Malembo Oyera
3 Nefi 15


Mutu 15

Yesu alengeza kuti lamulo la Mose lakwaniritsidwa mwa Iye—Anefi ndi nkhosa zina zimene Iye adaziyankhula mu Yerusalemu—Chifukwa cha kusaweruzika, anthu a Ambuye m’Yerusalemu sakudziwa za nkhosa zobalalika za Israeli. Mdzaka dza pafupifupi Yesu atabadwa 34.

1 Ndipo tsopano zidachitika kuti pamene Yesu adatha mawu awa adayang’ana maso ake pa khamulo, nanena nawo, Taonani, mudamva zimene ndidaphunzitsa ndisadakwere kwa Atate anga; kotero, amene akumbukira mawu anga awa, ndikuwachita, ameneyo ine ndidzamuwukitsa pa tsiku lotsiliza.

2 Ndipo zidachitika kuti pamene Yesu adanena mawu awa, adaona kuti padali ena mwa iwo amene adadabwa, ndipo adadabwa pa chimene akadanena chokhudzana ndi chilamulo cha Mose; pakuti sadamvetsetse mawu akuti zinthu zakale zidapita, ndi kuti zonse zidakhala zatsopano.

3 Ndipo adati kwa iwo, Musadabwe kuti ndidati kwa inu, kuti zakale zidapita, ndi kuti zonse zidakhala zatsopano.

4 Taonani, ndikunena kwa inu kuti chilamulo chakwaniritsidwa chimene chidaperekedwa kwa Mose.

5 Taonani, ndine iye amene ndidapereka lamulo, ndipo ine ndine amene ndidapangana ndi anthu anga Israeli; kotero lamulo mwa ine lakwaniritsidwa; pakuti ndabwera kudzakwaniritsa lamulo; kotero liri ndi mathero.

6 Taonani, sindikuwononga aneneri, pakuti onse amene sadakwaniritsidwe mwa ine, indetu ndinena kwa inu, onse adzakwaniritsidwa.

7 Ndipo chifukwa ine ndidati kwa inu kuti zinthu zakale zapita, ine sindikuwononga izo zimene zidayankhulidwa zokhudza zinthu zimene ziri nkudza.

8 Pakuti taonani, pangano limene ndapanga ndi anthu anga silidakwaniritsidwe lonse; koma chilamulo chimene chidapatsidwa kwa Mose chiri ndi mathero mwa ine.

9 Taonani, ine ndine chilamulo ndi kuunika. Yang’anani kwa ine, ndi kupilira kufikira chimaliziro, ndipo mudzakhala ndi moyo; pakuti kwa iye wakupilira kufikira chimaliziro, ine ndidzampatsa moyo wamuyaya.

10 Taonani, ndakupatsani inu malamulo; kotero sungani malamulo anga. Ndipo ichi ndi chilamulo ndi aneneri, pakuti adachitira umboni za ine ndithu.

11 Ndipo tsopano zidachitika kuti pamene Yesu adanena mawu awa, adanena kwa khumi ndi awiri amene adawasankhawo:

12 Inu ndinu ophunzira anga; ndipo inu ndinu kuwala kwa anthu awa, amene ali otsalira a nyumba ya Yosefe.

13 Ndipo taonani, ili ndi dziko la cholowa chanu; ndipo Atate adalipereka kwa inu.

14 Ndipo palibe pa nthawi iliyonse Atate adandipatsa ine lamulo kuti ine ndikawauze izo kwa abale anu ku Yerusalemu.

15 Ngakhale pa nthawi iliyonse Atate sadandipatse ine lamulo kuti ndiwauze iwo zokhudza mafuko ena a nyumba ya Israeli, amene Atate adawatsogolera kuwachotsa m’dzikolo.

16 Izi zambiri Atate adandilamulira ine, kuti ndikuyenera kuwauza iwo;

17 Kuti nkhosa zina ndili nazo, zomwe siziri za khola ili; izonso ndikuyenera kuzibweretsa, ndipo zidzamva mawu anga; ndipo padzakhala khola limodzi, ndi mbusa m’modzi.

18 Ndipo tsopano, chifukwa cha kusamva ndi kusakhulupilira iwo sadamvetse mawu anga; kotero ndidalamulidwa kuti ndisanenenso za Atate zokhudza chinthu ichi kwa iwo.

19 Koma, indetu, ine ndikunena kwa inu kuti Atate andilamulira ine, ndipo ine ndikukuwuzani izo kwa inu, kuti inu mudapatulidwa kuchokera pakati pawo chifukwa cha kusaweruzika kwawo; kotero ndi chifukwa cha kusaweruzika kwawo kuti iwo sakudziwa za inu.

20 Ndipo indetu, ndikunena kwa inunso, kuti mafuko enawo Atate adawalekanitsa kwa iwo; ndipo ndi chifukwa cha mphulupulu zawo kuti sadziwa za iwo.

21 Ndipo indetu ndikunena kwa inu, kuti muli iwo amene ndidanena za iwo: Nkhosa zina ndili nazo, zomwe siziri za khola ili; izonso ndikuyenera kuzibweretsa, ndipo zidzamva mawu anga; ndipo padzakhala khola limodzi, ndi m’busa m’modzi.

22 Ndipo iwo sadandimvetsetse ine, pakuti iwo ankaganiza kuti adali Amitundu; pakuti sadamvetse kuti Amitundu akuyenera kutembenuka kudzera mu kulalikira kwawo.

23 Ndipo sadandimvetse kuti ndidati iwo adzamva mawu anga; ndipo sadandimvetse ine kuti Amitundu sakuyenera kumva mawu anga nthawi ina iliyonse—kuti sindikuyenera kudzionetsera ndekha kwa iwo koma ndi Mzimu Woyera.

24 Koma taonani, inu mwamva mawu anga, ndi kundiona ine; ndipo inu ndinu nkhosa zanga, ndipo mukuwerengedwa mwa iwo amene Atate andipatsa ine.