Malembo Oyera
3 Nefi 19


Mutu 19

Ophunzira khumi ndi awiriwo atumikira kwa anthu ndi kupemphelera Mzimu Woyera—Ophunzira abatizidwa ndi kulandira Mzimu Woyera ndi utumiki wa angelo—Yesu apemphera pogwiritsa ntchito mawu amene sangalembedwe—Iye achitira umboni ku chikhulupiliro chachikulu kwambiri cha Anefi awa. Mdzaka za pafupifupi Yesu atabadwa 34.

1 Ndipo tsopano zidachitika kuti pamene Yesu adakwera kumwamba, khamu la anthu lidabalalika, ndipo mamuna aliyense adatenga mkazi wake ndi ana ake ndipo adabwelera ku nyumba yake.

2 Ndipo kudamveka phokoso pakati pa anthu nthawi yomweyo, usadadze mdima, kuti khamu la anthu lidaona Yesu, ndi kuti adatumikira kwa iwo, ndipo kuti iye akadzionetsanso iye mwini mawa kwa khamulo.

3 Inde, ndipo ngakhale usiku onse kudamveka phokoso lokhudza Yesu; ndipo kotero kuti iwo adatumiza kwa anthu kuti adalipo ambiri, inde, chiwerengero chachikulu kwambiri, chidagwira ntchito mopambana usiku onsewo, kuti akakhaleko mawa kumalo amene Yesu akadzionetsere yekha kwa khamulo.

4 Ndipo zidachitika kuti m’mawa mwake, pamene khamu la anthu lidasonkhana pamodzi, taonani, Nefi ndi m’bale wake amene adamuukitsa kwa akufa, amene dzina lake lidali Timoteyo, ndi mwana wake, amene dzina lake lidali Yona, ndiponso Matoni, ndi Matoniha, m’bale wake; ndi Kumeni, ndi Kumenoni, ndi Yeremiya, ndi Shemunoni, ndi Yonasi, ndi Zedekiya, ndi Yesaya—tsopano awa adali maina a ophunzira amene Yesu adawasankha—ndipo zidachitika kuti iwo adapita ndipo adaima pakati pa khamulo.

5 Ndipo taonani, khamulo lidali lalikulu kotero kuti iwo adapangitsa kuti ilo lilekanitsidwe mu magulu khumi ndi awiri.

6 Ndipo khumi ndi awiriwo adaphunzitsa khamulo; ndipo taonani, iwo adapangitsa kuti khamulo ligwade pansi pa nkhope ya dziko lapansi, ndipo likuyenera kupemphera kwa Atate m’dzina la Yesu.

7 Ndipo ophunzira adapempheranso kwa Atate m’dzina la Yesu. Ndipo zidachitika kuti adanyamuka ndipo adatumikira kwa anthuwo.

8 Ndipo pamene iwo adatumikira mawu omwewo amene Yesu adayankhula—popanda chosiyana ndi mawu amene Yesu adayankhula—taonani, iwo adagwadanso ndipo adapemphera kwa Atate m’dzina la Yesu.

9 Ndipo iwo adapemphelera chimene iwo ankachifuna kwambiri; ndipo adafuna kuti Mzimu Woyera upatsidwe kwa iwo.

10 Ndipo pamene iwo adapemphera motero adatsikira m’mphepete mwa madzi, ndipo khamu la anthulo lidawatsatira.

11 Ndipo zidachitika kuti Nefi adalowa m’madzi ndipo adabatizidwa.

12 Ndipo iye adatuluka m’madzimo ndi kuyamba kubatiza. Ndipo iye adabatiza iwo onse amene Yesu adawasankha.

13 Ndipo zidachitika pamene iwo onse adabatizidwa ndipo adatuluka m’madzimo, Mzimu Woyera udagwera pa iwo, ndipo iwo adadzadzidwa ndi Mzimu Woyera ndi moto.

14 Ndipo taonani, iwo adazingidwa ngati ndi moto; ndipo udatsika kuchokera kumwamba, ndipo khamu la anthu lidachitira umboni, ndipo lidachitira umboni; ndipo angelo adatsika kuchokera kumwamba ndipo adatumikira kwa iwo.

15 Ndipo zidachitika kuti pamene angelo adali kutumikira kwa ophunzirawo, taonani, Yesu adabwera ndikuyima pakati ndi kutumikira kwa iwo.

16 Ndipo zidachitika kuti adayankhula kwa khamulo, ndipo adawalamulira iwo kuti agwadenso pansi, ndiponso kuti ophunzira ake agwade pansi.

