Malembo Oyera
Alima 56


Mutu 56

Helamani atumiza kalata kwa Moroni, kufotokoza za m’mene nkhondo iliri ndi Alamani—Antipa ndi Helamani apeza chipambano chachikulu pa Alamani—Ana aamuna odzipereka a Helamani zikwi ziwiri amenya mwa mphamvu zodabwitsa, ndipo palibe mwa iwo adaphedwa. Ndime 1, pafupifupi 62 Yesu asadabadwe; ndime 2–19, pafupifupi 66 Yesu asadabadwe; ndi ndime 20–57, pafupifupi 65–64 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo tsopano zidachitika kumayambiliro kwa chaka cha makumi atatu cha ulamuliro wa oweruza, pa tsiku lachiwiri la mwezi woyamba, Moroni adalandira kalata yochokera kwa Helamani, kumuuza za zochitika za anthu mu chigawo chimenecho cha dzikolo.

2 Ndipo awa ndiwo mawu amene iye adalemba, kuti: Okondedwa m’bale wanga, Moroni, komanso mwa Ambuye monganso m’masautso a za nkhondo yathu; taona, m’bale wanga, ndili ndi zinazake zoti ndikuuze iwe zokhudzana ndi nkhondo yathu mu chigawo chino cha dziko.

3 Taona, ana aamuna zikwi ziwiri a anthu aja amene Amoni adabweretsa kuchoka ku dziko la Nefi—tsopano iwe ukuwadziwa kuti iwowa adali mbumba ya Lamani, amene adali mwana wankulu wa atate athu Lehi.

4 Tsopano sindikuyenera kufotokozera kwa iwe zokhudzana ndi miyambo yawo kapena kusakhulupilira kwawo, pakuti iwe ukudziwa zokhudzana ndi zinthu zonsezi—

5 Kotero zindikwanira ine kuti ndikuuze iwe kuti zikwi ziwiri za anyamatawa zatenga zida zawo zankhondo, ndipo akufuna kuti ine ndikhale mtsogoleri wawo; ndipo ife tabwera kudzateteza dziko lathu.

6 Ndipo tsopano iwenso ukudziwa zokhudzana ndi pangano limene makolo awo adapanga, kuti iwo sadzatenga zida zawo zankhondo motsutsana ndi abale awo kuti akhetse mwazi.

7 Koma mu chaka cha makumi awiri ndi chisanu n’chimodzi, pamene iwo adaona kuti masautso athu ndi mazunzo athu pa iwo, iwo adali pafupi kuphwanya pangano limene iwo adapanga ndi kutenga zida zawo zankhondo potiteteza ife.

8 Koma ine sindikadawalora iwo kuti aphwanye pangano limeneli limene iwo adapanga, poganiza kuti Mulungu adzatilimbitsa ife, kotero kuti ife tisamavutikebe chifukwa cha kukwaniritsa kwa lumbiro limene iwo adatenga.

9 Koma taona, tsopano pali chinthu chimodzi chimene ife tingasangalale nacho kwambiri. Pakuti taona, mu chaka cha makumi awiri ndi chisanu n’chimodzi, ine, Helamani, ndidaguba patsogolo pa anyamata zikwi ziwiriwa ku mzinda wa Yudeya, kukathandizira Antipa, amene iwe udamusankha mtsogoleri pa anthu a chigawo chimenecho cha dziko.

10 Ndipo ine ndidaphatikiza ana anga aamuna zikwi ziwiri, (pakuti iwo akuyenera kutchedwa ana aamuna) ku ankhondo a Antipa, mumphamvu yake Antipa adakondwera kwambiri; pakuti taona, ankhondo ake adali atachepetsedwa ndi Alamani chifukwa ankhondo awo adapha chiwerengero chochuluka cha anthu athu, pachifukwa ichi tikuyenera kulira.

11 Komabe, tikhonza kudzitonthonza tokha mu chinthu ichi, kuti iwo adafa pachifukwa cha dziko lawo ndi Mulungu wawo, inde, iwo ndi okondwa.

12 Ndipo Alamani adatenganso akaidi ambiri, onse mwa iwo ndi akulu ankhondo, pakuti ena onse sadasiye ndi moyo. Ndipo ife tikuganiza kuti iwo tsopano pa nthawi ino ali mu dziko la Nefi; zili choncho ngati sadaphedwe.

