Malembo Oyera
3 Nefi 1


Nefi Wachitatu

Buku la Nefi
Mwana wa Nefi, amene adali Mwana wa Helamani

Ndipo Helamani adali mwana wa Helamani, amene adali mwana wa Alima, amene adali mwana wa Alima, wokhala chidzukulu cha Nefi amene adali mwana wa Lehi, amene adatuluka mu Yerusalemu m’chaka choyamba cha ulamuliro wa Zedekiya, mfumu ya Yuda.

Mutu 1

Nefi, mwana wa Helamani, atuluka mu mzindawo, ndipo mwana wake Nefi asunga zolemba—Ngakhale zizindikiro ndi zodabwitsa zidalipo zochuluka, oipa apanga dongosolo lokupha olungama—Usiku wa kubadwa kwa Khristu ufika—Chizindikiro chiperekedwa, ndipo nyenyezi yatsopano ituluka—Mabodza ndi chinyengo zichuluka, ndipo achifwamba a Gadiyantoni apha ambiri. Mdzaka dza pafupifupi Yesu atabadwa 1–4.

1 Tsopano zidachitika kuti mu chaka cha makumi asanu ndi anayi mphambu imodzi chidali chitapita ndipo zidali dzaka mazana asanu ndi limodzi kuchokera pamene Lehi adachoka ku Yerusalemu; ndipo mudali m’chaka chimene Lakoniyo adali oweruza wamkulu ndi bwanamkubwa wa dzikolo.

2 Ndipo Nefi, mwana wa Helamani, adali atachoka m’dziko la Zarahemula, atapereka udindo kwa mwana wake Nefi, amene adali mwana wake wamkulu, zokhudzana ndi mapale a mkuwa, ndi zolemba zonse zimene zidasungidwa, ndi zinthu zonse zimene zidasungidwa zopatulika kuchokera pa kuchoka kwa Lehi kutuluka ku Yerusalemu.

3 Kenako iye adatuluka m’dzikomo, ndipo kumene adapitako, palibe munthu akudziwa; ndipo mwana wake Nefi adasunga zolemba m’malo mwake, inde, zolemba za anthu awa.

4 Ndipo zidachitika kuti chakumayambiliro kwa chaka cha makumi asanu ndi anayi mphambu ziwiri, taonani, mauneneri a aneneri adayamba kukwaniritsidwa mokwanira; pakuti kudayamba kukhala zizindikiro zazikulu ndi zozizwitsa zazikulu kuchitidwa mwa anthu.

5 Koma kudali ena amene adayamba kunena kuti nthawi idali itapita kuti mawu akwaniritsidwe, amene adayankhulidwa ndi Samueli, wa Chilamani.

6 Ndipo iwo adayamba kukondwera pa abale awo, nati, Taonani, nthawi yapita, ndipo mawu a Samueli sadakwaniritsidwe; kotero, chisangalalo chanu ndi chikhulupiliro chanu chokhudza chinthu ichi chakhala chachabechabe.

7 Ndipo zidachitika kuti adapanga chipolowe chachikulu pa dziko lonselo; ndipo anthu amene adakhulupilira adayamba kukhala ndi chisoni chachikulu, kuti kapena zinthu zimene zidanenedwa zitha kukhala osachitika.

8 Koma taonani, iwo adayang’anira mokhazikika kwa usana ndi usiku umenewo pa tsikulo lomwe lidzakhala ngati tsiku limodzi ngati kuti padalibe usiku, kuti adziwe kuti chikhulupiliro chawo sichidapite pachabe.

9 Tsopano zidachitika kuti padali tsiku lidapatulidwa ndi osakhulupilira, kuti onse amene adakhulupilira miyambo imeneyo adayenera aphedwe pokhapokha chizindikirocho chitachitika, chimene chidaperekedwa ndi Samueli mneneri.

10 Tsopano zidachitika kuti pamene Nefi, mwana wa Nefi, adaona kuipa kwa anthu ake, mtima wake udali wachisoni kwambiri.

11 Ndipo zidachitika kuti iye adapita ndipo adagwada pansi, ndipo adalilira mwamphamvu kwa Mulungu wake m’malo mwa anthu ake, inde, iwo amene adali pafupi kuwonongedwa chifukwa cha chikhulupiliro chawo mu miyambo ya makolo awo.

12 Ndipo zidachitika kuti adafuulira kwa Ambuye mwamphamvu tsiku lonselo; ndipo taonani, mawu a Ambuye adadza kwa iye, nati:

13 Kweza mutu wako ndipo khala okondwa; pakuti taona, nthawi yayandikira, ndipo pa usiku uno chizindikiro chikhala chaperekedwa, ndipo m’mawa ndibwera ku dziko lapansi, kuti ndidzaonetse ku dziko lapansi kuti ndidzakwaniritsa zonse zimene ndachititsa kuti zinenedwe m’kamwa mwa aneneri anga woyera.

14 Taona, ndibwera kwa anga, kudzakwaniritsa zonse zimene ndadziwitsa kwa ana a anthu kuyambira kumaziko a dziko lapansi, ndi kuchita chifuniro cha onse Atate ndi Mwana—cha Atate chifukwa cha ine, ndi cha Mwana chifukwa cha thupi langa. Ndipo taona, nthawi yayandikira, ndipo usiku uno chizindikiro chidzaperekedwa.

