Malembo Oyera
Tsamba Lamutu la Buku la Mormoni


Buku la Mormoni

Nkhani zolembedwa ndi
Manja a Mormoni
pa Mapale
Zotengedwa kuchokera ku Mapale a Nefi

Kotero, ndi chidule cha zolemba za anthu Anefi, komanso za Alamani—Zolembedwa kwa Alamani, amene ali otsalira a nyumba ya Israeli; komanso kwa Ayuda ndi Amitundu—Zidalembedwa mwa lamulo, komanso mwa mzimu wa uneneri ndi wa chivumbulutso—Zolembedwa ndi kutsindikizidwa, ndi kubisidwa kwa Ambuye, kuti izo zisawonongedwe—Kuti zidzabwere ndi mphatso ndi mphamvu ya Mulungu ku kumasulira kwake—Zidatsindikizidwa ndi dzanja la Moroni, ndipo dzidabisidwa kwa Ambuye, kuti zidzabwere mtsogolo mwa nthawi yake mwa njira ya Amitundu—Kuti kutanthauzira kwake kudzakhale ndi mphatso ya Mulungu.

Chidule chotengedwanso kuchokera mu Buku la Eteri, limene liri zolembedwa za anthu a Yaredi, amene adamwazikana pa nthawi imene Ambuye adasokoneza chinenero cha anthu, pamene ankamanga nsanja yopita kumwamba—Zimene zikuyenera kusonyeza kwa otsala a nyumba ya Israeli zinthu zazikulu zimene Ambuye adachitira makolo awo; ndi kuti iwo adziwe mapangano a Ambuye; kuti iwo sadatayidwe kwamuyaya—Ndi ku kutsimikizira Myuda ndi Wamitundu kuti Yesu ndiye Khristu Mulungu wa Muyaya, akudziwonetsera yekha kwa mitundu yonse—Ndipo tsopano, ngati pali zolakwika ndi zolakwitsa za anthu; kotero, musatsutse zinthu za Mulungu, kuti mudzapezedwe opanda banga pampando-wachiweruzo wa Khristu.

Kumasulira koyambilira kuchokera ku mapale kupita ku Chingerezi
ndi Joseph Smith, Jun.

Print