Mutu 27
Ambuye alamula Amoni kuti atsogolere anthu a Anti-Nefi-Lehi ku chitetezo—Atakumana ndi Alima, chisangalalo cha Amoni chimutha mphamvu—Anefi apereka dziko la Yeresoni kwa Aanti-Nefi-Lehi—Iwo atchedwa anthu a Amoni. Mdzaka dza pafupifupi 90–77 Yesu asadabadwe.
1 Tsopano zidachitika kuti pamene Alamani aja amene adapita kukamenya nkhondo ndi Anefi adapeza, potsatira zovuta zawo zambiri kuti awawononge iwo, kuti kudali kosatheka kufuna chiwonongeko chawo, adabweleranso ku dziko la Nefi.
2 Ndipo zidachitika kuti Aamaleki, chifukwa cha kulephera kwawo adali okwiya kwambiri. Ndipo pamene iwo adaona kuti sakadatha kubwezera kwa Anefi, adayamba kutakasira anthu ku mkwiyo wodana ndi azibale awo Aanti-Nefi-Lehi; kotero adayambiranso kuwawononga.
3 Tsopano anthu awa adakananso kutenga zida, ndipo adalolera kuti aphedwe molingana ndi zokhumba za adani awo.
4 Tsopano pamene Amoni ndi abale ake adaona ntchito yachiwonongekoyi pakati pa iwo amene adali okondedwa kwambiri, ndipo pakati pa iwo amene adali kuwakonda iwo—pakuti adasamalidwa monga ngati adali angelo otumidwa kuchokera kwa Mulungu kudzawapulutsa iwo ku chiwonongeko chosatha—kotero, pamene Amoni ndi abale ake adaona ntchito yaikulu yachiwonongekoyi, adakhudzika ndi chifundo, ndipo iwo adati kwa mfumu:
5 Tiyeni tisonkhanitse pamodzi anthu a Ambuyewa, ndipo tiyeni tipite ku dziko la Zarahemula kwa abale athu Anefi, ndipo tithawe kuchoka m’manja mwa adani athu, kuti ife tisawonongedwe.
6 Koma mfumuyo idati kwa iwo: Taonani, Anefi adzatiwononga ife, chifukwa cha kupha kochuluka ndi machimo amene ife tidachita motsutsana nawo.
7 Ndipo Amoni adati: Ine ndipita ndi kukafunsa kwa Ambuye, ndipo ngati atati kwa ine, pitani kwa abale anu, kodi inu mudzapita?
8 Ndipo mfumuyo idati kwa iye: Inde, ngati Ambuye atanene kwa ife tipite, ife tidzapita kwa abale athu, ndipo tidzakhala akapolo awo kufikira titakonza kwa iwo kupha kochuluka ndi machimo amene ife tidachita motsutsana nawo.
9 Koma Amoni adati kwa iyo: Ndizotsutsana ndi malamulo a abale athu, amene adakhazikitsidwa ndi atate anga, kuti padzikhala kapolo aliyense pakati pawo; kotero tiyeni tipite ndi kudalira pa zifundo za abale athu.
10 Koma mfumuyo idati kwa iye: Funsani kwa Ambuye, ndipo ngati iwo atanene kuti tipite, ife tidzapita; kupanda kutero ife tidzawonongeka mu dzikoli.
11 Ndipo zidachitika kuti Amoni adapita ndi kufunsa kwa Ambuye, ndipo Ambuye adati kwa iye:
12 Chotsani anthu awa mu dziko lino, kuti asawonongedwe; pakuti Satana wagwiritsa mitima ya Aamaleki, amene akusonkhezera Alamani ku mkwiyo wa abale awo kuti awaphe; kotero chokani inu mudziko lino; ndipo odala ndi anthu a m’badwo uwu, chifukwa ine ndidzawasunga iwo.
13 Ndipo tsopano zidachitika kuti Amoni adapita ndi kukauza mfumu mawu onse amene Ambuye adanena kwa iye.
14 Ndipo iwo adasonkhanitsa anthu awo wonse, inde, anthu wonse a Ambuye, ndi kusonkhanitsa pamodzi nkhosa zawo zonse ndi ng’ombe, ndipo adachoka mu dzikolo, ndi kubwera ku chipululu chimene chidagawa dziko la Nefi ku dziko la Zarahemula, ndipo adabwera kufupi ndi malire a dzikolo.
15 Ndipo zidachitika kuti Amoni adati kwa iwo: Taonani, ine ndi abale anga tipita ku Zarahemula, ndipo inu mudzatsalira konkuno kufikira ife titabwelera; ndipo ife tikayesa mitima ya abale athu, ngati adzalole kuti inu mubwere mu dziko lawo.
16 Ndipo zidachitika kuti pamene Amoni adali kupita ku dzikolo, kuti iye ndi abale ake adakumana ndi Alima, pamalo amene adayankhulidwa; ndipo taonani, uwu udali mkumano osangalatsa.
