Malembo Oyera
Alima 17


Nkhani ya ana aamuna a Mosiya, amene adakana maufulu awo ku ufumu chifukwa cha mawu a Mulungu, ndipo adapita ku dziko la Nefi kukalalikira kwa Alamani; kuvutika ndi kupulumutsidwa kwawo—molingana ndi zolemba za Alima.

Yophatikiza mitu 17 mpaka 27.

Mutu 17

Ana a Mosiya ali ndi mzimu wa uneneri ndi chivumbulutso—Apita njira zawo zingapo kukalalikira mawu kwa Alamani—Amoni apita ku dziko la Ismaeli ndi kukhala mdzakazi wa mfumu Lamoni—Amoni apulumutsa ziweto za mfumu ndi kupha adani ake pa madzi a Sebusi. Ndime 1–3, mdzaka dza pafupifupi 77 Yesu asadabadwe; ndime 4, mdzaka dza pafupifupi 91–77 Yesu asadabadwe; ndipo ndime 5–39, mdzaka dza pafupifupi 91 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo tsopano zidachitika kuti pamene Alima adali kuyenda kuchokera ku dziko la Gideoni chakum’mwera, kutali ndi dziko la Manti, taonani, mu kuzizwa kwake, adakumana ndi ana a Mosiya akuyenda molunjika dziko la Zarahemula.

2 Tsopano ana a Mosiya adali ndi Alima pa nthawi imene mngelo adaonekera koyamba kwa iye; kotero Alima adasangalala kwambiri kuona abale ake; ndipo chomwe chidawonjezera ku chisangalalo chake, adali abale akebe mwa Ambuye, inde, ndipo adakula mu mphamvu ya chidziwitso cha choonadi; pakuti adali anthu omvetsetsa bwino ndipo adafufuza malemba mwakhama, kuti adziwe mawu a Mulungu.

3 Koma izi sizokhazo; adadzipereka wokha ku mapemphero ochuluka, ndi kusala kudya, kotero adali ndi mzimu wa uneneri, ndi mzimu wa chivumbulutso, ndipo pamene ankaphunzitsa, ankaphunzitsa ndi mphamvu ndi ulamuliro wa Mulungu.

4 Ndipo iwo adali kuphunzitsa mawu a Mulungu kwa nthawi ya dzaka khumi ndi zinayi pakati pa Alamani, atakhala ndi chipambano m’kubweretsa ambiri ku chidziwitso cha choona; inde, mwa mphamvu ya mawu awo ambiri adabweretsedwa ku guwa la Mulungu, kuitanira pa dzina lake ndi kuvomereza machimo awo pamaso pake.

5 Tsopano izo ndizo zochitika zimene zidawachitikira iwo pa ulendo wawo, pakuti adali ndi masautso ochuluka; adavutika kwambiri, monse mu thupi ndi m’maganizo, monga njala, ludzu ndi kutopa, ndi kuthodwa ndi ntchito mu uzimu.

6 Tsopano awa ndiwo maulendo awo: Atatsanzikana ndi atate awo, Mosiya, mu chaka choyamba cha oweruza; atakana ufumu umene atate awo adafuna kupereka kwa iwo, ndiponso awa adali maganizo a anthu;

7 Komabe adachokako kudziko la Zarahemula, ndi kutenga malupanga awo, ndi mikondo yawo, ndi mauta awo, ndi mivi yawo, magulaye awo; ndipo izi adachita kuti akwanitse kupeza chakudya chawo pamene adali m’chipululu.

8 Ndipo motero adachoka kupita m’chipululu ndi chiwerengero chawo chimene iwo adasankha, kupita ku dziko la Nefi, kukalalikira mawu a Mulungu kwa Alamani.

9 Ndipo zidachitika kuti adayenda masiku ambiri m’chipululu, ndipo adasala kudya kwambiri ndi kupemphera kwambiri kuti Ambuye apereke kwa iwo gawo la Mzimu wake kuti lipite nawo, ndi kukhala ndi iwo, kuti akhale chipangizo m’manja a Mulungu kuti abweretse, ngati kudali kotheka, abale awo, Alamani, ku chidziwitso cha choonadi, ndi chidziwitso cha kupanda phindu kwa miyambo ya makolo awo, imene idali yosalondola.

10 Ndipo zidachitika kuti Ambuye adawayendera ndi Mzimu wake, ndikunena kwa iwo: Khalani otonthozedwa. Ndipo iwo adatonthozedwa.

11 Ndipo Ambuye adanenanso kwa iwo: Pitani pakati pa Alamani, abale anu, ndi kukhazikitsa mawu anga; koma mudzakhala oleza mtima m’kupilirako ndi masautso, kuti muonetse chitsanzo chabwino kwa iwo mwa ine, ndipo ndidzakupangani inu chipangizo m’manja mwanga ku chipulumutso cha miyoyo yambiri.

