Malembo Oyera
3 Nefi 20


Mutu 20

Yesu apereka mkate ndi vinyo mozizwitsa ndiponso apereka m’gonero kwa anthu—Otsalira a Yakobo adzafika ku chidziŵitso cha Ambuye Mulungu wawo ndipo adzalandira Amerika—Yesu ndi mneneri monga Mose, ndipo Anefi ali ana a aneneri—Ena a anthu a Ambuye adzasonkhanitsidwa ku Yerusalemu. Mdzaka za pafupifupi Yesu atabadwa 34.

1 Ndipo zidachitika kuti iye adalamula khamulo kuti lisiye kupemphera, ndiponso ophunzira ake. Ndipo iye adawalamura kuti asalekeze kupemphera m’mitima mwawo.

2 Ndipo iye adawalamura kuti anyamuke, ndikuyimilira pa mapazi awo. Ndipo adanyamuka, ndikuyimilira pa mapazi awo.

3 Ndipo zidachitika kuti iye adanyemanso mkate, ndikuwudalitsa, ndikupereka kwa ophunzira kuti adye.

4 Ndipo m’mene adadya adawalamura kuti anyeme mkate, ndi kupereka kwa khamulo.

5 Ndipo pamene iwo adapereka kwa khamulo iye adawapatsanso vinyo kuti amwe, ndipo adawalamura iwo kuti apereke kwa khamulo.

6 Tsopano, padalibe mkate, kapena vinyo, wobweretsedwa ndi ophunzira, kapena ndi khamulo;

7 Koma iye adawapatsadi mkate kuti adye, ndiponso vinyo kuti amwe.

8 Ndipo adati kwa iwo: Iye wakudya mkate uwu, adya thupi langa ku moyo wake; ndipo iye wakumwa vinyo uyu amwa mwazi wanga ku moyo wake; ndipo moyo wake sudzamva njala kapena ludzu, koma udzakhuta.

9 Tsopano, pamene khamu lonse lidadya ndi kumwa, taonani, adadzadzidwa ndi Mzimu; ndipo adafuula ndi liwu limodzi, ndikupereka ulemelero kwa Yesu, amene adamuona ndi kumumva.

10 Ndipo zidachitika kuti pamene onse adapereka ulemelero kwa Yesu, iye adati kwa iwo: Taonani tsopano ine ndikutsiriza lamulo limene Atate adandilamura ine lokhudzana ndi anthu awa, amene ali otsalira a nyumba ya Israeli.

11 Mukukumbukira kuti ndidayankhula kwa inu, ndipo ndidanena kuti pamene mawu a Yesaya akuyenera kukwaniritsidwa—taonani alembedwa, muli nawo pamaso panu, kotero fufuzani iwo—

12 Ndipo indetu, indetu, ine ndinena kwa inu, kuti pamene iwo adzakwaniritsidwa pamenepo ndi kukwaniritsidwa kwa pangano limene Atate adapanga kwa anthu ake, O nyumba ya Israeli.

13 Ndipo pamenepo otsala, amene adzabalalitsidwa kutali pa nkhope ya dziko lapansi, adzasonkhanitsidwa kuchokera kum’mawa, ndi kuchokera kumadzulo, ndi kuchokera kum’mwera, ndi kuchokera kumpoto; ndipo adzabweretsedwa ku chidziwitso cha Ambuye Mulungu wawo, amene adawawombola.

14 Ndipo Atate andilamura ine kuti ndipereke kwa inu dziko ili, ngati cholowa chanu.

15 Ndipo ine ndinena kwa inu, kuti ngati Amitundu sakulapa pambuyo pa dalitso limene iwo adzalandira, atabalalitsa anthu anga—

16 Pamenepo inu, otsalira a nyumba ya Yakobo, mudzapita pakati pawo; ndipo mudzakhala pakati pa iwo amene adzakhala ambiri; ndipo pakati pawo mudzakhala ngati mkango pakati pa zilombo za kuthengo, ndi ngati mwana wa mkango pakati pa nkhosa zoweta, umene ngati ulowa umapondereza pansi, ndi kukhadzula, ndipo palibe amene angapulumutse.

