Malembo Oyera
3 Nefi 11


Yesu Khristu adadzionetsera yekha kwa anthu a Nefi pamene khamu lidasonkhana pamodzi m’dziko la Chuluka, ndipo adatumikira kwa iwo; ndipo moteremu adadzionetsera yekha kwa iwo.

Kuyambira ndi mutu 11.

Mutu 11

Atate achitira umboni za Mwana wawo Wokondedwa—Khristu aonekera ndi kulengeza Chitetezero chake—Anthu agwira zipsera m’manja mwake ndi m’mapazi ndi mthiti mwake—Iwo afuula Hosana—Iye akhazikitsa njira ndi kachitidwe ka ubatizo—Mzimu wa mkangano ndi wa mdyerekezi—Chiphunzitso cha Khristu ndi chakuti anthu akuyenera kukhulupilira ndi kubatizidwa ndi kulandira Mzimu Woyera. Mdzaka dza pafupifupi Yesu atabadwa 34.

1 Ndipo tsopano zidachitika kuti kudali khamu lalikulu losonkhana pamodzi, la anthu a Nefi, mozungulira kachisi amene adali m’dziko la Chuluka; ndipo adazizwa, ndi kudabwa wina ndi mzake, ndipo adaonetsana wina ndi mzake kusintha kwakukulu ndi kodabwitsa kumene kudachitika.

2 Ndipo adali kukambirana za Yesu Khristu ameneyu, amene chizindikiro chokhudzana ndi imfa yake chidaperekedwa.

3 Ndipo zidachitika kuti pamene iwo adali kuyankhulana wina ndi mzake, iwo adamva mawu ngati kuti akuchokera kumwamba; ndipo iwo adaponya maso awo mozungulira, pakuti sadamvetse mawu amene adawamva; ndipo sadali mawu aukali, kapena mawu aakulu; komabe, ndipo posatengera iwo pokhala mawu aang’ono adapyoza iwo omwe adawamva mpaka mkati, kotero kuti padalibe gawo la thupi lawo limene sadawachititse kugwedezeka; inde, iwo adawapyoza mpaka kumoyo, ndi kuwatenthetsa mitima yawo.

4 Ndipo zidachitika kuti adamvanso mawuwo, ndipo iwo sadawamvetsetse.

5 Ndiponso nthawi yachitatu iwo adamva mawuwo, ndipo adatsegula makutu awo kuti awamve; ndipo maso awo adayang’ana ku phokoso lake; ndipo iwo adayang’ana mokhazikika patsogolo Kumwamba, kumene mawuwo adachokera.

6 Ndipo taonani, kachitatu adamvetsetsa mawu amene adamvawo; ndipo adati kwa iwo;

7 Taonani Mwana wanga Wokondedwa, mwa iye ndikondwera, mwa iye ndalemekeza dzina langa, mverani iye.

8 Ndipo zidachitika, pamene adamvetsetsa iwo adaponyanso maso awo kumwamba; ndipo taonani, adaona Munthu akutsika kuchokera kumwamba; ndipo adavala mwinjiro woyera; ndipo iye adatsika ndi kuima pakati pawo; ndipo maso a khamu lonse adatembenukira pa iye, ndipo sadayerekeze kutsegula pakamwa pawo, ngakhale wina ndi mzake, ndipo sadadziwe chomwe chimatanthauza, pakuti adayesa kuti adali mngelo amene adaonekera kwa iwo.

9 Ndipo zidachitika kuti iye adatambasula dzanja lake ndipo adayankhula kwa anthu, kuti:

10 Taonani, ndine Yesu Khristu, amene aneneri adamuchitira umboni, adzabwera ku dziko lapansi.

11 Ndipo taonani, ine ndine kuunika ndi moyo wa dziko lapansi; ndipo ndidamwa kuchokera ku chikho chowawa chimene Atate andipatsa ine; ndalemekeza Atate potenga pa ine machimo adziko lapansi, m’mene ndidalolera chifuniro cha Atate m’zinthu zonse kuyambira pa chiyambi.

12 Ndipo zidachitika kuti pamene Yesu adanena mawu awa, khamu lonse lidagwa pansi; pakuti iwo adakumbukira kuti kudaloseredwa pakati pawo kuti Khristu adzadzionetsera yekha kwa iwo atakwera kumwamba.

13 Ndipo zidachitika kuti Ambuye adayankhula kwa iwo kuti:

14 Nyamukani ndipo idzani kwa ine, kuti muike manja anu m’nthiti mwanga, ndiponso kuti mumve zipsera za misomali m’manja mwanga ndi m’mapazi anga, kuti mudziwe kuti ine ndine Mulungu wa Israeli, ndi Mulungu wa dziko lonse lapansi, ndipo ndidaphedwa chifukwa cha machimo adziko lapansi.

15 Ndipo zidachitika kuti khamulo lidapita, ndipo lidayika manja awo m’nthiti mwake, ndikukhudza zipsera za misomali m’manja mwake ndi m’mapazi ake; ndipo izo iwo adachita, akupita patsogolo m’modzim’modzi mpaka onse adapita, ndipo adaona ndi maso awo, ndikukhudza ndi manja awo, ndipo adadziwa ndithu, ndipo adachitira umboni, kuti adali iye amene adalembedwa ndi aneneri, amene akuyenera kudzabwera.

16 Ndipo pamene iwo onse adapita ndi kuchitira paokha umboni, iwo adafuula ndi mtima umodzi, kuti:

17 Hosana! Lidalitsike dzina la Mulungu Wam’mwambamwamba! Ndipo adagwa pa mapazi a Yesu, ndipo adamulambira.

18 Ndipo zidachitika kuti adayankhula kwa Nefi (pakuti Nefi adali pakati pa khamulo) ndipo adamulamulira iye kuti abwere.

