Tsopano pamene iye adanena izi, adapempha kuti Alima amupemphelere kwa Mulungu, kuti thembelero lichotsedwe pa iye.

55 Koma Alima adati kwa iye: Ngati thembelero ili likachotsedwa kwa iwe udzasocheretsanso kukasocheretsa mitima ya anthu awa; kotero, lidzakhala pa iwe monga m’mene Ambuye akufunira.

56 Ndipo zidachitika kuti thembelero silidachotsedwe pa Koriho; koma iye adaponyedwa kunja, ndipo adayenda kuchokera nyumba ndi nyumba kupempha chakudya chake.

57 Tsopano chidziwitso cha zomwe zidachitika kwa Koriho chidafalikira mwachangu ku dziko lonselo; inde, uthenga udatumizidwa ndi wamkulu oweruza pa anthu wonse mdzikolo, kulengeza kwa iwo amene adakhulupilira mu mawu a Koriho kuti alape mofulumira, kuopa chiweruzo chomwecho chingadze pa iwo.

58 Ndipo zidachitika kuti onse adatsimikiza za kuipa kwa Koriho; kotero onse adatembenukiranso kwa Ambuye; ndipo izi zidathetsa kusaweruzika monga mwa njira za Koriho. Ndipo Koriho adayenda kuchoka nyumba ndi nyumba, kupemphetsa chakudya choti adzithandizire.

59 Ndipo zidachitika kuti pamene iye adapita pakati pa anthu, inde, pakati pa anthu amene adadzilekanitsa okha kwa Anefi ndi kudzitcha okha Azoramu, potsogoleredwa ndi munthu amene dzina lake lidali Zoramu—ndipo pamene iye adapita pakati pawo, taonani, adathamangitsidwa ndi kupondedwa, kufikira iye adamwalira.

60 Ndipo choncho tikuona mathero a iye amene amapotoza njira za Ambuye; ndipo choncho tikuona kuti mdyerekezi sadzathandiza ana ake pa tsiku lomaliza, koma iye amawakokera mwachangu ku gahena.