Malembo Oyera
Alima 47


Mutu 47

Amalikiya agwiritsa ntchito chinyengo, kupha, ndi chiwembu kuti akhale mfumu ya Alamani—Anefi otsutsa akhala oyipitsitsa ndi ankhanza kuposera Alamani. Mdzaka dza pafupifupi 72 Yesu asadabadwe.

1 Tsopano tidzabwelera mu zolemba zathu kwa Amalikiya ndi iwo amene adathawa ndi iye kulowera m’chipululu; pakuti, taonani, iye adatenga iwo amene adapita ndi iye, ndipo adapita nawo ku dziko la Nefi pakati pa Alamani, ndipo adawautsa Alamani ku mkwiyo motsutsana ndi anthu a Nefi, kufikira kuti mfumu ya Alamani idatumiza chilengezo kudziko lonselo, pakati pa anthu ake onse, kuti adzisonkhanitse okha pamodzi kachiwiri kuti apite ku nkhondo motsutsana ndi Anefi.

2 Ndipo zidachitika kuti pamene chilengezo chidapita kwa iwo adali amantha kwambiri; inde, iwo adaopa kukhumudwitsa mfumu yawo, ndiponso adaopa kupita kunkhondo motsutsana ndi Anefi kuopa kuti angataye moyo wawo. Ndipo zidachitika kuti iwo sadafune, kapena gawo lambiri la iwo silidafune, kumvera lamulo la mfumuyo.

3 Ndipo tsopano zidachitika kuti mfumuyo idakwiya chifukwa cha kusamvera kwawo; kotero adampatsa Amalikiya ulamuliro wa gawo limenero la ankhondo ake limene lidali lomvera malamulo ake, ndipo adamulamula iye kuti apite ndi kuwakakamiza iwo ku zida.

4 Tsopano taonani, ichi chidali chokhumba cha Amalikiya; pakuti iye okhala munthu wochenjera kwambiri pochita zoipa kotero adayala dongosolo mu mtima mwake kuti achotse mfumu ya Alamani.

5 Ndipo tsopano iye adakhala ndi ulamuliro wa magawo amenewo a Alamani amene adali ogwirizana ndi mfumu; ndipo iye adafuna kuti apeze kukonderedwa kwa iwo amene adali osamvera; kotero iye adapita ku malo amene ankatchedwa Onida, pakuti kumeneko ndi komwe Alamani onse adathawira; pakuti adazindikira ankhondo akudza, ndipo, poganiza kuti akudza kudzawawononga, adathawira ku Onida, ku malo a zida.

6 Ndipo iwo adasankha munthu kuti akhale mfumu ndi mtsogoleri pa iwo, atakhazikitsa m’malingaliro awo ndi cholinga chotsimikizika kuti iwo sakagonjetsedwanso kuti apite komenyana ndi Anefi.

7 Ndipo zidachitika kuti iwo adadzisonkhanitsa okha pamodzi pa mwamba pa phiri limene linkatchedwa Antipa, pokonzekera nkhondo.

8 Tsopano sichidali cholinga cha Amalikiya kuwapatsa iwo nkhondo molingana ndi malamulo a mfumu; koma taonani, chidali cholinga chake kuti apeze kukonderedwa ndi ankhondo a Alamani, kuti iye adziike yekha pa mutu pawo ndi kuchotsa mfumuyo ndi kutenga ufumuwo.

9 Ndipo taonani, zidachitika kuti iye adachititsa ankhondo ake kukhoma mahema awo mu chigwa chimene chidali pafupi ndi phiri la Antipa.

10 Ndipo zidachitika kuti pamene udali usiku iye adatumiza akazembe achinsinsi ku phiri la Antipa, kufuna kuti mtsogoleri wa iwo amene adali pa phirilo, amene dzina lake lidali Lehonti, kuti iye atsike pansi kumusi kwa phirilo, pakuti iye adafuna kuti ayankhule naye.

