Malembo Oyera
3 Nefi 21


Mutu 21

Israeli adzasonkhanitsidwa pamene Buku la Mormoni lidzabwere—Amitundu adzakhazikitsidwa monga anthu aufulu mu Amerika—Adzapulumutsidwa ngati akhulupilira ndi kumvera; apo ayi, iwo adzadulidwa ndi kuwonongedwa—Israeli adzamanga Yerusalemu Watsopano, ndipo mafuko otayika adzabwelera. Mdzaka za pafupifupi Yesu atabadwa 34

1 Ndipo indetu ndinena kwa inu, ndipereka kwa inu chizindikiro, kuti inu mukadziwe nthawi imene zinthu izi ziti zidzachitike—kuti ndidzasonkhanitsa, kuchokera mu kubalalikana kwawo kwakutali, anthu anga, O nyumba ya Israeli, ndipo ndidzakhazikitsanso Ziyoni wanga pakati pawo;

2 Ndipo taonani, ichi ndi chinthu chimene ine ndidzapereka kwa inu monga chizindikiro—pakuti indetu ndinena kwa inu kuti pamene zinthu izi zimene ine ndikulengeza kwa inu, ndi zimene ine ndidzalengeza kwa inu patsogolo pa ine ndekha, ndi mwa mphamvu ya Mzimu Woyera umene udzaperekedwa kwa inu ndi Atate, zidzadziwika kwa Amitundu kuti iwo adziwe zokhudzana ndi anthu awa amene ali otsalira a nyumba ya Yakobo, ndi zokhudzana ndi anthu anga awa omwe adzabalalitsidwa ndi iwo;

3 Indetu, indetu, ndinena kwa inu, pamene zinthu izi zidzadziwika kwa iwo za Atate, ndipo zidzatuluka kuchokera kwa Atate, kuchokera kwa iwo kupita kwa inu;

4 Pakuti ndi nzeru mwa Atate kuti iwo akhazikitsidwe m’dziko lino, ndi kukhazikitsidwa monga anthu aufulu ndi mphamvu ya Atate, kuti zinthu izi zikathe kutuluka kuchokera kwa iwo kupita kwa otsalira a mbewu yanu, kuti pangano la Atate lithe kukwaniritsidwa limene adapangana ndi anthu awo, O nyumba ya Israeli;

5 Kotero, pamene ntchito izi ndi ntchito zimene zidzachitidwa pakati panu mtsogolo muno zidzatuluka kuchokera kwa Amitundu, kupita kwa mbewu yanu imene idzacheperachepera mu kusakhulupilira chifukwa cha kusaweruzika;

6 Ndipo choncho zidayenera Atate kuti zibwere kuchokera kwa Amitundu, kuti iwo athe kuwonetsa mphamvu yawo kwa Amitundu, chifukwa cha ichi kuti Amitundu, ngati saumitsa mitima yawo, kuti akathe kulapa ndi kubwera kwa ine ndi kubatizidwa m’dzina langa ndi kudziwa za mfundo zoona za chiphunzitso changa, kuti zikathe kuwerengedwa m’kati mwa anthu anga, O nyumba ya Israeli;

7 Ndipo pamene zinthu izi zidzachitika kuti mbewu yanu idzayamba kudziwa zinthu izi—chidzakhala chizindikiro kwa iwo, kuti iwo akadziwe kuti ntchito ya Atate yayamba kale m’kukwaniritsidwa kwa pangano limene iwo adapanga kwa anthu a m’nyumba ya Israeli.

8 Ndipo pamene tsiku limenelo lidzafika, zidzachitika kuti mafumu adzatseka pakamwa pawo; pakuti chimene sichidawuzidwe kwa iwo adzachiona; ndipo icho chimene iwo sadachimve iwo adzachilingalira.

9 Pakuti mu tsiku limenelo, chifukwa cha ine Atate adzagwira ntchito, imene idzakhala ntchito yaikulu ndi yodabwitsa pakati pawo; ndipo pakati pawo padzakhala amene sadzayikhulupilira, ngakhale munthu adzayilengeza kwa iwo.

10 Koma taonani, moyo wa mtumiki wanga udzakhala m’dzanja langa; kotero iwo sadzamchitira iye choipa, angakhale iye adzawonongeka chifukwa cha iwo. Komabe ine ndidzamuchiritsa iye, pakuti ine ndidzaonetsa kwa iwo kuti nzeru zanga ndi zazikulu kuposa chinyengo cha mdyerekezi.

