Malembo Oyera
Alima 12


Mutu 12

Alima ayankhula ndi Zeziromu—Zinsisi za Mulungu zikhonza kuperekedwa kwa okhulupilika okha—Anthu amaweruzidwa ndi maganizo awo, zikhulupiliro zawo, ndi ntchito—Oipa adzazunzika imfa ya uzimu—Moyo wachivundiwu ndi nyengo yongoyesedwera—Dongosolo la chiwombolo limabweretsa Chiukitso ndipo, kudzera m’chikhulupiliro, chikhululukiro cha machimo—Olapa ali ndi danga la chifundo kudzera mwa Mwana Wobadwa Yekha. Mdzaka dza pafupifupi 82 Yesu asadabadwe.

1 Tsopano Alima, poona kuti mawu a Amuleki adatseketsa pakamwa Zeziromu, pakuti iye adaona kuti Amuleki adamugwira iye mu bodza lake ndi chinyengo choti amuwononge iye, ndi poona kuti iye adayamba kunjenjemera pansi pakuzindikira kulakwa kwake, adatsekula pakamwa pake ndi kuyamba kuyankhula kwa iye, ndi kukhazikitsa mawu a Amuleki, ndikulongosola zinthu mopitiriza, kapena kutambasula malembo oyera kupitiriza zimene Amuleki adachita.

2 Tsopano mawu amene Alima adayankhula kwa Zeziromu adamvedwa ndi anthu ozungulira; pakuti khamulo lidali lalikulu, ndipo adayankhula motere:

3 Tsopano Zeziromu, poona kuti iwe watengedwa mu bodza lako ndi chinyengo, pakuti siudanamize anthu wokha koma iwe wanama kwa Mulungu; pakuti taona, iye amadziwa maganizo ako onse, ndipo ukuona kuti maganizo ako adziwitsidwa kwa ife mwa Mzimu wake;

4 Ndipo iwe ukuona kuti ife tikudziwa kuti dongosolo lako lidali dongosolo lochenjera kwambiri, monga kuchenjera kwa mdyerekezi, pakunamiza ndi kunyenga anthu awa kuti iwe uwapangitse kudana nafe, kuti atinyoze ife ndi kutithamangitsa ife—

5 Tsopano ili lidali dongosolo la mdani wako, ndipo iye wagwiritsa tchito mphamvu yake mwa iwe. Tsopano ndikufuna kuti iwe ukumbukire kuti zomwe ndikunena kwa iwe ndikunena kwa onse.

6 Ndipo taonani ndikunena kwa inu nonse kuti uwu udali msampha wa mdani, umene adautchera kuti agwire anthu awa, kuti iye akubweretseni inu kukamumvera iye, kuti iye akakuzingeni inu ndi maunyolo ake, kuti akumangeni inu mpaka ku chiwonongeko chosatha, molingana ndi mphamvu yake ya ukapolo.

7 Tsopano pamene Alima adayankhula mawu awa, Zeziromu adayamba kunjenjemera kwambiri, pakuti adakhutitsidwa kwambiri ndi mphamvu ya Mulungu; ndiponso adakhutitsidwa kuti Alima ndi Amuleki adali ndi chidziwitso cha iye, pakuti adakhutitsidwa kuti ankadziwa maganizo ndi zofuna za muntima wake; pakuti mphamvu idapatsidwa kwa iwo kuti athe kudziwa zinthu izi monga mwa mzimu wa uneneri.

8 Ndipo Zeziromu adayamba kufunsa kwa iwo molimbikira, kuti iye adziwe zambiri zokhudzana ndi ufumu wa Mulungu. Ndipo iye adati kwa Alima: Kodi zikutanthauza chiyani zimene Amuleki wanena zokhudzana ndi chiukitso cha akufa, kuti onse adzauka kwa akufa, onse wolungama ndi wosalungama womwe, ndipo adzabweretsedwa kuima pamaso pa Mulungu kuti aweruzidwe ku ntchito zawo?

9 Ndipo tsopano Alima adayamba kufotokoza zinthu izi kwa iye, nati: kwapatsidwa kwa ambiri kudziwa zinsisi za Mulungu; komabe zaikidwa pa lamulo lokhwima kuti asadzapereke kokha molingana ndi gawo la mawu ake amene iye amapereka kwa ana a anthu, molingana ndi kumvera ndi khama limene iwo amapereka kwa iye.

10 Ndipo kotero, iye amene adzalimbitsa mtima wake, yemweyo alandira gawo lochepa la mawu; ndipo iye amene sadzalimbitsa mtima wake, kwa iye kwapatsidwa gawo lalikulu la mawu, kufikira atapatsidwa kwa iye kuti adziwe zinsinsi za Mulungu kufikira atadziwa zonse kwathunthu.

11 Ndipo iwo amene adzalimbitsa mitima yawo, kwa iwo kwapatsidwa gawo lochepa la mawu kufikira sadzadziwa kanthu kokhudzana ndi zinsinsi zake; ndipo kenako atengedwa ukapolo ndi mdyerekezi, ndikutsogoleredwa ndi chifuniro chake kufika kuchiwonongeko. Tsopano izi ndi zimene zikutanthauza pa maunyolo a gahena.

