Malembo Oyera
Mawu Oyamba


Mawu Oyamba

Buku la Mormoni ndi buku la malemba opatulika olingana ndi Baibulo. Ndi zolembedwa za zochita za Mulungu ndi anthu akale a ku Amerika ndipo ili ndi chidzalo cha uthenga wabwino wosatha.

Bukuli lidalembedwa ndi aneneri ambiri akale ndi mzimu wa uneneri ndi vumbulutso. Mawu awo, olembedwa pa mapale a golide, adabwerezedwa ndi kufupikitsidwa ndi mneneri-wolemba za mbiri ya kale wotchedwa Mormoni. Nkhaniyi ikufotokoza za magulu aakulu awiri a anthu. Limodzi lidachokera ku Yerusalemu mdzaka dza 600 Yesu asadabadwe ndipo pambuyo pake lidapatulidwa mu mafuko awiri, odziwika monga Anefi ndi Alamani. Lina lidafika kale kwambiri pamene Ambuye adasokoneza ziyankhulo pa Nsanja ya Babeli. Gulu ili limadziwika kuti Ayeredi. Patatha dzaka zikwi zambiri, onse adawonongedwa kupatulapo Alamani, ndipo iwo ali pakati pa makolo a Amwenye achi Amerika.

Chochitika chofunika kwambiri cholembedwa mu Buku la Mormoni ndi utumiki waumwini wa Ambuye Yesu Khristu pakati pa Anefi, atangouka kumene. Limaonetsa ziphunzitso za uthenga wabwino, limafotokoza za dongosolo la chipulumutso, ndipo limauza anthu zimene ayenera kuchita kuti apeze mtendere m’moyo uno ndi chipulumutso chamuyaya m’moyo ulinkudza.

Atatha Mormoni kulemba zolemba zake, adapereka zolembazi kwa mwana wake Moroni, yemwe adawonjezera mawu ake ochepa ndipo adabisa mapalewo mu Phiri la Kumora. Pa Seputembala 21, 1823, Moroni yemweyo, amene adali waulemelero mu nthawiyi, woukitsidwa, adaonekera kwa Mneneri Joseph Smith ndi kumulangiza iye zokhudzana ndi zolemba zakale ndi kumasulira kwake komwe kuyenera kukhala mu Chingelezi.

Patapita nthaŵi mapalewo adaperekedwa kwa Joseph Smith, amene adawamasulira ndi mphatso ndi mphamvu ya Mulungu. Zolembedwazo tsopano zafalitsidwa m’zinenero zambiri monga umboni watsopano ndi owonjezera wakuti Yesu Khristu ndi Mwana wa Mulungu wamoyo ndi kuti onse amene adzabwera kwa Iye ndi kumvera malamulo ndi miyambo yoikika ya uthenga wabwino akhonza kupulumutsidwa.

Ponena za zolembedwa izi Mneneri Joseph Smith adati: “Ndidauza abalewo kuti Buku la Mormoni lidali lolondola kuposa buku lililonse padziko lapansi, ndi mwala wapangodya wa chipembedzo chathu, ndipo munthu angayandikire kwa Mulungu potsatira malamulo ake, kuposa buku lina lililonse.”

Kuwonjezela pa Joseph Smith, Ambuye adapereka kwa ena khumi ndi mmodzi kuti adziwonere okha mapale a golide ndi kukhala mboni zapadera za choonadi ndi umulungu wa Buku la Mormoni. Maumboni awo olembedwa adaphatikizidwa apa monga “Umboni wa Mboni Zitatu” ndi “Umboni wa Mboni Zisanu ndi Zitatu.”

Tikuitanira anthu onse kulikonse kuti awerenge Buku la Mormoni, kusinkhasinkha m’mitima yawo uthenga umene liri nawo, ndipo kenako kupempha Mulungu, Atate Wamuyaya, mu dzina la Khristu ngati bukuli ndi loona. Iwo amene amatsata njira imeneyi ndi kufunsa mwa chikhulupiliro adzapeza umboni wa choonadi chake ndi umulungu mwa mphamvu ya Mzimu Woyera. (Onani Moroni 10:3–5.)

Iwo amene amapeza umboni waumulungu uwu kuchokera kwa Mzimu Woyera adzadziwanso ndi mphamvu yomweyo kuti Yesu Khristu ndi Mpulumutsi wa dziko lapansi, kuti Joseph Smith ndiye ovumbulutsa ndi mneneri Wake m’masiku otsiriza ano, ndi kuti Mpingo wa Yesu Khristu wa Oyera Mtima M’masiku Otsiriza ndi ufumu wa Ambuye wokhazikitsidwanso padziko lapansi, kukonzekera Kudza Kwachiwiri kwa Mesiya.

Print