Malembo Oyera
3 Nefi 10


Mutu 10

M’dziko muli bata kwa maola ambiri—Mawu a Khristu alonjeza kusonkhanitsa anthu Ake monga nkhuku imasonkhanitsira anapiye ake—Mbali yolungama yochuluka ya anthu itetezedwa. Mdzaka dza pafupifupi Yesu atabadwa 34–35.

1 Ndipo tsopano taonani, zidachitika kuti anthu onse a m’dziko adamva mawu awa, ndipo adawachitira umboni. Ndipo zitatha zonenedwazi izi kudakhala chete pa dziko kwa nthawi ya maola ambiri;

2 Pakuti kwakukulu kudali kudabwitsika kwa anthuwo mwakuti iwo adasiya kulira ndi kukuwa chifukwa cha kutayika kwa abale awo amene adaphedwa; kotero padali bata pa dziko lonse kwa nthawi ya maola ambiri.

3 Ndipo zidachitika kuti mawu adadzanso kwa anthu, ndipo anthu onse adamva, ndikuchitira umboni za iwo nati;

4 O inu anthu a m’mizinda ikuluikulu iyi imene yagwa, amene muli zidzukulu za Yakobo, inde, amene muli a nyumba ya Israeli ndikangati ine ndakusonkhanitsani inu, monga nkhuku imasonkhanitsira anapiye ake m’mapiko ake, ndipo ndidakudyetsani inu.

5 Ndipo kenanso, ndikangati ndidafuna kusonkhanitsa inu, monga nkhuku imasonkhanitsira anapiye ake pansi pa mapiko ake, inde, O anthu a nyumba ya Israeli, amene mwagwa; inde, O inu anthu inu a nyumba ya Israeli, inu okhala mu Yerusalemu, monga inu amene mwagwa; ine, kangati ndikadakusonkhanitsani inu, monga nkhuku imasonkhanitsira anapiye ake, ndipo simudafune.

6 O inu nyumba ya Israeli amene ndakusiyani, ndikangati Ine ndidzakusonkhanitsani inu monga nkhuku imasonkhanitsira anapiye ake pansi pa mapiko ake, ngati inu mudzalapa ndi kubwelera kwa ine ndi cholinga chonse cha mtima.

7 Koma ngati sichoncho, O nyumba ya Israeli, malo okhalamo anu adzakhala pululu kufikira nthawi ya kukwaniritsidwa kwa pangano la makolo anu.

8 Ndipo tsopano zidachitika kuti anthu atamva mawu amenewa, taonani, adayambanso kulira ndi kukuwa chifukwa cha imfa ya abale awo ndi anzawo.

9 Ndipo zidachitika kuti motere adapita masiku atatu. Ndipo udali m’mawa ndipo mdimawo udabalalika kuchoka pa nkhope yadziko lapansi, ndipo dziko lidaleka kunjenjemera, ndipo miyala idaleka kung’ambika, ndipo kubuula koopsa kudatha, ndipo maphokoso onse adatha.

10 Ndipo dziko lapansi lidalumikizananso; kuti lidaima; ndipo kubuula, ndi kulira, ndi kufuura kwa anthu amene adasiyidwa ndi moyo kudaleka; ndipo kulira kwawo kudasandulika kukhala chisangalalo, ndipo maliro awo kukhala matamando ndi kuthokoza kwa Ambuye Yesu Khristu, Muwomboli wawo.

11 Ndipo kufikira tsopano malembo woyera amene adanenedwa ndi aneneri adakwaniritsidwa.

12 Ndipo lidali gawo la anthu olungama kwambiri limene lidapulutsidwa, ndipo ndi iwo amene adalandira aneneri, ndipo sadawaponye miyala; ndipo adali iwo amene sadakhetse mwazi wa woyera mtima, amene adapulumutsidwa—

13 Ndipo adapulumutsidwa ndipo sadamizidwe ndi kukwiliridwa mu nthaka; ndipo sadamizidwe mu kuya kwa nyanja; ndipo sadatenthedwa ndi moto, ngakhale iwo sadagwetsedwe ndi kuphwanyidwa; ndipo sadatengedwe ndi kamvuluvulu; kapena kugonjetsedwa ndi nthunzi wa utsi ndi wa mdima.

14 Ndipo tsopano, iye amene angawerenge, muloreni amvetsetse; iye amene ali nawo Malemba Woyera, muloreni awafufuze, ndipo aone, naona ngati imfa ndi kuwonongeka kwa moto konseku, ndi kwa utsi, ndi kwa manondwe, ndi kwa kamvuluvulu, ndi kutsegulidwa kwa nthaka kuti iwalandire, ndipo zinthu zonsezi siziri kukwaniritsidwa kwa mauneneri a ambiri a aneneri woyera.

15 Taonani, ndikunena kwa inu, Inde, ambiri achitira umboni za zinthu izi pa kudza kwa Khristu, ndipo adaphedwa chifukwa adachitira umboni za zinthu izi.

16 Inde, mneneri Zenosi adachitira umboni za zinthu izi, ndiponso Zenoki adayankhula zokhudza zinthu zimenezi, chifukwa adachitira umboni makamaka zokhudza ife, amene tiri otsalira a mbewu yawo.

17 Taonani, atate athu Yakobo adachitiranso umboni za otsalira a mbewu ya Yosefe. Ndipo taonani, kodi ife sitiri otsalira a mbewu ya Yosefe? Ndipo zinthu izi zimene zimachitira umboni za ife, kodi sizidalembedwe pa mapale a mkuwa amene atate athu Lehi adabweretsa kuchokera ku Yerusalemu?

18 Ndipo zidachitika kuti kumapeto kwa chaka cha makumi atatu ndi mphambu zinayi, taonani, ndidzakuonetsani kuti anthu a Nefi amene adasiyidwa, ndiponso iwo amene adatchedwa Alamani, amene adasiyidwa, adali ndi kukonderedwa kwakukulu komwe kudawonetsedwa kwa iwo, ndipo madalitso aakulu adatsanuliridwa pa mitu yawo, kotero kuti posakhalitsa kukwera kwa Khristu m’mwamba iye adadzionetsera yekha kwa iwo—

19 Kuonetsa thupi lake kwa iwo, ndi kuwatumikira; ndipo nkhani ya utumiki wake idzaperekedwa kutsogoloku. Kotero kwa nthawi ino ndamaliza mawu anga.