11 Ndipo zidachitika kuti pamene Lehonti adalandira uthenga iye sadayerekeze kutsika pansi kumusi kwa phirilo. Ndipo zidachitika kuti Amalikiya adatumizanso kwa nthawi yachiwiri, kufuna iye kuti atsike pansi. Ndipo zidachitika kuti Lehonti sadafune; ndipo iye adatumizanso kwa nthawi yachitatu.

12 Ndipo zidachitika kut pamene Amalikiya adapeza kuti iye sadamuthe Lehonti kuti atsike pansi pa phiri, iye adakwera pa phirilo, kuyandikana ndi msasa wa Lehonti; ndipo adatumizanso kwa nthawi yachinayi uthenga kwa Lehonti, kufuna kuti iye atsike pansi, ndipo kuti iye abweretse alonda ake ndi iye.

13 Ndipo zidachitika kuti pamene Lehonti adatsika pansi ndi alonda ake kwa Amalikiya, kuti Amalikiya adafuna iye kuti atsike pansi ndi ankhondo ake mu nthawi ya usiku, ndi kuzungulira anthu amene adali mu msasa wawo pa womwe mfumu adamupatsa iye ulamuliro, ndipo kuti iye adzawapereke iwo m’manja mwa Lehonti, ngati iye angamupange iye (Amalikiya) mtsogoleri wachiwiri pa ankhondo onse.

14 Ndipo zidachitika kuti Lehonti adatsika pansi ndi anthu ake ndipo adazungulira anthu a Amalikiya, kotero kuti asadadzuke pakucha pa tsiku iwo adali atazunguliridwa ndi ankhondo a Lehonti.

15 Ndipo zidachitika kuti pamene iwo adaona kuti iwo adali atazunguliridwa, adamupempha Amalikiya kuti awalore iwo alowerane ndi abale awo, kuti iwo asawonongedwe. Tsopano ichi chidali chinthu chomwecho chimene Amalikiya adafuna.

16 Ndipo zidachitika kuti iye adapereka anthu ake, mosemphana ndi malamulo a mfumu. Tsopano chinthu ichi ndi chimene Amalikiya adafuna, kuti akwaniritse madongosolo ake pochotsa mfumu.

17 Tsopano chidali chikhalidwe cha Alamani, ngati mtsogoleri wamkulu wawo waphedwa, kusankha mtsogoleri wachiwiri kukhala mtsogoleri wamkulu wawo.

18 Ndipo zidachitika kuti Amalikiya adachititsa kuti m’modzi mwa antchito ake apereke mankhwala achiphe pang’onopang’ono kwa Lehonti, mpaka iye adamwalira.

19 Tsopano, pamene Lehonti adamwalira, Alamani adasankha Amalikiya kuti akhale mtsogoleri wawo ndi mkulu wa ankhondo.

20 Ndipo zidachitika kuti Amalikiya adaguba ndi ankhondo ake (pakuti adapeza zokhumba zake) kupita ku dziko la Nefi, ku mzinda wa Nefi, umene udali mzinda waukulu.

21 Ndipo mfumu idabwera kudzakumana naye ndi alonda ake, pakuti idaganiza kuti Amalikiya adakwanilitsa malamulo ake, ndipo kuti Amalikiya adasonkhanitsa pamodzi ankhondo ochuluka kuti apite kukamenyana ndi Anefi ku nkhondo.

22 Koma taonani, pamene mfumu idatuluka kuti ikumane naye, Amalikiya adachititsa kuti antchito ake apite ndi kukakumana ndi mfumuyo. Ndipo adapita ndi kugwadira pamaso pa mfumuyo, ngati kuti akupereka ulemu chifukwa cha ukulu wake.

23 Ndipo zidachitika kuti mfumuyo idatambasula dzanja lake kuti iwadzutse iwo, monga chidali chikhalidwe cha Alamani, ngati chizindikiro cha mtendere, chimene chikhalidwecho adatengera kwa Anefi.

24 Ndipo zidachitika kuti pamene iye adadzutsa oyamba kuchokera pansi, taonani iye adalasa mfumuyo pa mtima, ndipo idagwa pansi.