15 Ndipo zidachitika kuti mawu amene adadza kwa Nefi adakwaniritsidwa, molingana ndi momwe adayankhulidwira; pakuti taonani, pakulowa kwa dzuwa kudalibe mdima; ndipo anthu adayamba kudabwa chifukwa kudalibe mdima pamene udafika usiku.

16 Ndipo padali ambiri, amene sadakhulupilire mawu a aneneri, amene adagwa pansi ndipo adakhala ngati kuti adali akufa, pakuti iwo adadziwa kuti dongosolo lalikulu la chiwonongeko limene iwo adaikira iwo amene adakhulupilira m’mawu a aneneri lidali litasokonezedwa; pakuti chizindikiro chimene chidapatsidwa chidali pafupi.

17 Ndipo adayamba kudziwa kuti Mwana wa Mulungu akuyenera kuonekera posachedwa; inde, mwachidule, anthu onse pa nkhope ya dziko lonse lapansi, kuyambira kumadzulo kufikira kum’mawa; onse m’dziko la kumpoto ndi m’dziko la kumwera, adali ozizwa mopambana kotero kuti adagwa pansi.

18 Pakuti adadziwa kuti aneneri adachitira umboni za zinthu izi kwa dzaka zambiri, ndipo kuti chizindikiro chimene chidaperekedwa chidali pafupi; ndipo adachita mantha chifukwa cha mphulupulu zawo ndi kusakhulupilira kwawo.

19 Ndipo zidachitika kuti kudalibe mdima usiku onsewo, koma kudawala ngati usana. Ndipo zidachitika kuti dzuwa lidatulukanso mam’mawa, monga mwa dongosolo lake; ndipo adadziwa kuti ndilo tsiku limene Ambuye akuyenera kubadwa, chifukwa cha chizindikiro chimene chidaperekedwa.

20 Ndipo izo zidachitika, inde, zinthu zonse, gawo lirilonse, monga mwa mawu a aneneri.

21 Ndipo zidachitikanso kuti nyenyezi yatsopano idaonekera, monga mwa mawuwo.

22 Ndipo zidachitika kuti kuyambira nthawi imeneyi kudayamba kukhala mabodza otumizidwa pakati pa anthu, ndi Satana, kuti aumitse mitima yawo, ndi cholinga chokuti asakhulupilire zizindikiro ndi zodabwitsa zomwe adaziona; koma pakusatengera mabodza ndi chinyengo ichi gawo lochuluka la anthu lidakhulupilira, ndipo lidatembenukira kwa Ambuye.

23 Ndipo zidachitika kuti Nefi adapita pakati pa anthu, ndiponso enanso ambiri, akuwabatiza ku kulapa, m’mene mudali chikhululukiro chachikulu cha machimo. Ndipo motero anthu adayambanso kukhala ndi mtendere m’dzikomo.

24 Ndipo padalibe mikangano, kupatula padali ochepa amene adayamba kulalikira, kuyesera kutsimikizira mwa malembo woyera kuti sikudali koyeneranso kusunga chilamulo cha Mose. Tsopano mu chinthu ichi adalakwitsa, popeza sadamvetse malemba woyera.

25 Koma zidachitika kuti posakhalitsa adakhala otembenuka, ndipo adakhutitsidwa mu kulakwa kumene iwo adalimo, pakuti kudadziwika kwa iwo kuti lamulo lidali lisadakwaniritsidwebe, ndipo kuti likuyenera kukwaniritsidwa mu kachigawo kalikonse; inde, mawu adadza kwa iwo kuti likuyenera kukwaniritsidwa; inde, kuti kalemba olo kamodzi kapena kadontho kamalemba kalikonse kasapite kufikira zonse zitakwaniritsidwa; kotero m’chaka chomwecho iwo adabweretsedwa ku chidziwitso cha kulakwa kwawo ndipo adavomereza zolakwa zawo.

26 Ndipo motero chaka cha makumi asanu ndi anayi mphambu ziwiri chidapita, ndikubweretsa uthenga wabwino kwa anthu chifukwa cha zizindikiro zomwe zidachitika, monga mwa mawu a uneneri wa aneneri onse woyera.

27 Ndipo zidachitika kuti chaka cha makumi asanu ndi anayi ndi zitatu chidapitanso mumtendere, kupatula iwo achifwamba a Gadiyantoni, amene adakhala pa mapiri, amene adawononga dziko; pakuti malo awo okhalamo ndi malo awo obisika adali amphamvu kwambiri kotero kuti anthu sadathe kuwagonjetsa; kotero iwo adapha kwambiri, ndipo adachita kupha kochuluka pakati pa anthu.

28 Ndipo zidachitika kuti mu chaka cha makumi asanu ndi anayi ndi chinayi adayamba kuwonjezeka mu mlingo waukulu, chifukwa padali opanduka ambiri a Anefi omwe adathawira kwa iwo, chimene chidachititsa chisoni chachikulu kwa Anefi awo amene adatsala m’dzikomo.

29 Ndipo kudalinso chochititsa chisoni chachikulu pakati pa Alamani; pakuti taonani, adali ndi ana ambiri amene adakula, ndikuyamba kukula kukhala amphamvu mdzaka, kuti iwo adakhala mwaokha; ndipo adatsogozedwa ndi ena amene adali Azoramu, ndi mabodza awo ndi mawu awo osyasyalika, kuti agwirizane ndi achifwamba a Gadiyantoni aja.

30 Ndipo motero Alamani adasautsidwanso, ndipo adayamba kuchepa ku chikhulupiliro ndi chilungamo chawo, chifukwa cha kuipa kwa m’badwo wachinyamatawa.

Print