Malembo Oyera
Alima 14


Mutu 14

Alima ndi Amuleki amangidwa ndi kukanthidwa—Okhulupilira ndi malembo oyera awo awotchedwa ndi moto—Ophedwa alandiridwa ndi Ambuye mu ulemelero—Makoma a ndende ang’ambika ndi kugwa—Alima ndi Amuleki apulumutsidwa, ndipo owazunza awo aphedwa. Mdzaka dza pafupifupi 82–81 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo zidachitika kuti atatha kumaliza zoyankhula kwa anthuwo ambiri a iwo adakhulupilira mu mawu ake, ndi kuyamba kulapa, ndi kusakatula malembo oyera.

2 Koma gawo lambiri la iwo lidali ndi chikhumbo choti awononge Alima ndi Amuleki; pakuti adakwiya ndi Alima, chifukwa cha kumvetsetseka kwa mawu ake kwa Zeziromu; ndipo adanenanso kuti Amuleki adanama kwa iwo, ndipo adanyoza chilamulo chawo ndinso azamalamulo ndi oweruza awo.

3 Ndipo adalinso ndi mkwiyo ndi Alima ndi Amuleki; ndipo chifukwa adachitira umboni momveka bwino motsutsana ndi zoipa zawo, iwo adafuna kuwachotsa iwo mwamseri.

4 Koma zidachitika kuti iwo sadakwanitse; koma adawatenga ndikuwamanga iwo ndi zingwe zolimba, ndi kuwatengera iwo pamaso pa oweruza wamkulu wa dzikolo.

5 Ndipo anthu adapita ndi kuchitira umboni motsutsana nawo—kuchitira umboni kuti iwo adanyoza lamulo, ndi azamalamulo awo ndi oweruza, ndiponso anthu onse amene adali m’dzikolo; ndiponso adachitira umboni kuti adaliko koma Mulungu m’modzi, ndi kuti iye adzatumiza Mwana wake pakati pa anthu, koma sadzawapulumutsa iwo; ndipo zinthu zambiri zotere anthuwa adachitira umboni motsutsana ndi Alima ndi Amuleki. Tsopano izi zidachitika pamaso pa oweruza wamkulu wa dzikolo.

6 Ndipo zidachitika kuti Zeziromu adazizwa ndi mawu amene adayankhulidwa; ndipo iye adadziwanso zokhudzana ndi khungu la m’maganizo, limene iye adachititsa pakati pa anthu chifukwa cha mawu ake abodza; ndipo moyo wake udayamba kutsutsika pansi pa chikumbumtima cha kulakwa kwake; inde, adayamba kuzingidwa ndi ululu wa gahena.

7 Ndipo zidachitika kuti iye adayamba kulira kwa anthu, nati: Taonani, ndine olakwa, ndipo anthu awa ndiwopanda banga pamaso pa Mulungu. Ndipo adayamba kuwadandaulira kuchokera panthawiyo; koma iwo adamunyoza iye, nati: kodi nawenso wagwidwa ndi mdyerekezi? Ndipo adamulavulira iye, ndipo adamuchotsa kuchokera pakati pawo, ndi onse amene adakhulupilira mu mawu amene adayankhulidwa ndi Alima ndi Amuleki; ndipo adawachotsa pakati pawo, ndi kutumiza anthu kuti akawaponye miyala.

8 Ndipo adabweretsa akazi awo ndi ana awo pamodzi, ndipo aliyense amene adakhulupilira kapena adaphunzitsidwa kuti akhulupilire mu mawu a Mulungu adapangidwa kuti aponyedwe pa moto; ndipo adabweretsanso zolemba zimene zidali ndi malembo oyera, ndi kuziponyanso pamoto, kuti ziwotchedwe ndi kuwonongedwa ndi moto.

9 Ndipo zidachitika kuti adatenga Alima ndi Amuleki, ndi kuwanyamulira iwo ku malo ofera okhulupilira, kuti akachitire umboni kuwonongedwa kwa iwo amene adawotchedwa ndi moto.

