Malembo Oyera
Alima 19


Mutu 19

Lamoni alandira kuwala kwa moyo wosatha ndipo aona Muwomboli—Am’nyumba mwake agwa m’masomphenya ndipo ambiri aona angelo—Amoni apulumutsidwa mozizwitsa—Iye abatiza ambiri ndipo akhazikitsa mpingo pakati pawo. Mdzaka dza pafupifupi 90 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo zidachitika kuti patatha usana uwiri ndi usiku uwiri iwo adali pafupi kuti atenge thupi lake ndi kuliyika m’manda, amene adapangidwa ndi cholinga choikamo anthu akufa.

2 Tsopano mfumukazi itamva za kutchuka kwa Amoni, kotero idakhumba ndi kutuma kuti abwere kwa iyo.

3 Ndipo zidachitika kuti Amoni adachita momwe adalamulidwira, ndipo adapita kwa mfumukazi, ndipo adakhumbira kudziwa chomwe iyo idafuna kuti achite.

4 Ndipo iyo idati kwa iye: Adzakazi a mwamuna wanga andidziwitsa ine kuti iwe ndi mneneri wa Mulungu oyera, ndipo kuti iwe uli ndi mphamvu zakuchita ntchito zamphamvu zambiri mu dzina lake;

5 Kotero, ngati izi ziri chomwechi, ndikufuna kuti ulowe ndi kumuona mwamuna wanga, pakuti iye wagonekedwa pa kama lake kwa nthawi ya masiku awiri; ndipo ena akuti iye sadamwalire, koma ena akuti iye wamwalira ndipo akununkha, ndipo kuti akuyenera kuikidwa m’manda; koma monga kwa ine mwini, iye sakununkha.

6 Tsopano, izi zidali zimene Amoni ankakhumbira, pakuti adadziwa kuti mfumu Lamoni adali pansi pa mphamvu ya Mulungu; adadziwa kuti chophimba cha mdima wakusakhulupilira chidachotsedwa m’maganizo mwake, ndipo kuwala kumene kudawala m’maganizo mwake, kumene kudali kuwala kwa ulemelero wa Mulungu, kumene kudali kuwala kodabwitsa kwa ubwino wake—inde, kuwala uku kudabweretsa chisangalalo choterocho m’moyo mwake, mtambo wa mdima udachotsedwa, ndipo kuti kuwala kwa moyo wosatha kudawalira m’moyo mwake, inde, iye adadziwa kuti izi zidagonjetsa thupi lake la chilengedwe, ndipo adatengedwa mwa Mulungu—

7 Kotero, zimene mfumukazi idakhumba kwa iye zidali chikhumbo chake chokha. Kotero, iye adalowa kukamuona mfumu monga m’mene mfumukazi idakhumbira, ndipo adaiona mfumuyo, ndipo adadziwa kuti iyo siyidamwalire.

8 Ndipo iye adati kwa mfumukazi: Iye sadamwalire, koma akugona mwa Mulungu, ndipo mawa adzadzukanso; kotero asakwiliridwe.

9 Ndipo Amoni adati kwa iyo: Mukukhulupilira izi? Ndipo iyo idati kwa iye: Sindidakhale ndi umboni kupatura mawu ako, ndi mawu a adzakazi athu; komabe ndikukhulupilira kuti zidzachitika monga iwe wanenera.

10 Ndipo Amoni adati kwa iyo: Odala ndi iwe chifukwa cha chikhulupiliro chako chachikulu: Ndikunena ndi iwe, mzimayi, sipadakhalepo chikhulupiliro chotere pakati pa anthu wonse a Anefi.

11 Ndipo zidachitika kuti iyo idayang’anira pa kama la mwamuna wake, kuchokera pa nthawiyo ngakhale mpaka nthawi ya m’mawa umene Amoni adaikiza kuti iye adzauka.

12 Ndipo zidachitika kuti iye adauka, molingana ndi mawu a Amoni; ndipo pamene adauka, adatambasula dzanja lake kwa mzimayi ndi kunena: Lidalitsike dzina la Mulungu, ndipo odala ndi iwe.