12 Ndipo Amuleki wayankhula momveka zokhudzana ndi imfa, ndikuwukitsidwa kuchokera ku chivundi ichi kupita ku chisavundi, ndi kubweretsedwa pamaso pa bwalo lamilandu la Mulungu, kukaweruzidwa molingana ndi ntchito zathu.

13 Ndiye ngati mitima yathu yakhala yolimba, inde, ngati ife talimbitsa mitima yathu motsutsana ndi mawu, mpakana kuti sadapezeke mwa ife, pamenepo tidzakhala mu mkhalidwe oopsa, pakuti pamenepo tidzatsutsidwa

14 Pakuti mawu athu adzatitsutsa ife, inde, ntchito zathu zonse zidzatitsutsa ife; sitidzapezeka opanda banga; ndipo maganizo athu adzatitsutsanso; ndipo mu mkhalidwe oopsa uwu sitidzayerekeza kuyang’ana kwa Mulungu wathu; ndipo tidzafunitsitsa bola tikadalamula miyala ndi mapiri kuti zigwere pa ife kutibisa pamaso pake.

15 Koma izi sizingatheke; tikuyenera kubwera ndi kuima pamaso pake mu ulemelero wake, ndi mu mphamvu yake, ndi mu nyonga zake, mu ukulu, ndi ulamuliro, ndi kuvomereza ku manyazi athu osatha kuti ziweruzo zake zonse ndi zolungama; kuti iye ndi wachilungamo mu ntchito zake zonse, ndipo kuti iye ndiwachifundo kwa ana a anthu, ndi kuti iye ali ndi mphamvu zonse zakupulumutsa munthu aliyense amene akhulupilira pa dzina lake ndi kubweretsa zipatso zoyenera kulapa.

16 Ndipo tsopano taonani, ndikunena kwa inu kenako kudzabwera imfa, ngakhale imfa yachiwiri, imene ndi imfa yauzimu; kotero ndi nthawi imene aliyense amene amwalira mu machimo ake, monga mwa imfa ya kuthupi, adzafanso imfa ya uzimu; iye adzafa monga mwa zinthu zokhudzana ndi chilungamo.

17 Kenako ndi nthawi imene kuzunzika kwawo kudzakhala ngati nyanja ya moto ndi sulufule, umene malawi ake akwera m’mwamba kunthawi za nthawi, ndipo pamenepo ndi nthawi imene iwo adzamangidwe maunyolo kunka kuchiwonongeko chosatha, molingana ndi mphamvu ndi ukapolo wa Satana, iye atawakhazika iwo molingana ndi chifuniro chake.

18 Pamenepo, ndikunena kwa inu, iwo adzakhala ngati kuti chiwombolo sichidachitike; pakuti sangawomboledwe monga mwa chilungamo cha Mulungu, ndipo sangafe, poona kuti palibenso chivundi.

19 Ndipo zidachitika kuti pamene Alima adamaliza kuyankhula mawu awa, anthu adayamba kuzizwa kwambiri;

20 Koma adalipo wina Antiona, amene adali mkulu olamulira pakati pawo, adabwera patsogolo nati kwa iye: Kodi ndi chiyani ichi chomwe wanena, kuti munthu adzauka kwa akufa ndipo adzasinthidwa kuchokera ku mkhalidwe wa chivundiwu kupita ku chisavundi, kuti mzimu siungafe?

21 Kodi malembo oyera akutanthauzanji, amene amanena kuti Mulungu adaika kerubi ndi lupanga la malawi a moto ku m’mawa kwa munda wa Edeni, kuopetsa kuti makolo athu oyamba angalowe ndi kudya chipatso cha mtengo wa moyo ndi kukhala ndi moyo kwamuyaya? Ndipo chotero tikuona kuti padalibe mwayi wakuthekera woti iwo akhale ndi moyo kwamuyaya.

22 Tsopano Alima adati kwa iye: ichi ndi chinthu chimene ndidali pafupi kufotokoza. Tsopano tikuona kuti Adamu adagwa mwa kudya chipatso choletsedwa, molingana ndi mawu a Mulungu; ndipo choncho tikuona, kuti chifukwa cha kugwa kwake, anthu onse adakhala osochera ndi anthu okugwa.

23 Ndipo tsopano taonani, ndikunena kwa inu kuti ngati kudali kotheka kwa Adamu kuti adye chipatso cha mtengo wa moyo pa nthawi imeneyo, kukadakhala kopanda imfa, ndipo mawu akadakhala opanda phindu, kupanga Mulungu wabodza, pakuti iye adati: Ngati utadye udzafa ndithu.

24 Ndipo tikuona kuti imfa imabwera pa anthu, inde, imfa imene yakambidwa ndi Amuleki, imene ili imfa ya thupi; komabe padali mpata operekedwa kwa munthu umene iye angathe kulapa, kotero moyo uno udakhala mkhalidwe woyembekezera; nthawi yokonzekera kukumana ndi Mulungu; nthawi yokonzekera mkhalidwe wopanda malire womwe wakambidwa ndi ife, umene uliko pakadzatha chiukitso cha akufa.

