Malembo Oyera
3 Nefi 24


Mutu 24

Mtumiki wa Ambuye adzakonza njira ya Kubwera Kwachiŵiri—Khristu adzakhala mu chiweruzo—Israeli alamulidwa kupereka chakhumi ndi zopereka—Buku la chikumbutso lisungidwa—Fananitsani ndi Malaki 3. Mdzaka za pafupifupi Yesu atabadwa 34.

1 Ndipo zidachitika kuti iye adawalamura iwo kuti iwo akuyenera kulemba mawu amene Atate adapereka kwa Malaki, amene iye ayenera kuwauza iwo. Ndipo zidachitika kuti atalembedwa iye adawafotokoza iwo. Ndipo awa ndi mawu amene iye adawawuza iwo, kuti: Motero adati Atate kwa Malaki—Taonani, Ndidzatumiza mtumiki wanga, ndipo adzakonza njira ine ndisadafike; ndipo Ambuye amene mukumfuna adzafika modzidzimutsa ku Kachisi wake, ngakhale mtumiki wa pangano, amene mumakondwera naye; taonani, iye adzafika, atero Ambuye wa makamu.

2 Koma ndani angapilire tsiku la kudza kwake, ndipo adzayima ndani pamene iye adzawonekere? Pakuti ali ngati moto wa woyenga, ndi monga sopo wa ochapa zovala.

3 Ndipo adzakhala pansi ngati woyenga ndi woyeretsa siliva; ndipo adzayeretsa ana a Levi, ndi kuwayeretsa ngati golidi ndi siliva, kuti akathe kupereka kwa Ambuye chopereka m’chilungamo.

4 Pamenepo chopereka cha Yuda ndi Yerusalemu chidzakhala chokondweretsa kwa Ambuye, monga m’masiku akale, ndi monga m’dzaka zakale.

5 Ndipo ndidzabwera chifupi ndi inu kuti ndiweruze; ndipo ndidzakhala mboni yofulumira yotsutsa amatsenga, ndi achigololo, ndi olumbira monama, ndi otsutsa iwo amene amapondereza waganyu pa malipiro ake, akazi amasiye ndi ana amasiye, ndi iwo amene amatembenukira kumbali mlendo, osandiopa ine; atero Ambuye wa makamu.

6 Pakuti ine Ambuye, sindisintha; kotero inu ana a Yakobo simunawonongedwe.

7 Ngakhale kuyambira masiku a makolo anu mwapatuka ku malamulo anga ndipo simudawasunge. Bwelerani kwa ine, ndipo ine ndidzabwelera kwa inu, atero Ambuye wa makamu. Koma inu mumati, tidzabwelera kuti?

8 Kodi munthu angabere Mulungu? Koma inu mwandibera. Koma inu mwanena, Takuberani bwanji? Mu chakhumi ndi zopereka.

9 Mwatembeleredwa ndi tembelero, pakuti mwandibera ine, ngakhale mtundu wonse uwu.

10 Bweretsani chakhumi chonse ku nyumba yosungira, kuti m’nyumba mwanga muthe kukhala chakudya; ndipo mundiyese ine tsopano ndi ichi, atero Ambuye wa makamu, ngati sindidzakutsegulirani mazenera a kumwamba, ndi kukukhuthulirani mdalitso kuti sipadzakhala malo okwanira kuwulandira.

11 Ndipo ndidzadzudzula zowononga chifukwa cha inu, ndipo iye sadzawononga zipatso za nthaka yanu; ngakhale mpesa wanu sudzataya zipatso zake nthawi isadakwane m’minda, atero Ambuye wa makamu.

12 Ndipo maiko onse adzakutchulani odala, pakuti mudzakhala dziko lokondweretsa, atero Ambuye wa makamu.

13 Mau anu akhala aukali motsutsa ine, atero Ambuye. Koma inu mukuti, Tanena chiyani chotsutsa inu?

14 Inu mwati: Kutumikira Mulungu n’kopanda pake, ndipo kupindula chiyani kuti tisunge miyambo yake ndiponso kuti tiyende mwachisoni pamaso pa Ambuye wa makamu?

15 Ndipo tsopano timatchula odzikuza osangalala; inde, iwo akuchita zoipa akhazikitsidwa; inde iwo amene amayesa Mulungu ngakhale apulumutsidwa.

16 Pamenepo iwo akuopa Ambuye adayankhulana kawirikawiri wina ndi mnzake, ndipo Ambuye adamvetsera ndipo adamva; ndi buku la chikumbutso lidalembedwa pamaso pake kwa iwo akuopa Ambuye, ndi amene amakumbukira pa dzina lake.

17 Ndipo iwo adzakhala anga, atero Ambuye wa makamu, m’tsiku limenelo pamene ndidzapanga miyala yanga yamtengo wapatali; ndipo ndidzawapulumutsa iwo monga mmene munthu amapulumutsira mwana wake amene amam’tumikira iye.

18 Pamenepo mudzabwelera ndi kuzindikira pakati pa wolungama ndi woipa, pakati pa iye amene amatumikira Mulungu ndi iye amene samamtumikira iye.

Print