10 Ndipo pamene Amuleki adaona ululu wa azimayi ndi ana amene ankapsa mu moto, nayenso adamva kuwawa; ndipo adati kwa Alima: kodi ife tingamaonelere bwanji chochitika choopsachi? Kotero tiyeni titambasule manja athu, ndi kuchita mphamvu ya Mulungu imene ili mwa ife, ndi kuwapulumutsa iwo ku malawi amoto.

11 Koma Alima adati kwa iye: Mzimu ukundikakamiza kuti ndisatambasule dzanja langa; pakuti taona Ambuye akuwalandira iwo kwa iye mwini, mu ulemelero; ndipo walora kuti iwo achite chinthu ichi, kapena kuti anthu achite chinthu ichi kwa iwo, molingana ndi kuuma kwa mitima yawo, kuti ziweruzo zimene iye adzachite pa iwo mu mkwiyo wake zidzakhale zolungama; ndipo mwazi wa osalakwa udzaima ngati mboni motsutsana nawo, inde, ndi kulira mwamphamvu motsutsana nawo pa tsiku lomaliza.

12 Tsopano Amuleki adati kwa Alima: Taona, kapena mwina atiwotchanso ife.

13 Ndipo Alima adati: Zikhale monga mwa chifuniro cha Ambuye. Koma, taona, ntchito yathu siyidathe; kotero iwo satiwotcha ife.

14 Tsopano zidachitika kuti pamene matupi a iwo amene adaponyedwa pa moto adanyekedwa, ndiponso zolemba zimene zidaponyedwa m’menemo ndi iwo, mkulu wa oweruza wa dzikolo adabwera ndikuima pamaso pa Alima ndi Amuleki, pamene adamangidwa; ndipo adapanda iwo ndi dzanja lake pa masaya awo, ndipo adanena kwa iwo: Patatha zomwe mwaonazi, kodi mudzalalikiranso kwa anthu awa, kuti adzaponyedwe mu nyanja ya moto ndi sulufule?

15 Taonani, mukuona kuti mudalibe mphamvu yopulumutsa iwo amene adaponyedwa mu moto; ngakhalenso Mulungu sadawapulumutse iwo chifukwa adali achikhulupiliro chanu. Ndipo oweruzayo adawapandanso iwo pa masaya awo, ndikufunsa: Kodi mudzinenera chiyani za inu eni?

16 Tsopano oweruzayi adali wa dongosolo ndi chikhulupiliro cha Nehori, amene adapha Gideoni.

17 Ndipo zidachitika kuti Alima ndi Amuleki sadamuyankhe kalikonse; ndipo iye adawapandanso, ndi kuwapereka iwo kwa adindo kuti awaponye mu ndende.

18 Ndipo pamene adawaponya mundende masiku atatu, kudabwera azamalamulo ambiri, ndi oweruza, ndi ansembe, ndi aphunzitsi, amene adali achipembedzo cha Nehori; ndipo adalowa mu ndende kudzawaona, ndipo adawafunsa iwo mawu ambiri; koma iwo sadawayankhe kanthu.

19 Ndipo zidachitika kuti oweruza adaima pamaso pawo ndipo adati: Chifukwa chiyani simukuyankha mawu a anthu awa? Kodi inu simukudziwa kuti ndili nayo mphamvu yokuperekani inu ku malawi a moto? Ndipo adawalamula kuti ayankhule; koma iwo sadayankhe kanthu.

20 Ndipo zidachitika kuti adachoka ndi kuyenda njira zawo, koma adabweranso m’mawa mwake; ndipo oweruza adapandanso iwo pa masaya awo. Ndipo ambiri adabweranso, ndi kuwapanda iwo, nati: Kodi mudzaimanso kachiwiri ndi kuweruza anthu awa, ndi kutsutsa lamulo lathu? Ngati muli ndi mphamvu yotere bwanji osadzipulumutsa nokha?

