Malembo Oyera
3 Nefi 8


Mutu 8

Namondwe, zivomelezi, moto, akamvuluvulu, ndi kugwedezeka kwachilengedwe zichitira umboni kupachikidwa kwa Khristu—Anthu ambiri awonongeka—Mdima ukuta dzikolo kwa masiku atatu—Amene iwo otsala alira za tsogolo lawo. Mdzaka dza pafupifupi Yesu atabadwa 33–34.

1 Ndipo tsopano zidachitika kuti molingana ndi zolemba zathu, ndipo tikudziwa zolemba zathu kukhala zoona, pakuti taonani, adali munthu wolungama amene adasunga zolembazi—pakuti iye adachitadi zozizwitsa zambiri mu dzina la Yesu; ndipo padalibe munthu aliyense amene akadatha kuchita chozizwitsa m’dzina la Yesu kupatula kuti iye adayeretsedwa kachigawo kalikonse ku mphulupulu zake—

2 Ndipo tsopano zidachitika, ngati padalibe kulakwitsa kudapangidwa ndi munthu uyu powerengera nthawi yathu, chaka cha makumi atatu ndi zitatu chidali chitatha.

3 Ndipo anthu adayamba kuyang’anira chizindikirocho mwa chidwi chachikulu chomwe chidaperekedwa ndi mneneri Samueli, wa Chilamani, inde, ku nthawi imene padzakhale mdima pa dziko lapansi masiku atatu.

4 Ndipo kudayamba kukhala kukaikira kwakukulu ndi mikangano pakati pa anthu, posatengera zizindikiro zambiri zidali zitaperekedwa.

5 Ndipo zidachitika mu chaka cha makumi atatu ndi mphambu zinayi, m’mwezi woyamba, tsiku lachinayi la mweziwo, padauka namondwe wachimphepo, chimene sichidadziwikepo konse m’dziko lonselo.

6 Ndipo padalinso namondwe wamkulu ndi oopsa; ndipo padali chibingu choopsya, kotero kuti chidagwedeza dziko lonse lapansi ngati kuti lidali pafupi kugawikana pakati.

7 Ndipo kudali mphenzi zazikulu, zomwe sizidadziwikepo konse m’dziko lonselo.

8 Ndipo mzinda wa Zarahemula udayaka moto.

9 Ndipo mzinda wa Moroni udamira m’kuya kwa nyanja, ndipo okhalamo adamizidwa.

10 Ndipo nthaka idanyamulidwa m’mwamba pa mzinda wa Moroniha, kuti m’malo mwa mzindawo mudakhala phiri lalikulu.

11 Ndipo padali chiwonongeko chachikulu ndi choopsya m’dziko la kummwera.

12 Koma taonani, kudali chiwonongeko chachikulu kwambiri ndi choopsya m’dziko la kumpoto; pakuti taonani, nkhope yonse ya dziko idasintha, chifukwa cha namondwe ndi akamvuluvulu, ndi mabingu ndi mphenzi, ndi kugwedezeka kwakukulu kwambiri kwa dziko lonse lapansi;

13 Ndipo misewu ikuluikulu idaduka, ndipo misewu yosalala idawonongeka, ndi malo ambiri osalazika adakhala okumbika.

14 Ndipo mizinda yambiri ikuluikulu ndi yodziwika idamira, ndipo yambiri idatenthedwa, ndipo yambiri idagwedezeka mpaka zomanga zake zidagwa pansi, ndipo okhalamo adaphedwa, ndipo malo adasiyidwa pululu.

15 Ndipo padali mizinda ina imene idatsala; koma kuwonongeka kwake kudali kwakukulu kwambiri, ndipo adali ambiri mwa iwo amene adaphedwa.

16 Ndipo padali ena amene adanyamulidwira kutali ndi kamvuluvulu; ndipo kumene iwo adapita palibe munthu akudziwa, kupatula iwo akudziwa kuti iwo adanyamulidwa.

17 Ndipo kotero nkhope ya dziko lonse lapansi idasintha maonekedwe, chifukwa cha namondwe, ndi mabingu, ndi mphenzi, ndi chivowerezi cha dziko.

18 Ndipo taonani, miyala idang’ambika pakati; idasweka pa nkhope ya dziko lonse lapansi, kotero kuti iyo idapezeka m’zidutswa zosweka, ndi m’misoko, ndi m’ming’alu, pa nkhope yonse ya dziko.

19 Ndipo zidachitika kuti pamene mabingu, ndi mphenzi, ndi mphepo ya mkuntho, ndi namondwe, ndi kugwedezeka kwa dziko kudatha—pakuti taonani zidatenga pafupifupi nthawi ya maola atatu; ndipo kudanenedwa ndi ena kuti nthawi idali yokulirapo; komabe, zinthu zonse zazikulu ndi zoopsa izi zidachitidwa pafupifupi nthawi ya maola atatu, ndipo taonani, padali mdima pa nkhope ya dziko.

20 Ndipo zidachitika kuti padali mdima wandiweyani pa nkhope yonse ya dziko, kotero kuti okhalamo amene sadagwe adamva nthunzi wa mdima;

21 Ndipo sikukadatheka kukhala kuwala kulikonse, chifukwa cha mdima, ngakhalenso nyali, kapena miuni; ngakhalenso sipadathe kuyaka moto ndi nkhuni zawo zabwino ndi zouma ndithu, kotero kuti padalibe kuwala kulikonse;

22 Ndipo padalibe kuwala kulikonse kudaoneka, ngakhale moto, kapena kunyezimira, ngakhale dzuwa, kapena mwezi, kapena nyenyezi, pakuti mdima wandiweyani udali waukulu kwambiri umene udali pa nkhope ya dzikolo.

23 Ndipo zidachitika kuti kudakhala nthawi ya masiku atatu komwe kuwala sikudaoneke; ndipo padali maliro aakulu, ndi kukuwa, ndi kulira kosalekeza pakati pa anthu onse; inde, kwakukulu kudali kubuula kwa anthu, chifukwa cha mdima ndi chiwonongeko chachikulu chimene chidadza pa iwo.

24 Ndipo m’malo amodzi adamvedwa kulira, kuti: O kuti tikadalapa lisadafike tsiku lalikulu ndi loopsya ili, ndipo pamenepo abale athu akadasiyidwa, ndipo sakadatenthedwa mu mzinda waukulu uja Zarahemula.

25 Ndipo m’malo ena adamveka kulira ndi kudandaula, kuti: O kuti ife tikadalapa lisadafike tsiku lalikulu ndi loopsya ili, ndipo tisadaphe ndi kuponya miyala aneneri, ndi kuwatulutsa iwo; pamenepo amayi athu ndi ana aakazi okongola athu, ndi ana athu akadasiyidwa, ndipo sakadakwiliridwa mu mzinda waukulu uja Moroniha. Ndipo motero kukuwa kwa anthu kudali kwakukulu ndi koopsa.