Malembo Oyera
3 Nefi 2


Mutu 2

Zoipa ndi zonyansa zikula pakati pa anthu—Anefi ndi Alamani agwirizana kuti adzitetezere wokha motsutsana ndi achifwamba a Gadiyantoni—Alamani otembenuka akhala oyera ndipo atchedwa Anefi. Mdzaka dza pafupifupi Yesu atabadwa 5–16.

1 Ndipo zidachitika kuti momwemonso chidatha chaka cha makumi asanu ndi anayi ndi zisanu, ndipo anthu adayamba kuyiwala zizindikiro ndi zodabwitsa zija zomwe adazimva, ndipo adayamba pang’ono ndi pang’ono kusadabwa ndi chizindikiro kapena chozizwa chochokera kumwamba, kufikira kuti adayamba kuuma m’mitima mwawo, ndi khungu m’maganizo mwawo, ndipo adayamba kusakhulupilira zonse zomwe adazimva ndi kuziona;

2 Kulingalira chinthu chachabechabe m’mitima mwawo, kuti zidachitidwa ndi anthu ndi mphamvu ya mdyerekezi, kusocheretsa ndi kunyenga mitima ya anthu; ndipo motero Satana adatenganso mitima ya anthu kachiwiri, kufikira kuti iye adachititsa khungu maso awo ndi kuwatsogolera iwo kutali kuti akhulupilire kuti chiphunzitso cha Khristu chidali chinthu chopusa ndi chopanda pake.

3 Ndipo zidachitika kuti anthu adayamba kukula mphamvu mu zoipa ndi zonyansa; ndipo sadakhulupilire kuti pakuyenera kukhala zizindikiro kapena zodabwitsa zinanso zodzaperekedwa; ndipo Satana adayendayenda, kusokeretsa mitima ya anthu; kuwayesa ndi kuwachititsa iwo kuti achite zoipa zazikulu m’dzikomo.

4 Ndipo motero chidatha chaka cha makumi asanu ndi anayi ndi mphambu zisanu ndi imodzi; komanso chaka cha makumi asanu ndi anayi kudza zisanu ndi ziwiri; ndiponso chaka cha makumi asanu ndi anayi kudza zisanu ndi zitatu; komanso chaka cha makumi asanu ndi anayi kudza zisanu ndi zinayi;

5 Komanso dzaka zana limodzi zidali zitatha kuchokera masiku a Mosiya, amene adali mfumu pa anthu a Anefi.

6 Ndipo dzaka mazana asanu ndi limodzi mphambu zisanu ndi zinayi zidali zitatha kuchokera pamene Lehi adachoka ku Yerusalemu.

7 Ndipo dzaka zisanu ndi zinayi zidali zitatha kuchokera nthawi imene chizindikiro chidaperekedwa, chimene chidanenedwa ndi aneneri, kuti Khristu adzabwera ku dziko lapansi.

8 Tsopano Anefi adayamba kuwerengera nthawi yawo kuyambira nthawi iyi pamene chizindikiro chidaperekedwa, kapena kuchokera pa kudza kwa Khristu; kotero, dzaka zisanu ndi zinayi zidali zitatha

9 Ndipo Nefi, amene adali atate a Nefi, amene adali ndi udindo wa zolemba, sadabwelere ku dziko la Zarahemula, ndipo sadapezeke paliponse m’dziko lonselo.

10 Ndipo zidachitika kuti anthu adatsalirabe mu kuipa, posatengera za kulalika kochuluka ndi kunenera kumene kudatumizidwa pakati pawo; ndipo kotero chidathanso chaka chakhumi; ndipo chaka chakhumi ndi chimodzi chidathanso m’kusaweruzika.

11 Ndipo zidachitika m’chaka chakhumi ndi chachitatu kudayamba kukhala nkhondo ndi mikangano m’dziko lonselo; pakuti achifwamba a Gadiyantoni adali atachuluka kwambiri, ndipo adapha ambiri a anthu, ndipo adasakaza mizinda yambiri, ndipo zidafalitsa imfa yochuluka ndi kuphana mu dziko lonse, kuti chidakhala chofunikira kuti anthu onse, onse Anefi ndi Alamani, adayenera kutenga zida motsutsana nawo.

12 Kotero, Alamani onse amene adatembenukira kwa Ambuye adagwirizana ndi abale awo, Anefi, ndipo adakakamizika, chifukwa cha chitetezo cha miyoyo yawo ndi akazi awo ndi ana awo, kuti atenge zida motsutsana ndi achifwamba a Gadiyantoniwo, inde, ndiponso kuti asunge maufulu awo, ndi mwayi wa mpingo wawo ndi wa kupembedza kwawo, ndi kumasuka kwawo ndi ufulu wawo.

13 Ndipo zidachitika kuti chaka chimenechi chakhumi ndi chachitatu chisadathe Anefi adawopsezedwa ndi chiwonongeko chotheratu chifukwa cha nkhondo iyi, yomwe idakhala yowawa kwambiri.

14 Ndipo zidachitika kuti Alamani amene adalumikizana ndi Anefiwo adawerengedwa pakati pa Anefi;

15 Ndipo thembelero lawo lidachotsedwa kwa iwo, ndipo khungu lawo lidakhala loyera monga la Anefi;

16 Ndipo anyamata awo ndi ana awo aakazi adakhala okongola mopambana, ndipo adawerengedwa pakati pa Anefi, ndipo adatchedwa Anefi. Ndipo motero chidatha chaka chakhumi ndi chitatu.

17 Ndipo zidachitika pachiyambi pa chaka chakhumi ndi chachinayi, nkhondo pakati pa achifwamba ndi anthu a Nefi idapitilira ndipo idakhala yowawa kwambiri; komabe, anthu a Nefi adapezapo mwayi wina pa achifwamba, kotero kuti iwo adawathamangitsira m’mbuyo kuchoka m’maiko awo kupita kumapiri ndi ku malo awo obisika.

18 Ndipo motero chidatha chaka chakhumi ndi chinayi. Ndipo m’chaka chakhumi ndi chisanu adatulukira kudzamenyana ndi anthu a Nefi; ndipo chifukwa cha zoipa za anthu a Nefi, ndi mikangano yawo yambiri ndi kusagwirizana, achifwamba a Gadiyantoni adapeza mwayi wambiri pa iwo.

19 Ndipo motero chidatha chaka chakhumi ndi chachisanu, ndipo motero anthu adali mumkhalidwe wa masautso ambiri; ndipo lupanga la chiwonongeko lidapachikidwa pa iwo, kufikira kuti iwo adali pafupi kukanthidwa nalo pansi, ndipo ichi chidali chifukwa cha kusaweruzika kwawo.