Malembo Oyera
Umboni wa Mboni Zisanu ndi Zitatu


Umboni wa Mboni Zisanu ndi Zitatu

Zidziwike kwa maiko onse, mafuko, zinenero, ndi anthu, kwa amene ntchito iyi idzafika: Kuti Joseph Smith, Jun., omasulira wa ntchito iyi, wasonyeza kwa ife mapale amene adayankhulidwa, amene ali ndi maonekedwe a golide; ndipo monga ambiri mwamasamba amene Smith wonenedwayo wamasulira ife tidagwira ndi manja athu; ndipo tidaonanso zozokotedwa pamenepo, zonse ziri ndi maonekedwe a ntchito zakale, ndi kachitidwe ka luso. Ndipo ichi tikuchitira umboni ndi mawu osamalitsa, kuti Smith wonenedwayo wasonyeza kwa ife, pakuti ife tawona ndi kunyamula, ndipo tikudziwa motsimikiza kuti Smith onenedwayo ali ndi mapale omwe ife tinenawo. Ndipo ife tikupereka maina athu ku dziko, kuchitira umboni ku dziko zimene taziwona. Ndipo sitikunama, Mulungu akuchitira umboni pa izo.

Christian Whitmer

Jacob Whitmer

Peter Whitmer, Jun.

John Whitmer

Hiram Page

Joseph Smith, Sen.

Hyrum Smith

Samuel H. Smith

Print