Malembo Oyera
3 Nefi 3


Mutu 3

Gidiyani, mtsogoleri wa Gadiyantoni, alamula kuti Lakoniyasi ndi Anefi adzipereke okha ndi maiko awo—Lakoniyasi asankha Gigidoni monga wamkulu wa ankhondo wa magulu ankhondo—Anefi asonkhana mu Zarahemula ndi Chuluka kuti adziteteze. Mdzaka dza pafupifupi Yesu atabadwa 16–18.

1 Ndipo tsopano zidachitika kuti m’chaka chakhumi ndi chisanu ndi chimodzi kuchokera kubwera kwa Khristu, Lakoniyasi, bwanamkubwa wa dziko, adalandira kalata kuchokera kwa mtsogoleri ndi bwanamkubwa wa gulu la achifwambalo; ndipo awa ndiwo mawu adalembedwa, nati:

2 Lakoniyasi, wolemekezeka ndi bwanamkubwa wamkulu wa dziko, taona, ndakulembera kalata iyi, ndipo ndikukupatsa iwe matamando aakulu chifukwa cha kulimba kwako, komanso kulimba kwa anthu ako, posunga zomwe ukuganiza kuti ndi mwayi ndi ufulu wanu; inde, mukuima bwino, monga ngati mukuthandizidwa ndi dzanja la mulungu, m’chitetezo cha ufulu wanu, ndi chuma chanu, ndi dziko lanu, kapena icho chimene mukuchitcha motero.

3 Ndipo zikuoneka zachisoni kwa ine, Lakoniyasi wolemekezeka, kuti ukakhale opusa ndi opanda pake monga mukuganizira kuti mungaimilire motsutsana ndi amuna olimba mtima ochuluka motere amene ali pa lamulo langa, amene tsopano pa nthawi ino aima m’zida zawo, ndipo akuyembekezera ndi nkhawa yaikukulu kwa mawu—Pitani kwa Anefi ndi kukawawononga.

4 Ndipo ine, podziwa za mzimu wawo wosagonjetseka, nditawatsimikizira iwo m’bwalo la nkhondo, ndipo podziwa za udani wawo wosatha pa inu chifukwa cha zoipa zambiri zimene mudawachitira iwo, kotero ngati iwo angatsikire kwa inu adzakuyenderani inu ndi chiwonongeko chotheratu.

5 Kotero ndalemba kalata iyi, ndikutsindikiza ndi dzanja langa, ndikumvelera ubwino wanu, chifukwa cha kulimba kwanu m’chimene mumakhulupilira kuti chiri cholondola, ndi mzimu wanu wolemekezeka m’bwalo la nkhondo.

6 Kotero ndakulemberani, ndikukhumba kuti mupereke kwa anthu anga awa, mizinda yanu, maiko anu, ndi chuma chanu, m’malo mokuti akuyendereni ndi lupanga ndi kuti chiwonongeko chidzakugwereni.

7 Kapena m’mawu ena, mudzipereke kwa ife, ndipo gwirizanani nafe ndi kukhala odziwa ntchito zathu zachinsinsi, ndipo khalani abale athu kuti mukhale ngati ife—osati akapolo athu, koma abale athu ndi ogwirizana nawo pa chuma chathu chonse.

8 Ndipo taonani, ndikulumbira kwa inu, ngati mukachita ichi, ndi lumbiro, simudzawonongeka; koma mukapanda kutero, ndikukulumbilirani ndi lumbiro, kuti m’mawa wa mwezi wa mawa ndidzalamulira magulu anga ankhondo akubwelereni, ndipo sadzatsekereza dzanja lawo, ndipo sadzakusiyani, koma adzakuphani; ndipo lupanga lidzakugwerani kufikira mpakana mudzatheratu.

9 Ndipo taona, ndi ine Gidiyani; ndipo ine ndine bwanamkubwa wa gulu lachinsinsi la Gadiyantoni; gulu lomwe ndi ntchito zake zomwe ndikuzidziwa kuti ndi zabwino; ndipo zidalembedwa kalekale ndipo zidapatsidwa kwa ife.

10 Ndipo ndikulemba kalatayi kwa iwe, Lakoniyasi, ndipo ndikuyembekeza kuti udzapereka maiko ako ndi chuma chako, popanda kukhetsa mwazi, kuti anthu anga awa alandirenso maufulu awo ndi boma, omwe adapatukana ndi iwe chifukwa cha zoipa zako powatsekerezera maufulu awo aulamuliro, ndipo pokhapokha mutachita izi, ndiwabwenzera zoipa zawo. Ndine Gidiyani.

11 Ndipo tsopano zidachitika pamene Lakoniya adalandira kalata iyi adadabwa kwambiri, chifukwa cha kulimba mtima kwa Gidiyani pofuna kulanda dziko la Anefi, ndiponso kuwopseza anthu ndi kubwenzera zolakwa za iwo amene sadalandire cholakwa chirichonse, kupatula kuti iwo adadzilakwira iwo okha pa kukadzilowetsa kwa achifwamba oipa ndi onyansa.

12 Tsopano taonani, uyu Lakoneyasi, bwanankubwa, adali munthu olungama, ndipo sadachite mantha ndi zofunazo komanso ziwopsezo za wachifwamba; kotero sadamvetsere kalata ya Gidiyani, bwanankubwa wa achifwamba; koma adapangitsa kuti anthu ake alilire kwa Ambuye kuti apeze mphamvu yozikonzekeretsera pa nthawi imene achifwamba adzabwera kudzamenyana nawo.