13 Ndipo tsopano iyi ndi mizinda imene Alamani adaitenga mwa kukhetsa mwazi wa ambiri mwa anthu athu amphamvu:

14 Dziko la Manti, kapena mzinda wa Manti, ndi mzinda wa Zeziromu, ndi mzinda wa Kumeni, ndi mzinda wa Antipara.

15 Ndipo iyi ndi mizinda imene iwo adailanda pamene ine ndidafika pa mzinda wa Yudeya; ndipo ndidapeza Antipa ndi anthu ake akugwira ntchito mwamphamvu kuti alimbitse mzindawo.

16 Inde, iwo adali osautsika mu thupi chimodzimodzinso mu mzimu, pakuti iwo adamenya nkhondo molimbika pa usana ndi kugwira ntchito usiku kuteteza mizinda yawo; ndipo motero iwo adazunzika ndi masautso aakulu a mtundu uliwonse.

17 Ndipo tsopano iwo adatsimikiza kugonjetsa malo amenewa kapena kufa; kotero iwe ukhonza kuganiza kuti ankhondo ochepawa amene ine ndidabwera nawo, inde, ana angawo, adawapatsa chiyembekezo chachikulu ndi chisangalalo chochuluka.

18 Ndipo tsopano zidachitika kuti pamene Alamani adaona kuti Antipa walandira mphamvu zochulukirapo ku ankhondo ake, iwo adakakamizika mwa malamulo a Amoroni kuti asabwere motsutsana ndi mzinda wa Yudeya, kapena motsutsana nafe, kunkhondo.

19 Ndipo motero ife tidakonderedwa ndi Ambuye; pakuti iwo akadabwera pa ife mu kufooka kwathu kumeneku mwina akadawononga ankhondo athu ochepawa; koma motero ife tidatetezeka.

20 Iwo adalamulidwa ndi Amoroni kuteteza mizindayo imene iwo adalanda. Ndipo motero chidatha chaka cha makumi awiri ndi zisanu ndi chimodzi. Ndipo kumayambiliro kwa chaka cha makumi awiri ndi zisanu ndi ziwiri tidakonzekeretsa mizinda yathu komanso ife eni kuchitetezo.

21 Tsopano ife tidali kukhumba kuti Alamani abwere pa ife; pakuti ife sitidafune kuti tikamenyane nawo m’malinga awo.

22 Ndipo zidachitika kuti ife tidaika akazitape mozungulira, kuyang’anira mayendedwe a Alamani, kuti iwo asatidutse ife pa usiku kapena usana kuti awukire mizinda yathu ina imene idali chakumpoto.

23 Pakuti ife tidadziwa mizindayo sidali yamphamvu zokwanira kukumana nawo; kotero ife tidali ndichikhumbo, ngati iwo angatidutse ife, tiwagwere chakumbuyo kwawo, ndipo motero nkuwabwenza m’mbuyo panthawi yomweyonso kukumana nawonso kutsogolo. Tidaganiza kuti tikadawagonjetsa iwo; koma taona, tidakhumudwa mu chokhumba chathuchi.

24 Iwo sadayerekeze kutidutsa ife ndi ankhondo awo onse, ngakhale kuyerekeza ndi gawo lomwe, kuopa kuti iwo asakhale ndi mphamvu zokwanira ndipo kuti agwe.

25 Ngakhale iwo sadayerekezenso kuguba motsutsana ndi mzinda wa Zarahemula; kapena kuyesera kuwoloka kumutu kwa Sidoni, kupita ku mzinda wa Nefiha.

26 Ndipo motero, ndi ankhondo awo, iwo adatsimikiza kuteteza mizindayo imene iwo adatenga.

27 Ndipo tsopano zidachitika kuti mu mwezi wachiwiri wa chakachi, kudabweretsedwa kwa ife zakudya zambiri kuchokera kwa mokolo a ana anga aamuna zikwi ziwiriwa.

28 Ndiponso kudatumizidwa anthu zikwi ziwiri kwa ife kuchokera ku dziko la Zarahemula. Ndipo motero ife tidakonzekera ndi anthu zikwi khumi, ndi chakudya chawo, ndiponso cha akazi awo ndi ana awo.

