Malembo Oyera
3 Nefi 22


Mutu 22

M’masiku otsiriza, Ziyoni ndi masiteki ake adzakhazikitsidwa, ndipo Israeli adzasonkhanitsidwa m’chifundo ndi modekha—Adzapambana—Fananizani ndi Yesaya 54 Mdzaka za pafupifupi Yesu atabadwa 34.

1 Ndipo pamenepo icho chimene chidalembedwa chidzachitika: Imba, iwe mayi wosabala, iwe amene sudabalepo; imba nyimbo, ndi kufuula mokweza, iwe amene sudamvepo ululu wa pobeleka; pakuti ochuluka ali ana a wosiyidwa koposa ana a mkazi wokwatiwa, atero Ambuye.

2 Kulitsa malo a hema wako, ndipo alore atambasule makatani ako okhalamo; usaleke, talikitsa zingwe zako, ndipo limbitsa zikhomo zako;

3 Pakuti iwe udzatulukira pa dzanja lamanja ndi lamanzere, ndipo mbewu yako idzalandira Amitundu, ndipo kuchititsa mizinda yabwinja kukhalamo anthu.

4 Usaope, pakuti sudzachita manyazi; kapena kusokonezedwa, pakuti sudzachititsidwa manyazi; pakuti udzaiwala manyazi a ubwana wako, ndipo sudzakumbukira chitonzo cha ubwana wako, ndipo sudzakumbukiranso chitonzo cha umasiye wako.

5 Pakuti mlengi wako, mwamuna wako, Ambuye wa Makamu ndi dzina lake; ndi Muwomboli wako, Woyera wa Israeli—Mulungu wa dziko lonse lapansi Iye adzatchedwa.

6 Pakuti Ambuye wakuitana iwe monga mkazi wosiyidwa ndi wozunzika mu mzimu, ndi mkazi wa kuubwana, pamene iwe udakanidwa, atero Mulungu wako.

7 Kwa kamphindi kakang’ono ndakusiya iwe, koma ndi chifundo chachikulu ndidzakusonkhanitsa iwe.

8 M’kukwiya pang’ono ndidabisa nkhope yanga kwa iwe kwa kanthawi, koma ndi kukoma mtima kosatha ndidzakuchitira chifundo, atero Ambuye Muwomboli wako.

9 Chifukwa cha ichi, madzi a Nowa kwa ine, pakuti monga ndidalumbira kuti madzi a Nowa sadzapitanso pa dziko lapansi, momwemonso ndalumbira kuti sindidzakukwiyira iwe.

10 Pakuti mapiri adzachoka ndipo zitunda zidzasunthika, koma kukoma mtima kwanga sikudzachoka kwa iwe, ngakhale pangano lamtendere wanga silidzachotsedwa, atero Ambuye amene ali ndi chifundo pa iwe.

11 O iwe wosautsidwa, wokanthidwa ndi namondwe, ndi wosatonthozedwa! Taona, ndidzayala miyala yako yamitundu yokongola, ndi kukhazika maziko ako ndi miyala ya safira.

12 Ndipo ndidzamanga mazenera ako ndi miyala yokongola ya agati, ndi zipata zako ndi miyala ya rubi, ndi malire ako onse ndi miyala yamtengo wapatali.

13 Ndipo ana ako onse adzaphunzitsidwa ndi Ambuye; ndipo waukulu udzakhala mtendere wa ana ako.

14 M’chilungamo udzakhazikitsidwa; udzakhala kutali ndi kuponderezedwa pakuti sudzaopa, ndi chiopsezo, pakuti sichidzakuyandikira iwe.

15 Taona, iwo adzakusonkhanira pamodzi kutsutsana nawe ndithu, osati ndi ine; amene adzasonkhana motsutsana nawe adzagwa chifukwa cha iwe.

16 Taonani, ndalenga wosula amene amawuzira makala pamoto, ndi amene amatulutsa chiwiya cha ntchito yake; ndipo ndalenga wowononga kuti awononge.

17 Palibe chida chimene chasulidwira iwe chidzapindule; ndipo lilime lirilonse limene lidzanyoza iwe m’chiweruzo udzalitsutsa. Ichi ndi cholowa cha atumiki a Ambuye, ndipo kulungama kwawo n’kochokera kwa ine, atero Ambuye.