Malembo Oyera
Kufotokoza Mwa Chidule za Buku la Mormoni


Kufotokoza Mwa Chidule za Buku la Mormoni

Buku la Mormoni ndi mbiri yopatulika ya anthu ku Amerika wakale ndipo lidazokotedwa pa mapale achitsulo. Malo omwe mbiriyi idapangidwa ndi awa:

  1. Mapale a Nefi, amene adali a mitundu iwiri: mapale aang’ono ndi aakulu. Oyamba adali okhazikika kwambiri ku zinthu zauzimu ndi utumiki ndi ziphunzitso za aneneri, pamene omalizirawo adali okamba kwambiri za mbiri yakale ya anthu okhudzidwa (1 Nefi 9:2–4). Kuchokera mu nthawi ya Mosiya, komabe, mapale aakuluwo adalinso ndi zinthu zofunika kwambiri zauzimu.

  2. Mapale a Mormoni, amene ali ndi chidule cha Mormoni kuchokera m’mapale akuluakulu a Nefi, ndi ndemanga zambiri. Mapale amenewa adalinso ndi kupitiriza kwa mbiri ya Mormoni ndi zowonjezeredwa ndi mwana wake Moroni.

  3. Mapale a Eteri, amene amapereka mbiri ya Ayeredi. Zolembedwa izi zidafupikitsidwa ndi Moroni, amene adaikapo ndemanga za iye mwini ndi kuphatikizira zolembedwazo ndi mbiri yonse pa mutu wa “Buku la Eteri.”

  4. Mapale a Mkuwa adabweretsedwa ndi anthu a Lehi kuchokera ku Yerusalemu mu 600 Yesu asadabadwe. Awa adali ndi “mabuku asanu a Mose, … komanso mbiri ya Ayuda kuyambira pa chiyambi, … mpaka kuchiyambi kwa ulamuliro wa Zedekiya, mfumu ya Yuda; komanso maulosi a aneneri oyera” (1 Nefi 5:11–13). Mawu ambiri ochokera m’mapale amenewa, akutchula za Yesaya ndi aneneri ena a m’Baibulo ndi ena osakhala a m’Baibulo, amene amapezeka mu Buku la Mormoni.

Buku la Mormoni lili ndi zigawo zazikulu khumi ndi zisanu, zodziwika, kupatulapo chimodzi, monga mabuku, omwe nthawi zambiri amatchulidwa ndi dzina la mlembi wawo wamkulu. Gawo loyamba (mabuku asanu ndi limodzi oyambilira, othera ndi Omuni) ndi zomasulira zochokera m’mapale aang’ono-ang’ono a Nefi. Pakati pa mabuku a Omuni ndi Mosiya pali loyikidwa lotchedwa Mawu a Mormoni. Loyikidwa ili likulumikiza zolemba zolembedwa pa mapale aang’ono ndi chidule cha Mormoni cha mapale aakulu.

Gawo lalitali kwambiri, kuchokera ku Mosiya mpaka Mormoni mutu 7, ndi kumasulira kwa chidule kwa Mormoni kwa mapale a Nefi aakulu. Chigawo chotsirizira, kuchokera ku Mormoni mutu 8 mpaka kumapeto kwa bukuli, chidalembedwa ndi mwana wamwamuna wa Mormoni, Moroni, amene, asadatsirize mbiri ya moyo wa atate ake, adafupikitsa zolemba za Yaredi (monga buku la Eteri) ndipo atatero adawonjezera mbali imene imadziwika kuti buku la Moroni.

M’chaka kapena pafupi pa kufa kwa Yesu 421, Moroni, womalizira wa mneneri-wolemba za mbiri yakale ya Anefi, adasindikiza zolemba zopatulikazi ndipo adazibisa kwa Ambuye, kuti zidzabweretsedwe m’masiku otsiriza, monga zidanenedweratu ndi mawu a Mulungu kudzera mwa aneneri Ake akale. Mu chaka cha 1823 Yesu Atafa, Moroni yemweyo, ali munthu owukitsidwa tsopano, adabwera kwa Mneneri Joseph Smith ndipo adapereka mapale ozokotedwa kwa iye.

Za zimenezi: Tsamba loyamba la mutu, lomwe limabwera tikangochoka pa tsamba la zamkatimu, limatengedwa m’mapale ndipo ndi gawo la malemba opatulika. Mawu oyambilira, amene asali mzilembo zopendekeka, monga mu 1 Nefi ndi kungodutsa pang’ono Mosiya mutu 9, alinso gawo la malemba opatulika. Mawu oyamba m’zilembo zopendekeka, monga mitu, sali apachiyambi koma ndi zongothandizira pophunzira zomwe zikuphatikizidwa kuti ziŵerengedwe mosavuta.

Zolakwitsa zina zing’onozing’ono mumalembowa zimapezeka m’mabuku akale a Buku la Mormoni lofalitsidwa m’Chingelezi. Mu buku ili muli zokonzedwa zomwe zimawoneka zoyenera kuti zolembazi zigwirizane ndi zomwe zidasindikizidwa pamanja ndi zolembedwa zoyambilira zolembedwa ndi Mneneri Joseph Smith.

Print