Malembo Oyera
3 Nefi 5


Mutu 5

Anefi alapa ndikusiya machimo awo—Mormoni alemba mbiri ya anthu ake ndipo alalikira mawu osatha kwa iwo—Israeli adzasonkhanitsidwa kuchokera mu kumwazika kwake kwakutali. Mdzaka dza pafupifupi Yesu atabadwa 22–26.

1 Ndipo taonani, padalibe munthu wamoyo pakati pa anthu onse a Anefi amene adakaikira ngakhale pang’ono mawu a aneneri onse woyera amene adayankhula; pakuti adadziwa kuti kukuyenera kuti zikuyenera kukwaniritsidwa.

2 Ndipo iwo ankadziwa kuti zikuyenera kukhala koyenera kuti Khristu adadza, chifukwa cha zizindikiro zambiri zomwe zidaperekedwa, monga mwa mawu a aneneri; ndipo chifukwa cha zinthu zomwe zidachitika kale iwo adadziwa kuti zikuyenera kukhala kuti zinthu zonse zikuyenera kuchitika molingana ndi zomwe zidayankhulidwa.

3 Kotero iwo adasiya machimo awo onse, ndi zonyansa zawo, ndi zadama zawo, ndipo adatumikira Mulungu ndi khama lawo lonse usana ndi usiku.

4 Ndipo tsopano zidachitika kuti pamene adatenga achifwamba onse ukaidi, kotero kuti palibe m’modzi amene adathawa amene sadaphedwe, adawaponya akaidi awo mu ndende, ndipo adapangitsa mawu a Mulungu kulalikidwa kwa iwo; ndipo ochuluka amene adalapa machimo awo ndi kulowa mu pangano kuti sadzaphanso adamasulidwa.

5 Koma ambiri amene sadalowe mupangano, ndipo amene adapitirizabe kukhala ndi kupha kwachinsinsiko m’mitima mwawo, inde, ambiri amene adapezedwa akuyankhura ziopsezo motsutsa abale awo adatsutsidwa ndi kulangidwa molingana ndi lamulo.

6 Ndipo motero iwo adathetsa zoipa zonsezo, ndi zachinsinsi, ndi gulu la zonyansa, limene lidachita zoipa zochuluka, ndi kupha kochuluka.

7 Ndipo motero chaka cha makumi awiri ndi ziwiri chidatha, ndi chaka cha makumi awiri ndi zitatu, ndi cha makumi awiri ndi zinayi, ndi cha makumi awiri ndi zisanu; ndipo motero zaka makumi awiri ndi zisanu zidatha.

8 Ndipo padali zinthu zambiri zidachitika, zimene m’maso mwa ena zikadakhala zazikulu ndi zodabwitsa; komabe, izo sizingalembedwe zonse mu buku ili; Inde, buku ili silingakhale ndi gawo limodzi mwa magawo zana a zimene zidachitidwa pakati pa anthu ochuluka mu nthawi ya zaka makumi awiri ndi zisanu;

9 Koma taonani pali zolemba zimene ziri ndi zochitika zonse za anthu awa; ndipo nkhani yayifupi koma yoona idaperekedwa ndi Nefi.

10 Kotero, ndapanga zolemba zanga za zinthu izi molingana ndi zolemba za Nefi, zomwe zidazokotedwa pamapale amene ankatchedwa mapale a Nefi.

11 Ndipo taonani, ndikupanga zolemba pa mapale zomwe ndapanga ndi manja anga.

12 Ndipo taonani, ndimatchedwa Mormoni, kutchedwa pambuyo pa dziko la Mormoni, dziko limene Alima adakhazikitsa mpingo pakati pa anthu, inde, mpingo woyamba umene udakhazikitsidwa pakati pawo pambuyo pa kulakwitsa kwawo.

13 Taonani, ndine wophunzira wa Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu. Ndaitanidwa ndi iye kuti ndilalikire mawu ake pakati pa anthu ake, kuti akhale nawo moyo wosatha.

14 Ndipo zakhala zoyenera kuti ine, molingana ndi chifuniro cha Mulungu, kuti mapemphero a iwo amene adachoka pano, amene adali woyera, akwaniritsidwe monga mwa chikhulupiliro chawo, kuti ndipange zolemba za zinthu izi zimene zidachitika—

15 Inde, zolemba zochepa za izo zimene zachitika kuchokera nthawi imene Lehi adachoka ku Yerusalemu, ngakhale mpakana nthawi ino.

16 Kotero ndikupanga zolemba zanga kuchokera ku zolemba zimene zidaperekedwa ndi iwo amene adalipo ine ndisadabadwe, mpaka kuchiyambi cha tsiku langa;

17 Ndipo kenako ndikupanga zolemba za zinthu zimene ndidaziona ndi maso anga.

18 Ndipo ndikudziwa zolemba zimene ndipange zikhala zolungama ndi zolemba zoona; komabe pali zinthu zambiri zomwe, molingana ndi chinenero chathu, sitingathe kuzilemba.

19 Ndipo tsopano ndikumaliza kunena za ine, ndipo ndikupitiriza kupereka nkhani ya zinthu zomwe zidakhalapo ndisadabadwe.

20 Ndine Mormoni, ndipo ndi chidzukulu chenicheni cha Lehi. Ndili ndi chifukwa chodalitsira Mulungu wanga ndi Mpulumutsi wanga Yesu Khristu, kuti adatulutsa makolo athu m’dziko la Yerusalemu, (ndipo palibe amene adadziwa koma iye yekha ndi iwo amene adawatulutsa m’dzikolo) ndipo adandipatsa ine ndi anthu anga chidziwitso chambiri ku chipulumutso cha miyoyo yathu.

21 Ndithudi wadalitsa nyumba ya Yakobo, ndipo wachitira chifundo mbewu ya Yosefe.

22 Ndipo monganso pamene ana a Lehi adasunga malamulo ake wawadalitsa ndi kuwachititsa monga mwa mawu ake.

23 Inde, ndipo ndithudi iye adzabweretsanso otsalira a mbewu ya Yosefe kuchidziwitso cha Ambuye Mulungu wawo.

24 Ndipo ndithudi monga Ambuye ali wa moyo, iye adzasonkhanitsa pamodzi kuchokera ku ngodya zinayi za dziko lapansi otsalira onse a mbewu ya Yakobo, amene adabalalitsidwa pa nkhope yadziko lonse lapansi.

25 Ndipo monga mene adapanganirana ndi nyumba yonse ya Yakobo, koteronso pangano limene adapangana nalo ndi nyumba ya Yakobo lidzakwaniritsidwa mu nthawi yake yoikika, pakubwenzeretsanso nyumba yonse ya Yakobo ku chidziwitso cha pangano lomwe adapangana nawo.

26 Ndipo pamenepo adzadziwa Muwomboli wawo, amene ali Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu; ndipo pamenepo iwo adzasonkhanitsidwa kuchokera ku ngodya zinayi za dziko lapansi kupita ku maiko awo, kumene adabalalitsidwa; inde, monga Ambuye ali wa moyo, momwemo zidzakhala. Ameni.