12 Ndipo zidachitika kuti mitima ya ana a Mosiya, ndiponso amene adali ndi iwo, idalimbikitsika kupita kwa Alamani ndi kukalalikira kwa iwo mawu a Mulungu.

13 Ndipo zidachitika pamene adafika ku malire a dziko la Alamani, adadzigawa okha ndi kupita kosiyanasiyana, kukhulupilira mwa Ambuye kuti adzakumananso pamapeto a kukolora kwawo; pakuti adaganiza kuti ndi yaikulu ntchito yomwe iwo adaiyamba.

14 Ndipo zoonadi idali yaikulu, pakuti iwo adayamba kulalika mawu a Mulungu kwa anthu oopsya, ovuta ndi ankhanza; anthu amene ankakondwera mu kupha Anefi, ndi kuwabera ndi kuwachita chiwembu; ndipo mitima yawo idakhazikika pa chuma, kapena pa golide ndi siliva, ndi miyala yamtengo wapatali; koma iwo adafunabe kulanda zinthu izi mwa kupha ndi chiwembu, kuti asazigwilire ntchito kwa iwo ndi manja awo.

15 Motero adali anthu aulesi ndithu, ambiri mwa iwo ankapembedza mafano, ndipo tembelero la Mulungu lidagwera pa iwo chifukwa cha zikhalidwe za makolo awo; posatengera malonjezano a Ambuye adatambasulidwa kwa iwo pa zikhalidwe za kulapa.

16 Kotero, ichi chidali chifukwa chimene ana a Mosiya adayamba ntchitoyo, kuti mwina awabweretse iwo kuti alape; kuti mwina angawabweretse iwo ku chidziwitso cha dongosolo la chiwombolo.

17 Kotero, adadzipatutsa okha wina ndi mzake, ndipo adapita pakati pawo, munthu aliyense payekha, molingana ndi mawu ndi mphamvu ya Mulungu imene idapatsidwa kwa iye.

18 Tsopano Amoni pokhala wamkulu pakati pawo, kapena kuti iye ankatumikira iwo, ndipo adawachokera, atatha kuwadalitsa molingana ndi magawo ochuluka antchito zawo, atagawira mawu a Mulungu kwa iwo, kapena atatumikira kwa iwo asadanyamuke, ndipo motero iwo adayamba maulendo awo ambiri kuzungulira dzikolo.

19 Ndipo Amoni adapita ku dziko la Ismaeli, dzikolo lidatchedwa potsatira ana a Ismaeli, amene adakhalanso Alamani.

20 Ndipo pamene Amoni adalowa mu dziko la Ismaeli, Alamani adamutenga iye ndi kumumanga, monga chidali chikhalidwe chawo kumanga a Anefi onse amene adagwa m’manja mwawo, ndi kuwatengera iwo pamaso pa mfumu; ndipo motero zidasiyidwa m’kukonda kwa mfumu kuti awaphe iwo, kapena kuwasiya mu ukapolo, kapena kuwaponya iwo mundende, kapena kuwathamangitsa iwo m’dzikolo, molingana ndi chifuniro ndi kukonda kwake.

21 ndipo kotero Amoni adatengedwa pamaso pa mfumu imene idali yolamulira dziko la Ismaeli, ndipo dzina lake lidali Lamoni; ndipo idali chidzukulu cha Ismaeli.

22 Ndipo mfumu idafunsa Amoni ngati chidali chikhumbo chake kuti akhale mu dzikolo pakati pa Alamani kapena pakati pa anthu ake.

23 Ndipo Amoni adati kwa iyo: Inde, ndikukhumba kukhala pakati pa anthu awa kwa kanthawi; inde, ndipo mwina kufikira tsiku lakufa kwanga.

24 Ndipo zidachitika kuti mfumu Lamoni idakondwera kwambiri ndi Amoni, ndikuchititsa kuti zingwe zake zimasulidwe; ndipo idafuna kuti Amoni atenge m’modzi mwa ana ake aakazi kukhala mkazi wake.

25 Koma Amoni adati kwa iyo: Ayi, koma ndidzakhala mdzakazi wanu. Kotero Amoni adakhala mdzakazi kwa mfumu Lamoni. Ndipo zidachitika kuti adaikidwa pakati pa adzakazi ena kuti adziyang’anira ziweto za Lamoni, monga mwa chikhalidwe cha Alamani.

26 Ndipo atakhala pa ntchito kwa mfumu masiku atatu, pamene iye adali ndi adzakazi Achilamani kupita ndi ziweto zawo ku malo omwetsera, amene ankatchedwa madzi a Sebusi, ndipo Alamani onse ankapititsa ziweto zawo kumeneko, kuti azimwetsere—

27 Kotero, pamene Amoni ndi adzakazi a mfumu adali kuyendetsa ziwetozo ku malo omwetsera, taonani, kudali gulu lina la Alamani, limene lidali ndi ziweto zawo kukamwetsera, adaima ndi kubalalitsa ziweto za Amoni ndi adzakazi a mfumu, ndipo adazibalalitsa mpakana zidathawira m’njira zambiri.

