Malembo Oyera
Alima 53


Mutu 53

Akaidi Achilamani agwiritsidwa ntchito yolimbitsa mzinda wa Chuluka—Migawaniko pakati pa Anefi ikulitsa chipambano cha Alamani—Helamani atenga ulamuliro wa zikwi ziwiri za ana aamuna achinyamata a anthu a Amoni. Mdzaka dza pafupifupi 64–63 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo zidachitika kuti iwo adaika alonda pa akaidi Achilamani, ndipo adawakakamiza kuti iwo apite ndi kukakwilira akufa awo, inde, ndiponso akufa Achinefi amene adaphedwa; ndipo Moroni adaika anthu pa iwo kuti awalondele pamene ankagwira ntchitoyo.

2 Ndipo Moroni adapita ku mzinda wa Muleki ndi Lehi, ndipo adatenga ulamuliro wa mzindawo ndi kuupereka kwa Lehi. Tsopano taonani, Lehi uyu adali munthu amene adali ndi Moroni mu magawo ambiri ankhondo zake; ndipo adali munthu ngati Moroni, ndipo adakondwera mu chitetezo cha wina ndi mzake; inde, adali okondana wina ndi mzake, ndiponso okondedwa ndi anthu onse a Nefi.

3 Ndipo zidachitika kuti atamaliza Alamani kukwilira akufa awo, ndiponso akufa Achinefi, adawagubitsa kubwelera ku dziko la Chuluka; ndipo Teyankumu, kudzera mu malamulo a Moroni, adachititsa kuti iwo ayambe ntchito yokumba dzenje lozungulira dzikolo, kapena mzinda wa Chuluka.

4 Ndipo iye adachititsa kuti iwo amange mpanda wamatabwa muchifuwa pa mulu wa dothi la mkati mwadzenie; ndipo adatulutsa dothi kunja kwa mpanda omangidwa ndi matabwa; ndipo motero iwo adachititsa kuti Alamani agwire ntchito kufikira atazungulira mzinda onse wa Chuluka ndi khoma lolimba la matabwa ndi dothi, lotalika kwambiri.

5 Ndipo mzinda umenewu udakhala olimba kwambiri kuchokera pamenepo; ndipo mu mzinda umenewu iwo ankalonderamo akaidi Achilamani, inde, ngakhale mkati mwa makoma amene iwo adachititsa kuti awamange ndi manja awo omwe. Tsopano Moroni adakakamizika kuti achititse kuti Alamani agwire ntchito, chifuwa kudali kosavuta kuwalondera iwo pamene iwo ankagwira ntchito; ndipo ankafuna ankhondo ake onse pamene iye angafune kuukira Alamani.

6 Ndipo zidachitika kuti Moroni adali atagonjetsa limodzi mwa magulu ankhondo aakulu kwambiri Achilamani, ndipo iye adalanda mzinda wa Muleki, umene udali umodzi mwa dera lolimba kwambiri la Alamani mu dziko la Nefi; ndipo motero iyenso adamanga malinga kuti asunge akaidi ake.

7 Ndipo zidachitika kuti iye sadayeserenso nkhondo ndi Alamani mu chaka chimenecho, koma iye adathandiza athu ake kukonzekera nkhondo, inde, ndipo adapanga malinga kuti adzitetezere kwa Alamani, inde, ndiponso kuwawombola azimayi awo ndi ana awo ku njala ndi masautso, ndi kupereka chakudya kwa ankhondo ake.

8 Ndipo tsopano zidachitika kuti ankhondo Achilamani, chakumadzulo kwa nyanja, cha kum’mwera, pamene Moroni adachoka chifukwa cha chiwembu pakati pa Anefi, chimene chidayambitsa kugawikana pakati pawo, adapeza mwayi pa Anefi, inde, kotero kuti adalanda mizinda ingapo ya chigawo chimenecho cha dzikolo.

9 Ndipo motero chifukwa cha kusaweruzika pakati pawo, inde, chifukwa cha kugawanika ndi chiwembu pakati pawo iwo adaikidwa mu nyengo yoopsya kwambiri.