13 Pakuti monga ndithu iwe ulimoyo, taona, ine ndaona Muwomboli wanga, ndipo iye adzabwera, ndikubadwa mwa mzimayi, ndipo adzawombola anthu onse amene akhulupilira mu dzina lake. Tsopano, pamene iye adanena mawu awa, mtima wake udadzadza mwa iye, ndipo adagwanso pansi m’chisangalalo ndipo mfumukaziyonso idagwa pansi, itagonjetsedwa ndi Mzimu.

14 Tsopano Amoni ataona Mzimu wa Ambuye udatsanuridwa monga mwa mapemphero ake kwa Alamani, abale ake, amene adali oyambitsa chisoni chachikulu pakati pa Anefi, kapena pakati pa anthu onse a Mulungu chifukwa cha mphulupulu zawo ndi miyambo yawo, iye adagwa pa mawondo ake, ndi kuyamba kutsanulira moyo wake mu pemphero ndi chiyamiko kwa Mulungu chifukwa cha zimene adachita kwa abale ake; ndipo iye adagonjetsedwa ndi chisangalalo, ndipo choncho atatu onse adagwa pansi.

15 Tsopano, pamene adzakazi a mfumu adaona izi kuti iwo agwa, iwonso adayambanso kufuula kwa Mulungu, pakuti kuopa kwa a Ambuye kudadza pa iwonso, pakuti adali iwowo amene adaima pamaso pamfumu ndi kuchitira umboni kwa iye zokhudzana ndi mphamvu yaikulu ya Amoni.

16 Ndipo zidachitika kuti onse adaitanira pa dzina la Ambuye, mu mphamvu zawo, ngakhale kufikira onse adagwa pansi, kupatula mzimayi m’modzi wachi-Lamani, amene dzina lake adali Abishi, atatembenukira kwa Ambuye kwa dzaka zambiri, chifukwa cha nkhani yodabwitsa ya masomphenya a atate ake—

17 Motero, atatembenukira kwa Ambuye, ndipo sadaulure za izi, kotero, pamene iye adaona kuti adzakazi onse a Lamoni adagwa pansi, komanso mbuye wake, mfumukaziyo, ndi mfumu, ndi Amoni adagona pansi, iye adadziwa kuti idali mphamvu ya Mulungu; ndipo poganiza kuti uwu udali mwayi, pakudziwitsa kwa anthu zomwe zidachitika pakati pawo, kuti pakuona chochitika ichi chikawapangitsa iwo kukhulupilira mu mphamvu ya Mulungu, kotero iye adathamanga kuchoka nyumba ndi nyumba, kudziwitsa kwa anthu.

18 Ndipo adayamba kusonkhana pamodzi ku nyumba ya mfumu. Ndipo kudabwera khamu la anthu, ndi kuzizwa kwawo, iwo adaona mfumu, ndi mfumukazi, ndi adzakazi awo atagwada pansi, ndipo iwo wonse adagona pamenepo ngati kuti amwalira; ndipo adaonanso Amoni, ndipo taonani, iye adali M’nefi.

19 Ndipo tsopano anthuwo adayamba kung’ung’udza pakati pawo; ena nanena kuti chidali choipa kwambiri chimene chidagwera pa iwo, kapena pa mfumu ndi nyumba yake, chifukwa iye adalolera kuti M’nefiyu akhalebe m’dzikolo.

20 Koma ena adawadzudzula iwo, nati: Mfumu yabweretsa choipachi pa nyumba yake, chifukwa iye adapha adzakazi ake amene adabalalitsidwira ziweto zawo pa madzi a Sebusi.

21 Ndipo iwonso adadzudzulidwa ndi iwo amene adaima pa madzi a Sebusi, ndi kubalalitsa ziweto zimene zidali za mfumu, pakuti iwo adakwiya ndi Amoni chifukwa cha chiwerengero chimene iye adapha mwa abale awo pa madzi a Sebusi, pamene ankateteza ziweto za mfumu.

22 Tsopano, m’modzi mwa iwo, amene m’bale wake adaphedwa ndi lupanga la Amoni, pokhala wokwiya kwambiri ndi Amoni, adasolora lupanga lake ndi kupita kuti alilore kuti ligwe pa Amoni, kuti amuphe iye; ndipo pamene iye adanyamula lupanga lake kuti amkanthe iye, taonani, adagwa ndi kufa.