17 Ndipo zidachitika kuti pamene iwo onse adagwada pansi, adalamulira ophunzira ake kuti apemphere.

18 Ndipo taonani, adayamba kupemphera; ndipo adapemphera kwa Yesu, kumutchula Iye Ambuye wawo ndi Mulungu wawo.

19 Ndipo zidachitika kuti Yesu adachoka pakati pawo, ndipo adapita patali pang’ono ndi iwo, nagwada pansi, ndipo adati:

20 Atate, ndikukuyamikani kuti mwapereka Mzimu Woyera kwa iwo amene ndawasankha; ndipo ndi chifukwa cha chikhulupiliro chawo mwa ine kuti ndidawasankha iwo kuchoka dziko lapansi.

21 Atate, ine ndikukupemphani inu kuti mudzapereke Mzimu Woyera kwa onse amene adzakhulupilire mu mawu awo.

22 Atate, inu mwawapatsa Mzimu Woyera, chifukwa amakhulupilira mwa ine; ndipo inu mwaona kuti akhulupilira ine chifukwa inu mwawamva iwo, ndipo akupemphera kwa ine; ndipo akupemphera kwa ine chifukwa ndili nawo.

23 Ndipo tsopano Atate, ine ndikuwapemphelera iwo kwa inu, ndiponso kwa onse amene adzakhulupilira mawu awo, kuti akhulupilire mwa ine, kuti ine ndikhale mwa iwo, monga inu, Atate, muli mwa ne, kuti tikhale amodzi.

24 Ndipo zidachitika kuti pamene Yesu adapemphera motero kwa Atate, adadza kwa ophunzira ake, ndipo taonani, iwo adapitirizabe, mosalekeza, kupemphera kwa iye; ndipo sadachulukitse mawu ambiri, pakuti kudapatsidwa kwa iwo chimene adayenera kupemphera, ndipo adadzadzidwa ndi chikhumbo.

25 Ndipo zidachitika kuti Yesu adawadalitsa iwo pamene iwo adapemphera kwa iye; ndipo nkhope yake idamwetulira pa iwo, ndipo kuwala kwa nkhope yake kudawalira pa iwo, ndipo taonani adali oyera ngati mawonekedwe a nkhope komanso zovala za Yesu; ndipo taonani kuyera kwake kudaposa kuyera konse, inde, ngakhale sipadakhalepo kalikonse padziko lapansi koyera monga kuyera kwake.

26 Ndipo Yesu adati kwa iwo, pempheranibe; komabe iwo sadalekeze kupemphera.

27 Ndipo adapatukanso kuchoka pa iwo, ndikuyenda pang’ono ndikuwerama pansi; ndipo adapempheranso kwa Atate, nati:

28 Atate, ndikukuthokozani kuti mwawayeretsa iwo amene ndawasankha, chifukwa cha chikhulupiliro chawo, ndipo ndikuwapemphelera iwo, komanso iwo amene adzakhulupilire mawu awo, kuti ayeretsedwe mwa ine, kudzera mu chikhulupiliro pa mawu awo, ngakhale monga iwo ayeretsedwa mwa ine.

29 Atate, sindikupemphelera dziko lapansi, koma iwo amene mwandipatsa ine m’dziko lapansi, chifukwa cha chikhulupiliro chawo, kuti ayeretsedwe mwa ine, kuti ine ndikhale mwa iwo, monga inu, Atate, muli mwa ine; kuti tikhale amodzi, kuti ine ndikathe kulemekezedwa mwa iwo.

30 Ndipo pamene Yesu adanena mawu awa adabweranso kwa ophunzira ake; ndipo taonani iwo adapemphera mokhazikika, mosalekeza, kwa iye; ndipo adamwetuliranso pa iwo; ndipo taonani iwo adali oyera, ngakhale monga Yesu.

31 Ndipo zidachitika kuti adapitanso patali pang’ono ndikupemphera kwa Atate;

32 Ndipo lilime silingathe kuyankhula mawu amene iye adapemphera, ngakhalenso munthu sangathe kulemba mawu amene iye adapemphera.

33 Ndipo khamulo lidamva ndikuchitira umboni; ndipo mitima yawo idatseguka ndipo adamvetsetsa m’mitima yawo mawu amene adapemphera.

34 Komabe, okulitsitsa ndi odabwitsa adali mawu amene iye adapemphera kuti iwo sangathe kulembedwa, ngakhale kuti sangathe kunenedwa ndi munthu.

35 Ndipo zidachitika kuti, pamene Yesu adatha kupemphera, adabweranso kwa ophunzirawo, ndipo adati kwa iwo, Chikhulupiliro chachikulu chotero sindidachionepo pakati pa Ayuda onse; kotero ine sindikadatha kuwonetsa kwa iwo zozizwitsa zazikulu chotero, chifukwa cha kusakhulupilira kwawo.

36 Indetu ndinena kwa inu, palibe olo mmodzi wa iwo amene adaona zinthu zazikulu monga momwe inu mwaonera; ngakhale sadamve zinthu zazikulu zotere monga mwazimvera inu.

Print