Malembo Oyera
Umboni wa Mneneri Joseph Smith


Umboni wa Mneneri Joseph Smith

Mawu a Mneneri Joseph Smith mwini wake ponena za kudza kwa Buku la Mormoni:

“Madzulo apa 21 Sepitembela [1823] … ndidadzipeleka ndekha ku pemphero ndi pembedzero kwa Mulungu Wamphamvu zonse. …

“Pamene ndidali kuitana kwa Mulungu motere, ndidazindikira kuwala kukuoneka m’chipinda mwanga, komwe kudapitilira kukula mpaka chipinda chidawala kuposa masana, nthawi, yomweyo munthu adawonekera pafupi ndi kama wanga, atayimilira mlengalenga, pakuti mapazi ake sadakhudze pansi.

“Iye adali atavala mwinjiro oyera kwambiri. Kudali kuyera kuposa chilichonse chapadziko lapansi chomwe ndidachionapo; ndiponso sindimakhulupilira kuti chinthu chilichonse chapadziko lapansi chingaoneke choyera ndi chonyezimira kwambiri. Manja ake adali wosavala, ndi mikono yakenso, pamwamba pang’ono pa dzanja; momwemonso mapazi ake adali wosavala, monganso miyendo yake; pamwamba pang’ono pa chidendene. Mutu ndi khosi zinalinso zosavala. Ndidazindikira kuti adalibe chovala china koma mwinjiro uwu, popeza udali wotseguka; kotero kuti ine ndidatha kuwona mu chifuwa chake.

“Sikuti mwinjiro wake wokha ndiumene udali oyera koposa; koma umunthu wake onse udali waulemelero osaneneka, ndi nkhope yake ngati mphezi. Chipindacho chidali chowala kwambiri, koma osati kuwala kwambiri kwa nthawi yomweyo kuzungulira umunthu wake. Pamene ndidamuyang’ana poyamba, ndidachita mantha; koma posakhalitsa mantha adandichoka.

“Adanditchula ine dzina, nati kwa ine kuti iye adali mthenga wotumidwa kwa ine kuchokera pamaso pa Mulungu, ndi kuti dzina lake linali Moroni; kuti Mulungu adali ndi ntchito yoti ndiichite; ndi kuti dzina langa lidziwike pa zabwino ndi zoipa pakati pa maiko onse, mafuko, ndi zinenero; kapena kuti likhala labwino ndi loipa poneneredwa mwa anthu onse.

“Iye adanena kuti pali buku losungidwa, lolembedwa pa mapale a golidi, lofotokoza za mbiri ya okhala kale a dziko lino; ndi gwero limene iwo adachokera. Adanenanso kuti chidzalo cha Uthenga Wabwino wosatha chili mmenemo, monga udaperekedwa ndi Mpulumutsi kwa okhalamo akale;

“Komanso, padali miyala iwiri mu mauta asiliva—ndipo miyala imeneyi, yomangidwa pa chapachifuwa; zidapanga chimene chimatchedwa Urimu ndi Tumimu—zidasungidwa ndi mapale; ndipo kukhala ndi miyala imeneyi ndi kuigwiritsa ntchito ndi zomwe zidapanga ‘owona’ akale kapena nthawi zakale; ndipo kuti Mulungu adaikonza ndi cholinga chomasulira bukulo. …

“Adandiuzanso kuti, pamene ine ndidzapeza mapale aja amene iye adanena—pakuti nthawi yoti iwo atengedwe idali isadakwaniritsidwe—Sindikuyenera kudzaonetsa kwa munthu aliyense; kapena chapachifuwa chokhala ndi Urimu ndi Tumimu; koma kwa iwo okha amene ndiyenera kudzalamulidwa kuwaonetsa; ngati nditero ndidzayenera kuonongedwa. Pamene amandiuza za mapale, masomphenya adatseguka m’maganizo mwanga moti ndidatha kuwona malo amene mapale adasungidwa; ndipo mudali mooneka bwino komanso momveka bwino kuti ndidawadziwanso malowa nditawaona.

“Titatha kuyankhulana uku, ndidaona kuwala mchipindamo kukuyamba kusonkhana nthawi yomweyo pafupi ndi munthu amene amalankhula nane, ndipo zidapitilira mpaka mchipindacho chidasiyidwanso ndi mdima, kupatula pomuzungulira iye; pamene nthawi yomweyo ndidawona ngati, njira yotseguka yopita kumwamba, ndipo adakwera mpaka adasowa, ndipo chipinda chidasiyidwa monga chidalili kusadawonekere kuwala kwa kumwamba.

