Malembo Oyera
3 Nefi 4


Mutu 4

Ankhondo a Nefi agonjetsa achifwamba a Gadiyantoni—Gidiyani aphedwa, ndipo mlowa m’malo wake; Zemunariha, apachikidwa—Anefi atamanda Ambuye chifukwa cha zipambano zawo. Mdzaka dza pafupifupi Yesu atabadwa 19–22.

1 Ndipo zidachitika kuti chakumapeto kwa chaka chakhumi ndi chachisanu ndi chitatu magulu ankhondo a achifwamba adali atakonzekera kumenya nkhondo, ndipo adayamba kutsika ndi kuyenda kuchokera kudzitunda, ndi kuchokera kumapiri, ndi kuchipululu, ndi kumalinga awo, ndi kumalo awo obisika, ndipo adayamba kutenga maiko, onse amene adali m’dziko lakummwera ndi amene adali m’dziko la kumpoto, ndipo adayamba kutenga maiko onse amene adali atasiyidwa ndi Anefi, ndi mizinda imene idasiyidwa yapululu.

2 Koma taonani, mudalibe zilombo zakuthengo kapena nyama zoweta m’maiko amenewo amene adali atasiyidwa ndi Anefi, ndipo mudalibe nyama iliyonse ya achifwambawa kupatula m’chipululu.

3 Ndipo achifwambawo sakadakhalamo kupatula m’chipululu chifukwa chakusowa chakudya; pakuti Anefi adali atasiya maiko awo pululu, ndipo adasonkhanitsa nkhosa zawo, ndi ng’ombe zawo, ndi chuma chawo chonse, ndikukakhala m’gulu limodzi.

4 Kotero, padalibe mwayi wa achifwambawa kuti akafunkhe ndi kupeza chakudya; kupatulapo kuti abwere ku nkhondo yapoyera kumenyana ndi Anefi; ndipo Anefi pokhala mu gulu limodzi, ndi pokhala ndi chiwerengero chachikulu chotero, ndipo pokhala atadzisungira iwo eni zakudya, ndi akavalo ndi ng’ombe, ndi zoweta za mtundu uliwonse, kuti athe kukhala ndi moyo kwa nthawi ya dzaka zisanu ndi ziwiri, m’nthawi imene iwo adayembekezera kuwononga achifwambawo kuchoka pa nkhope ya dzikolo; ndipo kotero chaka chakhumi ndi zisanu ndi zitatu chidatha.

5 Ndipo zidachitika kuti mu chaka chakhumi ndi zisanu ndi zinayi Gidiyani adaona kuti kudali koyenera kuti apite kukamenyana ndi Anefi, pakuti padalibe njira yoti akadatha kukhala ndi moyo kupatulapo kufunkha ndi kuba ndi kupha.

6 Ndipo sadayerekeze kudzifalitsa pa nkhope ya dziko kotero kuti akadatha kulima mbewu, kuopa kuti Anefi angabwere pa iwo ndi kuwapha; kotero Gidiyani adapereka lamulo kwa ankhondo ake kuti m’chaka chimenecho akuyenera kupita kukamenyana ndi Anefi.

7 Ndipo zidachitika kuti iwo adabweradi kunkhondo; ndipo udali mwezi wachisanu ndi chimodzi; ndipo taonani, lalikulu ndi loopsya lidali tsiku limene iwo adabwera kudzamenya nkhondo; ndipo adadzimangilira m’chiuno mwa machitidwe a achifwamba; ndipo adali ndi chikopa cha nkhosa m’chiuno mwawo, ndipo adapakidwa ndi mwazi, ndipo adametedwa mitu yawo, ndipo adali ndi zophimba pamutu; ndipo maonekedwe a ankhondo a Gidiyani adali aakulu ndi oopsa, chifukwa cha zida zawo, ndi chifukwa cha kudzipaka kwawo kwa mwazi.