17 Dzanja lako lidzakwezeka pa adani ako, ndipo adani ako onse adzadulidwa.

18 Ndipo ndidzasonkhanitsa anthu anga monga munthu amasonkhanitsira mitolo yake pansi.

19 Pakuti ine ndidzapanga anthu anga amene Atate adapangana nawo, inde, ine ndidzapanga nyanga yako chitsulo, ndipo ine ndidzapanga ziboda zako mkuwa. Ndipo udzaphwanya mitundu yambiri ya anthu; ndipo ndidzapatulira phindu lawo kwa Ambuye, ndi chuma chawo kwa Ambuye wa dziko lonse lapansi. Ndipo taonani, ine ndine amene ndikuchita ichi.

20 Ndipo zidzachitika, atero Atate, kuti lupanga la chilungamo langa lidzalendewela pa iwo tsiku limenelo; Ndipo pokhapokha atalapa lidzagwera pa iwo, akutero Atate, inde, ngakhale pa maiko onse a Amitundu.

21 Ndipo zidzachitika kuti ndidzakhazikitsa anthu anga, O nyumba ya Israeli.

22 Ndipo taonani, anthu awa ndidzawakhazikitsa m’dziko lino, mu kukwaniritsidwa kwa pangano limene ndidapangana ndi atate anu Yakobo; ndipo lidzakhala Yerusalemu Watsopano. Ndipo mphamvu zakumwamba zidzakhala pakati pa anthu awa; inde, ngakhale ine ndidzakhala pakati panu.

23 Taonani, ine ndine amene Mose adanena, nati, Ambuye Mulungu wanu adzakuwutsirani mneneri mwa abale anu, monga ine; mudzamvera iye mu zonse chirichonse chimene adzanena kwa inu. Ndipo zidzachitika kuti munthu aliyense wosamvera mneneriyo adzadulidwa kuchoka pakati pa anthu.

24 Indetu ndinena kwa inu, inde, ndipo aneneri onse kuyambira Samueli ndi iwo akutsata pambuyo pake, monga ambiri amene adayankhula, adachitira umboni za ine.

25 Ndipo taonani, muli ana a aneneri; ndipo inu ndinu a nyumba ya Israeli; ndipo inu muli a pangano limene Atate adapangana ndi makolo anu, kunena kwa Abrahamu: Ndipo mu mbewu yako mafuko onse a dziko lapansi adzadalitsidwa.

26 Atate atandiukitsa kwa inu poyamba, ndi kundituma ine kuti ndidalitse inu, pakubweza yense wa inu ku mphulupulu zake; ndipo izi chifukwa ndinu ana a pangano—

27 Ndipo zitatha zimenezo inu mudadalitsidwa pamenepo adakwaniritsa Atate pangano limene iwo adapangana ndi Abrahamu, kuti: Mu mbewu yako mafuko onse a dziko lapansi adzadalitsidwa—mu kutsanulidwa kwa Mzimu Woyera kudzera mwa ine pa Amitundu, dalitso limene pa Amitundu lidzawalimbitsa koposa onse, kufikira kubalalitsa anthu anga, O nyumba ya Israeli.

28 Ndipo iwo adzakhala chikwapu kwa anthu a m’dziko lino. Komabe, pamene iwo adzalandira chidzalo cha uthenga wanga wabwino, pamenepo ngati iwo adzaumitsa mitima yawo motsutsana ndi ine, ndidzabwenza mphulupulu zawo pa mitu yawo, akutero Atate.

29 Ndipo ndidzakumbukira pangano limene ndidapangana ndi anthu anga; ndipo ndidapangana nawo kuti ndidzawasonkhanitsa pamodzi mu nthawi yanga yomwe, kuti ndidzaperekanso kwa iwo dziko la makolo awo ngati cholowa chawo, chomwe chili dziko la Yerusalemu, limene liri dziko lolonjezedwa kwa iwo kwamuyaya, akutero Atate.