17 Tsopano chisangalalo cha Amoni chidali chachikulu zedi mpaka kusefukira; inde, iye adamezedwa m’chisangalalo cha Mulungu, ngakhale kufikira kutha mphamvu zake; ndipo iye adagwanso pansi.
18 Tsopano ichi sichidali chisangalalo choposa kodi? Taonani, ichi ndi chisangalalo chimene palibe amachilandira pokhapokha ali olapa moona ndi ofunafuna chimwemwe modzichepetsa.
19 Tsopano chisangalalo cha Alima pokumana ndi azibale ake chidalidi chachikulu, ndiponso chisangalalo cha Aroni, cha Omineri, ndi Himuni; koma taonani chisangalalo chawo sichidali choti n’kuposa mphamvu zawo.
20 Ndipo zidachitika kuti Alima adatsogolera abale ake ku dziko la Zarahemula; ngakhale kunyumba kwake. Ndipo iwo adapita ndi kuuza mkulu wa oweruza zinthu zonse zimene zidachitika kwa iwo mu dziko la Nefi, pakati pa abale awo, Alamani.
21 Ndipo zidachitika kuti mkulu wa oweruzayo adatumiza chilengezo m’dziko lonselo, kufuna mawu a anthu zokhudzana ndi kuvomeleza abale awo, amene adali anthu Aanti-Nefi-Lehi.
22 Ndipo zidachitika kuti mawu a anthu adafika, nati: Taonani, ife tidzapereka dziko lathu la Yeresoni, limene liri ku m’mawa kwa nyanja, limene limalumikizana ndi dziko Lochuluka, limene liri ku kum’mwera kwa dziko Lochuluka; ndipo dziko ili la Yeresoni ndi dziko limene ife tidzapereke kwa abale athu kukhala cholowa.
23 Ndipo taonani, ife tidzaika ankhondo athu pakati pa dziko la Yeresoni ndi dziko la Nefi, kuti tithe kuteteza abale athu mu dziko la Yeresoni; ndipo izi tikuchitira kwa abale athu, pa nkhani ya mantha awo kutenga zida motsutsana ndi abale awo kuopa kuti angachimwe; ndipo mantha awo aakulu awa abwera chifukwa cha kulapa kwawo kowawa kumene iwo adali nako, pa chifukwa cha mbiri ya kupha kwawo kochuluka ndi kuipa kwawo koopsya.
24 Ndipo tsopano taonani, izi ife tidzachitira kwa abale athu, kuti iwo alandire dziko la Yeresoni; ndipo ife tidzawateteza iwo kwa adani awo ndi ankhondo athu, pa mfundo yakuti iwo adzapereka gawo la chuma chawo kutithandiza ife kuti tidzithandizira ankhondo athu.
25 Tsopano, zidachitika kuti pamene Amoni adamva izi, adabwelera kwa anthu Aanti-Nefi-Lehi, ndipo Alima adalinso ndi iye, ku chipululu, kumene iwo adakhoma mahema awo, ndipo adawadziwitsa iwo zinthu zonsezi. Ndipo Alima nayenso adawauza iwo za kutembenuka kwake, ndi Amoni ndi Aroni, ndi abale ake.
26 Ndipo zidachitika kuti zidachititsa chisangalalo chachikulu pakati pawo. Ndipo iwo adapita ku dziko la Yeresoni, ndi kutenga dziko la Yeresoni; ndipo ankatchulidwa ndi Anefi kuti anthu a Amoni; kotero iwo ankasiyanitsidwa ndi dzina limeneli kuyambira pamenepo.
27 Ndipo iwo adali pakati pa anthu a Nefi, ndiponso adawerengedwa pakati pa anthu amene adali a mpingo wa Mulungu. Ndipo iwo ankadziwika chifukwa cha changu chawo kwa Mulungu, ndiponso kwa anthu; pakuti iwo adali woona mtima kotheratu ndi wowongoka pa zinthu zonse; ndipo adali olimba pa chikhulupiliro mwa Khristu, ngakhale mpaka kumapeto.
28 Ndipo iwo ankaona kukhetsa mwazi wa abale awo ndi kunyansidwa kwakukulu; ndipo sakadatha konse kukwanitsa kutenga zida kumenyana ndi abale awo; ndipo sankayang’ana pa imfa ndi mantha, chifukwa cha chiyembekezo chawo ndi maganizo awo pa Khristu ndi kuuka kwake; kotero, imfa idamezedwa kwa iwo pa chigonjetso cha Khristu pa iyo.
29 Kotero, iwo akadatha kuvutika imfa mu njira yowawa ndi yomvetsa chisoni imene abale awo akadawachitira, iwo asadanyamule lupanga kapena zikwanje kuti awakanthe iwo.
30 Ndipo motero iwo adali achangu ndi anthu okondedwa, anthu okondeledwa kwambiri a Ambuye.