8 Ndipo zidachitika kuti ankhondo a Anefi, pamene adaona kufika kwa gulu lankhondo la Gidiyani, onse adali atagwada pansi, ndipo adakweza kulira kwawo kwa Ambuye Mulungu wawo, kuti awapulumutse ndi kuwawombola iwo kuchokera m’manja mwa adani awo.

9 Ndipo zidachitika kuti pamene magulu ankhondo a Gidiyani adaona izi adayamba kufuula ndi mawu okweza, chifukwa cha chisangalalo chawo, pakuti adaganiza kuti Anefi adagwa ndi mantha chifukwa cha kuopsa kwa ankhondo awo.

10 Koma mu chinthu ichi iwo adakhumudwa, pakuti Anefi sadawaope; Koma adaopa Mulungu wawo ndipo adamupempha chitetezo; kotero, pamene ankhondo a Gidiyani adawathamangira iwo adali okonzeka kukumana nawo; inde, mu mphamvu ya Ambuye adawalandiradi.

11 Ndipo nkhondo idayamba mwezi wachisanu ndi chimodzi womwewo; ndipo nkhondo yakeyo idali yaikulu ndi yoopsya, inde, kuphana kwake kudali kwakukulu ndi koopsya, kotero kuti sikudadziwike konse kuphana kwakukulu koteroko pakati pa anthu onse a Lehi kuyambira pamene adachoka ku Yerusalemu.

12 Ndipo osatengera ziopsezo ndi malumbiro amene Gidiyani adapanga, taonani, Anefi adawamenya iwo, kotero kuti adabwelera m’mbuyo kuchokera pamaso pawo.

13 Ndipo zidachitika kuti Gidigidoni adawalamula ankhondo ake kuti akuyenera kuwathamangitsa mpaka kumalire a chipululu, ndi kuti asasiye aliyense wakugwa m’manja mwawo munjira; ndipo motero adawalondola, ndikuwapha; mpaka kumalire a chipululu, kufikira atakwaniritsa lamulo la Gidigidoni.

14 Ndipo zidachitika kuti Gidiyani, amene adaima ndi kumenya nkhondo molimba mtima, adatsatiridwa pamene ankathawa; ndipo pokhala otopa chifukwa cha ndewu yake yaikulu adagwidwa ndikuphedwa. Ndipo awa adali mathero a Gidiyani wachifwamba.

15 Ndipo zidachitika kuti ankhondo a Anefi adabweleranso kumalo awo achitetezo. Ndipo zidachitika kuti chaka chakhumi ndi zisanu ndi chinayichi chidapita, ndipo achifwamba sadabwerenso kunkhondo; ndipo sadabwerenso m’chaka cha makumi awiri.

16 Ndipo m’chaka cha makumi awiri ndi chimodzi iwo sadabwere kudzamenya nkhondo, koma adadza m’mbali zonse kuti awazinge mozungulira anthu a Nefi; pakuti adayesa kuti ngati atha kuwadula anthu a Nefi kuchokera m’maiko awo, ndi kuwatsekereza iwo m’mbali zonse, ndipo ngati angawadule kuchokera ku zinthu zawo zonse zakunja, kuti angawapangitse iwo kudzipereka iwo eni monga momwe akufunira.

17 Tsopano iwo adadzisankhira iwo eni mtsogoleri wina, amene dzina lake adali Zemunariha; kotero adali Zemunariha amene adachititsa kuti kuzingidwa uku kuchitike.

18 Koma taonani, uwu udali mwayi kwa Anefi; pakuti kudali kosatheka kuti achifwambawa awazinge kwa nthawi yokwanira kuti achitepo kanthu pa Anefi, chifukwa cha chakudya chawo chochuluka chomwe adachisunga,

19 Ndipo chifukwa chakuchepa kwa chakudya cha achifwambawo; pakuti taonani, iwo adalibe kalikonse kupatula nyama kuti akhale ndi moyo, nyama imene iwo adaipeza mu chipululu;

20 Ndipo zidachitika kuti nyama zakuthengo zidasowa m’chipululu moti achifwambawo adatsala pang’ono kufa ndi njala.

21 Ndipo Anefi adali akuguba mosalekeza usana ndi usiku, ndikuwakantha pa ankhondo awo, ndi kuwawononga zikwi ndi makumi azikwi.