29 Ndipo Alamani, motero poona ankhondo athu akuwonjezereka tsiku ndi tsiku, ndipo chakudya chidafika chotithandizira, iwo adayamba kukhala ndi mantha, ndi kuyamba kutuluka, ngati kudali kotheka kuti athetse kulandira chakudyacho ndi mphamvu zathu.

30 Tsopano pamene ife tidaona kuti Alamani ayamba kutekeseka pa ichi, tidakhumbira kubweretsa ndondomeko kuti igwire ntchito pa iwo, kotero Antipa adalamula kuti ndigube ndi ana anga aamuna ku mzinda woyandikira nawo, ngati kuti tanyamula chakudya kupita ku mzinda woyandikana nawo.

31 Ndipo tidayenera kugubira kufupi ndi mzinda wa Antipara, monga ngati tikupita ku mzinda wakuseli, kumalire a gombe lanyanja.

32 Ndipo zidachitika kuti ife tidaguba, monga ngati tili ndi chakudya, kupita ku mzinda umenewo.

33 Ndipo zidachitika kuti Antipa adagubira ndi gawo la ankhondo ake, kusiya otsalawo kuti ateteze mzindawo. Koma iye sadagube kufikira ine nditanyamuka ndi ankhondo anga ochepawo, ndi kufika ku mzinda wa Antipara.

34 Ndipo tsopano, mu mzinda wa Antipara mudali ankhondo amphamvu kwambiri Achilamani; inde, ochuluka kwambiri.

35 Ndipo zidachitika kuti pamene iwo adawuzidwa ndi akazitape awo, adabwera ndi ankhondo awo ndi kuguba motsutsana nafe.

36 Ndipo zidachitika kuti ife tidathawa pamaso pawo, chakumpoto. Ndipo motero tidatsogolera kutali ankhondo amphamvu kwambiri Achilamani.

37 Inde, ngakhale ku mtunda wautali, kotero kuti pamene iwo adaona ankhondo a Antipa akuwatsata iwo, ndi mphamvu zawo, iwo sadatembenukire kumanja kapena kumenzere, koma adapitiriza kuguba kwawo molunjika potsata ife; ndipo, monga ife tidaganizira, chidali cholinga chawo kuti atiphe ife Antipa asadawapeze, ndipo izi kuti iwo asazunguliridwe ndi anthu athu.

38 Ndipo tsopano Antipa, poona choopsya chathu, adafulumizitsa kuguba kwa ankhondo ake. Koma taonani, udali usiku; kotero iwo sadatipeze, ngakhalenso Antipa sadawapeze; kotero ife tidamanga msasa kwa usikuwo.

39 Ndipo zidachitika kuti usadafike m’bandakucha wa m’mawa, taonani, Alamani adali kutitsata ife. Tsopano ife tidalibe mphamvu zokwanira kuti tilimbane nawo; inde, sindikadalora kuti ana anga aang’ono agwere m’manja mwawo; kotero ife tidapitiriza kuguba kwathu, ndipo tidagubira m’chipululu.

40 Tsopano iwo sadayerekeze kutembenukira kumanja kapena kumanzere kuopa kuti angazunguliridwe; ngakhale inenso kutembenukira kumanja kapena kumanzere kuopa kuti angandipeze, ndipo sitikadatha kuima polimbana nawo, koma kuphedwa, ndipo iwo akadathawa; ndipo motero ife tidathawa mu tsiku lonselo m’chipululu, ngakhale kufikira m’dima udadza.

41 Ndipo zidachitika kuti kenako, pamene kuwala kwa m’mawa kudadza tidaona Alamani akubwera ndipo ife tidathawa pamaso pawo.

42 Koma zidachitika kuti iwo sadatithamangitsire ife kutali asadaime; ndipo udali m’mawa wa tsiku lachitatu la mwezi wachisanu ndi chiwiri.

43 Ndipo tsopano, kaya adapezedwa ndi Antipa ife sitikudziwa, koma ine ndidati kwa athu anga: Taonani, sitikudziwa koma iwo aima pacholinga choti ife tibwere motsutsana nawo, kuti iwo atigwire ife mu msampha wawo;

44 Kotero mukuti chiyani, ana anga, kodi mupita kukamenyana nawo ku nkhondo?

45 Ndipo tsopano ndinena kwa iwe, m’bale wanga okondedwa Moroni, kuti sindidaonepo kulimba mtima kwakukulu kotero, ayi, osati pakati pa Anefi onse.

