Malembo Oyera
3 Nefi 25


Mutu 25

Pa Kubwera Kwachiwiri, odzikuza ndi oipa adzawotchedwa ngati ziputu—Eliya adzabwelera lisadafike tsiku lalikulu ndi lowopsya ilo—Fananitsani ndi Malaki 4. Mdzaka za pafupifupi Yesu atabadwa 34.

1 Pakuti taonani, likudza tsiku limene lidzayaka ngati ng’anjo; ndipo onse odzikuza, inde, ndi onse ochita zoipa, adzakhala ngati chiputu; ndipo tsiku lomwe likudza lidzawatentha, atero Ambuye wa makamu, kuti silidzawasiyira muzu kapena nthambi.

2 Koma kwa inu amene mumawopa dzina langa, Mwana wa Chilungamo adzauka ndi machiritso m’mapiko ake; ndipo mudzapita ndi kukula ngati ana a ng’ombe m’khola.

3 Ndipo inu mudzapondereza oipa; pakuti adzakhala phulusa pansi pa zidendene za mapazi anu mu tsiku limene ine ndidzachita izi, akutero Ambuye wa makamu.

4 Kumbukilani inu chilamulo cha Mose mtumiki wanga, chimene ndidamulamura mu Horebu, cha kwa Aisraeli onse, ndi malamulo olembedwa ndi ziweruzo.

5 Taonani, ndidzakutumizirani Eliya mneneri, lisadadze tsiku lalikulu ndi loopsa la Ambuye;

6 Ndipo adzatembenuza mitima ya atate kwa ana, ndi mitima ya ana kwa atate awo, kuopa kuti ndingadze ndi kukantha dziko lapansi ndi thembelero.

Print