21 Ndipo zambiri zinthu zotere adazinena kwa iwo, kukukuta mano awo pa iwo, ndi kuwalavulira iwo, ndi kunena: Kodi tidzaoneka bwanji tikadzalangidwa?

22 Ndipo zinthu zambiri zotere, inde, mitundu yonse ya zinthu zotere iwo adanena kwa iwo: ndipo motere adaseka iwo kwa masiku ambiri. Ndipo adamana chakudya kwa iwo kuti akhale ndi njala, ndi madzi kuti akhale ndi ludzu; ndipo adawavulanso zovala zawo kuti akhale maliseche; ndipo motere adawamanga ndi zingwe zolimba ndi kuwaponya mundende.

23 Ndipo zidachitika atatha kuzunzika kotere kwa masiku ambiri, (ndipo lidali tsiku lakhumi ndi chiwiri, mu mwezi wakhumi, mu chaka chakhumi cha kulamulira kwa oweruza pa anthu a Nefi) kuti mkulu wa oweruza pa dziko la Amoniha ndi ambiri mwa aphunzitsi awo ndi azamalamulo awo adalowa mu ndende m’mene Alima ndi Amuleki adamangidwa ndi zingwe.

24 Ndipo mkulu wa oweruza adaima pamaso pawo, ndikuwamenyanso, ndipo adati kwa iwo: Ngati muli ndi mphamvu ya Mulungu, mudzipulumutse nokha kuzingwe izi, ndipo pamenepo ife tidzakhulupilira kuti Ambuye adzawononga anthu awa molingana ndi mawu anu.

25 Ndipo zidachitika kuti wonse adapita ndi kuwamenya iwo, nanena mawu omwewo, ngakhale kufikira omaliza, ndipo pamene omaliza adayankhula kwa iwo mphamvu ya Mulungu idali pa Alima ndi Amuleki, ndipo iwo adaimilila ndi kuima pa mapazi awo.

26 Ndipo Alima adafuula, nati: Kodi ife tidzavutika mpaka liti masautso aakulu awa, O Ambuye? O Ambuye, tipatseni ife mphamvu molingana ndi chikhulupiliro chathu chimene chili mwa Khristu, ngakhale ku chiwombolo. Ndipo adadula zingwe zimene iwo adamangidwa nazo; ndipo pamene anthu adaona izi, adayamba kuthawa, pakuti mantha a chiwonongeko adawafikira.

27 Ndipo zidachitika kuti aakulu adali mantha awo kotero kuti adagwa pansi, ndipo sadapeze khomo lotulukira mundende; ndipo nthaka idagwedezeka mwamphamvu, ndipo makoma a ndende adang’ambika pakati, kotero kuti adagwa pansi; ndipo oweruza wamkulu, ndi azamalamulo, ndi ansembe, ndi aphunzitsi, amene adamenya Alima ndi Amuleki, adaphedwa chifukwa cha kugwako.

28 Ndipo Alima ndi Amuleki adatuluka mu ndendemo, ndipo sadavulazidwe; pakuti Ambuye adawapatsa iwo mphamvu, molingana ndi chikhulupiliro chawo chimene chidali mwa Khristu. Ndipo pomwepo adaturuka mundendemo; ndipo adamasulidwa ku maunyolo awo; ndipo ndendeyo idali itagwa pansi, ndipo munthu aliyense mkati mwa makoma akewo, kupatula Alima ndi Amuleki, adaphedwa; ndipo pomwepo adabwera mu mzinda.

29 Tsopano anthu atamva phokoso lalikulu adabwera mothamanga pamodzi mwa makamu kuti adziwe chifukwa chake; ndipo pamene adaona Alima ndi Amuleki akubwera kutuluka mu ndende, ndipo makoma akewo adali atagwa pansi, adagwida ndi mantha aakulu, ndipo adathawa pamaso pa Alima ndi Amuleki ngati mbuzi ithawira ndi ana ake kwa mikango iwiri; ndipo adathawa kuchoka pamaso pa Alima ndi Amuleki.