Malembo Oyera
3 Nefi 17


Mutu 17

Yesu atsogolera anthu kuti asinkhesinkhe mawu Ake ndi kupemphelera kumvetsetsa—Achiritsa odwala awo—Iye apemphelera anthu, pogwiritsa ntchito chinenero chimene sichingalembedwe—Angelo atumikira ndipo moto uzinga ana awo aang’ono. Mdzaka dza pafupifupi Yesu atabadwa 34.

1 Taonani, tsopano zidachitika kuti pamene Yesu adayankhula mawu awa adayang’ana mozungulira khamulo, ndipo iye adanena nawo: Taonani, nthawi yanga yayandikira.

2 Ndikuona kuti muli ofooka, kuti simungathe kumvetsetsa mawu anga onse amene ndalamulidwa ndi Atate kuti ndiyankhule kwa inu pa nthawi ino.

3 Kotero, pitani inu ku nyumba zanu, ndi kusinkhasinkha pa zinthu zimene ine ndidayankhula, ndipo pemphani kwa Atate, m’dzina langa, kuti inu mukamvetsetse, ndi kukonzekeretsa malingaliro anu kwa mawa, ndipo ine ndidzabweranso kwa inu kachiwiri.

4 Koma tsopano ine ndikupita kwa Atate, ndiponso kuti ndikadzionetsere ndekha kwa mafuko otayika a Israeli, pakuti iwo sadatayike kwa Atate, pakuti iwo akudziwa kumene iwo adawatengera iwo.

5 Ndipo zidachitika kuti pamene Yesu adanena izi, adaponyanso maso ake mozunguliranso pa khamulo, ndipo adaona kuti adali m’misonzi, ndipo adayang’ana mokhazikika pa iye monga ngati amupempha kuti akhale nawo kanthawi pang’ono.

6 Ndipo adati kwa iwo, Taonani, zimphyo zanga zadzala ndi chifundo pa inu.

7 Kodi muli nawo aliwonse amene akudwala mwa inu? Abweretseni iwo kuno. Kodi muli nawo olumala, kapena akhungu, kapena otsimphina, kapena achilema, kapena akhate, kapena opuwala, kapena ogontha, kapena akusautsidwa mwanjira iliyonse? Abweretseni kuno, ndipo ndidzawachiritsa, pakuti ndili ndi chifundo pa inu; zimphyo zanga zadzala ndi chifundo.

8 Pakuti ine ndikudziwa kuti mukufuna kuti ndionetse kwa inu zimene ndachita kwa abale anu mu Yerusalemu, pakuti ndaona kuti chikhulupiliro chanu ndi chokwanira kuti ndikuchilitseni inu.

9 Ndipo zidachitika kuti, pamene adanena izi, khamu lonse lidatuluka ndi mtima umodzi, ndi odwala awo, ndi osautsika awo, ndi olumala awo, ndi akhungu awo, ndi osayankhula awo, ndi onse amene adali kusautsidwa mwanjira iliyonse; ndipo adawachiritsa onse pamene adabweretsedwa kwa iye.

10 Ndipo adatero onse, iwo amene adachiritsidwawo ndi iwo amene adali alungalunga, adagwada pa mapazi ake, ndi kumulambira; ndipo onse amene adatha kubwera a khamu la anthuli adampsompsona mapazi ake, kotero kuti adasambitsa mapazi ake ndi misonzi yawo.

11 Ndipo zidachitika kuti adalamula kuti tiana tawo tating’ono tibweretsedwe.

12 Kotero iwo adabweretsa tiana tawo tating’ono ndikutikhazika pansi mozungulira iye, ndipo Yesu adaimilira pakati; ndipo khamulo lidapereka njira kufikira adabwera nato tonse kwa iye.

13 Ndipo zidachitika kuti pamene iwo onse adabweretsedwa, ndipo Yesu adaimilira pakati, iye adalamulira khamulo kuti ligwade pansi.

14 Ndipo zidachitika kuti pamene lidagwada pansi, Yesu adabuula mwa iye yekha, ndi kuti: Atate, ndikusautsika chifukwa cha kuipa kwa anthu a nyumba ya Israeli.

15 Ndipo pamene adanena mawu awa, iye nayenso adagwada pansi; ndipo taonani, adapemphera kwa Atate, ndipo zinthu zimene adapemphera sizingathe kulembedwa, ndipo khamulo lidachitira umboni limene lidamumva iye.

16 Ndipo moteromu iwo akuchitira umboni: Diso silidaonepo, ngakhale khutu silidamvepo, zinthu zazikulu ndi zodabwitsa monga tidaona ndi kumva Yesu akuyankhula kwa Atate;

17 Ndipo palibe lilime lingathe kuyankhula, ngakhale sizingathe kulembedwa ndi munthu aliyense, ngakhale mitima ya anthu singathe kulingalira zinthu zazikulu ndi zodabwitsa monga momwe ife tidaonera ndi kumva Yesu akuyankhula; ndipo palibe amene angaganizire za chisangalalo chimene chidadzadza m’miyoyo yathu pa nthawi imene tidamumva iye akutipemphelera kwa Atate.

18 Ndipo zidachitika kuti pamene Yesu adamaliza kupemphera kwa Atate, adaimilira; koma chachikulu chidali chisangalaro cha khamulo kotero kuti lidagonjetsedwa.

19 Ndipo zidachitika kuti Yesu adayankhula nawo, ndi kuwawuza anyamuke.

20 Ndipo adanyamuka pansipo, ndipo adati kwa iwo, Odala muli inu chifukwa cha chikhulupiliro chanu. Ndipo tsopano taonani, chisangalalo changa ndichodzaza.

21 Ndipo pamene adanena mawu awa, iye adalira, ndipo khamu lidachitira umboni za izo, ndipo iye adatenga tiana tawo tating’ono, kamodzikamodzi, ndi kutidalitsa ito, ndipo adatipemphelera ito kwa Atate.

22 Ndipo pamene adachita ichi, iye adaliranso;

23 Ndipo iye adayankhula kwa khamulo, ndipo adanena nawo, Taonani tiwana tanu.

24 Ndipo pamene iwo adayang’ana kuti aone iwo adaponya maso awo ku thambo, ndipo iwo adaona kumwamba kutatseguka, ndipo iwo adaona angelo akutsika kuchokera kumwamba ngati iwo adali ngati pakati pa moto; ndipo adatsika pansi, ndikuzinga tiana tawo, ndipo tidazingidwa ndi moto; ndipo angelo adatumikira kwa iwo.

25 Ndipo khamulo lidaona, ndi kumva, ndi kuchitira umboni; ndipo akudziwa kuti umboni wawo uli woona pakuti iwo adaona ndi kumva, munthu aliyense payekha; ndipo adali mu chiwerengero chawo pafupifupi anthu zikwi ziwiri mphambu mazana asanu; ndipo adali amuna, akazi, ndi ana.

Print