Malembo Oyera
3 Nefi 12


Mutu 12

Yesu ayitana ndi kulamula ophunzira khumi ndi awiri—Iye apereka kwa Anefi chiphunzitso chofanana ndi cha Ulaliki wa pa Phiri—Iye ayankhula Mawu a Wodala—Ziphunzitso zake zipitilira ndi kupita patsogolo pa chilamulo cha Mose—Anthu alamulidwa kuti akhale angwiro monga Iye ndi Atate ake ali angwiro—Fananitsani Mateyu 5. Mdzaka dza pafupifupi Yesu atabadwa 34.

1 Ndipo zidachitika kuti pamene Yesu adayankhula mawu awa kwa Nefi, ndi kwa iwo amene adaitanidwa, (tsopano chiwerengero cha iwo amene adaitanidwa, ndikulandira mphamvu ndi ulamuliro wa kubatiza, adali khumi ndi awiri) ndipo taonani, adatambasula dzanja lake kwa khamulo, ndikufuulira kwa iwo, kuti: Wodala muli inu ngati mudzamvera mawu a khumi ndi awiri awa, amene ndawasankha mwa inu, kuti akutumikireni inu, ndi kukhala akapolo anu; ndipo kwa iwo ndapereka mphamvu kuti akabatize inu ndi madzi; ndipo mukatha kudzabatizidwa ndi madzi, taonani, ndidzakubatizani inu ndi moto ndi Mzimu Woyera; motero wodala muli inu ngati mudzakhulupilira mwa ine ndi kubatizidwa, mutatha kundiona ine ndi kudziwa kuti ndine.

2 Ndiponso, wodala kwambiri ndi iwo amene adzakhulupilira m’mawu anu chifukwa kuti mudzachitira umboni kuti mudandiona, ndi kuti mukudziwa kuti ndine. Inde, wodala iwo amene adzakhulupilira m’mawu anu, ndi kubwera mu kuya kwa kudzichepetsa ndi kubatizidwa, pakuti iwo adzayenderedwa ndi moto ndi Mzimu Woyera, ndipo adzalandira chikhululukiro cha machimo awo.

3 Inde, wodala ali osauka mu mzimu amene amadza kwa ine, pakuti ufumu wakumwamba ndi wawo.

4 Ndiponso, wodala ali onse amene akulira, pakuti iwo adzatonthozedwa.

5 Ndipo wodala ali akufatsa, chifukwa adzalandira dziko lapansi.

6 Ndipo wodala ali onse amene amva njala ndi ludzu la chilungamo, pakuti adzadzazidwa ndi Mzimu Woyera.

7 Ndipo wodala ali akuchita chifundo, pakuti adzalandira chifundo.

8 Ndipo wodala ali onse oyera mtima, pakuti adzaona Mulungu.

9 Ndipo wodala ali onse obweretsa mtendere, pakuti adzatchedwa ana a Mulungu.

10 Ndipo wodala ali onse amene amazunzidwa chifukwa cha dzina langa, pakuti ufumu wakumwamba uli wawo.

11 Ndipo wodala inu pamene anthu adzanyoza ndikukuzunzani inu, ndipo adzakunenerani zonama zoipa zilizonse chifukwa cha ine;

12 Pakuti mudzakhala ndi chisangalalo chachikulu ndi kukondwera kwakukulu, pakuti mphoto yanu idzakhala yaikulu m’mwamba; pakuti koteronso adazunza aneneri amene adakhalako inu kulibe.

13 Indetu, indetu, ndikunena kwa inu, ine ndikupatsani inu kuti mukhale mchere wa dziko lapansi; koma ngati mcherewo ukataya kukoma kwake, dziko lapansi lidzakomeretsedwa ndi chiyani? Mcherewo kuyambira pamenepo udzakhala wosathandiza kanthu, koma woti uponyedwe kunja, ndi kuponderezedwa ndi anthu.

14 Indetu, indetu, ndikunena kwa inu, ine ndikukupatsani inu kuti mukhale kuunika kwa anthu awa. Mzinda wokhala pamwamba pa phiri sungathe kubisika.

15 Taonani, kodi anthu amayatsa nyali ndi kuika pansi pa mbiya? Ayi, koma pa choyikapo nyali, ndipo imaunikira onse ali m’nyumbamo;

16 Kotero lorani kuwala kwanu kuunikire pamaso pa anthu awa, kuti athe kuona ntchito zanu zabwino, ndikulemekeza Atate anu a Kumwamba.

17 Musaganize kuti ndabwera kudzawononga chilamulo kapena aneneri; Sindidabwere kudzawononga, koma kudzakwaniritsa;

18 Pakuti indetu ndinena kwa inu, dontho limodzi kapena kolemba kamodzi sikadachoke kuchilamulo, koma mwa ine zonse zakwaniritsidwa.

19 Ndipo taonani, ndakupatsani inu chilamulo ndi malamulo a Atate anga, kuti mudzakhulupilire mwa ine, ndi kuti mudzalape machimo anu, ndi kudza kwa ine ndi mtima wosweka ndi mzimu wolapa. Taonani, muli nawo malamulo pamaso panu, ndipo chilamulo chakwaniritsidwa.