25 Tsopano, ngati pakadapanda dongosolo la chiwombolo, limene lidaikidwa kuchokera ku maziko a dziko lapansi, kukadakhala kopanda chiukitso cha akufa; koma pali dongosolo la chiwombolo loikidwa, limene lidzabweretse chiukitso cha akufa, chimene chakambidwa.

26 Ndipo tsopano taonani, kukadakhala kotheka kuti makolo akadatha kupita ndi kudya za mtengo wa moyo iwo akadakhala achisoni kwamuyaya, opanda nthawi yokonzekera; ndipo choncho dongosolo la chiwombolo likadasokonekera, ndipo mawu a Mulungu akadakhala opanda pake, osagwira tchito.

27 Koma taonani, sizidali choncho; koma kudaikika kwa anthu kuti akuyenera kudzafa; ndipo patatha imfa, iwo akuyenera kubwera ku chiweruzo, ngakhale chiweruzo chomwecho chimene chakambidwa, chimene chiri chimaliziro.

28 Ndipo Mulungu atakhazikitsa kuti zinthu izi zikuyenera kudzafika kwa munthu, taonani, kenako iye adaona kuti kudali kofunikira kuti munthu adziwe zinthu zokhudzana ndi zinthu zimene iye adasankhira kwa iwo;

29 Kotero iye adatumiza angelo kuti akayankhule ndi iwo, amene adachititsa anthu kuona ulemelero wake.

30 Ndipo iwo adayamba kuchokera m’nthawi imeneyo kuitanira pa dzina lake; kotero Mulungu adayankhula ndi anthu, ndi kudziwitsa kwa iwo dongosolo la chiwombolo, limene lidakonzedwa kuchokera pa maziko a dziko lapansi; ndipo izi iye adazidziwitsa kwa iwo molingana ndi chikhulupiliro chawo ndi kulapa ndi ntchito zawo zoyera.

31 Kotero, iye adapereka malamulo kwa anthu, iwo okhala oyamba kulakwira malamulo monga ku zinthu zimene zili zakuthupi, ndi kukhala monga milungu, odziwa chabwino kuchokera kuchoipa, kudziika okha mu chikhalidwe chakuchita, kapena kuikidwa mu chikhalidwe chakuchita monga zofuna zawo ndi zokondweretsa zawo, kaya kuchita zoipa kapena zabwino—

32 Kotero Mulungu adapereka kwa iwo malamulo, atatha kudziwitsa kwa iwo dongosolo la chiwombolo, kuti iwo asamachite zoipa, chilango chake kukhala imfa yachiwiri, imene idali imfa yosatha monga mwa zokhudzana ndi chilungamo; pakuti pa otero dongosolo la chiwombolo silikadakhala ndi mphamvu, pakuti ntchito za chilungamo zikadawonongeka, molingana ndi ubwino wopambana wa Mulungu.

33 Koma Mulungu adaitanira pa anthu, mu dzina la Mwana wake, (ili lokhala dongosolo la chiwombolo limene lidaikidwa) nati: Ngati inu mudzalape, ndi kusalimbitsa mitima yanu, pamenepo ndidzakuchitirani chifundo, kudzera mwa Mwana wanga Wobadwa Yekha.

34 Kotero, aliyense amene alapa, ndi kusalimbitsa mtima wake, adzakhala ndi kuyitanira pa chifundo kudzera mwa Mwana wanga Wobadwa Yekha, kuchikhululukiro cha machimo ake; ndipo amenewa adzalowa mu mpumulo wanga.

35 Ndipo aliyense amene adzalimbitsa mtima wake ndi kuchita mphulupulu, taonani, ndikulumbira mu mkwiyo wanga kuti sadzalowa mu mpumulo wanga.

36 Ndipo tsopano, abale anga, taonani ndikunena kwa inu, kuti ngati inu mudzalimbitsa mitima yanu simudzalowa mu mpumulo wa Ambuye; kotero mphulupulu zanu zidzaputa iye kuti adzatumiza mkwiyo wake pa inu monga mu kuputidwa woyamba, inde, monga mwa mawu ake mu kukwiyitsidwa komaliza komanso koyamba, kufikira ku chiwonongeko chosatha cha miyoyo yanu; kotero, molingana ndi mawu ake, kwa imfa yomaliza, monga ngati kwa yoyamba.

37 Ndipo tsopano, abale anga, poona tikudziwa zinthu izi, ndipo ndizoona, tiyeni tilape, ndi kusalimbitsa mitima yathu, kuti tisapute Ambuye Mulungu wathu kuti agwetse mkwiyo kwa ife mu malamulo ake achiwiri awa amene iye wapereka kwa ife; koma tiyeni tilowe mu mpumulo wa Mulungu, umene wakonzedwa molingana ndi mawu ake.

Print