Mutu 35
Kulalika kwa mawu kuwononga chinyengo cha Azoramu—Iwo achotsa otembenuka, amene pambuyo pake alumikizana ndi anthu a Amoni ku Yeresoni—Alima amva chisoni chifukwa cha kuipa kwa anthu. Mdzaka dza pafupifupi 74 Yesu asadabadwe.
1 Tsopano zidachitika kuti Amuleki atamaliza mawu awa, iwo adadzichotsa okha kuchoka pa khamulo ndi kubwera kudziko la Yeresoni.
2 Inde, ndipo abale onse, atamaliza kulalikira mawu kwa Azoramu, nawonso adabwera ku dziko la Yeresoni.
3 Ndipo zidachitika kuti atamaliza gawo lodziwika kwambiri la Azoramu lidafunsana pamodzi zokhudzana ndi mawu amene adalalikidwa kwa iwo, adakwiya chifukwa cha mawuwo, pakuti adawononga chinyengo chawo, kotero sadamvere mawuwo.
4 Ndipo adaitanitsa ndi kusonkhanitsa pamodzi dziko lonselo anthu onse, ndipo adafunsa iwo zokhudzana ndi mawu amene adayankhulidwa.
5 Tsopano olamulira awo ndi ansembe awo ndi aphunzitsi awo sadafune anthu adziwe zolinga zawo; kotero adapeza mwachinsinsi maganizo a anthu onse.
6 Ndipo zidachitika kuti atamaliza kupeza maganizo a anthu onse, iwo amene adali kugwirizana ndi mawu amene adayankhulidwa ndi Alima ndi abale ake adaponyedwa kunja kwa dzikolo; ndipo adalipo ambiri; ndipo adabweranso ku dziko la Yeresoni.
7 Ndipo zidachitika kuti Alima ndi abale ake adatumikira kwa iwo.
8 Tsopano anthu Azoramu adakwiya ndi anthu a Amoni amene adali ku Yeresoni, ndipo mkulu olamulira wa Azoramu, okhala munthu oipa kwambiri, adaitanitsa anthu a Amoni kufuna kuti awathamangitse mu dziko lawo onse amene adabwera kuchokera kwa iwo kupita kudziko lawo
9 Ndipo adayankhula mawu ambiri owopsyeza motsutsuna nawo. Ndipo tsopano anthu a Amoni sadaope mawu awo; kotero iwo sadawathamangitse, koma iwo adalandira onse osauka achizoramu kuti abwere kwa iwo; ndipo adawadyetsa iwo, ndi kuwaveka iwo, ndipo adawapatsa iwo malo amakolo awo; ndipo adatumikira kwa iwo molingana ndi zofuna zawo.
10 Tsopano izi zidasonkhezera Azoramu kukwiya ndi anthu a Amoni ndipo adayamba kusakanizana ndi Alamani ndi kuwasonkhezeranso iwo kuti akwiye nawo.
11 Ndipo motero Azoramu ndi Alamani adayamba zokonzekera kuchita nkhondo ndi anthu a Amoni, ndiponso ndi Anefi.
12 Ndipo choncho chidatha chaka cha khumi ndi zisanu ndi ziwiri za ulamuliro wa oweruza pa anthu a Nefi.
13 Ndipo anthu a Amoni adachoka ku dziko la Yeresoni, ndi kubwera ku dziko la Meleki, ndi kupereka malo mu dziko la Yeresoni kwa ankhondo Achinefi, kuti iwo amenyane ndi ankhondo Achilamani ndi ankhondo Achizoramu; ndipo choncho idayambika nkhondo pakati pa Alamani ndi Anefi, mu chaka cha khumi ndi chisanu ndi chitatu cha ulamuliro wa oweruza; ndipo nkhani za nkhondo zawo zidzaperekedwa patsogolo.
14 Ndipo Alima, ndi Amoni, ndi abale ake, ndiponso ana aamuna awiri a Alima adabwelera ku dziko la Zarahemula, atakhala zida m’manja mwa Mulungu pobweretsa ambiri mwa Azoramu m’kulapa; ndipo monga ambiri amene adabweretsedwa m’kulapa adathamangitsidwa m’maiko awo; koma iwo ali ndi malo acholowa chawo mu dziko la Yeresoni, ndipo iwo anyamula zida kudziteteza okha, ndi akazi awo, ndi ana awo, ndi dziko lawo.
15 Tsopano Alima, pokhala ndi chisoni chifukwa cha kusaweruzika kwa anthu ake, inde chifukwa cha nkhondo, ndi kukhetsa mwazi, ndi mikangano imene idali pakati pawo; ndipo atapita kokalalikira mawu, kapena kutumidwa kolalikira mawu, pakati pa anthu onse mu mzinda uliwonse; ndipo poona kuti mitima ya anthu idayamba kulimba, ndipo kuti adayamba kukhumudwa chifukwa cha kukhwimitsa kwa mawuwo, mtima wake udamva chisoni kwambiri.
16 Kotero, iye adachititsa kuti ana ake aamuna asonkhane pamodzi, kuti iye apereke kwa aliyense udindo wake, payekhapayekha, okhudzana ndi zinthu za chiyero. Ndipo tili ndi nkhani ya malamulo ake, amene iye adapereka kwa iwo molingana ndi mbiri yake yomwe.