20 Kotero idzani kwa ine ndipo mupulumutsidwe; pakuti indetu ndikunena kwa inu, kuti pokhapokha mutasunga malamulo anga, amene ine ndakulamulirani pa nthawi ino, inu simudzalowa konse mu ufumu wa kumwamba.

21 Inu mudamva kuti kudanenedwa ndi iwo akale, ndipo kwalembedwanso pamaso panu, kuti musaphe; ndipo yense amene adzapha adzakhala pachiwopsezo cha chiweruzo cha Mulungu;

22 Koma ine ndikunena kwa inu, kuti yense wokwiyira m’bale wake adzakhala pachiwopsezo cha chiweruzo chake. Ndipo amene adzanena kwa m’bale wake, Wopanda nzeru, adzakhala pachiwopsezo cha bwalo la akulu; ndipo amene adzanena, Chitsiru iwe, adzakhala pa chiwopsezo cha gahena wamoto.

23 Kotero, ngati inu mudzabwera kwa ine, kapena mudzakhumba kubwera kwa ine, ndi kukumbukira kuti m’bale wanu ali ndi kanthu kotsutsa iwe—

24 Pita kwa m’bale wako, ndikuyamba wayanjana ndi m’bale wako, ndipo ukatero kabwere kwa ine ndi cholinga chonse cha mtima, ndipo ndidzakulandira iwe.

25 Gwirizana ndi mdani wako msanga pamene uli naye panjira, kuopa pa nthawi ina iliyonse angakupeze, ndipo ungaponyedwe m’ndende.

26 Indetu, indetu, ndikunena ndi iwe, sudzatulukamo konse kufikira utalipira senine yotsiriza. Ndipo pamene muli m’ndende mukhonza kulipira ngakhale senine imodzi? Indetu, indetu, ndikunena kwa inu, Ayi.

27 Taonani, kwalembedwa ndi iwo akale, kuti usachite chigololo;

28 Koma ine ndinena kwa inu, kuti yense wakuyang’ana mkazi ndi kumkhumba iye, pamenepo wachita kale chigololo mumtima mwake.

29 Taonani, ndikupereka kwa inu lamulo, kuti musalore chilichonse cha zinthu izi kulowa mu mtima mwanu;

30 Pakuti ndi bwino kuti inu mukuyenera kudzikana inu nokha pa zinthu izi, pamene inu mudzasenzere mtanda wanu, kuposa kuti muponyedwe mu gahena.

31 Kwalembedwa, kuti aliyense wakuchotsa mkazi wake, ampatse iye kalata ya chisudzulo.

32 Indetu, indetu, ndinena kwa inu, kuti yense wakuchotsa mkazi wake, kopanda chifukwa cha dama, amuchititsa iye kuti achite chigololo; ndipo amene adzakwatira iye wosudzulidwayo achita chigololo.

33 Ndiponso kwalembedwa, Usalumbire wekha, koma udzachitira kwa Ambuye malumbiro ako;

34 Koma indetu, indetu, ndinena kwa inu, musalumbire konse; kapena pa kumwamba, pakuti kuli mpando wachifumu wa Mulungu;

35 kapena pa dziko lapansi, pakuti ndilo chopondapo mapazi ake;

36 Kapena usalumbilire ku mutu wako, popeza sungathe kulidetsa kapena kuliyeretsa tsitsi olo limodzi;

37 Koma kuyankhula kwanu kukhale Inde, inde; Ayi, ayi; pakuti chirichonse chobwera choposa izi chili choipa.

38 Ndipo taonani, kwalembedwa, diso ku diso, ndi dzino ku dzino;

39 Koma ndinena ndi inu, kuti musadzakane choipa, koma amene adzakupanda iwe pa tsaya lako lamanja, umtembenuzire linanso;

40 Ndipo ngati munthu aliyense afuna kusumira iwe kulamulo ndi kutenga malaya ako, umulore iye kutenganso chofunda chako;

41 Ndipo amene adzakukakamiza kupita naye mtunda umodzi, upite naye iwiri.

42 Kwa iye amene akukupempha iwe umpatse, ndipo kwa iye wofuna kukukongola usamubwenze pambuyo.

43 Ndipo taona kudalembedwanso, kuti udzikonda mnansi wako ndi kudana ndi mdani wako;

44 Koma taonani ndikunena kwa inu, kondani adani anu, dalitsani iwo amene amakutembelerani inu, chitani zabwino kwa iwo amene amadana nanu, ndipo pemphelerani iwo amene amakugwiritsani ntchito monyoza ndi kukuzunzani;

45 Kuti mukakhale ana a Atate anu a Kumwamba; pakuti iye amapangitsa dzuwa lake kukwera pa oipa ndi pa abwino.

46 Kotero zonse zimene zidali zakale, zimene zidali pansi pa chilamulo, mwa ine zakwaniritsidwa.

47 Zinthu zakale zatha, ndipo zonse zakhala zatsopano.

48 Kotero ine ndikufuna kuti inu mukhale angwiro monga ine, kapena Atate anu amene ali kumwamba ali angwiro.