Malembo Oyera
Alima 34


Mutu 34

Amuleki achitira umboni kuti mawu ali mwa Khristu ku chipulumutso—Pokhapokha chitetezero chichitidwe, anthu onse adzawonongeka—Lamulo lonse la Mose limaloza kwa nsembe ya Mwana wa Mulungu—Dongosolo la muyaya la chiwombolo lakhazikika pa chikhulupiliro ndi kulapa—Muzipempherera pa madalitso akuthupi ndi auzimu—Moyo uno ndi nthawi yokonzekera kukumana ndi Mulungu—Kangalikani pa chipulumutso ndi mantha pamaso pa Mulungu. Mdzaka dza pafupifupi 74 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo zidachitika kuti Alima atamaliza kuyankhula mawu awa kwa iwo iye adakhala pansi pa dothi, ndipo Amuleki adadzuka ndi kuyamba kuphunzitsa iwo nati:

2 Abale anga, ndikuganiza kuti ndizosatheka kuti inu mukhale osadziwa zinthu zimene zayankhulidwa zokhudzana ndi kubwera kwa Khristu, amene waphunzitsidwa kukhala Mwana wa Mulungu; inde, ndikudziwa kuti zinthu izi zidaphunzitsidwa kwa inu mochuluka inu musadagalukire kuchoka pakati pathu

3 Ndipo monga inu mwakhumbira kwa m’bale wanga wokondedwa kuti iye akudziwitseni inu zimene mukuyenera kuchita chifukwa cha masautso anu; ndipo iye wayankhula zinazake kwa inu kukukonzekeretsani maganizo anu; inde, ndipo iye wakulimbikitsani inu ku chikhulupiliro ndi kuleza mtima—

4 Inde, ngakhale kuti inu mukhale ndi chikhulupiliro chachikulu monga ngati kudzala mawu m’mitima mwanu, kuti muyesere kuyesa za ubwino wake.

5 Ndipo ife taona kuti funso lalikulu limene liri m’maganizo mwanu ndilo ngati mawuwa ali mwa Mwana wa Mulungu, kapena ngati sikudzakhala Khristu.

6 Ndipo inu mwaonanso kuti m’bale wanga watsimikizira kwa inu, mu nthawi zambiri, kuti mawu ali mwa Khristu ku chipulumutso.

7 M’bale wanga waitanira pa mawu a Zenosi, kuti chiwombolo chimabwera kudzera mwa Mwana wa Mulungu, ndiponso pa mawu a Zenoki; ndiponso iye wafikiranso kwa Mose, kutsimikizira kuti zinthu izi ndi zoona.

8 Ndipo tsopano taonani, ine ndidzachitira umboni kwa inu mwa ine mwini kuti zinthu izi ndi zoona. Taonani, ndikunena kwa inu, kuti ndikudziwa kuti Khristu adzabwera pakati pa ana a anthu, kudzatenga pa iye zolakwitsa za anthu ake, ndipo kuti iye adzatetezera ku machimo a dziko lapansi; pakuti Ambuye Mulungu wanena izi.

9 Pakuti ndikofunikira kuti chitetezero chipangidwe; pakuti molingana ndi dongosolo lalikulu la Mulungu wa Muyaya kukuyenera kukhala chitetezero chopangidwa, apo ayi anthu onse akuyenera kuwonongeka mosapeweka; inde, onse ndi olimba; inde, onse ndi okugwa, ndipo ndi osochera, ndipo akuyenera kuwonongedwa pokhapokha zitadzera mwa chitetezero chimene chili chofunikira kuti chipangidwe.

10 Pakuti kuli koyenera kuti kukhale nsembe yaikulu ndi yomaliza; inde, si nsembe ya munthu, kapena ya nyama, kapena ya mtundu uli wonse wa mbalame; pakuti siidzakhala nsembe ya munthu; koma ikuyenera kukhala nsembe yopanda malire ndi yamuyaya.

11 Tsopano kulibe munthu aliyense amene akhonza kupereka nsembe mwazi wake umene ungadzatetezere pa machimo amzake. Tsopano, ngati munthu apha, taonani kodi lamulo lathu, limene liri lolungama, lidzatenga moyo wa m’bale wake? Ndinena kwa inu, Ayi.

