Malembo Oyera
3 Nefi 26


Mutu 26

Yesu afotokoza zinthu zonse kuchokera ku chiyambi mpaka kumapeto—Makanda ndi ana ayankhula zinthu zodabwitsa zimene sizingathe kulembedwa—Amene ali mu Mpingo wa Khristu ali ndi zinthu zonse mogwirizana pakati pawo. Mdzaka za pafupifupi Yesu atabadwa 34.

1 Ndipo tsopano zidachitika kuti pamene Yesu adanena izi adazifotokozera kwa anthuwo; ndipo adawafotokozera zinthu zonse, zonse zazikulu ndi zazing’ono.

2 Ndipo iye adati: malembo oyera awa, amene mudalibe, Atate adalamura kuti ine ndipereke kwa inu; pakuti idali nzeru mwa iwo kuti izo zikuyenera kuperekedwa kwa mibadwo yamtsogolo.

3 Ndipo iye adafotokoza zinthu zonse, ngakhale kuchokera pachiyambi mpaka nthawi yakuti iye adzabwere mu ulemerero wake—inde, ngakhale zinthu zonse zimene zikuyenera kudza pa nkhope ya dziko lapansi, ngakhale mpaka zinthu zoyamba zidzasungunuka ndi kutentha kwakukulu, ndipo dziko lapansi likuyenera kukulungidwa ngati mpukutu, ndipo thambo ndi dziko lapansi zidzatha;

4 Ndipo ngakhale mpakana pa tsiku lalikulu ndi lotsiriza, pamene anthu onse, ndi mafuko onse, ndi maiko onse ndi zinenero zidzayimilira pamaso pa Mulungu, kuti ziweruzidwe chifukwa cha ntchito zawo, ngati zili zabwino kapena zoipa—

5 Ngati ali abwino, ku chiwukitso cha moyo wosatha; ndipo ngati ali oipa, ku chiwukitso cha chilango; kukhala mosiyana, wina ku dzanja limodzi ndi wina ku dzanja lina, monga mwa chifundo, ndi chilungamo, ndi chiyero chimene chili mwa Khristu, amene adalipo dziko lisadayambe.

6 Ndipo tsopano sipangathe kulembedwa mu buku ili ngakhale gawo limodzi mwa magawo zana la zinthu zimene Yesu adaphunzitsa moonadi kwa anthu;

7 Koma taonani mapale a Nefi ali ndi gawo lochuluka la zinthu zimene iye adaphunzitsa anthuwo.

8 Ndipo zinthu izi ndalemba, zomwe zili gawo laling’ono la zinthu zomwe iye adaphunzitsa anthu; ndipo ndalemba izo ndi cholinga chokuti izo zithe kubweretsedwa kachiwiri kwa anthu awa, ochokera kwa Amitundu, monga mwa mawu amene Yesu adayankhula.

9 Ndipo pamene iwo adzalandira ichi, chimene chili choyenera kuti iwo akhale nacho koyamba, kuti ayesere chikhulupiliro chawo, ndipo ngati kudzakhala kotero kuti iwo adzakhulupilira zinthu izi pamenepo zinthu zazikulu zidzaonetsedwa kwa iwo.

10 Ndipo ngati zidzakhala kuti iwo sadzakhulupilira zinthu izi, pamenepo zinthu zazikulu zidzabisidwa kwa iwo, ku kutsutsidwa kwawo.

11 Taonani, ndidali pafupi kuzilemba, zonse zimene zidalembedwa pa mapale a Nefi, koma Ambuye adaletsa izi, kuti: Ndidzayesa chikhulupiliro cha anthu anga.

12 Kotero, ine, Mormoni, ndalemba zinthu zimene ndalamulidwa ine ndi Ambuye. Ndipo tsopano ine, Mormoni, ndikutsiriza mawu anga, ndikupitiriza kulemba zinthu zimene ndalamulidwa ine.

13 Kotero, ndikufuna kuti muone kuti zowonadi Ambuye adaphunzitsa anthu, kwa nthawi ya masiku atatu; ndipo pambuyo pake adadziwonetsera yekha kwa iwo kawiri kawiri, ndipo adanyema mkate kawiri kawiri, ndi kuwudalitsa, ndi kuwupereka kwa iwo.

14 Ndipo zidachitika kuti iye adaphunzitsa ndi kutumikira kwa ana a khamu la amene lanenedwali, ndipo iye adamasula malilime awo, ndipo adayankhula kwa makolo awo zinthu zazikulu ndi zodabwitsa, ngakhale zazikulu kuposa zomwe adaululira kwa anthu; ndipo adamasula malilime awo kuti ayankhule.

15 Ndipo zidachitika kuti atakwera kumwamba—nthawi yachiwiri imene iye adadzionetsera kwa iwo, ndipo atapita kwa Atate, atachiritsa odwala awo onse, ndi olumala, ndi kutsegula maso a akhungu awo ndi kutsegula makutu a ogontha; ndipo ngakhale atachita machiritso amtundu uliwonse pakati pawo, ndipo atawukitsa munthu kuchokera kwa akufa, ndipo atawonetsa mphamvu yake kwa iwo, ndipo atakwera kwa Atate—

16 Taonani, zidachitika m’mawa kuti khamu la anthu lidadzisonkhanitsa lokha pamodzi, ndipo adaona ndi kumva ana awa; inde, ngakhale makanda adatsegula pakamwa pawo ndi kunena zinthu zodabwitsa; ndipo zinthu zimene adaziyankhula zidaletsedwa kuti zisalembedwe ndi munthu aliyense.

17 Ndipo zidachitika kuti ophunzira amene Yesu adawasankha adayamba kuyambira nthawi imeneyo kupita mtsogolo kubatiza ndi kuphunzitsa ambiri amene adadza kwa iwo; ndipo onse amene adabatizidwa m’dzina la Yesu adadzadzidwa ndi Mzimu Woyera.

18 Ndipo ambiri a iwo adaona ndi kumva zinthu zosaneneka, zimene ndi zosaloleka kulembedwa.

19 Ndipo iwo adaphunzitsa, ndipo adatumikirana wina ndi mzake; ndipo adali nazo zinthu zonse zofanana pakati pawo, munthu aliyense kuchita molungama, wina ndi mzake.

20 Ndipo zidachitika kuti iwo adachita zinthu zonse monga momwe Yesu adawalamulira iwo.

21 Ndipo iwo amene adabatizidwa mu dzina la Yesu adatchedwa mpingo wa Khristu.