25 Tsopano antchito a mfumuyo adathawa; ndipo antchito a Amalikiya adafuula, nati:

26 Taonani, antchito a mfumu amulasa iye pa mtima, ndipo wagwa ndipo iwo athawa, taonani, bwerani mudzaone.

27 Ndipo zidachitika kuti Amalikiya adalamula kuti ankhondo ake apite ndipo akaone chimene chidachitika kwa mfumuyo, ndipo pamene iwo adafika pamalopo, ndi kupeza mfumuyo itagona m’mwazi wake, ndipo Amalikiya adanamizira kukwiya, ndipo adati: Aliyense amene amaikonda mfumuyi, apite ndi kuthamangitsa antchitowo kuti iwo aphedwe.

28 Ndipo zidachitika kuti onse amene ankaikonda mfumuyo, pamene adamva mawu awa, adabwera ndi kuthamangitsa antchito a mfumuwo.

29 Tsopano pamene antchito a mfumuwo adaona ankhondo akuwathamangitsa, adawopanso, ndipo adathawira m’chipululu, ndipo adafika ku dziko la Zarahemula ndipo adagwirizana ndi anthu a Amoni.

30 Ndipo ankhondo amene ankawathamangitsawo adabwelera, atawathamangitsa iwo pa chabe; ndipo motero, Amalikiya, mwa chinyengo chake, adakopa mitima ya anthuwo.

31 Ndipo zidachitika kuti m’mawa mwake adalowa mu mzinda wa Nefi ndi ankhondo ake, ndi kutenga mzindawo.

32 Ndipo tsopano zidachitika kuti mfumukazi, pamene idamva kuti mfumu yaphedwa—pakuti Amalikiya adatumiza kazembe kwa mfumukaziyo kukaidziwitsa kuti mfumu yaphedwa ndi antchito ake, kuti iye adawathamangitsa iwo ndi ankhondo ake, koma padali pachabe, ndipo iwo adathawa—

33 Kotero, pamene mfumukaziyo idalandira uthenga umenewu idatumiza kwa Amalikiya, kufuna kwa iye kuti awaleke anthu ake mu mzindawo; ndipo idafunanso kwa iye kuti abwere kwa iye; ndipo idafunanso kwa iye kuti abweretse mboni kudzachitira umboni zokhudzana ndi imfa ya mfumuyo.

34 Ndipo zidachitika kuti Amalikiya adatenga antchito amene adapha mfumu, ndi onse amene adali naye, ndipo adapita kwa mfumukaziyo, ku malo amene idakhala; ndipo onse adachitira umboni kwa iyo kuti mfumu idaphedwa ndi antchito ake omwe; ndiponso adati: Iwo athawa; kodi izi sizikuchitira umboni motsutsana nawo? Ndipo motero iwo adakhutilitsa mfumukaziyo zokhudzana ndi imfa ya mfumu.

35 Ndipo zidachitika kuti Amalikiya adafuna kukonderedwa kwa mfumukaziyo, ndipo adaitenga kukhala mkazi wake; ndipo motero mwa chinyengo chake, ndi kuthandizidwa kwa antchito ake ochenjerawo, iye adatenga ufumu; inde, adavomerezedwa kukhala mfumu mu dziko lonselo, pakati pa anthu onse achilamani, amene adali opangidwa ndi Alamani, ndi Alemueli ndi Aismaeli, ndi onse ogalukira a Anefi, kuchokera ku ulamuliro wa Nefi kufikira ku nthawi imeneyi.

36 Tsopano ogalukirawa, pokhala ndi maphunziro ndi uthenga umodzi wa Anefi, inde, pokhala ophunzitsidwa mu chidziwitso chimodzi cha Ambuye, komabe, ndi zodabwitsa kufotokoza, posakhalitsa potsatira kusagwirizana kwawo iwo adakhala owuma kwambiri ndi osalapa, ndi aukali kwambiri, ndi oipa ndi ankhanza kuposera Alamani—akumwa mu chikhalidwe cha Alamani; kupereka njira ku ulesi, ndi zonyansa zamitundu yonse, inde, kuiwaliratu Ambuye Mulungu wawo.