12 Koma lamulo limafuna moyo wa iye amene wapha; kotero sikungakhale kanthu kamene kali koposa chitetezero chopanda malire chimene chidzakwanire pa machimo a dziko lapansi.

13 Kotero, kuli koyenera kuti payenera kukhala nsembe yaikulu ndi yotsiriza, ndipo pamenepo padzakhala, kapena kuyenera kukhala, kuleka kwa kukhetsa mwazi; pamenepo lamulo la Mose lidzakwaniritsidwa; inde, lonse lidzakwaniritsidwa, kanthu kolembedwa kena kalikonse ndi mutu, ndipo palibe kamene kadzapita.

14 Ndipo taonani, ili ndi tanthauzo lonse la lamulo, kachigawo kalikonse kuloza ku nsembe yaikulu ndi yomalizayo; ndipo kuti nsembe yaikulu ndi yomalizayo idzakhala Mwana wa Mulungu, inde, yopanda malire ndi yamuyaya.

15 Ndipo motero iye adzabweretsa chipulumutso kwa onse amene adzakhulupilire mu dzina lake; izi kukhala cholinga cha nsembe yake yomaliza, kubweretsa zimphyo zake zachifundo, zimene zimaposa chilungamo, ndi kubweretsa njira kwa anthu kuti iwo akhale ndi chikhulupiliro cha kulapa.

16 Ndipo motero chifundo chidzakwaniritsa zofuna za chilungamo, ndikuwazinga iwo m’manja a chitetezo, pemene iye amene sakhala ndi chikhulupiliro adzaikidwa poyera ku lamulo la zofuna za chilungamo; kotero yekhayo amene ali ndi chikhulupiliro cha kulapa wabweretseredwa dongosolo la chiwombolo lalikulu ndi lamuyaya.

17 Kotero Mulungu apereke kwa inu, abale anga, kuti muyambe kuwonetsa chikhulupiliro chanu cha kulapa, kuti muyambe kuitanira pa dzina lake loyera, kuti iye akhale ndi chifundo pa inu.

18 Inde, fuulani kwa iye pa chifundo; pakuti iye ndiwamphamvu zopulumutsa.

19 Inde, dzichepetseni nokha, ndi kupitiriza m’pemphero kwa iye.

20 Fuulani kwa iye pamene muli m’munda mwanu, inde pa ziweto zanu zonse.

21 Fuulani kwa iye mnyumba zanu, inde, pa banja lanu lonse, monse, m’mawa, masana ndi madzulo.

22 Inde, fuulani kwa iye motsutsana ndi mphamvu ya adani anu.

23 Inde, fuulani kwa iye motsutsana ndi mdyerekezi, amene ndi mdani wa chilungamo.

24 Fuulani kwa iye pa zomera za m’munda mwanu, kuti inu mupindule nazo.

25 Lirani pa nkhosa za m’munda mwanu, kuti zichulukane.

26 Koma izizi sizokhazo; mukuyenera kutsanulira mzimu wanu m’zipinda zanu, ndi malo anu obisika, ndi mzipululu zanu.

27 Inde, ndipo pamene inu simukufuula kwa Ambuye, lolani mitima idzale, kukopedwa m’pemphero kwa iye mosalekeza pa ubwino wanu, ndinso pa ubwino wa iwo amene akuzungulirani.

28 Ndipo tsopano taonani, abale okondedwa, ndikunena ndi inu, musaganize kuti izi ndi zonse; pakuti mutatha kuchita zinthu zonsezi, ngati mubweza osowa, ndi amaliseche, ndi kusayendera odwala ndi ovutika, ndi kugawira chuma chanu, ngati mwatero, kwa iwo amene akufuna thandizo—ndinena ndi inu, ngati simuchita zinthu izi, taonani, pemphero lanu liri chabe ndipo silipindula kanthu, ndipo muli achinyengo ngati iwo amene amakana chikhulupiliro.

29 Kotero, ngati inu simukumbukira kukhala achikondi, muli ngati zinyenyeswa zimene osula amazitaya, (izo zokhala zopanda phindu) ndipo zimapondedwa ndi mapazi a anthu.

30 Ndipo tsopano, abale anga, ndikufuna kuti, mutatha kulandira mboni zambiri, poona kuti malembo oyera achitira umboni wa zinthu izi, mubwere ndi kubweretsa zipatso za kulapa.