23 Tsopano tikuona kuti Amoni sakadaphedwa, pakuti Ambuye adanena kwa Mosiya, atate ake: ndidzamuteteza iye, ndipo zidzakhala kwa iye molingana ndi chikhulupiliro chako—kotero Mosiya adampereka iye kwa Ambuye.

24 Ndipo zidachitika kuti pamene khamulo lidaona kuti munthuyo adagwa ndi kufa, amene adasolora lupanga kuti amuphe Amoni, mantha adawagwira onse, ndipo sadayesere kuika manja awo kuti amkhudze iye kapena aliyense mwa iwo amene adagwa; ndipo adayamba kudabwanso pakati pawokha chimene chingachititse mphamvu zazikuluzi, kapena zimene zonsezi zingatanthauze.

25 Ndipo zidachitika kuti adalipo ambiri pakati pawo amene adanena kuti Amoni adali Mzimu Waukulu, ndipo ena adati iye adatumidwa ndi Mzimu Waukulu.

26 Koma ena adawadzudzula onsewo, kunena kuti iye adali chilombo, chimene chidatumizidwa ndi Anefi kuti chidzawazunze iwo.

27 Ndipo adalipo ena amene adanena kuti Amoni adatumizidwa ndi Mzimu Waukulu kuti adzawasautse iwo chifukwa cha mphulupulu zawo; ndipo kuti udali Mzimu Waukulu umene umakhala ndi Anefi nthawi zonse, umene adawapulumutsa iwo m’manja mwawo; ndipo iwo adati kuti udali Mzimu Waukulu umene udawononga abale awo ambiri, Alamani.

28 Ndipo choncho mkangano udayamba kukula kwambiri pakati pawo. Ndipo pamene iwo adali kukangana, m’dzakazi wamkazi amene adachititsa kuti khamulo lisonkhane pamodzi adabwera, ndipo pamene iye adaona mkangano umene udali pakati pa khamulo iye adali ndi chisoni kwambiri, ngakhale mpaka misozi.

29 Ndipo zidachitika kuti iye adapita ndi kumutenga mfumukaziyo pa dzanja, kuti mwina amudzutse pansipo; ndipo atangomugwira dzanja adadzuka ndi kuima pamapazi ake, ndipo adafuula ndi mawu amfuwu, nati: Inu odala Yesu, amene mwapulumutsa ine ku gahena oopsya! O odala Mulungu, chitirani chifundo anthu awa!

30 Ndipo pamene iye adanena izi, adaomba m’manja, podzadzidwa ndi chisangalalo, nayankhula mawu ambiri amene sadamveke; ndipo pamene adachita izi, adamtenga mfumu, Lamoni, pa dzanja, ndipo taonani, iye adadzuka ndi kuima pamapazi ake.

31 Ndipo iye, pomwepo, poona mkangano pakati pa anthu ake, adapita ndi kuyamba kudzudzula iwo, ndi kuwaphunzitsa iwo mawu amene iye adamva kuchokera pakamwa pa Amoni; ndipo ambiri amene adamva mawu ake adakhulupilira, ndipo adatembenukira kwa Ambuye.

32 Koma adalipo ambiri pakati pawo amene sadamvere mawu ake; kotero adapita njira yawo.

33 Ndipo zidachitika kuti pamene Amoni adaima ndi kutumikira kwa iwo, ndiponso adzakazi onse a Lamoni; ndipo onse adalengeza kwa anthu chinthu chomwecho—kuti mitima yawo yasinthidwa; kuti adalibe chikhumbo cha kuchita zoipa.

34 Ndipo taonani, ambiri adalengeza kwa anthu kuti iwo adaona angelo ndipo adayankhula nawo; ndipo motero adawauza iwo zinthu za Mulungu, ndi chilungamo chake.

35 Ndipo zidachitika kuti adalipo ambiri amene adakhulupilira mawu awo; ndipo ambiri onse amene adakhulupilira adabatizidwa; ndipo adakhala anthu olungama, ndipo adakhazikitsa mpingo pakati pawo.

36 Ndipo motero ntchito ya Ambuye idayambika pakati pa Alamani; motero Ambuye adayamba kutsanulira Mzimu wake pa iwo; ndipo tikuona kuti mkono wake watambasulidwa kwa anthu wonse amene adzalape ndi kukhulupilira mu dzina lake.