Malembo Oyera
Alima 38


Malamulo a Alima kwa mwana wake Shibuloni.

Yophatikiza mutu 38.

Mutu 38

Shibuloni adazunzidwa chifukwa cha chilungamo—Chipulumutso chili mwa Khristu, amene ali moyo ndi kuwala kwa dziko lapansi—Letsani zilakolako zanu zonse. Mdzaka dza pafupifupi 74 Yesu asadabadwe.

1 Mwana wanga, mvetsera ku mawu anga, pakuti ndikunena ndi iwe, monga m’mene ndidanenera kwa Helamani, kuti monga momwe iwe udzasunge malamulo a Mulungu udzachita bwino m’dzikoli; ndipo monga momwe iwe siudzasunga malamulo a Mulungu udzadulidwa kuchoka pamaso pake.

2 Ndipo tsopano, mwana wanga, ndikhulupilira kuti ndidzakhala ndi chisangalalo chachikulu mwa iwe, chifukwa cha kukhazikika kwako ndi kukhulupirika kwako kwa Mulungu; pakuti monga iwe wayambira m’chinyamata chako kuyang’ana kwa Ambuye Mulungu wako, momwemonso ine ndikuyembekeza kuti iwe udzapitiriza kusunga malamulo ake; pakuti wodala ndi iye amene apilira kufikira chimaliziro.

3 Ndikunena kwa iwe, mwana wanga, kuti ndakhala ndi chisangalalo chachikulu mwa iwe tsopano, chifukwa cha kukhulupirika kwako ndi khama lako, ndi kuleza mtima kwako, ndi chipiliro chako pakati pa anthu Achizoramu.

4 Pakuti ndikudziwa kuti iwe udamangidwa; inde, ndipo ndikudziwanso kuti iwe udagendedwa chifukwa cha mawu; ndipo iwe udapilira zinthu zonsezi ndi kuleza mtima chifukwa choti Ambuye adali nawe; ndipo tsopano iwe ukudziwa kuti Ambuye adakupulumutsa iwe.

5 Ndipo tsopano mwana wanga, Shibuloni, ndikufuna kuti ukumbukire, kuti monga momwe iwe udzayika chikhulupiliro chako mwa Mulungu ngakhale kochuluka kwambiri iwe udzapulumutsidwa kuchokera m’mayesero ako, ndi mu mavuto ako, ndi mu masautso ako, ndipo iwe udzakwezedwa pa tsiku lomaliza.

6 Tsopano, mwana wanga, sindikufuna kuti iwe uganize kuti ndikudziwa zinthu izi mwa ndekha, koma ndi Mzimu wa Mulungu umene uli mwa ine umene umadziwitsa za zinthu izi kwa ine; pakuti ngati ndidakapanda kubadwa mwa Mulungu sindikadadziwa zinthu izi.

7 Koma taona, Ambuye mu chifundo chawo chachikulu adatumiza mngelo kudzandiuza ine kuti ndisiye ntchito ya kuwononga pakati pa anthu ake; inde, ndipo ndidaona mngelo maso ndi maso, ndipo iye adayankhula nane, ndipo mawu ake adali ngati bingu, ndipo adagwedeza dziko lonse.

8 Ndipo zidachitika kuti ndidakhala masiku atatu usana ndi usiku mu ululu owawa kwambiri ndi kuwawidwa mzimu; ndipo ayi, kufikira nditalilira kwa Ambuye Yesu Khristu chifundo, ndidalandira chikhululukiro cha machimo anga. Koma taona, ndidalira kwa iye ndipo ndidapeza mtendere m’mzimu mwanga.

9 Ndipo tsopano, mwana wanga, ndakuuza izi kuti iwe uphunzire nzeru, kuti uphunzire kwa ine kuti palibe njira ina kapena kuthekera kumene munthu angapulumutsidwire, pokhapokha mwa ndi kudzera mwa Khristu basi. Taona, iye ndi moyo ndi kuwala kwa dziko lapansi. Taona, iye ndi mawu a choonadi ndi chilungamo.

10 Ndipo tsopano, monga iwe wayambira kuphunzitsa mawu ngakhale motero ine ndikufuna kuti upitilize kuphunzitsa; ndipo ndikufuna kuti ukhale wakhama ndi kudziletsa mu zinthu zonse.

11 Ona kuti usakhale odzikweza m’kunyada, inde, ona kuti sukudzitamandira mu nzeru zako, ngakhale mu mphamvu zako zambiri.

12 Gwiritsa ntchito kulimba mtima, koma osati kupondereza; ndiponso ona kuti wadziletsa zilakolako zako zonse, kuti udzadzidwe ndi chikondi; ona kuti ukupewa ulesi.

13 Usamapemphere monga Azoramu amachitira, pakuti iwe waona kuti iwo amapemphera kuti amvedwe ndi anthu, ndipo kuti atamandidwe chifukwa cha nzeru zawo.

14 Usamati: O Mulungu, ndikukuthokozani inu kuti ife ndife abwino kuposa abale athu; koma udziti; O Ambuye, mundikhululukire ine kusayenera kwanga, ndipo kumbukirani abale anga mu chifundo—inde, vomereza kusayenera kwako pamaso pa Mulungu.

15 Ndipo Ambuye adalitse mzimu wako, ndi kukulandira iwe pa tsiku lomaliza mu ufumu wake, kukhala pansi mu mtendere. Tsopano pita, mwana wanga, ndipo kaphunzitse mawu kwa anthu awa. Khala tcheru. Mwana wanga, tidzaonana.

Print