Malembo Oyera
3 Nefi 6


Mutu 6

Anefi achita bwino—Kunyada, chuma, ndi kusiyana kwa magulu kuyamba—Mpingo ugawikana ndi kusagwirizana—Satana atsogolera anthu m’kuukira poyerayera—Aneneri ambiri afuula kulapa ndipo aphedwa—Akupha awo apangana kuti atenge boma. Mdzaka dza pafupifupi Yesu atabadwa 26–30.

1 Ndipo tsopano zidachitika kuti anthu a Anefi onse adabwelera ku mayiko awo m’chaka cha makumi awiri mphambu zisanu ndi chimodzi, aliyense ndi banja lake, nkhosa zake ndi ziweto zake, akavalo ake ndi ng’ombe zake, ndi zonse adali nazo.

2 Ndipo zidachitika kuti sadadye zakudya zawo zonse; kotero adatenga zonsezo zimene iwo sadaziwononge, mbewu zawo zonse zamtundu uliwonse, golidi wawo, siliva wawo, ndi zinthu zawo zonse zamtengo wapatali, ndipo adabwelera ku maiko awo ndi katundu wawo, konse kumpoto ndi kumwera, konse ku dziko la chakumpoto ndi ku dziko la chakumwera.

3 Ndipo adawapatsa achifwamba awo amene adalowa m’pangano kusunga mtendere wa m’dziko, amene adali kufuna kukhalabe Alamani, malo, molingana ndi chiwerengero chawo, kuti akakhale nawo, ndi ntchito zawo, zimene angakhale nazo; ndipo motero iwo adakhazikitsa mtendere m’dziko lonselo.

4 Ndipo adayambanso kuchita bwino ndi kukula kwakukulu; ndipo dzaka makumi awiri ndi zisanu ndi chimodzi ndi zisanu ndi ziwiri zidatha, ndipo mudali dongosolo lalikulu m’dzikomo; ndipo iwo adali atapanga malamulo awo molingana ndi kupanda tsankho ndi chilungamo.

5 Ndipo tsopano kudalibe chinthu m’dziko lonse kuti chiletse anthu kuchita bwino kosalekeza, pokhapokha atagwa mu kulakwitsa.

6 Ndipo tsopano adali Gidigidoni, ndi oweruza, Lakoniyasi, ndi iwo amene adasankhidwa atsogoleri, amene adakhazikitsa mtendere waukulu uwu m’dzikolo.

7 Ndipo zidachitika kuti padali mizinda yambiri yomangidwa mwatsopano, ndipo padali mizinda yakale yambiri idakonzedwa.

8 Ndipo padali misewu yaikulu yambiri yomangidwa, ndipo misewu yambiri idapangidwa, yomwe inkayenda kuchokera ku mzinda ndi mzinda, ndi kuchokera ku dziko ndi dziko, ndi kuchokera ku malo ndi malo.

9 Ndipo kotero chidatha chaka cha makumi awiri ndi zisanu ndi zitatu, ndipo anthu adali ndi mtendere kosalekeza.

10 Koma zidachitika m’chaka cha makumi awiri mphambu zisanu ndi zinayi kudayamba mikangano pakati pa anthu; ndipo ena adali kukwezedwa mu kunyada ndi kudzitukumula chifukwa cha chuma chawo chochuluka, inde, ngakhale ku mazunzo aakulu;

11 Pakuti padali amalonda ambiri m’dzikomo, ndi azamalamulo ambiri, ndi adindo ambiri.

12 Ndipo anthu adayamba kukhala osiyanitsidwa mwa magulu, monga mwa chuma chawo ndi mwayi wawo wophunzira; inde, ena adali mbuli chifukwa za umphawi wawo, ndipo ena adalandira maphunziro ochuluka chifukwa cha chuma chawo.

13 Ena adali odzikuza m’kunyada, ndipo ena adali odzichepetsa kwambiri; ena adabwenza chitonzo chifukwa cha chipongwe, pamene ena adalandira chitonzo ndi mazunzo ndi mitundu yonse ya masautso, ndipo sadatembenuke ndi kunyoza kachiwiri, koma adali odzichepetsa ndi olapa pamaso pa Mulungu.

14 Ndipo motero kudakhala kusiyana kwakukulu m’dziko lonselo, kotero kuti mpingo udayamba kugawikana; inde, kotero kuti mu chaka cha makumi atatu mpingo udagawikana m’dziko lonse kupatulapo pakati pa owerengeka a Alamani amene adatembenukira ku chikhulupiliro choonadi; ndipo iwo sadapatuke ku chimenecho, pakuti iwo adali olimba, ndi okhazikika, ndi osasunthika, ofunitsitsa ndi khama lonse kusunga malamulo a Ambuye.

15 Tsopano choyambitsa kusaweruzika kwa anthu chidali ichi—Satana adali ndi mphamvu yaikulu ya kuwutsa anthu kuti achite zoipa za mtundu uliwonse, ndi kuwatukumula iwo ndi kunyada, kuwayesa iwo kuti afunefune mphamvu, ndi ulamuliro, ndi chuma, ndi zinthu zopanda pake za dziko lapansi.

