Malembo Oyera
3 Nefi 7


Mutu 7

Mkulu wa Oweruza aphedwa, boma liwonongedwa, ndipo anthu agawikana m’mafuko—Yakobo, okana Khristu, akhala mfumu ya gulu lachinsinsi—Nefi alalikira kulapa ndi chikhulupiliro mwa Khristu—Angelo amutumikira iye tsiku ndi tsiku, ndipo awukitsa m’bale wake kwa akufa—Ambiri alapa ndipo abatizidwa. Mdzaka dza pafupifupi Yesu atabadwa 30–33.

1 Tsopano taonani, ndidzakuonetsani kuti sadakhazikitse mfumu pa dziko; koma m’chaka chomwechi, inde, chaka cha makumi atatu, iwo adawononga pampando wa chiweruzo, inde, adapha mkulu wa oweruza wa dziko.

2 Ndipo anthu adagawikana wina ndi mzake; ndipo iwo adapatukana wina kuchokera kwa mzake kukhala mafuko, munthu aliyense molingana ndi banja lake ndi achibale ake ndi abwenzi; ndipo motero iwo adawononga boma la dzikolo.

3 Ndipo fuko lirilonse lidaika wamkulu kapena mtsogoleri wawo; ndipo motero adakhala mafuko ndi atsogoleri a mafuko.

4 Tsopano taonani, padalibe munthu pakati pawo kupatula iye adali ndi banja lalikulu ndi achibale ambiri ndi mabwenzi; motero mafuko awo adakula kwambiri.

5 Tsopano zonse izi zidachitika, ndipo kudalibe nkhondo pakati pawo; ndipo kusaweruzika konseku kudadza pa anthu chifukwa iwo adadzipereka okha ku mphamvu ya Satana.

6 Ndipo malamulo a boma adawonongedwa, chifukwa cha gulu lachinsinsi la abwenzi ndi achibale a iwo amene adapha aneneri.

7 Ndipo iwo adachititsa mkangano waukulu m’dziko, kotero kuti gawo lolungama kwambiri la anthu lidali litatsala pang’ono lonse kukhala loipa; inde padali anthu olungama ochepa okha pakati pawo.

8 Ndipo kotero dzaka zisanu ndi chimodzi zidali zisadathe kuchokera pamene ochuluka a anthu adatembenuka kuchoka ku chilungamo chawo, ngati galu ku masanzi ake, kapena ngati nkhumba kugudubuzika m’thope.

9 Tsopano gulu lachinsinsi ili, limene lidabweretsa kusaweruzika kwakukulu kotere pa anthu, lidadzisonkhanitsa pamodzi, ndipo lidaika pa mutu wawo munthu amene adamutcha Yakobo;

10 Ndipo iwo adamutcha iye mfumu; kotero adakhala mfumu pa gulu loipali; ndipo iye adali m’modzi wa akuluakulu, amene adayankhula mawu motsutsana ndi aneneri amene adachitira umboni za Yesu.

11 Ndipo zidachitika kuti adali amphamvu m’chiwerengo chawo, monga mwa mafuko a anthu, amene adali ogwirizana pamodzi, kupatula kuti atsogoleri awo adakhazikitsa malamulo awo, aliyense monga mwa fuko lake; komabe iwo adali adani; osatengera kuti iwo sadali anthu olungama, komabe iwo adali ogwirizana mu udani wa awo amene adalowa m’pangano kuti awononge boma.

12 Kotero, Yakobo poona kuti adani awo adali ochuluka kuposa iwo, iye pokhala mfumu ya gululo, kotero adalamula anthu ake kuti athawire ku gawo la kumpoto kwenikweni kwa dzikolo, ndipo kumeneko akadzimangire kwa iwo eni ufumu, mpaka adzalumikizane ndi opanduka (chifukwa adawakomedwetsa kuti padzakhala opanduka ambiri) ndipo adzakhala amphamvu mokwanira kuti alimbane ndi mafuko a anthu; ndipo adachita momwemo.

13 Ndipo kuguba kwawo kudali kofulumira kwambiri kotero kuti sikukadalepheretsedwa mpaka atapita kumene anthu sangawapeze. Ndipo motero chidatha chaka cha makumi atatu; ndipo motere zidali zochitika za anthu a Nefi.

