Malembo Oyera
3 Nefi 16


Mutu 16

Yesu adzayendera ena a nkhosa zotayika za Israeli—M’masiku otsiriza uthenga wabwino udzapita kwa Amitundu ndipo kenako ku nyumba ya Israeli—Anthu a Ambuye adzaona maso ndi maso pamene Iye adzabweretsanso Ziyoni. Mdzaka dza pafupifupi Yesu atabadwa 34.

1 Ndipo indetu, indetu, ine ndikunena kwa inu kuti ndili nazo nkhosa zina, zimene siziri za dziko lino, kapena za dziko la Yerusalemu, kapena m’madera aliwonse a dziko ilo mozungulira kumene ine ndakhala ndikutumikira.

2 Pakuti iwo amene ndikunena za iwo amene sadamve mawu anga; kapena sindidadzionetsere ndekha kwa iwo.

3 Koma ine ndalandira lamulo la Atate kuti ndidzapita kwa iwo, ndipo kuti iwo adzamva mawu anga, ndipo adzawerengedwa pakati pa nkhosa zanga, kuti pakhale khola limodzi ndi m’busa m’modzi; kotero ndipita kukadzionetsa ndekha kwa iwo.

4 Ndipo ndikukulamulirani kuti mulembe mawu awa nditachoka ine, kuti ngati anthu anga ali ku Yerusalemu, amene adandiona ine, ndi kukhala ndi ine mu utumiki wanga, sapempha Atate m’dzina langa, kuti alandire chidziwitso cha inu mwa Mzimu Woyera, ndiponso cha mafuko ena amene samawadziwa, kuti mawu awa amene mudzawalemba adzasungidwa ndipo adzaonetseredwa kwa amitundu, kuti mwa chidzalo cha amitundu, otsalira a mbewu yawo, amene adzabalalitsidwa pa nkhope ya dziko lapansi chifukwa cha kusakhulupilira kwawo, akhonza kubweretsedwa, kapena akhonza kubweretsedwa ku chidziwitso cha ine, Muwomboli wawo.

5 Ndipo pamenepo ine ndidzawasonkhanitsa iwo kuchokera ku zigawo zinayi za dziko lapansi; ndipo pamenepo ndidzakwaniritsa chipangano chomwe Atate apanga kwa anthu onse a nyumba ya Israeli.

6 Ndipo wodala ali Amitundu, chifukwa cha chikhulupiliro chawo mwa ine, ndi mwa Mzimu Woyera, amene amachitira umboni kwa iwo za ine ndi Atate.

7 Taonani, chifukwa cha chikhulupiliro chawo mwa ine, akutero Atate, ndi chifukwa cha kusakhulupilira kwanu, O nyumba ya Israeli, m’tsiku lotsiriza choonadi chidzafika kwa Amitundu, kuti chidzalo cha zinthu izi chidzadziwika kwa iwo.

8 Koma tsoka, atero Atate, kwa osakhulupilira a Amitundu—pakuti pakusatengera iwo abwera pankhope ya dziko lino, ndipo abalalitsa anthu anga omwe ali a nyumba ya Israeli; ndipo anthu anga amene ali a nyumba ya Israeli adathamangitsidwa pakati pawo, ndi kuponderezedwa pansi pamapazi ndi iwo;

9 Ndipo chifukwa cha zifundo za Atate kwa Amitundu, ndiponso ziweruzo za Atate pa anthu anga amene ali a nyumba ya Israeli, indetu, indetu, ine ndikunena kwa inu, kuti pambuyo pa zonsezi, ndipo ine ndachititsa anthu anga amene ali a nyumba ya Israeli kumenyedwa, ndi kusautsidwa, ndi kuphedwa, ndi kuthamangitsidwa pakati pawo, ndi kukhala odedwa ndi iwo, ndi kukhala chitsogozo ndi mphekesera pakati pawo;

10 Ndipo motero adalamulira Atate kuti ndinene kwa inu: Pa tsiku limenelo pamene Amitundu adzachimwira uthenga wanga, ndipo adzakana chidzalo cha uthenga wanga, ndipo adzadzikuza m’kunyada kwa mitima yawo pamwamba pa maiko onse, ndi pamwamba pa anthu onse a dziko lapansi, ndipo adzadzazidwa ndi mitundu yonse ya mabodza, ndi chinyengo, ndi kufuntha, ndi mitundu yonse ya chinyengo, ndi kupha, ndi zaunsembe zachinyengo, ndi zadama, ndi zonyansa zobisika; ndipo ngati iwo adzachita zinthu zonsezo, ndipo adzakana chidzalo cha uthenga wanga wabwino, taonani, akutero Atate, ndidzapangitsa chidzalo cha uthenga wanga kuchoka pakati pawo.

11 Ndipo kenako ndidzakumbukira pangano langa limene ndapanga kwa anthu anga, O nyumba ya Israeli, ndipo ndidzabweretsa uthenga wanga wabwino kwa iwo.

12 Ndipo ndidzaonetsa kwa inu, O nyumba ya Israeli, kuti Amitundu sadzakhala ndi mphamvu pa inu; koma ndidzakumbukira chipangano changa kwa inu, O nyumba ya Israeli, ndipo inu mudzafika ku chidziwitso cha chidzalo cha uthenga wanga wabwino.

13 Koma ngati Amitundu adzalapa ndi kubwelera kwa ine, akutero Atate, taonani iwo adzawerengedwa pakati pa anthu anga, O nyumba ya Israeli.

14 Ndipo sindidzalora anthu anga, amene ali a nyumba ya Israeli, kudutsa pakati pawo, ndi kuwapondaponda, akutero Atate.

15 Koma ngati iwo satembenukira kwa ine, ndi kumvetsera mawu anga, ndidzawalora iwo, inde, ndidzalora anthu anga, O nyumba ya Israeli, kuti iwo adzadutse pakati pawo, ndipo adzawapondereza iwo pansi, ndipo adzakhala ngati mchere wotayika kukoma kwake, umene kuyambira pamenepo suli wothandiza kanthu koma kuponyedwa kunja, ndi kuponderezedwa kuphazi kwa anthu anga, O nyumba ya Israeli.

16 Indetu, indetu, ndinena kwa inu, motero Atate andilamulira ine—kuti ndipereke kwa anthu awa dziko lino ngati cholowa chawo.

17 Ndipo Kenako mawu a mneneri Yesaya adzakwaniritsidwa, amene akuti:

18 Alonda ako adzakweza mawu; ndi mawuwo pamodzi adzayimba, pakuti adzaonana maso ndi maso pamene Ambuye adzabweretsanso Ziyoni.

19 Sangalalani, imbani pamodzi, inu mabwinja a Yerusalemu; pakuti Ambuye watonthoza anthu ake, iye wawombola Yerusalemu.

20 Ambuye watambasula dzanja lake loyera pamaso pa amitundu onse; ndipo malekezero onse a dziko lapansi adzaona chipulumutso cha Mulungu.

Print