22 Ndipo kotero chidakhala chokhumba cha anthu a Zemunariha kuti asiye zimene amachita, chifukwa cha chiwonongeko chachikulu chimene chidawagwera usiku ndi usana.

23 Ndipo zidachitika kuti Zemunariha adapereka lamulo kwa anthu ake kuti achoke mu kuzingako, ndi kugubira ku madera akutali a dziko la kumpoto.

24 Ndipo tsopano, Gidigidoni podziwa zomwe iwo amapanga, ndi kudziwa za kufooka kwawo chifukwa cha kusowa chakudya, ndi kupha kwakukulu kumene kudachitika pakati pawo adatumiza ankhondo ake mu nthawi ya usiku, ndipo adadula njira yawo yothawira, ndipo adaika magulu ankhondo ake m’njira yothawira yawo.

25 Ndipo izi adachita mu nthawi ya usiku, ndipo adayenda ulendo wawo kupitilira achifwambawo, kotero kuti m’mawa mwake, pamene achifwambawo adayamba ulendo wawo, adakumana ndi magulu ankhondo a Anefi konse kutsogolo kwawo ndi kumbuyo kwawo.

26 Ndipo achifwamba omwe adali kummwera adadulidwanso m’malo awo othawirako. Ndipo zinthu zonsezi zidachitika mwa lamulo la Gidigidoni.

27 Ndipo adalipo zikwi zambiri amene adadzipereka okha ukaidi kwa Anefi, ndipo otsala a iwo adaphedwa.

28 Ndipo mtsogoleri wawo, Zemunariha, adatengedwa ndikupachikidwa pamtengo, inde, ngakhale pamwamba pake mpaka adamwalira. Ndipo pamene adampachika iye kufikira atamwalira, iwo adagwetsa pansi pamtengowo, ndipo adafuula ndi mawu aakulu, kuti:

29 Ambuye asunge anthu ake m’chilungamo ndi m’chiyero cha mtima, kuti iwo akathe kuchititsa kugwa pansi onse amene atadzafune kuwapha chifukwa cha mphamvu ndi magulu achinsinsi, ngakhale chimodzimodzi munthu uyu wagwera pansi.

30 Ndipo iwo adasangalala ndi kufuula ndi mawu amodzi, nati, Mulungu wa Abrahamu, ndi Mulungu wa Isake, ndi Mulungu wa Yakobo, ateteze anthu awa m’chilungamo, nthawi yonse imene adzaitanira pa dzina la Mulungu wawo kuti awateteze.

31 Ndipo zidachitika kuti iwo adatuluka, onse pamodzi, mu kuyimba, ndi kutamanda Mulungu wawo chifukwa cha chinthu chachikulu chimene adawachitira, powateteza kuti asagwere m’manja mwa adani awo.

32 Inde, adafuula: Hosana kwa Mulungu Wam’mwambamwamba. Ndipo iwo adafuula nati: Lidalitsike dzina la Ambuye Mulungu Wamphamvu zonse, Mulungu Wam’mwambamwamba.

33 Ndipo mitima yawo idadzadzidwa ndi chisangalalo, mpaka kukhetsa misozi yambiri, chifuka cha ubwino waukulu wa Mulungu m’kuwombola iwo kuchoka m’manja mwa adani awo; ndipo iwo adadziwa kuti chidali chifukwa cha kulapa kwawo ndi kudzichepetsa kwawo kuti iwo adawomboledwa kuchokera ku chiwonongeko chosatha.

Print