14 Ndipo zidachitika m’chaka cha makumi atatu ndi chimodzi kuti iwo adagawidwa m’mafuko, munthu aliyense monga mwa banja lake, achibale ndi mabwenzi; komabe iwo adagwirizana kuti sadzapita ku nkhondo wina ndi mzake; koma iwo sadali ogwirizana monga mwa malamulo awo, ndi kachitidwe ka boma kawo, pakuti iwo adakhazikitsidwa molingana ndi malingaliro a iwo amene adali mafumu awo ndi atsogoleri awo. Koma iwo adakhazikitsa malamulo okhwima kwambiri kuti fuko limodzi lisalakwire linzake, kotero kuti pamlingo wina iwo adali ndi mtendere m’dziko; komabe mitima yawo idatembenuzidwa kuchoka kwa Ambuye Mulungu wawo, ndipo adaponya miyala aneneri, nawatulutsa pakati pawo.

15 Ndipo zidachitika kuti Nefi—atayenderedwa ndi angelo komanso mawu a Ambuye, kotero ataona angelo, ndi kukhala mboni ya pamaso, ndi kukhala ndi mphamvu yopatsidwa kwa iye kuti athe kudziwa zokhudza utumiki wa Khristu, komanso kukhala mboni ya pamaso ku kubwelera kwawo kofulumira kuchokera ku chilungamo kupita ku zoipa zawo ndi zonyansa;

16 Kotero, pokhala ndi chisoni chifukwa cha kuuma kwa mitima yawo ndi khungu la maganizo awo—adapita pakati pawo m’chaka chomwecho, ndipo adayamba kuchitira umboni, molimba mtima, kulapa ndi kukhululukidwa kwa machimo kudzera m’chikhulupiliro mwa Ambuye Yesu Khristu.

17 Ndipo adatumikira zinthu zambiri kwa iwo; ndipo zonsezo sizingalembedwe, ndipo gawo limodzi la izo silikadakwanira, choncho sizidalembedwe m’buku ili. Ndipo Nefi adatumikira ndi mphamvu ndi ulamuliro waukulu.

18 Ndipo zidachitika kuti adamukwiyira, ngakhale kuti iye adali ndi mphamvu zazikulu kuposa iwo, pakuti sikudali kotheka kuti athe kusakhulupilira mawu ake, pakuti chikhulupiliro chake chidali chachikulu mwa Ambuye Yesu Khristu mwakuti angelo ankatumikira kwa iye tsiku ndi tsiku.

19 Ndipo m’dzina la Yesu adatulutsa ziwanda ndi mizimu yonyansa; ndipo ngakhale m’bale wake adamuwukitsa kwa akufa, ataponyedwa miyala, ndikuphedwa ndi anthu.

20 Ndipo anthu adaona, ndikuchitira umboni, ndipo adakwiya naye chifukwa cha mphamvu yake; ndipo adachitanso zozizwitsa zina zambiri, pamaso pa anthu, m’dzina la Yesu.

21 Ndipo zidachitika kuti chaka cha makumi atatu ndi chimodzi chidapita, ndipo padali owerengeka amene adatembenukira kwa Ambuye; koma ochuluka amene adatembenukira adasonyeza moonadi kwa anthu kuti adayenderedwa ndi mphamvu ndi Mzimu wa Mulungu, umene udali mwa Yesu Khristu, amene iwo adakhulupilira.

22 Ndipo ochuluka omwe adali ndi ziwanda zitatulutsidwa kuchoka kwa iwo, ndipo adachiritsidwa ku matenda awo ndi zofooka zawo, adaonetsera moonadi kwa anthu kuti iwo adapangidwa ndi Mzimu wa Mulungu, ndipo adali atachiritsidwa; ndipo iwo adaonetsa zizindikironso ndipo adachita zozizwitsa zina pakati pa anthu.

23 Motero chidathanso chaka cha makumi atatu ndi ziwiri. Ndipo Nefi adalilira kwa anthu kumayambiliro kwa chaka cha makumi atatu ndi zitatu; ndipo adalalikira kwa iwo kulapa ndi chikhululukiro cha machimo.

24 Tsopano ndikufuna kuti inu mukumbukirenso, kuti padalibe aliyense amene adabweretsedwa ku kulapa amene sadabatizidwe ndi madzi.

25 Kotero, adadzozedwa ndi Nefi, anthu ku utumiki uwu, kuti onse otero amene akadza kwa iwo akuyenera kubatizidwa ndi madzi, ndipo ichi monga mboni ndi umboni pamaso pa Mulungu, ndi kwa anthu, kuti iwo adalapa ndi kulandila chikhululukiro cha machimo awo.

26 Ndipo padali ambiri m’chiyambi cha chaka chimenechi amene adabatizidwa ku kulapa; ndipo motero chigawo chambiri cha chaka chidatha.

Print