Malembo Oyera
Alima 39


Malamulo a Alima kwa mwana wake Koriyantoni.

Yophatikiza mitu 39 mpaka 42.

Mutu 39

Tchimo lachiwerewere ndi lonyansa—Machimo a Koriyantoni adakanikitsa Azoramu kulandira mawu—Chiwombolo cha Khristu ndi chotsatira pakupulumutsa okhululupirika amene adayambilira. Mdzaka dza pafupifupi 74 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo tsopano, mwana wanga, ndili ndi zina zoti ndinene kwa iwe zowonjezera kuposera zomwe ndidanena kwa m’bale wako; pakuti taona, kodi sudaone kukhazikika kwa m’bale wako, kukhulupirika kwake, ndi khama lake m’kusunga malamulo a Mulungu? Taona, kodi iye sadapereke chitsanzo chabwino kwa iwe?

2 Pakuti iwe sudamvetsere kwambiri ku mawu anga monga m’mene adachitira m’bale wako, pakati pa anthu Achizoramu. Tsopano izi ndi zomwe ndili kutsutsana nawe; iwe udapita m’kudzitamandira mu mphamu zako ndi nzeru zako.

3 Ndipo izi si zonse, mwana wanga. Iwe udachita chimene chili chowawa kwa ine; pakuti udasiya utumiki, ndi kupita ku dziko la Sironi pakati pa malire a Alamani, kutsata mkazi wachigololo Isabelo.

4 Inde, iye adatenga mitima ya anthu ambiri; koma sichidali chifukwa kwa iwe, mwana wanga. Iwe udayenera kusamala utumiki umene iwe udapatsidwa.

5 Kodi sukudziwa, mwana wanga, kuti zinthu izi ndi zonyansa pamaso pa Ambuye; inde, zonyansa kwambiri kuposa machimo onse kupatula kukhetsa kwa mwazi wa osalakwa kapena kukana Mzimu Woyera?

6 Pakuti taona, ngati iwe ukana Mzimu Woyera pamene udali ndi malo mwa iwe, ndipo iwe ukudziwa kuti waukana, taona, ili ndi tchimo limene silingakhululukidwe; inde aliyense amene aphe motsutsana ndi kuwala ndi chidziwitso cha Mulungu, ndi kovuta kwa iye kulandira chikhululukiro; inde, ndikunena ndi iwe, mwana wanga, kuti ndikosavuta kwa iye kulandira chikhululukiro.

7 Ndipo tsopano, mwana wanga, ndikufunitsa kwa Mulungu kuti iwe usakhale olakwa ndi tchimo lalikululi. Sindikadafuna kukhazikika pa zolakwa zako, kukhumudwitsa mzimu wako, ngati sikudali kwa ubwino wako.

8 Ndipo taona, iwe sungabise zolakwa zako kwa Mulungu; ndipo pokhapokha utalapa zidzaima ngati umboni otsutsana nawe patsiku lomaliza.

9 Tsopano mwana wanga, ndikufuna kuti iwe ulape ndi kusiya machimo ako, ndipo usapitenso kutsatira zilakolako za maso ako, koma udzikanize wekha muzinthu zonsezi; pakuti pokhapokha uchite izi siungalandire ufumu wa Mulungu. O, kumbukira, ndi kuchitenga pa iwe, ndi kudzikaniza wekha mu zinthu izi.

10 Ndipo ndikukulamula iwe kuti utenge pa iwe langizo la akulu ako mu zochita zako, pakuti taona, iwe uli mu chinyamata chako, ndipo ukufunikira kusamalidwa ndi abale ako. Ndi kumvetsera malangizo awo.

11 Usadzilole wekha kuti usocheretsedwe ndi zachabechabe kapena zinthu zopusa; usalore kuti mdyerekezi asocheretse mtima wako kachiwiri kutsatira akazi achigololo oipawo. Taona, O mwana wanga, n’kwakukulu motani kuipa zimene udabweretsa kwa Azoramu; pakuti taona pamene iwo adaona zochita zako iwo sadakhukhulupilire mu mawu anga.

12 Ndipo tsopano Mzimu wa Ambuye ukunena kwa ine: Lamulira ana ako kuchita zabwino, kuopa angasochoretse mitima ya anthu ambiri kuchiwonongeko; kotero ndikukulamula iwe, mwana wanga, m’kuopa kwa Mulungu, kuti udziletse ku mphulupulu zako.

13 Kuti iwe utembenukire kwa Ambuye ndi nzeru zako zonse, ndi nyonga ndi mphamvu; kuti usasocheletsenso mitima ya ena kuchita zoipa; koma makamaka bwelera kwa iwo, ndi kuvomeleza kulakwitsa kwako, ndi zolakwika zimene iwe wazichita.

14 Usafune chuma kapena zinthu zachabechabe za dziko lapansili; pakuti taona, siungathe kuzinyamula ndi iwe.

15 Ndipo tsopano, mwana wanga, ndikufuna kunena pang’ono kwa iwe zokhudzana ndi kubwera kwa Khristu. Taona, ndikunena ndi iwe, kuti ndi iyeyo amene adzabwere ndithu kudzachotsa machimo a dziko lapansi; inde, iye ali nkudza kudzalalikira Uthenga Wabwino wa chipulumutso kwa anthu ake.

16 Ndipo tsopano, mwana wanga, uwu ndi utumiki umene iwe udaitanidwira, kukalalikira uthenga wabwino umenewu kwa anthu awa, kukakonzekeretsa malingaliro awo; kuti mwina kapena chipulumutso chingabwere kwa iwo, kuti iwo akonzekeretse malingaliro a ana awo kukamvera mawu pa nthawi yakubwera kwake.

17 Ndipo tsopano ine ndipeputsa malingaliro ako pa mutu uwu. Taona, iwe ukudabwa chifukwa chiyani zinthu izi zikuyenera kudziwika kale nthawi isadakwane. Taona, ndikunena ndi iwe, kodi moyo pa nthawi ino siwamtengo wapatali kwa Mulungu monga moyo udzakhale pa nthawi ya kubwera kwake?

18 Kodi sikoyenera kuti dongosolo la chiwombolo lidziwike kwa anthu awa chimodzimodzi ndi kwa ana awo?

19 Kodi sikophweka pa nthawi ino kwa Ambuye kutumiza angelo kukalalikira uthenga wabwino kwa ife monga kwa ana athu, kapena monga potsatira kubwera kwake?

Print