13 Inde, adatumiza chilengezo pakati pa anthu onse, kuti asonkhanitse pamodzi akazi awo, ndi ana awo, nkhosa zawo ndi ng’ombe zawo, ndi chuma chawo chonse, kupatula nthaka lawo, kumalo amodzi.

14 Ndipo iye adapangitsa kuti mipanda yolimba imangidwe mozungulira iwo, ndipo mphamvu yake ikhale yaikulu kwambiri. Ndipo iye adapangitsa kuti magulu ankhondo, onse a Anefi ndi a Alamani, kapena a onse amene adawerengedwa pakati pa Anefi, adayenera kuikidwa ngati alonda mozungulira kuti ayang’anire iwo, ndi kuwalondera iwo kwa achifwambawo usana ndi usiku.

15 Inde, adati kwa iwo, monga Ambuye ali wamoyo, pokhapokha ngati mutalape mphulupulu zanu zonse, ndi kulilira kwa Ambuye, inu simudzawomboledwa mwanjira ina iliyonse kuchoka m’manja mwa achifwamba a Gadiantoniwo.

16 Ndipo mawu ndi mauneneri a Lakoniya adali aakulu ndi odabwitsa kwambiri kuti iwo adachititsa mantha kudza pa anthu onse; ndipo adalimbika mu mphamvu zawo kuchita monga mwa mawu a Lakoneyasi.

17 Ndipo zidachitika kuti Lakoniyasi adasankha akulu a nkhondo pamwamba pa ankhondo onse a Anefi, kuti adziwalamulira iwo pa nthawi yomwe achifwamba adzabwera kuchokera ku chipululu kudzamenyana nawo.

18 Tsopano wamkulu pakati pa akulu ankhondo onse ndi wamkulu wa ankhondo onse wa Anefi adasankhidwa, ndipo dzina lake adali Gidigidoni.

19 Tsopano udali mwambo pakati pa Anefi onse kuti posankha akulu a nkhondo, (kupatula mu nthawi za kuipa kwawo) asankhe munthu amene adali ndi mzimu wa vumbulutso komanso uneneri; kotero, uyu Gidigidoni adali mneneri wamkulu pakati pawo, monganso adali oweruza wamkulu.

20 Tsopano anthu adati kwa Gidigidoni: Pempherani kwa Ambuye, ndipo tiyeni tikwere pamwamba pa mapiri ndi m’chipululu, kuti tingakagwere pa achifwamba ndi kuwawononga m’mayiko awo.

21 Koma Gidigidoni adanena nawo: Ambuye akuletsa; pakuti ngati tingapite kokamenyana nawo Ambuye akatipereka m’manja mwawo; kotero tidzakonzekera pakati pa maiko athu, ndipo tidzasonkhanitsa ankhondo athu onse, ndipo sitidzapita kukamenyana nawo, koma tidzadikira mpaka adzabwere kudzamenyana nafe; kotero monga Ambuye ali wamoyo, tikachita ichi adzawapereka iwo m’manja mwathu.

22 Ndipo zidachitika m’chaka chakhumi ndi chisanu ndi chiwiri, kumapeto kwa chaka, chilengezo cha Lakoniya chidamveka pa nkhope yonse ya dziko, ndipo iwo adatenga akavalo awo, ndi magareta awo, ndi ng’ombe zawo, ndi nkhosa zawo zonse, ndi ziweto zawo, ndi chimanga chawo, ndi chuma chawo chonse, ndipo adaguba m’zikwi ndi makumi a zikwi, kufikira onse atapita ku malo amene adaikidwiratu kuti asonkhane pamodzi, kuti adziteteze okha motsutsa adani awo.

23 Ndipo dziko limene lidaikidwa lidali dziko la Zarahemula, ndipo dziko limene lidali pakati pa dziko la Zarahemula ndi dziko la Chuluka, inde, mpaka ku mzere umene udali pakati pa dziko la Chuluka ndi dziko la Bwinja.

24 Ndipo padali anthu zikwi zambiri zochuluka amene ankatchedwa Anefi, amene adadzisonkhanitsa iwo okha m’dzikoli. Tsopano Lakoniyasi adapangitsa kuti iwo adzisonkhanitse pamodzi m’dziko lakummwera, chifukwa cha thembelero lalikulu limene lidali pa dziko la kumpoto.

25 Ndipo iwo adadzilimbitsa okha motsutsana ndi adani awo; ndipo adakhala pamalo amodzi, ndi gulu limodzi, ndipo iwo adaopa mawu amene adayankhulidwa ndi Lakoniyasi, kotero kuti adalapa machimo awo onse; ndipo iwo adaika mapemphero awo kwa Ambuye Mulungu wawo, kuti adzawawombole pa nthawi imene adani awo adzabwera kudzamenyana nawo kunkhondo.

26 Ndipo adali ndi chisoni chachikulu chifukwa cha adani awo. Ndipo Gidigidoni adachititsa kuti apange zida zankhondo zamtundu uliwonse, ndipo iwo akhale amphamvu za zida, ndi zishango, ndi zishango zam’mikono, monga mwa mwambo wa malangizo ake.