19 Ndipo Nefi adadzuka ndikupita, ndikugwada pamaso pa Ambuye, ndikumumpsompsona mapazi ake.

20 Ndipo Ambuye adamulamura kuti iye amuke. Ndipo adanyamuka, ndikuima pamaso pake.

21 Ndipo Ambuye adati kwa iye: ine ndikukupatsa iwe mphamvu kuti udzabatiza anthu awa pamene ine ndikweranso kumwamba.

22 Ndipo Ambuye adaitananso ena, ndikunena kwa iwo momwemonso; ndipo adawapatsa mphamvu yakubatiza. Ndipo iye adati kwa iwo: Munjira iyi mudzabatiza inu; ndipo pasakhale mikangano pakati panu.

23 Indetu ndikunena kwa inu, kuti amene walapa machimo ake kudzera m’mawu anu, ndi kufuna kubatizidwa m’dzina langa, m’njira iyi mudzawabatiza iwo—Taonani, mudzapita ndi kuima m’madzi, ndipo m’dzina langa inu mudzawabatiza iwo.

24 Ndipo tsopano taonani, awa ndi mawu amene mudzanene, kuwatchula iwo mayina awo, kuti:

25 Pokhala nawo ulamuliro wopatsidwa kwa ine wa Yesu Khristu, ine ndikukubatiza iwe mu dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera. Ameni.

26 Ndipo pamenepo mudzawamiza iwo m’madzi, ndi kuwatulutsanso m’madzi.

27 Ndipo munjira yotere mudzabatiza m’dzina langa; pakuti taonani, indetu ndikunena kwa inu, kuti Atate, ndi Mwana, ndi Mzimu Woyera ali amodzi; ndipo ine ndili mwa Atate, ndipo Atate ali mwa ine, ndipo Atate ndi ine tili amodzi.

28 Ndipo monga momwe ine ndakulamulirani inu motero inu mudzabatiza. Ndipo sipadzakhala mikangano pakati panu, monga yakhala ikuchitika mpaka pano; kapena sipadzakhala mikangano pakati panu zokhudzana ndi mfundo za chiphunzitso changa, monga zakhala zikuchitika mpaka pano.

29 Pakuti indetu, indetu ndikunena kwa inu, iye amene ali ndi mzimu wa mkangano sali wa ine, koma ali wa mdyerekezi, amene ali tate wa mikangano, ndipo amautsa mitima ya anthu m’kukangana ndi mkwiyo, wina ndi mzake.

30 Taonani, ichi sichili chiphunzitso changa, cha kuutsa mitima ya anthu ndi mkwiyo, wina ndi mnzake; koma ichi ndi chiphunzitso changa, kuti zinthu zotere zikuyenera kuthetsedwa.

31 Taonani, indetu, indetu, ndikunena kwa inu, ndilalikira kwa inu chiphunzitso changa.

32 Ndipo ichi ndi chiphunzitso changa, ndipo chili chiphunzitso chimene Atate adapereka kwa ine; ndipo ine ndimachitira umboni wa Atate, ndipo Atate amachitira umboni wa ine, ndipo Mzimu Woyera umachitira umboni wa Atate ndi ine; ndipo ine ndikuchitira umboni kuti Atate amalamulira anthu onse, kulikonse, kuti alape ndi kukhulupilira mwa ine.

33 Ndipo amene akhulupilira mwa ine, ndikubatizidwa, yemweyo adzapulumutsidwa; ndipo iwo ndiwo amene adzalandira Ufumu wa Mulungu.

34 Ndipo amene sakhulupilira mwa ine, ndipo sadabatizidwe, adzatembeleredwa.

35 Indetu, indetu, ndikunena kwa inu, kuti ichi ndi chiphunzitso changa, ndipo ndikuchitira umboni za icho kuchokera kwa Atate; ndipo iye amene akhulupilira mwa ine akhulupiliranso mwa Atate; ndipo kwa iye Atate adzachitira umboni wa ine, pakuti iye adzamuyendera iye ndi moto ndi Mzimu Woyera.

36 Ndipo motero Atate adzachitira umboni za ine, ndipo Mzimu Woyera udzachitira umboni kwa iye wa Atate ndi ine; pakuti Atate, ndi ine, ndi Mzimu Woyera ndife amodzi.

37 Ndipo ndikunenanso kwa inu, mukuyenera kulapa, ndi kukhala monga mwana wamng’ono, ndi kubatizidwa m’dzina langa, kupanda apo simungathe munjira iliyonse kulandira zinthu izi.

38 Ndipo ndikunenanso kwa inu, mukuyenera kulapa, ndi kubatizidwa m’dzina langa, ndi kukhala monga mwana wamng’ono, kupanda apo simungalandire munjira iliyonse ufumu wa Mulungu.

39 Indetu, indetu, ndikunena kwa inu, kuti ichi ndi chiphunzitso changa, ndipo amene amanga pa ichi amanga pa thanthwe langa, ndipo zipata za gahena sizidzawagonjetsa iwo.

40 Ndipo amene adzalalikira mochuluka kapena mochepera kuposa izi, ndi kuchikhazikitsa icho kukhala chiphunzitso changa, chomwechi chikudza mwa oipa, ndipo sichidamangidwe pa thanthwe langa; koma amanga pa maziko amchenga, ndipo zipata za gahena ziyima zotseguka kuti zilandire otere pamene madzi osefukira adzabwera ndi mphepo zikawomba pa iwo.

41 Kotero, pitani kwa anthu awa, ndipo lengezani mawu amene ndayankhula, ku malekezero a dziko lapansi.