11 Kotero zidzachitika kuti aliyense amene sadzakhulupilira mawu anga, amene ndine Yesu Khristu, amene Atate adzamuchititsa kuti abweretse kwa Amitundu, ndipo adzamupatsa mphamvu kuti awabweretsere iwo kwa anthu a mitundu ina, (zidzachitika ngakhale monga Mose adanenera) adzadulidwa pakati pa anthu anga amene ali m’chipanganocho.

12 Ndipo anthu anga amene ali otsalira a Yakobo adzakhala pakati pa Amitundu, inde, pakati pawo ngati mkango pakati pa zilombo za kuthengo, ngati mkango waung’ono pakati pa magulu a nkhosa, amene, ngati awadutsa onse awiri apondedwapondedwa ndi kukhadzulidwa mzidutswa, ndipo palibe amene angapulumutse.

13 Dzanja lawo lidzakwezeka pa adani awo, ndipo adani awo onse adzawonongedwa.

14 Inde, tsoka likhale kwa Amitundu pokhapokha iwo atalapa; pakuti zidzachitika mu tsiku lomwelo, atero Atate, kuti ndidzawononga akavalo anu pakati panu, ndi kuwononga magareta ako;

15 Ndipo ndidzawononga midzi ya dziko lanu, ndi kupasula malinga ako onse;

16 Ndipo ndidzachotsa anyanga m’dziko lanu, ndipo simudzakhalanso ndi alosi obwebweta;

17 Mafano anu osema ndidzachotsanso, ndi mafano anu oyimilira pakati panu; ndipo simudzalambiranso ntchito za manja anu;

18 Ndipo ndidzazula mitengo yanu pakati panu; kuti ndidzawononge midzi yanu.

19 Ndipo zidzachitika kuti mabodza onse, ndi zinyengo, ndi kaduka, ndi mikangano, ndi zaunsenbe zolakwika, ndi zadama, zidzathetsedwa.

20 Pakuti zidzachitika, atero Atate, kuti pa tsiku limenelo aliyense amene sadzalapa ndi kubwera kwa Mwana wanga Wokondedwa, iwo ndidzawadula kuchokera pakati pa anthu anga, O nyumba ya Israeli;

21 Ndipo ndidzabwenzera chilango ndi mkwiyo pa iwo, monga pa achikunja, monga iwo amene sadamve.

22 Koma ngati angalape ndi kumvetsera mawu anga, ndi kusaumitsa mitima yawo, ndidzakhazikitsa mpingo wanga pakati pawo, ndipo adzalowa m’pangano ndi kuwerengedwa pakati pa otsalira awa a Yakobo, kwa iwo amene ndawapatsa dziko lino ku cholowa chawo.

23 Ndipo adzathandiza anthu anga, otsalira a Yakobo, ndiponso ambiri a nyumba ya Israeli amene adzabwera, kuti akathe kumanga mzinda, umene udzatchedwa Yerusalemu Watsopano.

24 Ndipo kenaka iwo adzathandiza anthu anga kuti akasonkhanitsidwe m’menemo, amene adabalalitsidwa pa nkhope yonse ya dzikolo, mpaka ku Yerusalemu Watsopanoyo.

25 Ndipo pamenepo mphamvu ya Kumwamba idzatsika pakati pawo; ndipo inenso ndidzakhala pakatipo.

26 Ndipo pamenepo ntchito ya Atate idzayamba pa tsiku limenelo, ngakhale pamene uthenga wabwino uwu udzalalikidwa pakati pa otsalira a anthu awa. Indetu ndinena kwa inu, pa tsiku limenelo ntchito ya Atate idzayamba pakati pa obalalika onse a anthu anga, inde, ngakhale mafuko amene atayika, amene Atate adawatsogolera kuchokera mu Yerusalemu.

27 Inde, ntchito idzayambika pakati pa obalalika onse a anthu anga, ndi Atate kukonza njira imene iwo angadzere kwa ine, kuti iwo akayitanire pa Atate m’dzina langa.

28 Inde, ndipo pamenepo, ntchito idzayamba, ndi Atate pakati pa mitundu yonse pokonza njira imene anthu awo adzasonkhanitsidwira kwawo ku dziko la cholowa chawo.

29 Ndipo adzatuluka mwa mitundu yonse; ndipo sadzatuluka mwaliwiro, kapena kupita mothawa, pakuti ine ndidzapita patsogolo pawo, atero Atate, ndipo ndidzakhala pambuyo pawo.