28 Tsopano adzakazi a mfumu adayamba kung’ung’udza, nati: Tsopano mfumu idzatipha ife, monga idachitira abale athu chifukwa cha ziweto zawo zidabalalitsidwa ndi kuipa kwa anthu awa. Ndipo adayamba kulira kwambiri, nati: Taonani, ziweto zathu zabalalika kale.

29 Tsopano adalira chifukwa cha mantha ophedwa. Tsopano pamene Amoni adaona izi mtima wake udadzadza mkati mwake ndi chisangalalo; pakuti, iye adati, ndidzaonetsa mphamvu yanga kwa adzakazi anzangawa, kapena mphamvu imene ili mwa ine, pakubwenzeretsa ziwetozi kwa mfumu, kuti ndikope mitima ya adzakazi anzangawa, kuti ndiwatsogolere iwo kukhulupilira mu mawu anga.

30 Ndipo tsopano, amenewa adali maganizo a Amoni, pamene adaona masautso a iwo amene iye adawatcha kuti abale ake.

31 Ndipo zidachitika kuti iye adawakomedwetsa ndi mawu ake, nati: Abale anga, limbani mtima, ndipo tiyeni tipite kukasaka ziweto, ndipo tidzazisonkhanitsa pamodzi ndi kuzibweretsa kumadzi; ndipo motero tidzateteza ziweto za mfumu ndipo iyo siyidzatipha ife.

32 Ndipo zidachitika kuti iwo adapita kukasaka ziwetozo, ndipo adatsatira Amoni, ndipo adathamangira ndi liwiro lalikulu ndipo adazipeza ziweto za mfumu, ndipo adazisonkhanitsanso pamodzi pa malo omwetsera.

33 Ndipo anthu aja adaimanso kuti abalalitse ziwetozo; koma Amoni adati kwa abale ake: Zungulirani ziwetozi kuti zisathawe; ndipo ine ndipita ndi kumenyana ndi anthu awa amene akubalalitsa ziweto zathu.

34 Kotero, adachita momwe Amoni adawalamulira iwo, ndipo iye adapita ndi kuima kuti amenyane ndi iwo amene adaima pa madzi a Sebusi; ndipo chiwerengero chawo sichidali chochepa.

35 Kotero iwo sadaope Amoni; pakuti adaganiza kuti m’modzi mwa iwo akhonza kumupha monga mwa kukondweretsedwa kwawo, pakuti iwo sadadziwe kuti Ambuye adalonjeza Mosiya kuti adzapulumutsa ana ake m’manja mwawo; kapena iwo sadadziwenso zokhudzana ndi Ambuye; kotero iwo ankasangalala mu kuwonongeka kwa abale awo; ndipo pachifukwa ichi adaima ndikubalalitsa ziweto za mfumu.

36 Koma Amoni adaima ndipo adayamba kuponya miyala pa iwo ndi legeni yake; inde, ndi mphamvu zochuluka adagenda miyala pakati pawo, ndipo motero adapha angapo a iwo kufikira mokuti adayamba kuzizwa ndi mphamvu zake; komabe iwo adakwiya chifukwa cha kuphedwa kwa abale awo, ndipo adatsimikizika kuti iye agwe; kotero, poona kuti sakadatha kumugenda iye ndi miyala yawo, adabwera ndi zibonga zawo kuti amuphe.

37 Koma taonani, aliyense amene adanyamula chibonga chake kuti amukanthe Amoni, iye adakantha manja awo ndi lupanga lake; pakuti iye adazinda nkhonya zawo podula mikono yawo ndi lupanga lake lokuthwa, kotero kuti adayamba kuzizwa, ndipo adayamba kuthawa pamaso pake; inde ndipo sadali ochepa pa chiwerengero; ndipo iye adachititsa kuti iwo athawe ndi mphamvu za mkono wake.

38 Tsopano asanu ndi m’modzi mwa iwo adagwa ndi legeni yake, koma sadaphe aliyense kupatula mtsogoleri wawo ndi lupanga lake; ndipo adadula yambiri ya mikono yawo imene idakwezedwa motsutsana naye, ndipo sadali ochepa.

39 Ndipo pamene iye adawathamangitsira iwo kutali, adabwelera ndipo adamwetsera ziweto zawo ndikubwelera kukhola la mfumu, ndipo kenako adapita kwa mfumu, atanyamula mikono imene idadulidwa ndi lupanga la Amoni, ya iwo amene ankafuna kumupha iye, ndipo idanyamulidwa kwa mfumu ngati umboni wa zinthu zomwe zidachitika.