16 Ndipo motere Satana adatsogolera mitima ya anthu kuchita zoipa zamtundu uliwonse; kotero adali atasangalala ndi mtendere koma mu dzaka zochepa chabe.

17 Ndipo motero, kumayambiliro kwa chaka cha makumi atatu—anthu ataperekedwa kwa nthawi yaitali kuti atengeke ndi mayesero a mdyerekezi kulikonse kumene iye adafuna kuwatengera iwo, ndi kuchita mphulupulu zirizonse zimene iye adafuna kuti iwo achite—Ndipo motero kumayambiliro kwa ichi, chaka cha makumi atatu, iwo adali mu mkhalidwe wa kuipa koopsya.

18 Tsopano iwo sadachimwe mosadziwa, pakuti ankadziwa chifuniro cha Mulungu chokhudza iwo, pakuti chidali chitaphunzitsidwa kwa iwo; kotero iwo adapandukira Mulungu mwadala.

19 Ndipo tsopano adali m’masiku a Lakoniyasi, mwana wa Lakoniyasi, pakuti Lakoniyasi adakhala pa mpando wa atate ake ndipo adalamulira anthu chaka chimenecho.

20 Ndipo kudayamba kukhala anthu odziwitsidwa kuchokera kumwamba ndipo adatumizidwa, kuimilira pakati pa anthu m’dziko lonselo, kulalikira ndi kuchitira umboni molimba mtima za machimo ndi mphulupulu za anthu, ndi kuchitira umboni kwa iwo zokhudzana ndi chiwombolo chimene Ambuye apange kwa anthu ake, kapena m’mawu ena, chiukitso cha Khristu; ndipo adachitira umboni molimba mtima za imfa ndi mazunzo ake.

21 Tsopano padali ambiri a anthu amene adali okwiya kwambiri chifukwa cha iwo amene adachitira umboni za zinthu izi; ndipo iwo amene adakwiya adali makamaka akulu a oweruza, ndi iwo amene adali akulu ansembe ndi azamalamulo; inde, onse amene adali azamalamulo adakwiya nawo amene adachitira umboni za izi.

22 Tsopano padalibe wazamalamulo, kapena oweruza, kapena mkulu wa ansembe amene akadatha kukhala ndi mphamvu zoweruza munthu aliyense kuti aphedwe pokhapokha kuti kutsutsidwa kwawo kudali kosainidwa ndi bwanamkubwa wa dzikolo.

23 Tsopano padali ambiri a iwo amene adachitira umboni za zinthu zokhudza Khristu amene adachitira umboni molimba mtima, amene adatengedwa ndi kuphedwa mwachinsinsi ndi oweruza, kuti chidziwitso cha imfa yawo chisafike kwa bwanamkubwa wa dziko kufikira itachitika imfa yawo.

24 Tsopano taonani, ichi chidali chotsutsana ndi malamulo a dziko, kuti munthu aliyense akaphedwe pokhapokha atakhala ndi mphamvu kuchokera kwa bwanamkubwa wa dziko—

25 Kotero dandaulo lidafika ku dziko la Zarahemula, kwa bwanamkubwa wa dziko, motsutsa oweruza awa amene adatsutsa aneneri a Ambuye kuti aphedwe, mosalingana ndi malamulo.

26 Tsopano zidachitika kuti iwo adatengedwa ndi kubweretsedwa pamaso pa oweruza, kuti aweruzidwe pa mlandu umene iwo adachita, molingana ndi lamulo limene lidaperekedwa ndi anthu.

27 Tsopano zidachitika kuti oweruza amenewo adali ndi abwenzi ambiri ndi achibale; ndipo otsalawo, inde, ngakhale pafupifupi azamalamulo onse ndi akulu ansembe, adasonkhana pamodzi, ndipo adagwirizana ndi achibale a oweruza amenewo amene adayenera kuzengedwa mulandu molingana ndi lamulo.

28 Ndipo adalowa mu pangano wina ndi mzake, inde, ngakhale mu pangano limenelo lomwe lidaperekedwa ndi iwo akale, pangano lomwe lidaperekedwa ndi kutumikiridwa ndi mdyerekezi, kukaphatikizana motsutsana ndi chilungamo chonse.

29 Kotero iwo adasonkhanitsana motsutsana ndi anthu a Ambuye, ndi kulowa m’pangano kuti awononge iwo, ndi kuwombola iwo amene adali olakwa pakupha kuchoka muchilungamo, chimene chidali pafupi kuchitidwa monga mwa lamulo.

30 Ndipo iwo adanyoza lamulo ndi maufulu a dziko lawo; ndipo adapangana pangano wina ndi mzake kuti awononge bwanankubwa, ndi kukhazikitsa mfumu m’dzikolo, kuti dzikolo lisakhalenso laufulu, koma likhale lomvera mafumu.