30 Ndipo zidzachitika kuti nthawi ikudza, pamene chidzalo cha uthenga wanga wabwino chidzalalikidwa kwa iwo;

31 Ndipo adzakhulupilira mwa ine, kuti ine ndine Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu, ndipo adzapemphera kwa Atate m’dzina langa.

32 Pamenepo alonda awo adzakweza mawu awo, ndipo ndi mawu pamodzi adzaimba; pakuti adzaona maso ndi maso.

33 Kenako Atate adzawasonkhanitsanso iwo pamodzi, ndi kuwapatsa iwo Yerusalemu kukhala dziko la cholowa chawo.

34 Kenako iwo adzasangalala—Imbani pamodzi, inu mabwinja a Yerusalemu; pakuti Atate atonthoza anthu awo, iwo awombola Yerusalemu.

35 Atate atambasula mkono wawo woyera pamaso pa maiko onse; ndipo malekezero onse a dziko lapansi adzaona chipulumutso cha Atate; ndipo Atate ndi Ine ndife amodzi.

36 Ndipo pamenepo zidzakwaniritsidwa zimene zidalembedwa: Dzuka, galamuka kachiwiri, ndi kuvala mphamvu yako, O Ziyoni; vala zovala zako zokongola, Yerusalemu, mzinda woyera, pakuti kuyambira tsopano sadzalowanso mwa iwe wosadulidwa ndi wodetsedwa.

37 Dzisase wekha kufumbi; dzuka, khala pansi, O Yerusalemu; masula maunyolo a pakhosi pako, iwe mwana wamkazi wam’nsinga wa Ziyoni.

38 Pakuti motero akutero Ambuye: Mwadzigulitsa nokha pachabe, ndipo mudzawomboledwa opanda ndalama.

39 Indetu, indetu, ndinena kwa inu, kuti anthu anga adzadziwa dzina langa; inde, tsiku limenelo adzadziwa kuti ine ndine amene ndikuyankhula.

40 Ndipo pamenepo iwo adzati: Ndiokongola bwanji pa mapili ali mapazi a iye amene amabweretsa nkhani yabwino kwa iwo, amene amafalitsa mtendere; amene amabweretsa nkhani yabwino kwa iwo amene amafalitsa chipulumutso; amene amanena kwa Ziyoni, Mulungu wako alamulira;

41 Ndipo pamenepo padzamveka mfuu: Chokani inu, chokani inu, tulukani inu kumeneko, musakhudze chimene chili chodetsedwa; tulukani inu pakati pake; khalani oyera inu amene mumanyamula zotengera za Ambuye.

42 Pakuti simudzatuluka mwaliwiro, kapena kupita mothawa; pakuti Ambuye adzapita patsogolo panu, ndipo Mulungu wa Israeli adzakhala pambuyo panu.

43 Taonani, mtumiki wanga adzachita zinthu mwanzeru; iye adzakwezedwa, ndikudzayamikidwa, ndipo adzakhala wamkulu koposa.

44 Monga ambiri adazizwa pa iwe—nkhope yake idali yowonongeka, koposa munthu aliyense, ndipo maonekedwe ake kuposa ana a anthu—

45 Choncho iye adzawaza mitundu yambiri; mafumu adzatseka pakamwa pawo, pakuti chimene sichidawuzidwe kwa iwo adzachiona; ndipo icho chimene sadachimve adzachilingalira.

46 Indetu, indetu, ndinena kwa inu, zinthu zonsezi zidzafika ndithu, monga momwe Atate adandilamulira ine. Pamenepo pangano ili limene Atate adapangana ndi anthu ake lidzakwaniritsidwa; ndipo kenako Yerusalemu adzakhalidwanso ndi anthu anga, ndipo lidzakhala dziko la cholowa chawo.

Print