“Ine ndidagona kusinkhasinkha pa chochitika chimenechi, ndi kuzizwa kwambiri ndi zimene ndidauzidwa ndi mthenga wodabwitsayu; pamene, m’kusinkhasinkha kwanga, ndidazindikira kuti chipinda changa chidayambanso kuwala, ndipo nthawi yomweyo, monga zidaliri, mthenga wa kumwamba yemweyo adalinso pafupi ndi kama wanga.

“Iye adayambanso kufotokoza zinthu zomwezo zimene adachita pa ulendo wake woyamba, popanda kusiyana kulikonse; zomwe atachita, adandiuza za chiweruzo chachikulu chimene chidali kubwera padziko lapansi, ndi zipasuko zazikulu ndi njala, lupanga, ndi mliri; ndi kuti ziweruzo zowawa izi zidzafika pa dziko lapansi mu m’badwo uno. Ndipo m’mene adanena izi, adakweranso monga adachitira poyamba.

“Pa nthawi imeneyi, zithunzithunzi zozama kwambiri zidapangidwa m’maganizo mwanga, mpaka tulo lidathawa m’maso mwanga ndipo ndidagona odzadzidwa ndi kudabwa ndi zimene ndidaziona ndi kuzimva. Koma chidali chodabwitsa nditaonanso mtumiki yemweyo pafupi ndi kama wanga ndipo ndidamumva iye akubwerezabwereza kapena kubwerezanso kwa ine zinthu zomwezo monga kale; ndipo adaonjezera chenjezo kwa ine, kundiuza ine kuti Satana ayesera kundiyesa (chifukwa cha umphawi wa banja la abambo anga), kuti nditenge mapale ndi cholinga cholemelera. Izi adandiletsa, nati ndisakhale ndi cholinga china potenga mapale koma kulemekeza Mulungu; ndipo sindikuyenera kukopedwa ndi cholinga china chirichonse koma chokhacho chomanga ufumu wake; kupanda kutero sindikadatha kuwapeza.

“Atabwera ulendo wachitatu uwu, adakweranso kumwamba monga kale; ndipo ndidasiyidwanso kusinkhasinkha pa zachilendo za zomwe ndidali nditangokumana nazo; pamene mosakhalitsa mthenga wa kumwamba atakweranso kumwamba kuchokera kwa ine kachitatu; tambala adalira, ndipo ndidapeza kuti tsiku likuyandikira, kotero kuti zoyankhulana zathu ziyenera kuti zidatenga usiku wonsewo.

“Posakhalitsa ndidadzuka pakama wanga, ndipo monga mwa masiku onse, ndidapita ku ntchito zofunika za tsiku; koma, poyesa kugwira ntchito monga nthawi zina, Ndidaona kuti mphamvu zanga zidatheratu moti ndidalephera kuchita chilichonse. Bambo anga, amene ankagwira ntchito limodzi nane, adapeza kuti pali vuto ndi ine, ndipo adandiuza kuti ndipite kunyumba. Ndidayamba ndi cholinga chopita kunyumba; koma, poyesera kuwoloka mpanda kunja kwa munda womwe tidali, mphamvu zanga zidandithera, ndipo ndidagwa pansi mopanda mphamvu, ndipo kwa nthawi ndithu ndidali wosazindikira chilichonse.

“Chinthu choyamba chimene ine ndikhonza kukumbukira chidali mawu oyankhulidwa kwa ine, kunditchula ine dzina. Ndidayang’ana m’mwamba, ndipo ndidaona mthenga yemwe uja atayima pamutu panga; atazingidwa ndi kuwala monga kale. Kenako adandiuza zonse zomwe adandiuza usiku wapitawo, ndipo adandiuza ine kuti ndipite kwa bambo anga ndi kukawauza iwo za masomphenya ndi malamulo amene ine ndidalandira.

“Ndidamvera; Ndidabwelera kwa atate anga kumunda; ndipo ndidawafotokozera iwo nkhani yonse. Adandiyankha kuti zidachokera kwa Mulungu. ndipo adandiuza kuti ndipite ndikachite monga adalamulira mthengayo. Ndidachoka kumundako, ndipo ndidapita kumalo kumene mthengayo adandiuza kuti mapale adasungidwa; Ndipo chifukwa cha kuzindikirika kwa masomphenya amene ndidali nawo okhudza iwo; Ndidadziwa malo nthawi yomwe ndidafika kumeneko.

“Pafupi ndi mudzi wa Manchester, Dera la Ontario, New York, kuli phiri lalikulu kwambiri, ndipo ndi lalitali kwambiri kuposa lili lonse lapafupi. Kumbali ya kumadzulo kwa phirili, osati patali ndi pamwamba pake, pansi pa mwala wokulirapo, padayikidwa ma palewo; osungidwa mu bokosi la miyala. Mwala uwu udali waukulu ndi wozungulira pakati, mbali ya pamwamba, ndi wopyapyala m’mbali mwake; kotero kuti mbali yake yapakati idawoneka pamwamba pa nthaka; koma m’mphepete mwake munali dothi lowuzungulira.