31 Inde, ndikufuna kuti inu mubwere ndipo musalimbitsebe mitima yanu; pakuti taonani, ino ndi nthawi ndi tsiku la chipulumutso chanu; ndipo kotero, ngati inu mulapa ndi kusalimbitsa mitima yanu, mosachedwa dongosolo la chiwombolo lalikulu lidzabweretsedwa kwa inu.

32 Pakuti taonani, moyo uno ndi nthawi yoti anthu akonzekere kukumana ndi Mulungu; inde, taonani tsiku la moyo uno ndi tsiku loti anthu agwire ntchito zawo.

33 Ndipo tsopano, monga ndanena kwa inu kale, monga mwakhala ndi mboni zochuluka, kotero, ndikukupemphani inu kuti musachedwetse tsiku lakulapa kwanu kufikira kumapeto; pakuti pakutha pa tsiku ili la moyo, limene lapatsidwa kwa ife kuti tikonzekere muyaya, taonani, ngati sitikonza nthawi yathu imene ili m’moyo uno, ndiye kudzabwera usiku wa mdima umene sikudzagwiridwa ntchito.

34 Simunganene, pamene mwabweretsedwa ku zovuta zoopsyazo, kuti ndilapa, kuti ndibwelera kwa Mulungu wanga. Ayi, simunganene izi; pakuti mzimu omwewo umene umakhala m’nthupi mwanu pa nthawi yomwe inu mukuchoka m’moyo uno, ndi mzimu omwewo umene udzakhale ndi mphamvu yokhala ndi thupi lanu mu dziko lamuyayalo.

35 Pakuti taonani, ngati inu mwachedwetsa tsiku la kulapa kwanu ngakhale kufikira imfa, taonani, mudzaperekedwa ku mzimu wa mdyerekezi, ndipo iye wakutsindikizani kukhala ake; kotero, Mzimu wa Ambuye wachoka mwa inu, ndipo alibe malo mwa inu, ndipo mdyerekezi ali ndi mphamvu zonse pa inu; ndipo ichi ndicho chikhalidwe chomaliza cha oipa.

36 Ndipo ichi ndikudziwa, chifukwa Ambuye anena kuti samakhala mu kachisi odetsedwa, koma m’mitima ya olungama iye amakhalamo; inde, ndipo iye anenanso kuti olungama adzakhala pansi mu ufumu wake, sadzatulukamonso; koma zovala zawo zidzayeretsedwa ndi mwazi wa mwana wa Nkhosa.

37 Ndipo tsopano, abale anga okondedwa, ndikufuna kuti mukumbukire zinthu izi, ndipo kuti mugwire ntchito ya chipulumutso chanu ndi mantha pamaso pa Mulungu, ndipo kuti musakanenso zakubwera kwa Khristu.

38 Kuti musalimbanenso ndi Mzimu Woyera, koma kuti inu muulandira, ndi kutengera pa inu dzina la Khristu; kuti mudzichepetse nokha ngakhale ku fumbi, ndi kupembedza Mulungu, mu malo ena aliwonse amene mungakhale, mu Mzimu ndi choonandi; kuti inu mukhale chiyamiko tsiku lilironse, pa zifundo zambiri ndi madalitso amene iye amapereka kwa inu.

39 Inde, ndiponso ndikukulimbikitsani inu, abale anga, kuti mukhale tcheru pa pemphero mosalekeza, kuti musasocheletsedwe ndi mayesero a mdyerekezi, kuti iye asakugonjetseni inu, kuti inu musakhale anthu ake pa tsiku lomaliza, pakuti taonani, iye samapereka mphoto yabwino kwa inu.

40 Ndipo tsopano abale anga okondedwa, ndikukulimbikitsani inu kuti mukhale oleza mtima, ndipo kuti mupilire masautso osiyanasiyana; kuti musanyoze amene akuthamangitsani inu chifukwa cha kusauka kwanu kochuluka, kuti mungakhale ochimwa ngati iwo.

41 Koma kuti mukhale oleza mtima, ndikupilira masautsowo, ndi chiyembekezo chokhwima kuti tsiku lina mudzapumule ku masautso anu onse.