46 Pakuti monga ndidawatcha iwo ana anga (pakuti onsewo adali achichepere kwambiri) ngakhale choncho iwo adati kwa ine: Atate, taonani Mulungu wathu ali nafe, ndipo sadzalora kuti ife tigwe; ndiye tiyeni tipite; sitikawapha abale athuwo ngati iwo atisiye tokha; kotero tiyeni tipite, kuopa angagonjetse ankhondo a Antipa.

47 Tsopano iwo adali asadamenyanepo, koma iwo sadaope imfa; ndipo ankaganizira kwambiri za ufulu wa makolo awo kuposa m’mene amachitira pa miyoyo yawo; inde, iwo adali ataphunzitsidwa ndi azimayi awo, kuti ngati iwo sakayikira, Mulungu adzawapulumutsa iwo.

48 Ndipo iwo adandifotokozera ine mawu a azimayi awo, kuti: Ife sitikukayika azimayi athu adadziwa ichi.

49 Ndipo zidachitika kuti ine ndidabwelera ndi zikwi ziwiri zanga kukatsutsana ndi Alamaniwa amene ankatitsata ife. Ndipo tsopano taona, ankhondo a Antipa adali atawapeza, ndipo nkhondo yoopsya idali itayambika.

50 Ankhondo a Antipa pokhala atatopa, chifukwa cha kutalika kwa koguba kwawo mu kamphindi kochepa ka nthawi, adali pafupi kugwa m’manja mwa Alamani; ndipo ndikadapanda kubwelera ndi zikwi ziwiri zangazo iwo akadapeza zolinga zawo.

51 Pakuti Antipa adali atagwa ndi lupanga, ndi ambiri mwa atsogoleri ake, chifukwa cha kutopa kwawo, kumene kudadza chifukwa cha liwiro la kuguba kwawo—kotero anthu a Antipa, pokhala osokonezeka chifukwa cha kugwa kwa atsogoleri awo, adayamba kupereka mpata pamaso pa Alamani.

52 Ndipo zidachitika kuti Alamani adayamba kulimba mtima, ndipo adayamba kuwatsatira iwo, ndipo motero Alamaniwo ankawatsatira iwo mwa mphamvu zazikulu pamene Helamani adabwera patsogolo pawo ndi zikwi ziwiri zake, ndi kuyamba kuwapha kwambiri, kufikira kuti ankhondo onse achilamani adaima ndipo adatembenukira kwa Helamani.

53 Tsopano pamene anthu a Antipa adaona kuti Alamani atembenuka, iwo adasonkhanitsa pamodzi anthu awo ndipo anabweranso pambuyo pa Alamani.

54 Ndipo tsopano zidachitika kuti ife, anthu a Nefi, anthu a Antipa, ndipo ine ndi zikwi ziwiri zanga, tidazungulira Alamani, ndipo tidawapha; inde, kotero kuti iwo adakakamizika kupereka zida zawo zankhondo ndiponso iwo eni monga akaidi a nkhondo.

55 Ndipo tsopano zidachitika kuti pamene iwo adadzipereka iwo eni kwa ife, taonani, ndidawerenga achinyamata amene adamenya nane, kuopa kuti adalipo ambiri amene adaphedwa.

56 Koma taona, mu chisangalalo changa chachikulu, padalibe munthu m’modzi wa iwo amene adagwa pansi; inde, ndipo iwo adamenya monga ngati ndi mphamvu ya Mulungu; inde, palibe anthu adadziwika konse kuti adamenyapo ndi mphamvu zodabwitsa chotere; ndipo ndi mphamvu zazikulu chotere iwo adagwera pa Alamani, mpaka iwo adawopsezedwa; ndipo pachifukwa ichi Alamani adadzipereka okha ngati akaidi ankhondo.

57 Ndipo popeza tidalibe malo a akaidi athu, kuti tikadatha kuwalondera iwo kuti tiwabise iwo kwa ankhondo Achilamani, kotero tidawatumiza iwo ku dziko la Zarahemula, ndi gawo la iwo anthu amene sadaphedwe a Antipa, ndi iwo; ndipo otsalawo ndidawatenga ndi kuwaphatikiza kwa achinyamata anga a Amoni, ndipo tidayamba kuguba kubwelera ku mzinda wa Yudeya.