“Nditachotsa dothilo, ndidapeza chindodo, chimene ndidachiika pansi pa nsonga ya mwala; ndipo ndi kulimbika pang’ono ndidaudzutsa. Ndidayang’ana mkati, ndipo m’menemo ndidaonadi mapale, Urimu ndi Tumimu, ndi chapachifuwa, monga adanenera mthenga. Bokosi limene adaikamo lidapangidwa mwa kuyala miyala pamodzi mu mtundu wina wa simenti. Pansi pa bokosilo mudali miyala iwiri yopingasa bokosilo, ndipo pa miyala iyi mudayikidwa mapale ndi zinthu zina pamodzi ndi iwo.

“Ndidayesera kuwatulutsa, koma ndidaletsedwa ndi mnthenga; ndipo ndidauzidwanso kuti sidafike nthawi yowatulutsa; ngakhalenso, mpaka zaka zinayi kuyambira nthawi imeneyo; koma adandiuza kuti ndidzifika kumalo kumeneko pachaka kamodzi kuyambira nthawiyo; ndipo adzidzakumana ndi ine kumeneko, ndi kuti ndipitilize kutero mpaka nthawi itakwana yotenga mapalewo.

“Kotero, monga ndidalamulidwa, ndinkapita kumapeto kwa chaka chilichonse, ndipo nthawi zonse ndidapeza mthenga yemweyo, ndipo ndidalandira malangizo ndi nzeru kuchokera kwa iye pa zokambirana zathu zonse, kulemekeza zomwe Ambuye adzachite, ndi mmene ndi m’njira yotani ufumu wake uyenera kuyendetsedwera m’masiku otsiriza. …

“M’kupita kwa nthaŵi idafika nthawi yotenga mapale, Urimu ndi Tumimu, ndi chapachifuwa. Pa tsiku la makumi awiri mphambu ziwiri la Sepitembala, chikwi chimodzi mazana asanu ndi atatu mphambu makumi awiri kudza zisanu ndi ziwiri, nditapita monga mwa nthawi zonse kumapeto kwa chaka china kumalo kumene adayikidwa, mthenga wakumwamba yemweyo adawapereka kwa ine ndi lamulo ili: kuti ine ndiyenera kukhala ndi udindo pa iwo; kuti ngati ndiwalola apite mosasamala, kapena mwa kunyalanyaza kwanga kuli konse, ndidzaonongedwa; koma kuti ngati nditagwiritsa ntchito zonse zomwe ndingathe kuwasunga, kufikira Mtumiki atawaitanitsa, atetezedwe.

“Posakhalitsa ndidapeza chifukwa chake chimene ndidalandira malamulo okhwima ngati amenewa kuti ndiwateteze, ndipo chifukwa chimene mthenga adanenera kuti ndikachita zomwe zidafunikira pa dzanja langa, adzawaitanitsa. Pakuti posakhalitsa zidadziŵika kuti ndidali nawo, kuposa ntchito zolemetsa kwambiri zomwe zidagwiritsidwa ntchito kuti zitengedwe kwa ine. Njira iliyonse yomwe ingapangidwe idagwiritsidwa ntchito kuti ikwaniritse cholinga chimenecho. Mazunzowo adakhala owawa kwambiri kuposa kale, ndipo makamuwo adali tcheru mosalekeza kuti awalande kwa ine ngati nkotheka. Koma mwa nzeru za Mulungu, iwo adakhala otetezeka m’manja mwanga, mpaka ine nditakwaniritsa mwa iwo chimene chidafunika pa dzanja langa. Pamene Mthenga adawaitanitsa monga mwa dongosolo. Ndidawapereka kwa iye; ndipo ali nawo mu utsogoleri wake kufikira lero, pokhala tsiku lachiwiri la Meyi, chikwi chimodzi mazana asanu ndi atatu mphambu makumi atatu kudza asanu ndi atatu.”

Kuti mumve zambiri, onani Joseph Smith—Mbiri mu Ngale ya Mtengo Wapatali.

Zolembedwa Zakale Zoterozo zidatulutsidwa kuchokera pansi panthaka monga mawu a anthu olankhula kuchokera ku fumbi, ndi kumasuliridwa m’chilankhulo cha makono mwa mphatso ndi mphamvu ya Mulungu monga momwe kwachitiridwa umboni ndi kutsimikiziridwa Kwa umulungu, zidafalitsidwa koyamba ku dziko m’Chingelezi m’chaka cha 1830 monga The Book of Mormon.