10 Ndipo tsopano taonani, ndili ndi zina zoti ndinene zokhudzana ndi anthu a Amoni, amene, pachiyambi, adali Alamani; koma chifukwa cha Amoni ndi abale ake, kapena kuti chifukwa cha mphamvu ndi mawu a Mulungu, iwo adatembenukira kwa Ambuye; ndipo adabweretsedwa ku dziko la Zarahemula, ndipo ankatetezedwa kuyambira pamenepo ndi Anefi.

11 Ndipo chifukwa cha lumbiro lawo iwo sankaloledwa kutenga zida motsutsana ndi abale awo; chifukwa iwo adatenga lumbiro kuti sadzakhetsanso mwazi; ndipo molingana ndi lumbiro lawo iwo akadatha kutaika; inde, akadadzilora okha kugwa m’manja mwa abale awo, pakadapanda chisoni ndi chikondi chachikulu chimene Amoni ndi abale ake adali nacho kwa iwo.

12 Ndipo pachifukwa ichi iwo adabweretsedwa ku dziko la Zarahemula; ndipo iwo ankatetezedwa ndi Anefi.

13 Koma zidachitika kuti pamene iwo adaona choopsya, ndi mazunzo ambiri ndi zosautsa zimene Anefi adazinyamula chifukwa cha iwo, iwo adasunthidwa ndi chifundo ndipo adali ndi chikhumbo chonyamula zida kuti ateteze dziko lawo.

14 Koma taonani, pamene iwo adali pafupi kutenga zida zawo zankhondo, iwo adagonjetsedwa ndi kunyengelera kwa Helamani ndi abale ake, pakuti iwo adali pafupi kuphwanya lumbiro limene iwo adapanga.

15 Ndipo Helamani adaopa kuti pakutero iwo adzataya miyoyo yawo; kotero onse amene adalowa mu pangano limeneli adakakamizidwa kuwonelera abale awo akugwa muzosautsa zawo, mu nyengo zawo zoopsya pa nthawiyi.

16 Koma taonani, zidachitika kuti iwo adali ndi ana aamuna ambiri, amene sadalowe nawo mu pangano loti sadzatenga zida za nkhondo kudzitetezera okha motsutsana ndi adani awo; kotero iwo adadzisonkhanitsa okha pamodzi pa nthawiyi, ochuluka amene akadatha kunyamula zida, ndipo adadzitcha okha Anefi.

17 Ndipo iwo adalowa mu pangano loti adzamenyera ufulu wa Anefi, inde, kutetezera dziko mpaka kutaya pansi miyoyo yawo, inde, ngakhale kupangana kuti iwo sadzapereka konse ufulu wawo, koma iwo adzamenya muzochitika zonse kuti ateteze Anefi ndi iwo eni ku ukapolo.

18 Ndipo tsopano, adalipo zikwi ziwiri za achinyamatawo, amene adalowa mu panganoli ndipo adatenga zida zawo za nkhondo kuteteza dziko lawo.

19 Ndipo tsopano taonani, monga sipadakhalepo zovuta pa Anefiwa, iwo adakhala tsopano pa nyengo ya nthawiyi thandizo lalikulu; pakuti iwo adatenga zida zawo zankhondo, ndipo adafuna kuti Helamani akhale mtsogoleri wawo.

20 Ndipo onse adali achinyamata, ndipo adali olimba mtima kwambiri, ndiponso amphamvu ndi amachitachita; koma taonani, izi sizidali zokhazo—adali anthu amene adali woona mtima pa nthawi zonse mu chinthu chinachilichonse chimene iwo adadaliridwa

21 Inde, iwo adali anthu a choonadi ndi odziretsa, pakuti adali ataphunzitsidwa kusunga malamulo a Mulungu ndi kuyenda moongoka pamaso pake.

22 Ndipo tsopano zidachitika kuti Helamani adaguba patsogolo pa ankhondo ake achinyamata zikwi ziwiri, kukathandizira anthu a kumalire kwa dzikolo chakum’mwera kwa nyanja yakumadzulo.

23 Ndipo motero chidatha chaka cha makumi awiri ndi zisanu n’chitatu cha ulamuliro wa oweruza pa anthu a Nefi.

Print